Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chipembedzo Chimalimbikitsa Kuchita Zabwino Kapena Zoipa?

Kodi Chipembedzo Chimalimbikitsa Kuchita Zabwino Kapena Zoipa?

 Kodi Chipembedzo Chimalimbikitsa Kuchita Zabwino Kapena Zoipa?

“NDIKUTHOKOZA Chikristu chifukwa cha zimene chandichitira, ndipo ndikukhulupirira kuti anthu amene akhudzidwa ndi zochita zachikristu m’zaka 2000 zapitazi akuthokozanso chimodzimodzi,” amatero mawu oyamba m’buku lakuti Two Thousand Years​—The First Millennium: The Birth of Christianity to the Crusades.

Mawu oyamikira “Chikristu” ameneŵa ndi a Mngelezi wina wolemba mabuku ndi kuulutsa nkhani pa TV, Melvyn Bragg. Mawu ake akusonyeza maganizo a anthu ambiri padziko lapansi pano amene amaona kuti ndi pofunika kuyamikira kwambiri ndiponso kukhala wokhulupirika ku zipembedzo zosiyanasiyana. Iwo amakhulupirira kuti chipembedzo chawalimbikitsa kwambiri kuchita zabwino pamoyo wawo. Mwachitsanzo, wolemba mabuku wina ananena kuti Chisilamu “chalimbikitsa anthu kukhala moyo wotukuka kwambiri . . . [zimene] zathandiza dziko lonse.”

Kodi Chipembedzo Chimagwira Ntchito Yabwino Kapena Yoipa?

Komabe, zimene Bragg ananena kenako zikudzutsa funso lofunika kwambiri lonena ngati chipembedzo chalimbikitsadi anthu kuchita zabwino. Iye ananenanso kuti: “Chikristu chikufunikanso kuimbidwa mlandu.” Chifukwa chiyani? Iye anati: “Chifukwa cha kusagwirizana, zoipa, kuchita zinthu zauchinyama ndiponso umbuli wochita kufuna zimene n’zofalanso kwambiri ‘m’mbiri’ ya Chikristu.”

Anthu ambiri anganene kuti kusagwirizana, zoipa, kuchita zinthu zauchinyama, ndiponso umbuli wochita kufuna zakhala zikuchitika m’zipembedzo zambiri za m’dzikoli m’mbiri yonse. Iwo amaganiza kuti chipembedzo chimangooneka ngati chothandiza anthu​—chimanamizira kukhala cha makhalidwe abwino ndiponso choyera, koma kwenikweni chili chodzala ndi chinyengo ndi mabodza. (Mateyu 23:27, 28) “Palibe uthenga wina wofala m’mabuku athu ngati wakuti chipembedzo ndi chofunika kwambiri pankhani ya chitukuko,” limatero buku lakuti A Rationalist Encyclopædia. Ndipo limanenanso kuti: “Kunena zoona mawu ameneŵa si oona malinga ndi zimene zachitika m’mbiri.”

Masiku ano kungoŵerenga nyuzipepala ina iliyonse, mungapeze zitsanzo zambiri za atsogoleri a chipembedzo amene amalalikira za chikondi, mtendere, ndi chifundo koma amene amalimbikitsa udani ndiponso amagwiritsa ntchito dzina la Mulungu kuti nkhondo za nkhanza zimene amamenya zizioneka ngati zololeka. Sizodabwitsa kuti anthu ambiri amaona kuti chipembedzo nthaŵi zambiri chimalimbikitsa kuchita zoipa.

Kodi Zikanakhala Bwino Kukanapanda Chipembedzo?

Ena afika ponena zimene Mngelezi wina wafilosofi Bertrand Russell ananena, kuti zikanakhala bwino ngati nthaŵi ina “kukanakhala kopanda  chikhulupiriro china chilichonse cha chipembedzo.” Iwo amaganiza kuti kutha kwa chipembedzo ndiyo njira yokhayo imene ingathetseretu mavuto onse a anthu. Komabe, amaiŵala dala kuti anthu amene sapembedza angayambitse udani ndi kusagwirizana monganso mmene anthu opembedza amachitira. Wolemba nkhani zachipembedzo wina Karen Armstrong akutikumbutsa kuti: “Mwa zina, kupha anthu kwa Anazi kunasonyeza kuti mfundo zosakhala zachipembedzo [zingakhale] zowononga kwambiri monganso mmene ingakhalire nkhondo ina iliyonse yachipembedzo.”​—The Battle for God​—Fundamentalism in Judaism, Christianity and Islam.

Choncho kodi chipembedzo chimalimbikitsadi kuchita zabwino, kapena ndicho kwenikweni chikuchititsa mavuto a anthu? Kodi njira yothetsera mavuto ameneŵa ingakhale kungothetsa zipembedzo zonse? Onani zimene Baibulo likunena pamfundoyi mu nkhani yotsatira. Mudabwa yankho lake.