Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungapezere Zinthu Zauzimu Zimene Mumafunikira

Mmene Mungapezere Zinthu Zauzimu Zimene Mumafunikira

 Mmene Mungapezere Zinthu Zauzimu Zimene Mumafunikira

“M’ZAKA khumi zapitazi, m’nyumba zogulitsira mabuku mwakhala mukupezeka mabuku oposa 300 amene amafotokoza mmene kukonda zinthu zauzimu kumathandizira kuntchito, kuyambira pa buku la Jesus CEO kufika pa buku la The Tao of Leadership,” linatero lipoti la U.S.News & World Report. Zimenezi zikungosonyeza kuti m’mayiko ambiri olemera, anthu ambiri akufuna malangizo auzimu pa moyo wawo. Pofotokozapo za nkhaniyi, magazini ya zamalonda  yakuti Training & Development, inati: “Nthaŵi ino pamene luso la zaumisiri likukhudza pafupifupi mbali iliyonse ya moyo wathu, tikufunafuna tanthauzo lenileni la moyo ndi cholinga chake, ndiponso tikufuna kukhala osangalala kwambiri.”

Koma kodi mungapeze kuti malangizo auzimu ogwira mtima? Kale, anthu ankapita ku zipembedzo kuti zikawathandize kupeza “tanthauzo lenileni” ndi “cholinga” cha moyo. Masiku ano, anthu ambiri asiya kudalira zipembedzo. Kafukufuku amene anachita kwa akuluakulu a makampani okwana 90 anapeza kuti “anthu amasiyanitsa kwambiri pakati pa chipembedzo ndi kukonda zinthu zauzimu,” inatero magazini ya Training & Development. Anthu amene anafunsidwa pa kafukufukuyo ankaona kuti chipembedzo ndi “chosalolera maganizo a ena ndiponso chogaŵanitsa,” pamene kukonda zinthu zauzimu “n’kopezeka ponseponse ndipo munthu aliyense akhoza kuchita zimenezo.”

Achinyamata ambiri m’mayiko amene sakonda kwenikweni zopembedza monga ku Australia, New Zealand, United Kingdom, ndi ku Ulaya, amaonanso kusiyana kotereku pa nkhani ya chipembedzo ndi kukonda zinthu zauzimu. Pulofesa Ruth Webber analemba m’magazini ya Youth Studies Australia kuti: “Achinyamata ambiri amakhulupirira Mulungu kapena chinthu chinachake champhamvu kuposa munthu koma saona kuti tchalitchi n’chofunika kapena kuti chingawathandize kusonyeza kukonda kwawo zinthu zauzimu.”

Chipembedzo Choona Chimalimbikitsa Kukonda Zinthu Zauzimu

Kukayikira zipembedzo kumeneku n’komveka. Zipembedzo zochuluka zikukhudzidwa kwambiri ndi nkhani zandale ndiponso zimachita chinyengo. Zili ndi mlandu wakupha kapena wovomereza kuphedwa kwa anthu osalakwa m’nkhondo zachipembedzo zambirimbiri. Komabe, pokana zipembedzo zimene zimachita zachinyengo, anthu ena alakwitsa mwa kukananso Baibulo, limene akuganiza kuti limavomereza makhalidwe oterowo.

Komatu, Baibulo limatsutsa chinyengo ndi makhalidwe oipa kapena kuti kusayeruzika. Yesu anauza atsogoleri achipembedzo a m’nthaŵi yake kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala mkatimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m’kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika.”​—Mateyu 23:27, 28.

Ndiponso Baibulo limalimbikitsa Akristu kusaloŵerera m’nkhani zandale. M’malo molimbikitsa anthu okhulupirira kuti aziphana, limalangiza kuti azikhala okonzeka kuferana. (Yohane 15:12, 13; 18:36; 1 Yohane 3:10-12) Chipembedzo choona chimene chimatsatira mfundo za m’Baibulo, m’malo mokhala “chosalolera maganizo a ena ndiponso chogaŵanitsa,” n’choti “munthu aliyense akhoza” kuloŵamo. Mtumwi Petro anati: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Baibulo Ndi Buku Lodalirika Limene Lingatithandize Kukhala ndi Moyo Wauzimu Wabwino

Baibulo limatiuza kuti anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu. (Genesis 1:26, 27) Ngakhale kuti zimenezi sizikutanthauza kuti anthu akufanana ndi mmene Mulungu amaonekera, zimatanthauza kuti anthu angathe kusonyeza makhalidwe a Mulungu, kuphatikizapo kukonda zinthu zauzimu.

Popeza zili choncho, m’pomveka kukhulupirira kuti Mulungu angatipatsenso njira yopezera zinthu zauzimu zimene timafunikira, pamodzinso ndi malangizo oyenera amene angatithandize kusiyanitsa zinthu zimene zingatipindulitse ndi zimene zingawononge moyo wathu wauzimu. Monga mmene Mulungu analengera matupi athu amene ali ndi mphamvu yotiteteza kumatenda yapamwamba kwambiri imene imalimbana ndi matenda ndi kutithandiza kukhala ndi thanzi labwino, anatipatsanso chikumbumtima, kapena kuti mawu a m’kati mwathu. Chikumbumtimachi chingatithandize kusankha zochita mwanzeru ndi kupeŵa kuchita zinthu zimene zingawononge thupi lathu ndi moyo wathu wauzimu. (Aroma 2:14, 15) Monga mmene tikudziŵira, mphamvu ya thupi lathu yotiteteza kumatenda kuti igwire ntchito yake, tiyenera kuidyetsa bwino. Mofanana ndi zimenezi, kuti chikumbumtima chathu chigwire ntchito yake, tifunika kuchidyetsa chakudya chabwino chauzimu.

Yesu pofotokoza za chakudya chimene chingatithandize kuti tikhale athanzi mwauzimu anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha,  koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Mawu a Yehova analembedwa m’Baibulo, ndipo “[a]pindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero.” (2 Timoteo 3:16) Motero, zili ndi ife kuchita khama kudya chakudya chauzimu choterocho. Tikadziŵa kwambiri Baibulo ndi kuyesetsa kugwiritsa ntchito mfundo zake za makhalidwe abwino pa moyo wathu, tidzapindulanso kwambiri mwauzimu ndiponso pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku.​—Yesaya 48:17, 18.

Kodi Pali Chifukwa Chilichonse Chochitira Khama?

N’zoona kuti zimafuna nthaŵi kuti tilimbitse thanzi lathu lauzimu mwa kuŵerenga Baibulo, ndipo zikuoneka kuti nthaŵi ikusoŵa kwambiri. Koma phindu limene timapeza pochita zimenezo n’chifukwa chokwanira chochitira khama. Tamvani zifukwa zimene akatswiri ena a ntchito zosiyanasiyana otanganidwa kwambiri afotokoza zosonyeza kuti kupatula nthaŵi kuti asamalire thanzi lawo lauzimu n’kofunika kwambiri kwa iwo.

Marina, yemwe ndi dokotala, anati: “Ndinali ndisanaganizire kwenikweni zokonda zinthu zauzimu mpaka pamene ndinayamba kugwira ntchito kuchipatala ndipo ndinayamba kumva chisoni kwambiri ndi mmene anthu ena anali kuvutikira. Ndiyeno ndinazindikira kuti ndiyenera kuvomereza kuti ndikufunikira zinthu zauzimu ndipo ndiyenera kuzipeza ngati ndikufuna kukhala wosangalala komanso kukhala ndi mtendere, popeza kutanganidwa ndiponso kusamalira mavuto a anthu ena kungakhale kolemetsa kwa munthu amene amagwira ntchito imene ndikugwira ineyi.

“Tsopano ndimaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kuphunzira kumeneku kumandithandiza kuonanso zochita ndi zolinga zanga moyenera ndipo kumaphunzitsa maganizo anga kuti ndizilingalira zinthu zabwino. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti moyo wanga ndiziuona moyenera. Ntchito imene ndikugwira imandisangalatsa kwambiri. Komabe, kuphunzira Baibulo n’kumene kwandithandiza kuti ndikhale ndi maganizo abwinopo, zimene zandithandiza kuchepetsa kuganizira zinthu zofooketsa, kuchepetsa nkhaŵa, ndiponso kukhala woleza mtima ndi wachifundo kwambiri kwa anthu. Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kwathandizanso ukwati wanga. Koposa zonsezi, ndadziŵa Yehova ndipo ndaonadi mzimu woyera ukugwira ntchito mwa ine ndipo zimenezi zachititsa moyo wanga kukhala watanthauzo.”

Nicholas, yemwe ndi katswiri wolemba mapulani omangira nyumba, anati: “Ndisanayambe kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinalibe chidwi ndi zinthu zauzimu. Cholinga changa chachikulu pa moyo chinali choti ndikhale wotsogola pantchito imene ndinasankha. Kuphunzira kwanga Baibulo kwandithandiza kuona kuti pali zinanso zofunika pa moyo ndipo kuchita zimene Yehova akufuna kungachititse munthu kupeza chimwemwe chenicheni ndiponso chokhalitsa.

“N’zoona kuti ntchito imene ndimagwira imandisangalatsadi, koma Baibulo ndi limene landiphunzitsa kufunika kokhala ndi moyo wosalira zambiri, mwa kuika maganizo pa zinthu zauzimu. Mwakuchita zimenezo, ine ndi mkazi wanga tapeŵa nkhaŵa zambiri zimene zimabwera chifukwa chokhala ndi moyo wokondetsa chuma. Tapezanso mabwenzi enieni ambiri mwa kucheza ndi anthu amene amakonda zinthu zauzimu pa moyo wawo mofanana ndi ifeyo.”

Vincent, yemwe ndi loya, anati: “Ntchito yabwino imene munthu  amagwira ikhoza kumamusangalatsadi, komabe ndaona kuti pali zambiri zimene zikufunika kuti munthu apeze chimwemwe ndikukhala wosangalala. Ndisanadziŵe zimene Baibulo limaphunzitsa pankhani imeneyi, ndikukumbukira kuti ndinkavutika mumtima poganizira kupanda pake kwa moyo, kuti anthu timabadwa, kukula, kukwatira kapena kukwatiwa, kugwira ntchito kuti tipeze zofunika pamoyo polera ana athu, kuwaphunzitsa anawo kuchitanso zomwezi, ndipo kenako kukalamba ndi kumwalira.

“Nditaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova m’pamene ndinapeza mayankho ogwira mtima a mafunso amene ndinali nawo okhudza cholinga cha moyo. Kuphunzira Baibulo kwandithandiza kudziŵa kuti Yehova ndi weniweni ndipo ndinayamba kumukonda kwambiri. Zimenezi zimandichititsa kukhalabe ndi thanzi labwino lauzimu pamene ndikuyesetsa kutsatira pa moyo wanga zimene ndikudziŵa kuti ndizo cholinga chake. Tsopano, ine ndi mkazi wanga tikusangalala kudziŵa kuti tikugwiritsa ntchito moyo wathu m’njira yosonyeza kuti uli ndi cholinga.”

Inunso moyo wanu ukhoza kukhala ndi cholinga ndiponso kukhala watanthauzo mwa kuphunzira Baibulo. Mboni za Yehova n’zokondwa kukuthandizani. Monga mmene anachitira Marina, Nicholas, ndi Vincent, mungapeze chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chophunzira za Yehova ndi zolinga zake, kwa anthu onse ndiponso kwa inu panokha. Mudzasangalala kupeza zinthu zauzimu zimene mumafunikira pakalipano komanso mudzakhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha pamene anthu adzakhala ndi thanzi langwiro. Anthu amene angakhale ndi chiyembekezo chimenechi ndi okhawo amene “amazindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.”​—Mateyu 5:3, NW.

Njira imodzi imene tingakulitsire kukonda zinthu zauzimu ndiyo kupemphera. Yesu anapatula nthaŵi kuti aphunzitse ophunzira ake mmene angapempherere ndipo anawapatsa pemphero limene nthaŵi zambiri limatchedwa Pemphero la Ambuye. Kodi pemphero limenelo lili ndi tanthauzo lotani kwa inu masiku ano? Kodi mungapindule nalo bwanji? Mupeza mayankho a mafunso ameneŵa m’nkhani ziŵiri zotsatirazi.

[Zithunzi patsamba 6]

Marina

[Zithunzi patsamba 7]

Nicholas

[Zithunzi patsamba 7]

Vincent