Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mgonero wa Ambuye Tiziukumbukira Motani?

Kodi Mgonero wa Ambuye Tiziukumbukira Motani?

 Kodi Mgonero wa Ambuye Tiziukumbukira Motani?

POFOTOKOZA za kukumbukira Mgonero wa Ambuye, mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti: “Ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate; ndipo mmene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa. Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga; chitani ichi, nthaŵi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa. Pakuti nthaŵi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.”​—1 Akorinto 11:23-26.

Monga mmene Paulo ananenera, Yesu anakhazikitsa Mgonero wa Ambuye “usiku uja [Yesu] anaperekedwa” ndi Yudasi Iskariote kwa atsogoleri achipembedzo achiyuda omwe anaumiriza Aroma kuti apachike Kristu. Mgonero umenewu unachitika Lachinayi madzulo pa March 31, mu 33 C.E. Yesu anamwalira pa mtengo wozunzirapo Lachisanu madzulo, pa April 1. Popeza masiku a kalendala ya Chiyuda amayambira madzulo a tsiku lina kudzafika madzulo a tsiku lotsatira, Mgonero wa Ambuye ndiponso imfa ya Yesu Kristu zinachitika tsiku limodzi, pa Nisan 14, mu 33 C.E.

Anthu amene angadye mkate ndi kumwa vinyo ayenera ‘kumachita ichi’ pokumbukira Yesu. Malinga ndi Baibulo lina, Yesu anati: “Chitani ichi monga chikumbutso changa.” (1 Akorinto 11:24, The Jerusalem Bible) Mgonero wa Ambuye umatchedwanso Chikumbutso cha imfa ya Kristu.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukumbukira Imfa ya Yesu?

Yankho la funso limeneli lagona pa cholinga cha imfa yakeyo. Yesu anafa monga wokhalira mbali wamkulu wa ulamuliro wa Yehova. Motero, iye anatsimikizira kuti Satana, yemwe ananena kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa cha phindu limene amapezapo, ndi wabodza. (Yobu 2:1-5; Miyambo 27:11) Ndiponso, mwa imfa yake monga munthu wangwiro, Yesu ‘anapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Adamu atachimwira Mulungu, anataya moyo wangwiro ndi zinthu zonse zimene akanakhala nazo chifukwa cha moyo umenewo. Koma “Mulungu anakonda dziko lapansi [lomwe ndi anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Inde, “mphotho yake ya uchimo ndi  imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”​—Aroma 6:23.

Motero, imfa ya Yesu Kristu imasonyeza njira ziŵiri zazikulu koposa pamene chikondi chinasonyezedwa. Njira zimenezi ndizo chikondi chachikulu chimene Yehova anasonyeza kwa anthu popereka Mwana wake, ndiponso chikondi chodzimana chimene Yesu anasonyeza kwa anthu popereka modzifunira moyo wake monga munthu. Chikumbutso cha imfa ya Yesu chimachititsa kuti njira ziŵiri za chikondi zimenezi zionekere. Popeza ife ndi amene tasonyezedwa chikondi choterechi, kodi sitiyenera kuyamikira? Njira imodzi yosonyezera kuyamikira kwathu ndiyo kupezekapo pa chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye.

Zimene Mkate ndi Vinyo Zimaimira

Pokhazikitsa Mgonero wa Ambuye, Yesu anagwiritsa ntchito mkate ndi chikho cha vinyo wofiira monga zizindikiro. Yesu anatenga mkate, ndipo “mmene adayamika, ananyema, nati, Ichi [mkate] ndi thupi langa la kwa inu.” (1 Akorinto 11:24) Mkatewo anaunyema kuti awugaŵe ndi kudya popeza unali wopyapyala, wosavuta kunyema ndipo anaupanga pogwiritsa ntchito ufa ndi madzi popanda chotupitsa. M’Malemba, chotupitsa chimaimira uchimo. (Mateyu 16:11, 12; 1 Akorinto 5:6, 7) Yesu sanali wochimwa. Motero, thupi lake langwiro monga munthu linakhala nsembe ya dipo yoyenerera yoperekera anthu. (1 Yohane 2:1, 2) Ndiyetu n’zoyenerera kuti mkate umene ungagwiritsidwe ntchito kuimira thupi la Kristu lopanda uchimo uyenera kukhala wopanda chotupitsa.

Yesu anayamikanso chifukwa cha chikho chimene munali vinyo wofiira weniweni ndipo anati: “Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga.” (1 Akorinto 11:25) Vinyo wofiira amene anali m’chikhomo amaimira mwazi wa Yesu. Monga mmene mwazi wa ng’ombe ndi mbuzi zimene zinaperekedwa nsembe zinatsimikizira pangano la Chilamulo pakati pa Mulungu ndi mtundu wa Israyeli mu 1513 B.C.E., mwazi wa Yesu umene anautaya pa imfa yake unatsimikizira pangano latsopano.

Kodi Ndani Ayenera Kudya?

Kuti tidziŵe amene angadye zizindikiro za pa Chikumbutso moyenerera, tifunika kumvetsa kuti pangano latsopano n’lotani ndipo ndani amene ali m’panganolo. Baibulo limati: “Taonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda . . . ndidzaika chilamulo changa m’kati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, nadzakhala iwo anthu anga . . . ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira tchimo lawo.”​—Yeremiya 31:31-34.

Pangano latsopano lachititsa kuti pakhale ubale wapadera kwambiri ndi Yehova Mulungu. Mwa pangano limeneli, gulu lina la anthu limakhala anthu ake ndipo iye amakhala Mulungu wawo. Lamulo la Yehova limalembedwa m’kati mwawo, m’mitima yawo, ndipo ngakhale amene sali Ayuda odulidwa angaloŵe m’pangano latsopano limeneli ndi Mulungu. (Aroma 2:29) Luka, wolemba Baibulo, analemba zokhudza cholinga cha Mulungu ‘choyang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.’ (Machitidwe 15:14) Malinga ndi 1 Petro 2:10, ameneŵa ‘kale sanali anthu, koma tsopano ali anthu a Mulungu.’ Malemba amatcha anthu ameneŵa kuti “Israyeli wa Mulungu,” kutanthauza Israyeli wauzimu. (Agalatiya 6:16; 2 Akorinto 1:21) Motero, pangano latsopano ndi pangano la pakati pa Yehova Mulungu ndi Israyeli wauzimu.

Pa usiku womaliza ali ndi ophunzira ake, Yesu anapangana nawonso pangano lina. Anawauza kuti: “Ndikuikirani ufumu, monganso Atate  wanga anandiikira Ine.” (Luka 22:29) Limeneli ndi pangano la Ufumu. Chiŵerengero cha anthu opanda ungwiro amene atengedwa kuloŵa m’pangano la Ufumuli ndi 144,000. Akadzaukitsidwa n’kupita kumwamba, adzalamulira pamodzi ndi Kristu monga mafumu ndi ansembe. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-4) Motero, anthu amene ali m’pangano latsopano ndi Yehova Mulungu alinso m’pangano la Ufumu ndi Yesu Kristu. Ameneŵa ndi anthu okhawo amene amadya moyenerera zizindikiro za Mgonero wa Ambuye.

Kodi anthu amene akuyenerera kudya zizindikiro za pa Chikumbutso amadziŵa bwanji kuti ali pa ubwenzi wapadera ndi Mulungu ndiponso kuti adzakhala olamulira anzake a Kristu? Paulo anafotokoza kuti: “Mzimu [woyera wo]kha uchita umboni pamodzi ndi mzimu wathu [maganizo athu], kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso oloŵa nyumba; inde oloŵa nyumba ake a Mulungu, ndi oloŵa anzake a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi iye.”​—Aroma 8:16, 17.

Pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito, Mulungu amadzoza olamulira anzake a Kristu. Zimenezo zimawachititsa kukhala otsimikiza kuti ndi oloŵa Ufumu. Mzimuwo umawachititsa Akristu odzozedwa kukhala ndi chiyembekezo chopita kumwamba. Amaona zonse zimene Baibulo limanena zokhudza moyo wakumwamba kuti likunena za iwowo. Ndiponso, ndi okonzeka kusiya zinthu zonse za padziko lapansi, kuphatikizapo moyo wa padziko lapansi ndi mgwirizano uliwonse wa anthu. Ngakhale kuti Akristu odzozedwa ndi mzimu amadziŵa kuti moyo padziko lapansi la Paradaiso udzakhala wabwino kwambiri, iwo sakhala ndi chiyembekezo chimenecho. (Luka 23:43) Amakhala ndi chiyembekezo chosasintha chopita kumwamba ndipo motero amadya moyenerera zizindikiro za pa Chikumbutso. Sachita zimenezi chifukwa cha mfundo zonyenga zachipembedzo koma chifukwa chakuti mzimu wa Mulungu wagwira ntchito mwa iwo.

Ndiye tinene kuti munthu sakutsimikiza kwenikweni kuti ali m’pangano latsopano ndiponso m’pangano la Ufumu. Bwanji ngatinso alibe umboni wa mzimu wa Mulungu wotsimikizira kuti ndi wolamulira mnzake wa Kristu? Ngati zili choncho, kungakhale kulakwa kudya nawo zizindikiro za Chikumbutso. Inde, Mulungu sangasangalale ndi munthu amene mwadala akudziimira ngati munthu amene akuyembekezera kupita kumwamba kukakhala mfumu ndi wansembe pamene kwenikweni alibe chiyembekezo chimenecho.​—Aroma 9:16; Chivumbulutso 22:5.

Kodi Mgonerowu Uzikumbukiridwa Kangati?

Kodi imfa ya Yesu iyenera kukumbukiridwa mlungu uliwonse kapenanso ngakhale tsiku lililonse? Chabwino, Kristu anakhazikitsa Mgonero wa Ambuye ndiponso anaphedwa mopanda chilungamo pa Tsiku la Paskha. Pa Paskha anali kukumbukira kumasulidwa kwa Aisrayeli ku ukapolo ku Igupto ndipo ankachita Paskhayo kamodzi pachaka, pa Nisan 14. (Eksodo 12:6, 14; Levitiko 23:5) Motero, imfa ya ‘Kristu, Paskha wathu’ iyenera kukumbukiridwa kamodzi kokha pachaka, osati mlungu uliwonse kapena tsiku lililonse. (1 Akorinto 5:7) Pochita chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye, Akristu amatsatira mmene Yesu anachitira pamene anakhazikitsa chikumbutsochi.

Nanga kodi zimene Paulo ananena kuti: “Nthaŵi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye,” zikutanthauza chiyani? (1 Akorinto 11:26) Iye anali kutanthauza kuti nthaŵi iliyonse pamene Akristu odzozedwa akadya zizindikirozo, adzakhala akulengeza chikhulupiriro chawo mu nsembe ya dipo ya Yesu.

Akristu odzozedwa anali oti adzakumbukira  imfa ya Kristu “kufikira akadza iye.” Chikumbutsochi chinali kudzapitiriza kuchitika mpaka pamene Yesu adzafika kudzatenga otsatira ake odzozedwa kupita nawo kumwamba mwa kuwaukitsira ku moyo wauzimu panthaŵi ya “kufikanso [“kukhalapo, NW]” kwake. (1 Atesalonika 4:14-17) Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Kristu anauza atumwi okhulupirika 11, pamene anati: “Ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.”​—Yohane 14:3.

Kodi Uli ndi Tanthauzo Lotani kwa Inu?

Kodi n’koyenera kudya zizindikiro za pa Chikumbutso pofuna kupindula ndi nsembe ya Yesu n’kudzalandira moyo wosatha padziko lapansi? Ayi. M’Baibulo, palibe pamene amasonyeza kuti anthu oopa Mulungu monga Nowa, Abrahamu, Sara, Isake, Rebeka, Yosefe, Mose, ndi Davide, akadzaukitsidwa padziko lapansi adzadya zizindikiro zimenezi. Komabe, anthu ameneŵa pamodzi ndi anthu ena onse amene akufuna kudzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi adzafunika kukhulupirira Mulungu ndi Kristu ndiponso nsembe ya dipo ya Yesu imene Yehova anapereka. (Yohane 3:36; 14:1) Kuti mukhale ndi moyo kosatha, inunso mufunika kukhala ndi chikhulupiriro. Kupezeka kwanu pa chikumbutso cha imfa ya Kristu chimene chimachitika kamodzi pachaka kudzakukumbutsani za nsembe yaikulu imeneyi ndipo kuyenera kukulitsa kuyamikira kwanu nsembeyo.

Mtumwi Yohane anatsindika kufunika kwa nsembe ya Yesu pamene anati: “Izi ndikulemberani [odzozedwa anzanga], kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiwombolo cha machimo athu; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yohane 2:1, 2) Odzozedwa anganene kuti nsembe ya Yesu ndiyo chiwombolo cha machimo awo. Koma imfa yakeyo ndi nsembenso ya machimo a dziko lonse lapansi, imene ikuchititsa kuti anthu omvera adzathe kukhala ndi moyo kosatha.

Kodi mudzapezekapo pa April 4, 2004, kuti mudzakumbukire imfa ya Yesu? Mboni za Yehova zidzachita mwambo wa chikumbutso umenewu padziko lonse lapansi pa malo amene zimasonkhanira. Ngati mungakapezekeko, mudzapindula kumvetsera nkhani yofunika kwambiri ya m’Baibulo. Mudzakumbutsidwa zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu atichitira. Zidzakhalanso zopindulitsa kusonkhana ndi anthu amene amalemekeza kwambiri Mulungu ndi Kristu ndiponso nsembe ya dipo ya Yesu. Mwambowu ukhozanso kukulimbikitsani kufuna kulandira chifundo cha Mulungu, chimene chingakuthandizeni kudzakhala ndi moyo kosatha. Musalole chinachake kukulepheretsani. Dzapezekeni pa chikumbutso chokhudza mtima chimenechi chimene chimalemekeza ndi kusangalatsa Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu.

[Chithunzi patsamba 5]

Imfa ya Yesu ikusonyeza njira ziŵiri zazikulu koposa pamene chikondi chinasonyezedwa

[Chithunzi patsamba 6]

Mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo ndi zizindikiro zoyenerera za thupi lopanda uchimo la Yesu ndi mwazi wake umene anakhetsa