Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Matchalitchi Apulumuka Mavuto Awo?

Kodi Matchalitchi Apulumuka Mavuto Awo?

 Kodi Matchalitchi Apulumuka Mavuto Awo?

“ANTHU ku Britain amakhulupirirabe Mulungu koma safuna kudzipereka kwa Kristu,” anatero Stephen Tirwomwe, mtsogoleri wachipembedzo wa ku Uganda. Pafupifupi zaka 20 zapitazo, iye anapulumuka ku Uganda pamene ankachotsa anthu mowakakamiza m’tchalitchi chake. Masiku ano amalalikira m’makalabu a azibambo mu mzinda wa Leeds ku England, kwa mphindi khumi anthuwo asanayambe kuseŵera maseŵera a makadi otchedwa bingo.

Kuchoka ku Britain, gulu longokhazikitsidwa kumene la Anglican Mission ku America likulimbana ndi mavuto auzimu ofananawo. “Panopa mwa anthu olankhula Chingelezi padziko lonse, ku United States n’kumene kuli anthu ambiri opanda tchalitchi ndiponso osasamala zinthu zauzimu,” inatero nkhani ina ya pakompyuta ya gululi yolumikizidwa ku Intaneti. “M’dzikoli mwayamba kufunika amishonale.” Gulu latsopanoli pokhumudwa chifukwa cholephera kusintha tchalitchi chawo, linaleka kutsatira mfundo zimene chipembedzo chawo chakhala chikutsatira ndipo linayamba kukachita nawo “ntchito za umishonale ku United States,” zimene atsogoleri a ku Asia ndi a ku Africa amachita.

Koma kodi n’chifukwa chiyani amishonale a ku Africa, Asia, ndi Latin-America ‘akupulumutsa anthu’ m’mayiko a ku Ulaya ndi North America amene amati ndi achikristu?

Kodi Ndani Akupulumutsa Mnzake?

Kwa zaka zoposa 400, amishonale odzipereka a ku Ulaya anakhala akupita ku madera ambiri olamulidwa ndi mayiko a ku Ulaya, monga ku Africa, Asia, Pacific, ndi South America. Cholinga chawo chinali chakuti chipembedzo chawo chifike kwa anthu otchedwa achikunja a m’maderawo. Patapita nthaŵi, mayiko olamulidwa ndi America, amene amati amatsatira mfundo za Chikristu, anayamba kuchita zomwezo, mapeto ake anachita zambiri pokhazikitsa mishoni za Evanjeliko padziko lonse kusiyana ndi amishonale anzawo a ku Ulaya. Tsopano zinthu zasintha.

 “Dera limene [Chikristu cha dzina lokha] chinali ndi mphamvu kwambiri lasintha,” anatero Andrew Walls, amene anapeza ndiponso ndi mkulu wa Centre for the Study of Christianity in the Non-Western World. Mu 1900, anthu 80 pa anthu 100 alionse amene ankati ndi Akristu anali a ku Ulaya kapena ku North America. Komabe, masiku ano anthu 60 pa anthu 100 alionse amene amadzitcha kuti ndi Akristu amakhala ku Africa, Asia, ndi Latin America. Nyuzipepala ina posachedwapa inati: “Matchalitchi a Katolika ku Ulaya amadalira ansembe a ku Philippines ndi ku India,” ndipo “pa ansembe sikisi alionse amene akutumikira m’matchalitchi a Katolika ku America, mmodzi ndi wochokera ku dziko lina.” Anthu a ku Africa atchalitchi cha Evanjeliko amene ali ku Netherlands, omwe ambiri a iwo ndi a ku Ghana, amadziona ngati “tchalitchi cha amishonale m’dziko la akunja.” Ndipo alaliki ochokera ku Brazil tsopano akuchititsa misonkhano m’madera osiyanasiyana a ku Britain. Wolemba nkhani wina anati: “Kumene kumafunika amishonale achikristu n’kumene kukuchoka amishonale.”

Zikhoza Kubutsa Mkangano M’tsogolo

Mwachionekere amishonale akufunika m’mayiko a ku Ulaya ndi North America kumene anthu achikunja akuchulukirachulukira. “Ku Scotland anthu osakwana 10 pa Akristu 100 alionse ndiwo amapita ku tchalitchi nthaŵi zonse,” inatero magazini ina. Ku France ndi Germany anthu ochepa kuposa pamenepa ndi amene amapita kutchalitchi. Atachita kafukufuku anapeza kuti, “anthu pafupifupi 40 pa anthu 100 alionse a ku America ndiponso anthu 20 pa anthu 100 alionse a ku Canada anati amapita ku tchalitchi nthaŵi zonse,” inatero nyuzipepala ina. Mosiyana ndi zimenezi, ku Philippines akuti anthu pafupifupi 70 pa anthu 100 alionse amapita ku tchalitchi, ndipo ndi mmene zililinso m’mayiko ena amene akutukuka kumene.

Chochititsanso chidwi kwambiri n’chakuti, anthu amene amapita ku tchalitchi a ku chigawo cha Kummwera cha Dziko Lapansili amakonda kutsatira miyambo yachipembedzo kusiyana ndi anthu a ku chigawo cha Kumpoto. Mwachitsanzo, Akatolika a ku United States ndi a ku Ulaya akafunsidwa, salephera kunena kuti sakhulupirira atsogoleri achipembedzo ndipo amafuna kuti anthu wamba azichita nawo zinthu zochuluka ndiponso kuti akazi azichita nawo zinthu zimene amuna amachita. Koma Akatolika a ku chigawo cha Kummwera cha Dziko Lapansili, amatsatira kwambiri mwambo wa tchalitchichi pankhani zimenezi. Chifukwa chakuti dera limene kuli anthu okonda kupita ku tchalitchi lasintha, pakhoza kubuka mkangano m’tsogolo. Philip Jenkins, katswiri wamaphunziro a mbiri yakale ndiponso yachipembedzo, ananeneratu kuti: “N’zoonekeratu kuti m’zaka 10 kapena 20 zikubwerazo Akristu a m’zigawo zimenezi sazidzaona Akristu a m’chigawo china ngati Akristu okwanira kapena enieni.”

Poona zimenezi, Walls anati mfundo yofunika kwambiri ndi kuona “mmene Akristu a ku Africa, Asia, Latin America, North America ndi a ku Ulaya angakhalire mogwirizana m’tchalitchi chimodzi, ndi kumanena chikhulupiriro chimodzi molondola.” Kodi mukuganiza bwanji? Kodi matchalitchi angapulumuke ku mavuto ameneŵa m’dziko logaŵanikali? Kodi ndi chiyani chimene chili maziko a umodzi wa Akristu oona? Nkhani yotsatirayi ipereka mayankho a m’Malemba, pamodzi ndi umboni woonekeratu wakuti gulu logwirizana la Akristu likukula padziko lonse lapansi.

[Chithunzi patsamba 4]

Ichi kale chinali tchalitchi tsopano ndi modyera ndi kuimbirako nyimbo

[Mawu a Chithunzi]

AP Photo/​Nancy Palmieri