Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Kwaniritsani Utumiki Wanu’

‘Kwaniritsani Utumiki Wanu’

 ‘Kwaniritsani Utumiki Wanu’

“Chita utumiki wako mokwanira.”​—2 TIMOTEO 4:5, Byington.

1, 2. Ngakhale kuti Akristu onse ndi alaliki, kodi Malemba amafuna kuti akulu azichita chiyani?

KODI ndinu wolengeza Ufumu? Ngati ndi choncho, thokozani Yehova Mulungu chifukwa cha mwayi wapadera umenewu. Kodi ndinu mkulu mu mpingo? Umenewu ndi mwayi winanso wochokera kwa Yehova. Koma tisaiŵale kuti si maphunziro a kusukulu kapena luso lathu lodziŵa kulankhula bwino zimene zimatiyeneretsa kutumikira kapena kuyang’anira mpingo. Yehova ndiye amatiyeneretsa kukhala atumiki, ndipo amuna ena mwa ife amakhala ndi mwayi wotumikira monga oyang’anira chifukwa chakuti akwanitsa ziyeneretso zinanso zomwe Malemba amafuna.​—2 Akorinto 3:5, 6; 1 Timoteo 3:1-7.

2 Akristu onse odzipatulira amachita ntchito yolalikira, koma makamaka oyang’anira, kapena kuti akulu, afunika kusonyeza chitsanzo chabwino mu utumiki. Mulungu ndi Kristu, kuphatikizaponso ena a Mboni za Yehova amaona akulu amene “akuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso.” (1 Timoteo 5:17; Aefeso 5:23; Ahebri 6:10-12) Nthaŵi zonse, zophunzitsa za mkulu ziyenera kuthandiza omvera kukhala athanzi mwauzimu, chifukwa mtumwi Paulo anauza Timoteo yemwe anali woyang’anira kuti: “Idzafika nthaŵi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m’khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: ndipo adzalubza dala pa choonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zachabe. Koma iwe, khala maso m’zonse, imva zoŵaŵa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.”​—2 Timoteo 4:3-5.

3. Kodi m’pofunika kuchita chiyani kuti ziphunzitso zonyenga zisaopseze mpingo mwauzimu?

3 Pofuna kutsimikizira kuti ziphunzitso zonyenga sizikuopseza mpingo mwauzimu, woyang’anira afunika kutsatira malangizo a Paulo akuti: “Khala tcheru pa mbali iliyonse, . . . chita utumiki wako mokwanira.” (2 Timoteo 4:5, Byington) Zoonadi, mkulu afunika ‘kuchita utumiki wake mokwanira.’ Afunika kuchita zonse zomwe zikufunika, osasiya chilichonse. Mkulu amene amachita utumiki wake mokwanira amasamalira kwambiri maudindo ake onse, sanyalanyaza chilichonse kapena kuchichita mosakwanira. Munthu wotero ndi wokhulupirika ngakhale pazinthu zazing’ono.​—Luka 12:48; 16:10.

4. Kodi n’chiyani chingatithandize kukwaniritsa utumiki wathu?

4 Sinthaŵi zonse pamene kukwaniritsa utumiki wathu kumafuna nthaŵi yambiri, koma pamafunika kuti munthu agwiritse ntchito bwino nthaŵi yake. Kuchita zinthu mosadumphadumpha kungathandize Akristu onse kukwaniritsa zinthu zosiyanasiyana mu utumiki. Kuti mkulu azikhala nthaŵi yaitali mu utumiki wa kumunda, afunika kukhala munthu wadongosolo kuti ndandanda yake yochitira zinthu ikhale yabwino ndiponso kuti adziŵe ntchito zomwe angapatse ena komanso mmene angawapatsire ntchitozo. (Ahebri 13:17) Mwachibadwa, mkulu amene amalemekezedwa amachitanso mbali yake, monga Nehemiya, amene anamanga nawo malinga a Yerusalemu. (Nehemiya 5:16) Ndipo atumiki onse a Yehova ayenera kuchita ntchito yolalikira Ufumu nthaŵi zonse.​—1 Akorinto 9:16-18.

5. Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pankhani ya utumiki?

5 Tinalamulidwa kugwira ntchito yosangalatsa kwambiri yolengeza Ufumu wakumwamba womwe unakhazikitsidwa. Kunena zoona timanyadira mwayi womwe tili nawo wolalikira uthenga wabwino padziko lonse chimaliziro chisanafike. (Mateyu 24:14) Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, tingalimbikitsidwe ndi mawu a Paulo  akuti: “Tili nacho chuma [cha utumiki] ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.” (2 Akorinto 4:7) Inde, n’zotheka kuchita utumiki wovomerezeka, koma pokhapokha Mulungu atatipatsa mphamvu ndi nzeru.​—1 Akorinto 1:26-31.

Kuonetsa Ulemerero wa Mulungu

6. Kodi panakhala kusiyana kotani pakati pa Israyeli wakuthupi ndi Israyeli wauzimu?

6 Ponena za Akristu odzozedwa, Paulo ananena kuti Mulungu “anatiyeneretsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano.” Mtumwiyu anasiyanitsa pangano latsopano lomwe Mulungu anapanga ndi Israyeli wauzimu kudzera mwa Yesu Kristu ndi pangano la Chilamulo lakale lomwe anapanga ndi Israyeli wakuthupi kudzera mwa Mose. Paulo ananenanso kuti Mose atatsika m’phiri la Sinai ali ndi miyala yomwe panali Malamulo Khumi, nkhope yake inaŵala kwambiri moti Aisrayeli sanathe kumuyang’anitsitsa. Koma patapita nthaŵi, panachitika zinthu zina zoopsa kwambiri kuposa zimenezi chifukwa chakuti “maganizo awo anaumitsidwa” ndipo mitima yawo inaphimbidwa. Komano, chophimbachi chimachoka munthu akatembenukira kwa Yehova ndi kudzipereka kwa iye ndi mtima wonse. Kenako, ponena za utumiki umene anthu a m’pangano latsopanoli anapatsidwa, Paulo anati: “Ife tonse, . . . ndi nkhope zosaphimbika timaonetsa ulemerero wa Yehova monga akalilore.” (2 Akorinto 3:6-8, 14-18, NW; Eksodo 34:29-35) Nazonso “nkhosa zina” za Yesu masiku ano zili ndi mwayi woonetsa ulemerero wa Yehova.​—Yohane 10:16.

7. Kodi anthu angaonetse motani ulemerero wa Mulungu?

7 Popeza kuti palibe munthu angaone nkhope ya Mulungu n’kukhala ndi moyo, kodi anthu ochimwa angaonetse motani ulemerero wake? (Eksodo 33:20) Tiyenera kudziŵa kuti kuwonjezera pa ulemerero umene Yehova ali nawo, cholinga chakenso chotsimikizira kuti iye ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse pogwiritsa ntchito Ufumu wake n’chaulemerero. Mfundo zokhudza Ufumu umenewu ndi zina mwa “zazikulu za Mulungu” zomwe anthu amene analandira mzimu woyera pa Pentekoste mu 33 C.E. anayamba kulengeza. (Machitidwe 2:11) Motsogoleredwa ndi mzimuwo, iwo anatha kukwaniritsa utumiki womwe anapatsidwa.​—Machitidwe 1:8.

8. Pankhani ya utumiki, kodi Paulo anatsimikiza mtima kuchita chiyani?

8 Paulo anatsimikiza mtima kusalola chilichonse kumulepheretsa kukwaniritsa utumiki wake. Analemba kuti: “Popeza tili nawo utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifoka; koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.” (2 Akorinto 4:1, 2) Mwa zimene Paulo anatchula kuti “utumiki umene,” anthu akuzindikira choonadi ndipo kuunika kwauzimu kukufalikira kutali.

9, 10. Kodi kuonetsa ulemerero wa Yehova kumatheka motani?

9 Ponena za Gwero la kuunika kwenikweni ndi kuunika kwauzimu, Paulo analemba kuti: “Mulungu amene anati, Kuunika kudzaŵala kutuluka mumdima, ndiye amene anaŵala m’mitima  yathu kutipatsa chiŵalitsiro cha chidziŵitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.” (2 Akorinto 4:6; Genesis 1:2-5) Popeza kuti tapatsidwa mwayi waukulu kwambiri wokhala atumiki a Mulungu, tiyeni tikhale oyera kotero kuti tionetse ulemerero wa Yehova monga akalilore.

10 Anthu omwe ali mumdima wauzimu sangaone ulemerero wa Yehova kapena kuuona ukuŵala mwa Yesu Kristu, yemwe ndi Mose Wamkulu. Koma ife monga atumiki a Yehova, timalandira kuunika kwamphamvu kuchokera m’Malemba ndi kukuonetsa kwa ena. Kuti anthu amene panopo ali mumdima wauzimu asadzawonongedwe, akufunikira kuunika kochokera kwa Mulungu. Motero, timalabadira mosangalala ndiponso mwachangu lamulo la Mulungu lakuti tiŵalitse kuunika mumdima kuti Yehova alemekezedwe.

Kuunika Kwanu Kuŵale pa Maphunziro a Baibulo a Panyumba

11. Kodi Yesu ananenanji pankhani yoŵalitsa kuunika kwathu, ndipo njira imodzi yochitira zimenezi mu utumiki wathu ndi iti?

11 Yesu anauza otsatira ake kuti: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika. Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m’mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m’nyumbamo. Chomwecho muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:14-16) Khalidwe lathu labwino lingachititse ena kulemekeza Mulungu. (1 Petro 2:12) Ndipo mbali zosiyanasiyana za ntchito yathu yolalikira zimatipatsa mipata yambiri yoŵalitsira kuunika kwathu. Chimodzi mwa zolinga zathu zikuluzikulu ndicho kuŵalitsa kuunika kwauzimu kochokera m’Mawu a Mulungu mwa kuchititsa maphunziro a Baibulo a panyumba ogwira mtima. Iyi ndi njira yofunika kwambiri yokwaniritsira utumiki wathu. Kodi ndi mfundo ziti zomwe zingatithandize kuchititsa maphunziro a Baibulo ofika pamtima anthu ofunafuna choonadi?

12. Kodi pemphero limagwirizana motani ndi ntchito yochititsa maphunziro a Baibulo a panyumba?

12 Kupemphera kwa Yehova za nkhaniyi kumasonyeza kuti tikufunitsitsa kuti tizichititsa maphunziro a Baibulo. Komanso, zimasonyeza kuti tikuona kufunika kothandiza ena kudziŵa za Mulungu. (Ezekieli 33:7-9) Yehova adzayankha mapemphero athu ndiponso kudalitsa zimene timachita ndi mtima wonse mu utumiki. (1 Yohane 5:14, 15) Koma sikuti timangopemphera n’cholinga chopeza munthu amene tingachite naye phunziro la Baibulo la panyumba. Tikakhazikitsa phunziro, kupempherera ndiponso kusinkhasinkha zofunika za wophunzira Baibuloyo kudzathandiza kuti tizichita naye phunziro lililonse mogwira mtima.​—Aroma 12:12.

13. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizichititsa maphunziro a Baibulo a panyumba ogwira mtima?

13 Kuti tichititse maphunziro a Baibulo a panyumba ogwira mtima, tiyenera kukonzekera bwino phunziro lililonse. Ngati tikuona kuti ndife opereŵera penapake, mwina zingathandize kwambri kuonerera mmene woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo amachititsira phunzirolo mlungu uliwonse. Mwinanso nthaŵi zina tingathe kuyenda limodzi ndi ofalitsa Ufumu amene amachititsa bwino kwambiri maphunziro a Baibulo a panyumba. Ndipo maganizo komanso njira zomwe Yesu Kristu ankagwiritsa ntchito pophunzitsa ndi zofunika kuti tiziziganizira.

14. Kodi tingatani kuti tim’fike pamtima wophunzira Baibulo?

14 Yesu ankasangalala kwambiri ndi kuchita chifuno cha Atate wake ndiponso kuuza ena za Mulungu. (Salmo 40:8) Anali wofatsa ndipo ankatha kuwafika pamtima anthu omwe anali kum’mvetsera. (Mateyu 11:28-30) Motero tiyeni tiziyesetsa kuwafika pamtima anthu omwe tikuphunzira nawo Baibulo. Kuti tithe kuchita zimenezi tifunika kukonzekera phunziro lililonse tikuganizira mmene zinthu zilili ndi wophunzirayo. Mwachitsanzo, ngati iye pachikhalidwe chawo salidziŵa bwino Baibulo, mwina tingafunike kum’thandiza kuti akhutire kuti Baibulo ndi loona. Ngati zili choncho, n’zoonekeratu kuti tidzafunika kuŵerenga malemba ambiri ndi kuwafotokoza.

 Thandizani Wophunzira Kumvetsa Mafanizo

15, 16. (a) Kodi tingam’thandize motani wophunzira amene sakumvetsa fanizo limene lagwiritsidwa ntchito m’Baibulo? (b) Kodi tingachite chiyani ngati buku lathu linalake lili ndi fanizo lomwe wophunzira Baibulo sakulimvetsa?

15 N’kutheka kuti wophunzira Baibulo sakudziŵa bwino fanizo linalake lomwe linagwiritsidwa ntchito m’Malemba. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti iye sadziŵa zomwe Yesu ankatanthauza polankhula za kuika nyali pa choikapo chake. (Marko 4:21, 22) Yesu anali kunena za nyali yakale yoyaka ndi chingwe. Nyali yoteroyo inkakhala ndi malo ake oikapo ndipo akatero inkatha kuunika malo akulu ndithu m’nyumba. Pangafunike kuchita kafukufuku wa nkhani zimenezi m’mabuku athu achikristu kuti timveketse bwino fanizo la Yesu limeneli. Koma zimapindulitsa kwambiri kufika pa phunziro la Baibulo muli ndi mfundo zomwe wophunzira angamve ndi kusangalala nazo.

16 Buku lothandiza kuphunzira Baibulo lingakhale ndi fanizo lomwe wophunzira wina sangalimvetse. M’fotokozereni bwino, kapena gwiritsani ntchito fanizo lina lomwe lili ndi mfundo yofanana nalo. N’kutheka kuti buku lina likutsindika mfundo yakuti mu ukwati mumafunika kukhala ndi mnzako wabwino komanso kuchita zinthu mogwirizana. Popereka fanizo la zimenezi, bukulo lingatchule za katswiri wa maseŵera a pidigoli amene akulekerera katungwe amene ali m’mwamba kwambiri, ndipo akudalira mzake amene akuseŵera naye kuti amuwakhe. Ngati fanizoli sanalimvetse, mwachionekere kufunika kokhala ndi mkazi kapena mwamuna wodalirika komanso kuchita zinthu mogwirizana kungafanizidwe ndi mmene antchito amakhalira ogwirizana akamaponyerana makatoni powatsitsa m’bwato.

17. Kodi tingaphunzirenji kwa Yesu pankhani ya mafanizo?

17 Kuti tigwiritse ntchito fanizo lina pangafunike kukonzekereratu. Komatu, imeneyi ndiye njira yosonyezera chidwi chathu mwa wophunzira Baibuloyo. Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo osavuta kumva pofuna kumveketsa nkhani zovuta kwambiri. Ulaliki wake wa pa Phiri uli ndi zitsanzo za mfundoyi, ndipo Baibulo limasonyeza kuti zophunzitsa zake zinathandiza kwambiri omvera ake. (Mateyu 5:1–7:29) Yesu ankafotokoza zinthu mofatsa chifukwa chakuti anali ndi chidwi ndi anthu ena.​—Mateyu 16:5-12.

18. Kodi tikulimbikitsidwa kuchitanji ndi malemba amene sanagwidwe mawu amene ali m’mabuku athu?

18 Kukhala ndi chidwi mwa anthu ena kudzatilimbikitsa kuti ‘tikambirane nawo za m’Malemba.’ (Machitidwe 17:2, 3, NW) Izi zimafuna kuti tiphunzire mwakhama ndiponso kupemphera komanso kugwiritsa ntchito mwanzeru mabuku omwe tikupeza kudzera mwa “mdindo wokhulupirika.” (Luka 12:42-44) Mwachitsanzo, buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha linagwira mawu malemba ambiri. * Chifukwa cha kuchepa kwa malo, malemba ena anangoikidwamo osawagwira mawu. Pamene tikuchititsa phunziro la Baibulo, tifunika kuŵerenga ndi kufotokoza ena mwa malemba omwe sanagwidwe mawuwo. Ndipotu, zophunzitsa zathu zimachokera m’Mawu a Mulungu, ndipo ndi amphamvu kwambiri. (Ahebri 4:12) Fotokozani za Baibulo paphunziro lonselo, ndipo gwiritsani ntchito mobwerezabwereza malemba omwe ali pandime. Thandizani wophunzirayo kuona zomwe Baibulo limanena pankhani kapena zochitika zosiyanasiyana. Yesetsani kum’sonyeza  mmene adzapindulire mwa kumvera Mulungu.​—Yesaya 48:17, 18.

Funsani Mafunso Ochititsa Munthuyo Kuganiza

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito mafunso ochititsa munthu kuganiza pamene tikuchititsa phunziro la Baibulo la panyumba? (b) Kodi tingachite chiyani ngati nkhani ina ikufunika kuionanso?

19 Kugwiritsa ntchito bwino mafunso komwe Yesu ankachita kunkathandiza anthu kuganiza. (Mateyu 17:24-27) Ngati tifunsa mafunso ochititsa munthu kuganiza omwe sakuchititsa manyazi wophunzira Baibulo, mayankho ake angasonyeze zomwe amaganiza pankhani zina. Mwina tingaone kuti iye amakhulupirirabe mfundo zomwe sizigwirizana ndi malemba. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti iye amakhulupirira za Utatu. Buku la Chidziŵitso, m’chaputala 3, limati mawu akuti “Utatu” sapezeka m’Baibulo. Bukuli lili ndi malemba ogwidwa mawu ndi osagwidwa mawu posonyeza kuti Yehova ndi Yesu ndi osiyana komanso kuti mzimu woyera ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, simunthu ayi. Mwina kuŵerenga ndi kukambirana malemba a m’Baibulo ameneŵa kungakhale kokwanira. Koma bwanji ngati pakufunika zina zowonjezera? Mwina nthaŵi zonse pambuyo pa phunziro lotsatira, tingapatule nthaŵi yokambirana zinthu zaphindu zokhudza nkhaniyi za m’buku lina la Mboni za Yehova, monga bulosha lakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? Kenako, tingadzapitirize phunzirolo pogwiritsa ntchito buku la Chidziŵitso.

20 Tiyerekeze kuti yankho la wophunzirayo pafunso lomwe lamuchititsa kuganiza ndi lodabwitsa mwinanso lokhumudwitsa kumene. Ngati zikukhudza kusutsa fodya kapena nkhani ina yofunika kwambiri, tingamuuze kuti tipitirize phunzirolo ndipo tidzakambirana nkhaniyo nthaŵi ina m’tsogolo. Kudziŵa kuti wophunzirayo akupitirizabe kusuta fodya kungatithandize kupeza nkhani ya m’mabuku athu yomwe ingam’thandize kuti apite patsogolo mwauzimu. Pamene tikuyesetsa kum’fika pamtima wophunzirayo, tingapemphere kwa Yehova kuti am’thandize kukula mwauzimu.

21. Kodi chingachitike n’chiyani ngati tigwirizanitsa njira zathu zophunzitsira ndi zofunika za wophunzira Baibulo?

21 Mosakayikira, mwa kukonzekera bwino ndiponso ndi thandizo la Yehova, tidzatha kugwirizanitsa njira zathu zophunzitsira ndi zofunika za wophunzira Baibulo. M’kupita kwa nthaŵi, tingam’thandize kuti azikonda kwambiri Mulungu. Tingamuthandizenso munthuyo kulemekeza ndi kuyamikira gulu la Yehova. Ndipo zimasangalatsa kwambiri munthu wophunzira Baibulo akavomereza kuti ‘Mulungu ali ndithu mwa ife’! (1 Akorinto 14:24, 25) Ndiyetu tiyeni tizichititsa maphunziro a Baibulo ogwira mtima ndi kuchita zonse zomwe tingathe pothandiza ena kukhala ophunzira a Yesu.

Chuma Chofunika Kuchisamalira

22, 23. Kuti tikwaniritse utumiki wathu kodi pakufunika chiyani?

22 Kuti tikwaniritse utumiki wathu, tiyenera kudalira mphamvu zimene Mulungu amapereka. Ponena za utumiki, Paulo analembera Akristu anzake odzozedwa, kuti: “Tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.”​—2 Akorinto 4:7.

23 Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” tili ngati zipangizo zadothi zosalimba. (Yohane 10:16) Koma Yehova angatipatse mphamvu zofunika kuti tikwaniritse maudindo athu ngakhale titakumana ndi zopinga. (Yohane 16:13; Afilipi 4:13) Motero tiyeni tim’dalire kwambiri Yehova, tisamalire chuma chathu cha utumiki, ndi kukwaniritsa utumiki wathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi akulu angatani kuti akwaniritse utumiki wawo?

• Kodi tingatani kuti tikhale ogwira mtima pa maphunziro athu a Baibulo a panyumba?

• Kodi mungachite chiyani ngati wophunzira Baibulo sanamvetse fanizo kapena ngati akufunika kudziŵa zinthu zinanso pankhani inayake?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Akulu achikristu amaphunzitsa mu mpingo ndipo amathandiza kuphunzitsa okhulupirira anzawo mu utumiki

[Chithunzi patsamba 18]

Kuchititsa maphunziro a Baibulo a panyumba ogwira mtima ndi njira imodzi yoŵalitsira kuunika kwathu