Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mitengo ya Mulungu Yadzala ndi Madzi”

“Mitengo ya Mulungu Yadzala ndi Madzi”

 Kukongola kwa Chilengedwe cha Yehova

“Mitengo ya Mulungu Yadzala ndi Madzi”

KODI munayamba mwaima m’nkhalango cheza cha dzuŵa chikuŵala m’mitengo italiitali? kodi munamva kaphokoso pamene mphepo inali kuwomba masamba?​—Yesaya 7:2.

M’madera ena padziko lapansi pano nthaŵi ina pachaka, masamba a mitengo yosiyanasiyana ofiira, achikasu, ndi amitundu ina amawala kwambiri. Inde, nkhalango imangooneka ngati ikuyaka moto. Izi zikugwirizana kwambiri ndi mawu akuti: “Imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m’menemo.”​—Yesaya 44:23. *

Pafupifupi gawo limodzi mwa magawo atatu a Dziko Lapansili ndi nkhalango. Mwa njira yodabwitsa kwambiri, nkhalango ndi zamoyo zambiri zopezekamo zimalemekeza Wolinganiza ndi Mlengi wawo, Yehova Mulungu. Wamasalmo wouziridwa anaimba kuti: “Lemekezani Yehova . . . mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse.”​—Salmo 148:7-9.

“Mitengo ndi yofunika kwambiri pamoyo wa munthu ndiponso kuti azisangalala,” limatero buku lakuti The Trees Around Us. Nkhalango zimateteza, zimasunga, ndipo zimathandiza kuti madzi a anthu akhale abwino. Mitengo imathandizanso mpweya kukhala wabwino. Mwa njira yodabwitsa kwambiri imene mitengo imapangira chakudya yotchedwa photosynthesis, maselo a m’masamba amasintha mpweya wa carbon dioxide, madzi, mchere wa m’nthaka, ndiponso kuwala kwa dzuŵa kukhala zakudya zake ndiponso mpweya wa oxygen.

Nkhalango ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha chinthu chokongola ndi chopangidwa mwaluso. Nthaŵi zambiri mitengo ikuluikulu ndi imene imakhala yochititsa chidwi kwambiri m’nkhalango. M’mitengo imeneyi mumapezekanso zomera zopanda maluŵa, ndere, ziyangoyango, zithukuluzi, ndi zitsamba. Zomera zimenezi zimadalira mitengo, zimamera m’mithunzi ya mitengo ndi kugwiritsa ntchito chinyezi chopezeka pa mitengoyo.

Nkhalango zina zimene zili ndi mitengo yoyoyola masamba, mitengo ya pa ekala imodzi ya nkhalangoyo imatha kuyoyola masamba okwana teni miliyoni chakumapeto kwa chaka. N’chiyani chimachitikira masambawo? M’kupita kwanthaŵi zomera monga bowa, nyongolotsi, ndi tizilombo tina zimasintha zinthu zonsezi kukhala manyowa, zimene zimathandiza kwambiri kuti dothi likhale lachonde. Inde, palibe chimene chimawonongeka pamene ogwira ntchito mwakachetechete ameneŵa akukonza dothi kuti pamere zinthu zatsopano.

Kunsi kwa masamba oyoyokawo, dothi la m’nkhalangoyo limakhala ndi zamoyo zambiri. Malinga ndi buku lakuti The Forest, “zinthu zamoyo zoposa 1,350 . . . zingapezeke pamalo aakulu masentimita 30 mbali zonse zinayi ndi akuya masentimita 2.5, osaŵerengera zamoyo zimene sitingazione ndi maso athu zimene tingazipeze padothi lililonse lodzaza dzanja.” Komanso, m’nkhalango mumakhala nyama zokwawa, mbalame, ndi nyama zimene zimayamwitsa. Kodi ndani ayenera kulandira ulemu chifukwa cha zinthu zokongola ndi zosiyanasiyana zimenezi? Moyenerera Mlengi wa zimenezi anati: “Zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, ndi ng’ombe za pa mapiri zikwi.”​—Salmo 50:10.

Nyama zina zinalengedwa ndi luso lochititsa chidwi kwambiri lotha kubisala nthaŵi yaitali ndiponso kukhalabe ndi moyo panthaŵi yozizira kwambiri komanso panthaŵi yachilala. Komabe, si nyama zonse zimene zimabisala. Ngakhale m’katikati mwa chisanu, mutha kuona gulu la mbawala zikuthamangathamanga m’munda. Mbawala sizibisala kapena kusunga chakudya, koma zimafunafuna chakudya, kubudula nthambi zanthete ndi zophukira kumene, monga momwe mukuonera pa chithunzichi chomwe ndi cha ku Germany.

Malemba amatchulatchula zomera. Malinga  n’kuŵerenga kwina, Baibulo limatchula mitundu pafupifupi 130 ya zomera, kuphatikizapo mitundu 30 ya mitengo. Poona kuchuluka kwa maulendo amene Baibulo limatchula zomera, katswiri wina wa zomera Michael Zohary anati: “Ngakhale m’mabuku wamba, palibe buku limene limatchula kwambiri kugwirizana kwa zomera ndi mbali zosiyanasiyana za moyo monga mmene limachitira Baibulo.”

Mitengo ndiponso nkhalango ndi mphatso zabwino kwambiri zochokera kwa Mlengi wachikondi. Ngati tinakhala m’nkhalango nthaŵi ina, ndithudi tingavomereze mawu a wamasalmo akuti: “Mitengo ya Mulungu yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebano imene anaioka; m’mwemo mbalame zimanga zisa zawo.”​—Salmo 104:16, 17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Kalendala ya 2004 ya Mboni za Yehova, January/​February.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 9]

Umodzi mwa mitengo yazipatso yosangalatsa kwambiri ku Middle East ndi mtengo wa mchiwu. Kumayambiriro kwa chaka​—kuposa pafupifupi mitengo ina yonse​—umagalamuka ku tulo take. Ahebri akale ankatcha mtengo wa mchiwu kuti wogalamuka, chifukwa chakuti umayambirira kuchita maluŵa. Mtengowu kwenikweni umaoneka kuti wagalamuka uli ndi maluŵa ofiirira kapena oyera.​—Mlaliki 12:5.

Pa mitundu ya mbalame pafupifupi 9,000 yomwe ikudziŵika, mitundu pafupifupi 5,000 ili m’gulu la mbalame zoimba. Nyimbo zawo zimapangitsa kuti m’katikati mwa nkhalango musakhale bata. (Salmo 104:12) Mwachitsanzo, nyimbo ya timba ndi yosangalatsa kwambiri. Mbalame zotchedwa mourning warbler, ngati imene mukuiona pachithunzipa, ndi zoimba ndipo n’zanthenga zokongola kwambiri zotuwa, zachikasu, ndi mtundu wom’kera kobiriŵira.​—Salmo 148:1, 10.

[Chithunzi patsamba 9]

Nkhalango ya ku Normandy, ku France