Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kapolo” Amene Ali Wokhulupirika ndi Wanzeru

“Kapolo” Amene Ali Wokhulupirika ndi Wanzeru

 “Kapolo” Amene Ali Wokhulupirika ndi Wanzeru

“Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anam’khazika woyang’anira banja lake?”​—MATEYU 24:45.

1, 2. N’chifukwa chiyani masiku ano kuli kofunika kwambiri kuti tizilandira chakudya chauzimu nthaŵi ndi nthaŵi?

LACHIŴIRI masana, pa Nisani 11, mu 33 C.E., ophunzira a Yesu anam’patsa funso lomwe lili ndi tanthauzo kwambiri kwa ifeyo masiku ano. Anam’funsa kuti: “Chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] kwanu n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” Powayankha, Yesu anapereka ulosi wapadera kwambiri. Anatchula za nthaŵi yovuta kwambiri ya nkhondo, njala, zivomezi, ndiponso matenda. Ndipo zimenezi zinali kudzakhala ‘chiyambi [chabe] cha zowawa.’ Zinthu zinali kudzafika pena poipitsitsa kwambiri. Ankayembekezera zinthu zochititsa mantha kwambiri!​—Mateyu 24:3, 7, 8, 15-22; Luka 21:10, 11.

2 Kuchokera mu 1914, mbali zambiri za ulosi wa Yesu zakwaniritsidwa. Anthu akuvutika kwambiri ndi “zowawa.” Komabe, Akristu oona sakufunika kuchita mantha. Yesu analonjeza kuti adzawathandiza powapatsa chakudya chauzimu. Poti Yesu ali kumwamba tsopano, kodi wakonza zotani kuti ifeyo padziko lapansi pano tizilandira chakudya chathu chauzimu?

3. Kodi Yesu anakonza zotani kuti tizilandira “zakudya panthaŵi yake”?

3 Yesu mwiniyo anapereka yankho la funso limenelo. Ali m’kati mopereka ulosi wake waukuluwu, iye anafunsa kuti: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anam’khazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya panthaŵi yake?” Kenako anati: “Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzam’peza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzam’khazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyu 24:45-47) Zoonadi, panali kudzakhala “kapolo” amene anadzapatsidwa ntchito yopereka chakudya chauzimu, “kapolo” amene anali kudzakhala wokhulupirika ndi wanzeru. Kodi kapolo ameneyo anali munthu mmodzi yekha, anthu osiyanasiyana omwe ankalandirana ntchitoyi, kapena osati zimenezi? Tikufuna kudziŵa yankho lake popeza kuti kapolo wokhulupirikayu akupereka chakudya chauzimu chofunika kwambiri.

Munthu Mmodzi Kapena Kagulu?

4. Kodi tikudziŵa bwanji kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” sangakhale munthu mmodzi?

4 “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ameneyu sangakhale munthu mmodzi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kapoloyu anayamba kupereka chakudya chauzimu kale kwambiri, m’zaka 100 zoyambirira, ndipo malinga ndi Yesu, kapoloyu anali kudzakhala akuchitabe zimenezi pamene Mbuye anafika mu 1914. Apo pakanafunika kuti munthu mmodzi akhale akutumikira mokhulupirika zaka 1,900. Ngakhale Metusela sanakhale nthaŵi yaitali choncho!​—Genesis 5:27.

5. Fotokozani chifukwa chomwe mawu akuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” saimira Mkristu aliyense payekhapayekha.

 5 Ndiyeno, kodi mawu akuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” angaimire Mkristu aliyense payekha? Ndi zoona kuti Akristu onse afunika kukhala okhulupirika ndiponso anzeru; komabe n’zoonekeratu kuti Yesu anali ndi mfundo ina m’maganizo pamene ankanena za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Kodi tikudziŵa bwanji zimenezo? Chifukwa iye ananena kuti ‘pakufika mbuye’ adzakhazika kapoloyu ‘woyang’anira zinthu zake zonse.’ Kodi zingatheke bwanji kuti Mkristu aliyense payekha apatsidwe ntchito yoyang’anira chilichonse, zinthu “zonse” za Mbuye? Sizingatheke!

6. Kodi Mulungu anakonza zoti mtundu wa Israyeli uzigwira ntchito motani monga “mtumiki,” kapena kuti “kapolo” wake?

6 Motero mfundo yokha yomveka pankhaniyi ndi yoti Yesu anali kunena za kagulu ka Akristu kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Kodi n’zothekadi kuti mawuŵa amanena za gulu lonse la kapolo? Inde. Zaka mazana asanu ndi aŵiri Kristu asanabwere, Yehova anatcha mtundu wonse wa Israyeli kuti “mboni zanga” ndi ‘mtumiki wanga, amene ndakusankha.’ (Yesaya 43:10) Aliyense wa mu mtundu wa Israyeli kuchokera mu 1513 B.C.E., pamene Chilamulo cha Mose chinaperekedwa, mpaka kudzafika pa Pentekoste mu 33 C.E. anali m’gulu la mtumikiyu. Aisrayeli ambiri sankagwira nawo mwachindunji ntchito yoyang’anira zochita za mtunduwo kapena kuyang’anira ntchito youdyetsa mwauzimu. Yehova ankagwiritsa ntchito mafumu, oweruza, aneneri, ansembe, ndi Alevi kuchita ntchito zimenezo. Komabe, monga mtundu, Israyeli anafunika kuimira ufumu wa Yehova ndi kumutamanda m’mitundu ya anthu. Mwisrayeli aliyense anafunika kukhala mboni ya Yehova.​—Deuteronomo 26:19; Yesaya 43:21; Malaki 2:7; Aroma 3:1, 2.

“Mtumiki” Achotsedwa Ntchito

7. N’chifukwa chiyani mtundu wakale wa Israyeli sunayenererenso kukhala “mtumiki” wa Mulungu?

7 Popeza kuti Israyeli anali “mtumiki” wa Mulungu zaka mazana ambiri zapitazo, kodi analinso kapolo amene Yesu ananena? Ayi, chifukwa chakuti Israyeli wakale anakhala wosakhulupirika komanso wopanda nzeru, zomwe zinali zomvetsa chisoni kwambiri. Paulo anafotokoza mwachidule zimene zinachitika pamene anagwira mawu omwe Yehova anauza mtunduwo, kuti: “Dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu.” (Aroma 2:24) Inde, mbiri yaitali ya kupanduka kwa Israyeli inafika pachimake penipeni pamene iwo anakana Yesu, ndipo apa m’pamene Yehova anawakana.​—Mateyu 21:42, 43.

8. Kodi “mtumiki” anasankhidwa liti kuti aloŵe m’malo mwa Israyeli, ndipo zinachitika bwanji?

8 Kusakhulupirika kwa “mtumiki,” Israyeli, sikunatanthauze kuti olambira okhulupirika sadzalandiranso chakudya chauzimu mpaka kalekale. Pa Pentekoste mu 33 C.E., patatha masiku 50 kuchokera pa kuukitsidwa kwa Yesu, mzimu woyera unathiridwa pa ophunzira ake 120 omwe anasonkhana m’chipinda china chapamwamba mu Yerusalemu. Nthaŵi imeneyo, panabadwa mtundu watsopano. Moyenerana ndi zimenezi, kubadwa kwake kunalengezedwa pamene anthu a mtunduwu molimba mtima anayamba kuuza anthu mu Yerusalemu “zazikulu za Mulungu.” (Machitidwe 2:11) Motero, mtundu watsopanowo, womwe ndi wauzimu, unakhala “mtumiki” amene akanalengeza ulemerero wa Yehova kwa mitundu ya anthu ndi kupereka chakudya panthaŵi yake. (1 Petro 2:9) Ndipo m’poyenera kuti mtunduwu  unayamba kutchedwa kuti “Israyeli wa Mulungu.”​—Agalatiya 6:16.

9. (a) Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndani? (b) Kodi “banja” ndani?

9 Aliyense wa “Israyeli wa Mulungu” ndi Mkristu wodzipatulira ndiponso wobatizidwa, anadzozedwa ndi mzimu woyera ndipo akuyembekezera kupita kumwamba. Motero, mawu akuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amaimira anthu onse a mtundu wodzozedwa wauzimu umenewo monga kagulu omwe ali ndi moyo padziko lapansi pano panthaŵi ina iliyonse kuchokera mu 33 C.E. mpaka panopo. Zimenezi zili monga momwe Mwisrayeli aliyense yemwe anakhala ndi moyo nthaŵi ina iliyonse kuchokera mu 1513 B.C.E. mpaka pa Pentekoste mu 33 C.E. ankakhalira mbali ya gulu la mtumiki Chikristu chisanayambe. Komano, “banja” lomwe limalandira chakudya chauzimu kuchokera kwa kapoloyu ndani? M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Mkristu aliyense ankayembekezera kupita kumwamba. Motero, nalonso banjalo linali Akristu odzozedwa, osati monga kagulu koma aliyense payekhapayekha. Onse, kuphatikizapo amene anali ndi maudindo mu mpingo, ankafunika kudya chakudya chauzimu chochoka kwa kapoloyo.​—1 Akorinto 12:12, 19-27; Ahebri 5:11-13; 2 Petro 3:15, 16.

“Kwa Munthu Aliyense Ntchito Yake”

10, 11. Kodi tikudziŵa bwanji kuti si onse a kagulu ka kapolo amene ali ndi ntchito yofanana?

10 Ngakhale kuti “Israyeli wa Mulungu” ndi kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndipo kali ndi ntchito yoti kagwire, aliyense wa kaguluka alinso ndi ntchito yakeyake. Tikumvetsa zimenezi ndi mawu a Yesu a pa Marko 13:34. Iye anati: ‘Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamulira wapakhomo adikire.’ Motero aliyense wa kagulu ka kapoloka anapatsidwa ntchito​—kuti achulukitse zinthu zapadziko lapansi za Kristu. Aliyense amagwira ntchito yake mogwirizana ndi nzeru zake ndiponso mipata yomwe ali nayo.​—Mateyu 25:14, 15.

11 Komanso mtumwi Petro anauza Akristu odzozedwa a m’nthaŵi yake kuti: ‘Monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu.’ (1 Petro 4:10) Motero odzozedwawo ali ndi udindo wotumikirana pogwiritsa ntchito mphatso zomwe Mulungu anawapatsa. Komanso, mawu a Petro akusonyeza kuti si Akristu onse amene angakhale ndi nzeru, ntchito, kapena mautumiki ena apadera ofanana. Komabe, aliyense wa kagulu ka kapoloka akanathandiza mwanjira inayake kuti mtundu wauzimuwo ukule. Motani?

12. Kodi aliyense wa kagulu ka kapolo, kaya mwamuna kapena mkazi, anathandiza bwanji kuti gulu la kapololi likule?

12 Choyamba, aliyense anafunika kukhala mboni ya Yehova, kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Yesaya 43:10-12; Mateyu 24:14) Atangotsala pang’ono kukwera kumwamba, Yesu analamula ophunzira ake onse okhulupirika, amuna  pamodzi ndi akazi omwe, kuti akhale aphunzitsi. Anati: ‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.’​—Mateyu 28:19, 20.

13. Kodi odzozedwa onse anali ndi mwayi wogwira nawo ntchito iti?

13 Ophunzira atsopano atapezeka, ankafunika kuwaphunzitsa bwinobwino kuti asunge zinthu zonse zomwe Kristu anali atalamulira ophunzira ake. M’kupita kwa nthaŵi, anthu omwe ankalabadira anayenerera kukhala ophunzitsa ena. Chakudya chauzimu chopatsa thanzi chinkaperekedwa kwa anthu a m’mitundu yambiri omwe m’kupita kwa nthaŵi anadzakhala a kagulu ka kapolo. Akristu onse odzozedwa, amuna ndi akazi, anagwira nawo ntchito yopanga ophunzira. (Machitidwe 2:17, 18) Ntchito imeneyi inali yoti idzapitirira kuchokera panthaŵi yomwe kapoloyu anayamba kugwira ntchito yake mpaka mapeto a nthaŵi ya pansi pano.

14. Kodi ndani okha anapatsidwa ntchito yophunzitsa mu mpingo, ndipo akazi odzozedwa omwe anali okhulupirika ankamva bwanji ndi zimenezo?

14 Odzozedwa ongobatizidwa kumene anakhala mbali ya kapoloyu, ndipo mosaganizira kuti ndani anawaphunzitsa poyambirira, iwo ankalandiranso malangizo kuchokera kwa anthu a mu mpingo omwe anali oyenerera mwa Malemba kutumikira monga akulu. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:6-9) Motero amuna oikidwa ameneŵa anali ndi mwayi wothandiza nawo mwapadera kuti mtunduwo ukule. Akazi odzozedwa achikristu omwe anali okhulupirika sanakhumudwe poona kuti amuna okha achikristu ndiwo anali kupatsidwa ntchito yophunzitsa mu mpingo. (1 Akorinto 14:34, 35) M’malomwake anali kusangalala kuti akupindula chifukwa cha ntchito yaikulu ya amuna a mu mpingo ndipo anali kuyamikira kwambiri ntchito zimene akazi akanatha kugwira, kuphatikizapo ntchito youza ena uthenga wabwino. Alongo odzozedwa omwe ndi achangu masiku ano amasonyezanso kudzichepetsa koteroko, kaya akulu akhale odzozedwa kapena ayi.

15. Kodi njira imodzi yaikulu yomwe chakudya chauzimu chinkapezekera m’zaka 100 zoyambirira inali iti, ndipo ndani anali kutsogolera pogaŵa chakudyacho?

15 Chakudya chauzimu chomwe chinali chofunika kwambiri chomwe chinkaperekedwa m’zaka 100 zoyambirira chinkachokera mwachindunji m’makalata a atumwi ndi ophunzira ena omwe anali kutsogolera. Makalata omwe iwo analemba​—makamaka amene ali m’mabuku 27 ouziridwa omwe amapanga Malemba Achigiriki Achikristu​—ankatumizidwa kumipingo ndipo mosakayikira zinthu zomwe akulu m’mipingoyo ankaphunzitsa zinkachokera m’makalatawo. Mwanjira imeneyi, oimira kapolo ankagaŵira mokhulupirika chakudya chauzimu chochuluka kwa Akristu oona mtima. Kagulu ka kapolo ka m’zaka 100 zoyambirira kanagwira mokhulupirika ntchito yomwe kanapatsidwa.

‘Kapoloyu’ Patatha Zaka Pafupifupi 1,900

16, 17. Kodi kagulu ka kapolo kanasonyeza motani kuti kanali kokhulupirika pogwira ntchito yake m’zaka zodzafika mu 1914?

16 Nanga bwanji masiku ano? Kukhalapo kwa Yesu kutayamba mu 1914, kodi iye anapeza kagulu ka Akristu odzozedwa omwe anali kupereka mokhulupirika chakudya panthaŵi yake? Inde, anatero. Kaguluka kanadziŵika bwino chifukwa cha zipatso zabwino zomwe kanali kutulutsa. (Mateyu 7:20) Kuchokera nthaŵi imeneyo, mbiri yasonyeza kuti kagulu kake n’komweko ndithu.

17 Pamene Yesu ankafika, anthu pafupifupi 5,000 a kaguluka anali kalikiliki kufalitsa choonadi cha Baibulo. Antchito anali ochepa, koma kapoloyu anagwiritsa ntchito njira zingapo zatsopano kuti afalitse uthenga wabwino. (Mateyu 9:38) Mwachitsanzo, analinganiza zoti maulaliki a nkhani za m’Baibulo asindikizidwe m’nyuzipepala pafupifupi 2,000. Mwanjira imeneyi choonadi cha Mawu a Mulungu chinafika panthaŵi imodzi kwa anthu zikwi zambiri oŵerenga nyuzipepalazo. Kuwonjezera apo, anakonza pulogalamu ya maola asanu ndi atatu yophatikiza zithunzi zosayenda zakalala ndi zithunzi zoyenda. Mwanjira yatsopanoyi, uthenga wa Baibulo, kuyambira pa chiyambi cha Chilengedwe mpaka mapeto a Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu, unafika kwa anthu oposa mamiliyoni asanu ndi anayi a m’makontinenti atatu. Njira inanso yomwe  anagwiritsa ntchito inali mabuku. Mwachitsanzo, mu 1914, makope 50,000 a magazini ino anasindikizidwa.

18. Kodi ndi liti pamene Yesu anakhazika kapolo kukhala woyang’anira zinthu zake zonse, ndipo chifukwa chiyani?

18 Inde, pamene Mbuye anafika, anapeza kapolo wake wokhulupirika akuyesetsa kwambiri kudyetsa banja komanso kulalikira uthenga wabwino. Maudindo akuluakulu tsopano anali kumuyembekezera kapoloyu. Yesu anati: “Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzam’khazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyu 24:47) Yesu anachita izi mu 1919, kapoloyu atatha kuyesedwa. Komano, n’chifukwa chiyani “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ameneyu analandira maudindo akuluakulu? Chifukwa chakuti zinthu za Mbuye zinali zitachuluka. Yesu analandira ufumu mu 1914.

19. Fotokozani mmene zosoŵa zauzimu za a “khamu lalikulu” zakhala zikusamalidwira.

19 Kodi ndi zinthu zotani zomwe Mbuye wongolongedwa kumene Ufumuyo anakhazika kapolo wake wokhulupirika kuti ayang’anire? Zinthu zake zonse zauzimu zomwe zili padziko lapansi pano. Mwachitsanzo, patatha zaka makumi aŵiri kuchokera pamene Kristu anaikidwa pampando wachifumu mu 1914, panadziŵika kuti pali “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.” (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Aŵa sanali anthu odzozedwa a “Israyeli wa Mulungu,” anali amuna ndi akazi oona mtima oyembekeza kudzakhala padziko lapansi, omwe ankakonda Yehova ndiponso ankafuna kumutumikira monga momwe odzozedwa anali kuchitira. Pochita zimenezi, iwo ananena kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Akristu ongobatizidwa chakumeneŵa anali kudya chakudya chofanana ndi chomwe banja la odzozedwa linkadya, ndipo magulu aŵiriŵa akhala akudyera limodzi chakudya chauzimu kuchokera nthaŵi imeneyo. Awatu ndi madalitso aakulu kwambiri kwa a “khamu lalikulu”!

20. Kodi “khamu lalikulu” lachita zotani pa kuchulukitsa zinthu za Mbuye?

20 A “khamu lalikulu” anagwirizana mosangalala ndi a kagulu ka odzozedwa pantchito yolalikira uthenga wabwino. Pamene anali kulalikira, zinthu zapadziko lapansi za Mbuye zinawonjezeka, zomwe zinachititsa kuti maudindo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” awonjezeke. Pamene chiŵerengero cha anthu ofuna choonadi chinali kukula, panafunika kuwonjezera nyumba zosindikizira mabuku pofuna kuti pazikhala mabuku okwanira ofotokoza Baibulo. Maofesi a nthambi za Mboni za Yehova anali kukhazikitsidwa m’mayiko ambiri. Amishonale anatumizidwa “kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Kuchoka pa anthu ngati zikwi zisanu odzozedwa omwe analipo m’chaka cha 1914, chiŵerengero cha anthu otamanda Mulungu chawonjezeka kuposa pa sikisi miliyoni lerolino, ndipo ambiri mwa iwo ndi a “khamu lalikulu.” Inde, zinthu za Mfumu zawonjezeka kwambiri kuchokera pamene iye analongedwa Ufumu mu 1914!

21. Kodi m’phunziro lathu lotsatirali tidzapenda mafanizo aŵiri ati?

21 Zonsezi zikusonyeza kuti kapoloyu wakhala “wokhulupirika ndi wanzeru.” Atangotha kufotokoza za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” Yesu anapereka mafanizo aŵiri omwe anasonyeza kukhulupirika ndi nzeru kapena kuti kuchenjera: fanizo la anamwali ochenjera ndi ena opusa ndiponso fanizo la matalente. (Mateyu 25:1-30) Tili ndi chidwi chofuna kudziŵa zimenezi! Kodi mafanizo ameneŵa ali ndi tanthauzo lotani kwa ife lerolino? Tidzapenda funso limeneli m’nkhani yotsatirayi.

Kodi Mukuganiza Bwanji?

• Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndani?

• Kodi “banja” ndani?

• Kodi ndi liti pamene kapolo wokhulupirika anam’khazika woyang’anira zinthu zonse za Mbuye, ndipo n’chifukwa chiyani anam’khazika panthaŵi imeneyo?

• Kodi ndani athandiza kuchulukitsa zinthu za Mbuye m’zaka makumi angapo zapitazi, ndipo achita motani zimenezo?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 10]

Kagulu ka kapolo ka m’zaka 100 zoyambirira kanali kokhulupirika pantchito yake