Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Okalamba ndi Ofunika Kwambiri pa Ubale Wathu Wachikristu

Okalamba ndi Ofunika Kwambiri pa Ubale Wathu Wachikristu

 Okalamba ndi Ofunika Kwambiri pa Ubale Wathu Wachikristu

“Iwo owokedwa m’nyumba ya Yehova, adzaphuka . . . Atakalamba adzapatsanso zipatso.”​—SALMO 92:13, 14.

1. Kodi ambiri amawaona motani anthu okalamba?

YEHOVA amakonda atumiki ake onse okhulupirika, kuphatikizapo okalamba. Koma malinga ndi zimene ena ananena, chaka chilichonse anthu okalamba pafupifupi 500,000 ku United States amavutitsidwa kapena kunyalanyazidwa. Malipoti ofanana ndi lipoti limeneli ochokera padziko lonse akusonyeza kuti kuvutitsa anthu okalamba kukuchitika padziko lonse. Chimene chikuchititsa zimenezi ndi zimene bungwe lina linatchula kuti “maganizo ofala a anthu ambiri . . . akuti anthu okalamba ndi otha ntchito, alibe phindu, ndipo amadalira kwambiri anthu ena.”

2. (a) Kodi Yehova amaona motani atumiki ake okhulupirika okalamba? (b) Kodi ndi mawu olimbikitsa otani amene timawapeza pa Salmo 92:12-15?

2 Yehova Mulungu amaona kuti atumiki ake okhulupirika okalamba ndi ofunika kwambiri. Iye amaona kwambiri ‘umunthu wam’kati mwathu,’ kutanthauza mmene moyo wathu wauzimu ulili, osati kufooka kwa thupi lathu. (2 Akorinto 4:16) Mawu ake, Baibulo, amatitsimikizira zinthu zolimbikitsa kwambiri zotsatirazi: “Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebano. Iwo owokedwa m’nyumba ya Yehova, adzaphuka m’mabwalo a Mulungu wathu. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriŵiri: Kulalikira kuti Yehova n’ngolunjika.” (Salmo 92:12-15) Kupenda mavesi ameneŵa kutisonyeza zinthu zina zofunika kwambiri zimene okalambanu mungachite pa ubale wathu wachikristu.

‘Kupatsa Zipatso Atakalamba’

3. (a) N’chifukwa chiyani olungama akuyerekezedwa ndi migwalangwa? (b) Kodi n’chiyani chingathandize okalamba ‘kupatsa zipatso atakalamba’?

3 Wamasalmo anayerekezera olungama ndi migwalangwa ‘yowokedwa m’mabwalo a Mulungu wathu.’ Iwo amapitiriza ‘kupatsa zipatso atakalamba.’ Kodi simukuvomereza kuti imeneyi ndi mfundo yolimbikitsa? M’mabwalo a nyumba za panthaŵiyo za ku mayiko otchulidwa m’Baibulo, sizinali zachilendo kupeza migwalangwa yokongola ndi yowongoka bwino. Kuwonjezera pa kukongoletsa malo, anthu ankaonanso kuti migwalangwa ndi yofunika kwambiri chifukwa chakuti imabala kwambiri, ndipo ina imakhala ikubala kwa zaka zoposa 100. * Mwa kupitiriza kukhala okhazikika pa kulambira koona, nanunso mungapitirize  “kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino.”​—Akolose 1:10.

4, 5. (a) Kodi ndi chipatso chofunika chiti chimene Akristu afunika kubala? (b) Perekani zitsanzo za m’Malemba za anthu okalamba amene anabala “chipatso cha milomo.”

4 Yehova amafuna kuti Akristu abale “chipatso cha milomo,” chimene ndi mawu oyamikira Iye ndi zolinga zake. (Ahebri 13:15) Kodi zimenezi zikukukhudzani inu monga munthu wokalamba? Inde, zikukukhudzani.

5 Baibulo lili ndi zitsanzo za anthu okalamba amene analalikira mopanda mantha dzina ndiponso zolinga za Yehova. Mose anali atapitirira “zaka makumi asanu ndi aŵiri” pamene Yehova anamutuma kuti akhale mneneri ndiponso womuimira. (Salmo 90:10; Eksodo 4:10-17) Ukalamba sunalepheretse mneneri Danieli kulalikira molimba mtima za ufulu wa kulamulira wa Yehova. Mwachionekere Danieli anali atapitirira zaka 90 pamene Belisazara anamuitanitsa kuti amasulire zilembo zosadziŵika zimene zinalembedwa pakhoma. (Danieli, chaputala 5) Nanga bwanji za mtumwi wokalamba Yohane? Chakumapeto kwa ntchito imene anakhala akuigwira kwa nthaŵi yaitali, mtumwiyu anatumizidwa kundende pachisumbu cha Patmo “chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 1:9) Mosakayikira, mungathe kukumbukira anthu ena ambiri otchulidwa m’Baibulo amene anabala “chipatso cha milomo” paukalamba wawo.​—1 Samueli 8:1, 10; 12:2; 1 Mafumu 14:4, 5; Luka 1:7, 67-79; 2:22-32.

6. Kodi Yehova wagwiritsa ntchito motani okalamba kuti alosere m’masiku otsiriza ano?

6 Pogwira mawu a mneneri wachihebri Yoweli, mtumwi Petro anati: “Kudzali m’masiku otsiriza, anena Mulungu, Ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse [kuphatikizapo ‘akulu,’ kapena kuti okalamba], ndipo . . . adzanenera.” (Machitidwe 2:17, 18; Yoweli 2:28) Mogwirizana ndi zimenezi, m’masiku otsiriza ano Yehova wagwiritsa ntchito anthu okalamba a kagulu ka odzozedwa ndiponso a “nkhosa zina” kulengeza zolinga zake. (Yohane 10:16) Ena mwa anthu ameneŵa akhala akubala zipatso za Ufumu mokhulupirika kwa zaka zambiri.

7. Fotokozani mmene okalamba akupitirizira kubala chipatso cha Ufumu ngakhale kuti matupi awo ndi ofooka.

7 Taganizirani za a Sonia, amene anakhala mlaliki wanthaŵi zonse wa Ufumu mu 1941. Ngakhale kuti anadwala matenda aakulu kwa nthaŵi yaitali, nthaŵi zonse anali kuchititsa maphunziro a Baibulo kunyumba kwawo. “Kulalikira uthenga wabwino ndi mbali ya moyo wanga,” anatero a Sonia. “Kwenikweni ndiwo moyo wanga. Sindifuna kusiya kulalikira.” Posachedwapa, a Sonia ndi akulu awo, a Olive, anafotokoza uthenga wopatsa chiyembekezo wa m’Baibulo kwa Janet, amene anakumana naye kuchipatala m’chipinda choyembekezera kulandira chithandizo ndipo anali kudwala kwambiri. Amayi ake a Janet, omwe ndi Mkatolika wodzipereka, anachita chidwi ndi chikondi choterechi moti anavomera phunziro la Baibulo lapanyumba ndipo pano akupita patsogolo kwambiri. Kodi nanunso mungagwiritse ntchito mipata yoteroyo kuti mubale chipatso cha Ufumu?

8. Kodi Kalebe wokalamba anasonyeza motani kukhulupirira kwake Yehova, ndipo Akristu okalamba angatengere motani chitsanzo chake?

8 Mwa kupitiriza molimba mtima kugwira ntchito yolalikira za Ufumu ngakhale kuti pali zinthu zomwe sangachite chifukwa cha ukalamba, Akristu okalamba akutsatira mapazi a Mwisrayeli wokhulupirika Kalebe, amene anatsagana ndi Mose m’chipululu kwa zaka makumi anayi.  Kalebe anali ndi zaka 79 pamene anawoloka mtsinje wa Yordano kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Atakhala zaka zisanu ndi chimodzi monga msilikali wa gulu lankhondo la Israyeli limene linkagonjetsa mitundu ina, iye akanatha kukhutitsidwa ndi zimenezo n’kumangokhala. Koma sanatero. Iye anapempha molimba mtima kuti agwire ntchito yovuta yolanda “midzi yaikulu ndi yamalinga” m’chigawo chamapiri cha dziko la Yuda. Aanaki, omwe anali anthu akuluakulu misinkhu, ndiwo ankakhala m’derali. Mothandizidwa ndi Yehova, Kalebe ‘anawaingitsadi monga ananena Yehova.’ (Yoswa 14:9-14; 15:13, 14) Khalani ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ali nanu, monga mmene anachitira ndi Kalebe, pamene mukupitiriza kubala chipatso cha Ufumu mu ukalamba. Ndipo ngati mukhalabe wokhulupirika, iye adzakupatsani malo m’dziko lake latsopano lomwe walonjeza.​—Yesaya 40:29-31; 2 Petro 3:13.

“Adzadzazidwa ndi Madzi Nadzakhala Abiriŵiri”

9, 10. Kodi Akristu okalamba amatani kuti akhale olimba m’chikhulupiriro ndi kupitirizabe kukhala amphamvu mwauzimu? (Onani bokosi patsamba 13.)

9 Posonyeza mmene atumiki okalamba a Yehova amabalira zipatso, wamasalmo anaimba kuti: “Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebano. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriŵiri.”​—Salmo 92:12, 14.

10 Kodi mungatani kuti mukhalebe achangu pa zinthu zauzimu ngakhale kuti ndinu wokalamba? Chimene chimachititsa kuti mgwalangwa uzikhala wokongola nthaŵi zonse ndicho kukhala pamalo amadzi abwino nthaŵi zonse. N’chimodzimodzinso ndi inu. Mungapeze mphamvu m’madzi a choonadi a m’Baibulo mwa kuphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kusonkhana ndi gulu lake. (Salmo 1:1-3; Yeremiya 17:7, 8) Kulimba kwanu mwauzimu kumapangitsa kuti mukhale wofunika kwambiri kwa okhulupirira anzanu. Taonani umboni wa mfundoyi pa chitsanzo cha Mkulu wa Ansembe Yehoyada, amene anali wokalamba.

11, 12. (a) Kodi ndi zinthu zofunika zotani zimene Yehoyada anachita m’mbiri ya ufumu wa Yuda? (b) Kodi Yehoyada anagwiritsa ntchito motani mphamvu zake polimbikitsa kulambira koona?

11 Mwachionekere Yehoyada anali atapitirira zaka 100 pamene Mfumukazi Ataliya, imene inkafunitsitsa kukhala wolamulira, inatenga mphamvu zolamulira Yuda mwa kupha adzukulu ake. Kodi Yehoyada wokalambayo akanachita chiyani? Kwa zaka zisanu ndi chimodzi iye ndi mkazi wake anabisa Yoasi m’kachisi, yemwe anali mwana mmodzi yekha wa mbewu yachifumu amene anapulumuka. Kenako, mwadzidzidzi, Yehoyada analengeza kuti Yoasi amene anali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri ndi mfumu ndipo anakonza zoti Ataliya aphedwe.​—2 Mbiri 22:10-12; 23:1-3, 15, 21.

12 Monga munthu amene anali kusunga mfumuyi, Yehoyada anagwiritsa ntchito mphamvu zake polimbikitsa kulambira koona. “Anachita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova.” Atalamulidwa ndi Yehoyada, anthu anagwetsa nyumba ya mulungu wonama Baala ndi kuchotsa maguwa ake ansembe, mafano ake, ndiponso wansembe wake. Komanso anali malangizo a Yehoyada amene anachititsa Yoasi kubwezeretsa ntchito za pakachisi komanso kuchita ntchito zofunika kwambiri zokonzanso kachisi. “Yoasi anachita zowongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, mmene anam’langizira wansembe Yehoyada.” (2 Mbiri 23:11, 16-19; 24:11-14; 2 Mafumu 12:2) Atamwalira ali ndi zaka 130, Yehoyada anapatsidwa ulemu waukulu woikidwa m’manda a mafumu chifukwa “anachita zabwino m’Israyeli, ndi kwa Mulungu, ndi ku nyumba yake.”​—2 Mbiri 24:15, 16.

13. Kodi Akristu okalamba ‘angachitire zabwino Mulungu woona ndi nyumba yake’ motani?

13 N’kutheka kuti kufooka kwa thupi kapena zinthu zina zikukulepheretsani kuchita zambiri polimbikitsa kulambira koona. Komabe, ngakhale zili choncho, mungathe ‘kuchitira zabwino Mulungu ndi nyumba yake.’ Mungasonyeze changu panyumba yauzimu ya Yehova mwa kupezeka pamisonkhano ndi kutengamo mbali ndiponso mwa kuchita utumiki wa kumunda pamene mungathe kutero. Ubale wachikristu udzalimba chifukwa cha kulandira kwanu mosanyinyirika uphungu wa m’Baibulo ndiponso  kuthandiza kwanu mokhulupirika “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndiponso mpingo. (Mateyu 24:45-47) Komanso mungathe kufulumiza olambira anzanu ku “chikondano ndi ntchito zabwino.” (Ahebri 10:24, 25; Filemoni 8, 9) Ndipo ena adzapindula kwambiri ngati mutsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama [“olimba,” Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono] m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiriro. Momwemonso akazi okalamba akhale nawo makhalidwe oyenera anthu oyera, osadyerekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma.”​—Tito 2:2-4.

14. Kodi oyang’anira achikristu omwe atumikira kwa nthaŵi yaitali angatani polimbikitsa kulambira koona?

14 Kodi mwatumikira monga mkulu mu mpingo kwa zaka zambiri? Mwamuna wina amene watumikira kwa nthaŵi yaitali monga mkulu mumpingo anapereka malangizo otsatiraŵa: “Gwiritsani ntchito mopanda dyera nzeru zimene mwapeza chifukwa chokhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali. Muzigaŵirako ena zina mwa ntchito zanu, ndipo ena amene akufuna kuphunzira, muziwauzako zimene mukudziŵa . . . Muzitha kuzindikira luso limene ena ali nalo. Athandizeni kukulitsa luso limenelo. Muzikonzekera za m’tsogolo.” (Deuteronomo 3:27, 28) Chidwi chimene muli nacho pa ntchito ya Ufumu yomwe ikukula nthaŵi zonse chidzapindulitsa ena a abale athu achikristu.

‘Lalikirani Kuti Yehova N’ngolunjika’

15. Kodi Akristu okalamba ‘amalalikira motani kuti Yehova n’ngolunjika’?

15 Atumiki okalamba a Mulungu amachita mosangalala udindo wawo ‘wolalikira kuti Yehova n’ngolunjika.’ Ngati ndinu Mkristu wokalamba, zonena ndi zochita zanu zingasonyeze ena kuti ‘Yehova ndiye thanthwe lanu, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.’ (Salmo 92:15) Mgwalangwa umapereka mwakachetechete umboni wa makhalidwe apamwamba a Mlengi wake. Koma Yehova wapatsa inu mwayi wapadera wochitira umboni za iye kwa anthu amene panopo akuphunzira kulambira koona. (Deuteronomo 32:7; Salmo 71:17, 18; Yoweli 1:2, 3) N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

16. Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Baibulo chomwe chikusonyeza kufunika ‘kolalikira kuti Yehova n’ngolunjika’?

16 Pamene Yoswa, mtsogoleri wa Aisrayeli, “adakalamba nakhala wa zaka zambiri . . . anaitana  Aisrayeli onse, akuluakulu awo, ndi akulu awo, ndi oweruza awo, ndi akapitao awo,” ndi kuwakumbutsa zochita zolungama za Mulungu. Iye anati: “Pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu.” (Yoswa 23:1, 2, 14) Kwa kanthaŵi ndithu, mawu ameneŵa analimbikitsa anthuwo kufunitsitsa kukhalabe okhulupirika. Koma Yoswa atamwalira, ‘kunauka mbadwo wina . . . wosadziŵa Yehova kapena ntchitoyi adaichitira Israyeli. Ndipo ana a Israyeli anachita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala.’​—Oweruza 2:8-11.

17. Kodi Yehova wawachitira zotani anthu ake m’masiku athu ano?

17 Kukhulupirika kwa mpingo wachikristu wa masiku ano sikudalira pa umboni wapakamwa wochokera kwa atumiki okalamba a Mulungu. Komabe, kukhulupirira kwathu Yehova ndi malonjezo ake kumakula tikamva anthu akutiuza zimene iwo aona pa “ntchito yaikulu” imene iye wachitira anthu ake m’masiku otsiriza ano. (Oweruza 2:7; 2 Petro 1:16-19) Ngati mwakhala m’gulu la Yehova kwa zaka zambiri, mwina mukukumbukira nthaŵi yomwe m’dera kapena m’dziko mwanu munali olengeza Ufumu ochepa kapena pamene anthu ankatsutsa kwambiri ntchito yolalikira. M’kupita kwa nthaŵi, mwaona Yehova akuchotsa zopinga zina ndi ‘kufulumizitsa’ kuwonjezeka kwa ofalitsa. (Yesaya 54:17; 60:22) Mwaona choonadi cha Baibulo chikumveketsedwa bwino ndiponso kusintha kwa zinthu m’gulu looneka la Mulungu. (Miyambo 4:18; Yesaya 60:17) Kodi mumafuna kulimbikitsa ena mwa kuwafotokozera zomwe mwaona zokhudza zochita zolungama za Yehova? Zimenezi zingawalimbikitse kwambiri abale athu achikristu.

18. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti ‘kulalikira kwa ena kuti Yehova n’ngolunjika’ kumakhudza anthu kwa nthaŵi yaitali. (b) Kodi inu panokha mwaona motani kuti Yehova n’ngolunjika?

18 Bwanji za nthaŵi zomwe munaona kuti Yehova akukusamalirani bwino ndi kukutsogolerani m’moyo wanu? (Salmo 37:25; Mateyu 6:33; 1 Petro 5:7) Mlongo wina wokalamba, dzina lake Martha, ankalimbikitsa ena ndi mawu akuti: “Kaya pachitike zinthu zotani, osasiya Yehova. Adzakuthandizani.” Malangizo ameneŵa anawathandiza kwambiri a Tolmina, mmodzi wa anthu amene a Martha anaphunzira nawo Baibulo ndipo anabatizidwa chakumayambiriro kwa m’ma 1960. A Tolmina anati: “Mwamuna wanga atamwalira, zinandifoola kwambiri, koma mawu amenewo anandithandiza kuonetsetsa kuti ndisaphonye msonkhano ngakhale umodzi. Ndipo Yehova anandilimbikitsadi kuti ndipitirize.” Nthaŵi yonseyi a Tolmina akhalanso akupereka malangizo omweŵa kwa anthu ambiri amene aphunzira nawo Baibulo. Inde, mwa kulimbikitsa ena ndi kuwafotokozera zochita zolungama za Yehova, mungathandize kwambiri kulimbitsa chikhulupiriro cha okhulupirira anzanu.

 Yehova Amaona Kuti Okalamba Okhulupirika Ndi Amtengo Wapatali

19, 20. (a) Kodi Yehova amaona motani ntchito za atumiki ake okalamba? (b) Kodi nkhani yotsatirayi ifotokoza zotani?

19 Dziko lamasiku ano losayamikali siliganizira kwenikweni okalamba. (2 Timoteo 3:1, 2) Akakumbukira okalamba, nthaŵi zambiri ndi chifukwa cha zomwe anachita m’mbuyomu, kuti anali ndani panthaŵiyo, m’malo mwa mmene iwo alili panopa. Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limati: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.” (Ahebri 6:10) N’zoona kuti Yehova Mulungu amakumbukira ntchito zanu zokhulupirika za m’mbuyomu. Koma amakuonaninso kuti ndinu wamtengo wapatali chifukwa cha zomwe mukupitiriza kuchita pomutumikira. Inde, amaona okalamba okhulupirika kuti ndi obala zipatso, olimba mwauzimu, ndiponso kuti ndi Akristu amphamvu amene moyo wawo ukupereka umboni wa mphamvu Zake.​—Afilipi 4:13.

20 Kodi mumaona anthu okalamba omwe ali mu ubale wathu wachikristu ngati mmene Yehova amawaonera? Ngati mumatero, mudzalimbikitsidwa kuwasonyeza kuti mumawakonda. (1 Yohane 3:18) Nkhani yotsatirayi ifotokoza njira zina zosonyezera chikondi choterocho posamalira zosoŵa zawo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ku tsango lililonse la zipatso za mtengowu kumatha kukhala zipatso 1,000 ndipo tsangolo limatha kulemera makilogalamu eyiti kapena kupitirira pamenepo. Wolemba mabuku wina anati “munthu akakhala ndi mitengo yobereka [ya migwalangwa] amatha kupeza zipatso zolemera matani aŵiri kapena atatu pa mtengo uliwonse panthaŵi yomwe mtengowo uli ndi moyo.”

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi okalamba ‘amabala zipatso’ motani?

• N’chifukwa chiyani kulimba mwauzimu kwa Akristu okalamba kuli kwamtengo wapatali?

• Kodi okalamba ‘angalalikire motani kuti Yehova n’ngolunjika’?

• N’chifukwa chiyani Yehova amaona kuti atumiki ake omwe am’tumikira kwa nthaŵi yaitali ndi amtengo wapatali?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 13]

Zimene Zawathandiza Kukhalabe Olimba M’chikhulupiriro

Kodi n’chiyani chimene chathandiza anthu amene akhala Akristu kwa nthaŵi yaitali kukhalabe olimba m’chikhulupiriro ndiponso amphamvu mwauzimu? Nazi zina zimene ena ananena:

“Kuŵerenga malemba ofotokoza ubwenzi wathu ndi Yehova n’kofunika kwambiri. Nthaŵi zambiri usiku, ndimalakatula pamtima Masalmo 23 ndi 91.”​—Olive, amene anabatizidwa mu 1930.

“Ndimaonetsetsa kuti ndizipezeka pa nkhani iliyonse ya ubatizo ndi kuimvetsera mwatcheru kwambiri, ngati kuti ndi paubatizo wanga. Kukumbukira nthaŵi zonse kuti ndinadzipatulira kwandithandiza kwambiri kuti ndikhalebe wokhulupirika.”​—Harry, amene anabatizidwa mu 1946.

“Kupemphera tsiku ndi tsiku n’kofunika kwambiri​—kum’pempha Yehova nthaŵi zonse kuti atithandize, atiteteze, ndiponso kuti atidalitse, ‘kum’lemekeza m’njira zathu zonse.’” (Miyambo 3:5, 6)​—Antônio, amene anabatizidwa mu 1951.

“Kumvetsera zinthu zimene zinachitikira anthu amene atumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri kumandilimbikitsa kuti ndipitirizebe kukhala wokhulupirika kwa iye.”​—Joan, amene anabatizidwa mu 1954.

“Ndi bwino kuti munthu usamadzimve kuti ndiwe wofunika kwambiri. Zimene tili nazo tazipeza chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu. Kuona zinthu mwanjira imeneyi kumatithandiza kudziŵa kumene tingapeze chakudya chauzimu chofunika kwambiri kuti tipirire mpaka mapeto.”​—Arlene, amene anabatizidwa mu 1954.

[Chithunzi patsamba 11]

Okalamba amabala zipatso za Ufumu zamtengo wapatali kwambiri

[Chithunzi patsamba 14]

Kulimba mwauzimu kwa okalamba n’kwamtengo wapatali