Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitonthozo kwa Ovutika

Chitonthozo kwa Ovutika

 Chitonthozo kwa Ovutika

KALE, amuna ndi akazi okhulupirika akavutika, ankapemphera kwa Mulungu ndi mtima wonse kuti awathandize. Komanso, ankachita zinthu zofunika kuti achepetse kuvutika kwawo, monga kugwiritsa ntchito luntha kuti athaŵe owazunza. Mwachitsanzo, kudalira Yehova pamodzi ndi kuyesetsa kunathandiza Davide kupirira mavuto ake. Bwanji ifeyo masiku ano?

Mukamavutika, mwachionekere mumachita zotheka kuti muthetse vuto lanulo. Mwachitsanzo, ngati muli paulova, kodi simumayesetsa kuyang’ana ntchito yabwino yoti ikuthandizeni pamodzi ndi banja lanu? (1 Timoteo 5:8) Kapena ngati mukudwala, kodi simumayang’ana chithandizo chokwanira cha mankhwala? N’zochititsa chidwi kuti Yesu, amene anapatsidwa mphamvu ndi Mulungu zochiritsira matenda alionse, anadziŵa kuti ‘odwala amafuna sing’anga.’ (Mateyu 9:12) Komabe, sikuti nthaŵi zonse mavuto anu adzachotsedwa; mungafunike kupitiriza kupirira nawo pamlingo wina wake.

Bwanji osauza Yehova Mulungu za vutolo m’pemphero? Mwachitsanzo, poyang’ana ntchito, kudalira Mulungu mwapemphero kungatithandize kukana chiyeso chilichonse choloŵa ntchito yosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Tidzapeŵanso ‘kusochera n’kutaya chikhulupiriro’ chifukwa cha dyera kapena kukonda ndalama. (1 Timoteo 6:10) Inde, posankha zochita pankhani zikuluzikulu zokhudza ntchito, banja kapena matenda, tingatsatire langizo la Davide lakuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”​—Salmo 55:22.

Pemphero lochokera pansi pamtima limatithandizanso kukhalabe okhazikika maganizo kuti mavuto athu asatithetse nzeru. Mtumwi Paulo yemwe anali Mkristu weniweni, analemba kuti: “M’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” Kodi pemphero lochokera pansi pamtima lingatitonthoze bwanji? “Mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Mtendere wa Mulungu ‘umapambana  chidziŵitso chonse.’ Choncho, ungatikhazikitse mtima m’malo pamene tikuvutika ndi maganizo. ‘Udzasunga mitima yathu ndi maganizo athu,’ motero udzatithandiza kupeŵa kuchita zinthu mopupuluma ndiponso mopanda nzeru, zimene zingawonjezere mavuto athu.

Pemphero likhozanso kusintha mmene zinthu zingayendere. Pamene mtumwi Paulo anali mkaidi ku Roma, modzichepetsa anapempha Akristu anzake kuti azimupempherera. N’chifukwa chiyani Paulo anawapempha zimenezi? Iye anawalembera kuti: ‘Ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumizidwe.’ (Ahebri 13:19) M’mawu ena tinganene kuti, Paulo ankadziŵa kuti nthaŵi yoti iye amasulidwe ingathe kusintha Yehova akamamva kulimbikira kupemphera kwa okhulupirira anzake.​—Filemoni 22.

Kodi pemphero lingasinthe zotsatira za vuto lathu? Likhoza kutero. Komabe, tiyenera kudziŵa kuti Yehova Mulungu nthaŵi zina sangayankhe mapemphero athu mmene tikufunira. Paulo anapemphera maulendo angapo za “munga m’thupi,” n’kutheka kuti anali matenda enaake. Koma, m’malo mochotsa vutolo Mulungu anauza Paulo kuti: “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m’ufoko.”​—2 Akorinto 12:7-9.

Choncho, vuto lathu silingachoke nthaŵi yomweyo. Komabe, udzakhala mwayi wathu kuti tisonyeze kudalira Atate wathu wakumwamba. (Yakobo 1:2-4) Titsimikize kuti ngakhale Yehova Mulungu atapanda kuchotsa vuto lathu, akhoza ‘kuika populumukirapo, kuti tikhoze kupirira.’ (1 Akorinto 10:13) N’zosangalatsa kuti Yehova amatchedwa “Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Mulungu akhoza kutipatsa zimene timafunika kuti tipirire, ndipo tikuyembekezera moyo wosatha.

Mawu a Mulungu, Baibulo, amalonjeza kuti Yehova “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Kodi n’zovuta kukhulupirira kuti nthaŵi ina dziko lidzakhala lopanda mavuto? Zingakhale choncho ngati mwazoloŵera kukhala movutika. Komabe, kumasuka ku mantha ndi mavuto ndi zimene Mulungu walonjeza, ndipo zimene amafuna zidzachitika ndithu.​—Yesaya 55:10, 11.

[Zithunzi patsamba 9]

Kuchoka povutika maganizo kufika polimbikitsidwa