Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru?

Kodi Mungatani Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru?

 Kodi Mungatani Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru?

SOLOMO, mfumu ya ku Israyeli wakale, anati: “Wanzeru amve, nawonjezere kuphunzira.” Ambirife nthaŵi ina sitinasankhe bwino zochita chifukwa chakuti sitinamvere malangizo a anthu ena.​—Miyambo 1:5.

Patapita nthaŵi, mawu a Solomo amenewo analembedwa m’Baibulo, pamodzi ndi ina mwa “miyambo zikwi zitatu” imene iye analemba. (1 Mafumu 4:32) Kodi tingapindule mwa kudziŵa komanso kumvera miyambi yake yanzeruyo? Inde, tingapindule. Imatithandiza “kudziŵa nzeru ndi mwambo; kuzindikira mawu ozindikiritsa; kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika.” (Miyambo 1:2, 3) Tiyeni tikambirane mfundo za m’Baibulo zisanu zimene zingatithandize kusankha zochita mwanzeru.

Ganizirani Zotsatira Zanthaŵi Yaitali

Zina zimene timasankha kuchita zimakhala ndi zotsatira zazikulu. Chotero, yesani kuoneratu kuti zimenezi zidzakhala zotani. Peŵani mapindu anthaŵi yomweyo kukulepheretsani kuona zotsatira zopweteka zimene zingakhalepo kwanthaŵi yaitali. Miyambo 22:3 imachenjeza kuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”

Zingakhale zothandiza kulemba pa pepala zotsatira zanthaŵi yomweyo ndiponso zanthaŵi yaitali zimene zingakhalepo. Zotsatira zanthaŵi yomweyo za ntchito inayake zingakhale malipiro abwino ndiponso ntchito yosangalatsa. Koma kodi zotsatira zanthaŵi yaitali zingaphatikizepo kuloŵa ntchito yopanda tsogolo lenileni? Kodi m’kupita kwa nthaŵi mudzafunika kusamukira kwinakwake chifukwa cha ntchitoyo, mwina kutali ndi mabwenzi anu kapena banja lanu? Kodi idzakupangitsani kukhala m’malo oipa kapena ingakhale yosasangalatsa kwambiri moti ingakupangitseni kukhala wokhumudwa kwambiri? Onani ubwino ndi kuipa kwake, ndiyeno onani kuti zofunika kwambiri n’ziti.

Osapupuluma

Sitingasankhe zochita mwanzeru ngati tisankha mopupuluma. Miyambo 21:5 imachenjeza kuti: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphaŵi.” Mwachitsanzo, achinyamata amene ali m’chikondi chongotengeka maganizo sayenera kupupuluma kumanga banja. Apo phuluzi, adzaona zimene William Congreve, wolemba maseŵero achingelezi m’zaka za m’ma 1700 ananena, kuti: “Ukafulumira kuloŵa m’banja, umadzanong’oneza bondo pambuyo pake.”

Koma, kusapupuluma pochita zinthu tisakusokoneze ndi kuzengereza. Zina zimene timasankha kuchita n’zofunika kwambiri moti ndi nzeru kuzichita mofulumira momwe tingathere. Kuzengereza popanda chifukwa chenicheni kungawonongetse zinthu zathu zambiri kapena za  ena. Kuzengereza posankha zochita kungakhale kusankha zochita pakokha​—mwinanso kopanda nzeru.

Mverani Malangizo

Popeza palibe zochitika ziŵiri zofanana ndendende, anthu aŵiri nthaŵi zonse sangasankhe zochita zofanana pamene ali ndi vuto lofanana. Komabe, zimathandiza kumva mmene ena anachitira ndi nkhani zofanana ndi zathuzo. Afunseni mmene panopo amaonera zimene anasankha kuchitazo. Mwachitsanzo, posankha ntchito, funsani amene ali kale pa ntchito ngati imeneyo kuti akuuzeni ubwino ndi kuipa kwake. Kodi apindulanji ndi zimene anasankhazo, ndipo kodi apeza mavuto otani kapena ndi ngozi zotani zimene zingakhalepo?

Timachenjezedwa kuti: “Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.” (Miyambo 15:22) N’zoona kuti pofunsa malangizo ndiponso pophunzirapo pa zimene ena akumana nazo, tiyenera kuchita zimenezo tikudziŵa bwinobwino kuti pamapeto pake ifeyo patokha ndi amene tiyenera kusankha choyenera kuchita ndiponso kudziŵa kuti sitingadzaimbe mlandu munthu wina ngati chinachake chitalakwika.​—Agalatiya 6:4, 5.

Mverani Chikumbumtima Chophunzitsidwa Bwino

Chikumbumtima chingatithandize kusankha zochita mogwirizana ndi mfundo zazikulu zimene tinasankha kuzitsatira pamoyo wathu. Kwa Mkristu izi zikutanthauza kuphunzitsa chikumbumtima chake kutsatira maganizo a Mulungu. (Aroma 2:14, 15) Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:6) N’zoona kuti pankhani zina anthu aŵiri​—onse a chikumbumtima chophunzitsidwa bwino​—angakhale ndi maganizo osiyana ndipo pachifukwa chimenechi angasankhe zochita zosiyana.

Komabe, munthu amene ali ndi chikumbumtima chophunzitsidwa bwino sangachite zimenezi ngati zochitazo n’zoletsedwa mwachidunji m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, chikumbumtima chimene sichinaphunzitsidwe mfundo za m’Baibulo chingalole mwamuna ndi mkazi kuloŵana asanakwatirane pofuna kuyesa ngati ali oyenererana. Angaganize kuti asankha mwanzeru, n’kumati zimenezi ziwathandiza kupeŵa kupupuluma kumanga banja ndi munthu wosayenerana naye. Chikumbumtima chawo sichingawatsutse. Komabe, aliyense amene ali ndi maganizo ofanana ndi a Mulungu pankhani ya kugonana ndi ukwati sangasankhe kuchita zinthu zosakhalitsa ndiponso zoipa ngati zimenezo.​—1 Akorinto 6:18; 7:1, 2; Ahebri 13:4.

Onani Mmene Zosankha Zanu Zikhudzire Ena

Nthaŵi zambiri, zimene mumasankha kuchita zimakhudza anthu ena. Choncho musasankhe dala zinthu zoipa​—ngakhale zopusa​—zimene zingasokoneze ubwenzi wanu wamtengo wapatali ndi anthu ena ndiponso achibale kapenanso, koposa zonsezi, ndi Mulungu. Miyambo 10:1 imati: “Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.”

Komanso, dziŵani kuti nthaŵi zina n’kofunika kusankha mabwenzi. Mwachitsanzo, mungasankhe kusiya maganizo achipembedzo amene tsopano mukudziŵa kuti sagwirizana ndi Malemba. Kapena mungasankhe kusintha kwambiri umunthu wanu chifukwa chakuti mukufuna kutsatira mfundo za Mulungu zimene tsopano mwazilandira.  Mabwenzi ndi achibale anu ena sangasangalale ndi zimene mwasankha kuchita, koma chilichonse chimene mwasankha kuchita chomwe chili chokondweretsa Mulungu n’chabwino.

Sankhani Mwanzeru Chinthu Chofunika Kwambiri

Anthu ambiri sadziŵa kuti aliyense masiku ano akufunika kusankha pakati pa moyo ndi imfa. Aisrayeli akale ali m’malire mwa Dziko Lolonjezedwa mu 1473 B.C.E. anafunika kuchitanso zomwezo. Mose monga wom’lankhulira Mulungu anawauza kuti: “Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira iye, pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.”​—Deuteronomo 30:19, 20.

Ulosi wa m’Baibulo ndiponso momwe Baibulo limafotokozera zikusonyeza kuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” ndiponso kuti “zochitika padzikoli zikusintha.” (2 Timoteo 3:1; 1 Akorinto 7:31, NW) Kusintha kumene analoseraku kudzafika pachimake pa kuwonongedwa kwa maboma a anthu opanda makhalidwe abwino ameneŵa, n’kuloŵedwa m’malo ndi dziko latsopano lolungama la Mulungu.

Tili pakhomo penipeni padziko latsopano limenelo. Kodi mudzaloŵamo kuti musangalale ndi moyo wosatha padziko lapansi lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu? Kapena mudzachotsedwa m’dziko lapansi pamene dongosolo la Satanali likuchotsedwa? (Salmo 37:9-11; Miyambo 2:21, 22) Ndi udindo wanu kusankha zochita pakalipano, ndithudi kusankha pankhani ya moyo kapena imfa. Kodi mungakonde kukuthandizani kuti musankhe bwino, mwanzeru?

Kusankha moyo kumafunika kuphunzira kaye zimene Mulungu amafuna. Matchalitchi kwakukulukulu alephera kunena zinthu zofunika zimenezi molondola. Atsogoleri awo nthaŵi zambiri asokoneza anthu kukhulupirira mabodza ndiponso kuchita zinthu zosakondweretsa Mulungu. Alephera kufotokoza kufunika koti munthu aliyense payekha asankhe kulambira Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) N’chifukwa chake anthu ambiri sachita zimenezi. Koma onani zimene Yesu ananena: “Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.”​—Mateyu 12:30.

Mboni za Yehova zimasangalala kuthandiza anthu kuwadziŵa bwino Mawu a Mulungu. Nthaŵi zonse zimakambirana nkhani za m’Baibulo ndi munthu aliyense payekha kapena timagulu panthaŵi komanso malo abwino kwa anthuwo. Amene akufuna kupindula ndi makonzedwe ameneŵa ayenera kulankhula ndi Mboni za kumene akukhalako kapena kulembera kalata kwa amene amafalitsa Nsanja ya Olonda.

Inde, n’kutheka kuti ena akudziŵa kale zinthu zoyambirira zimene Mulungu amafuna. Mwinanso amakhulupirira kuti Baibulo n’loona komanso lodalirika. Komabe, ambiri a iwo akuzengereza kusankha zoti adzipatulire kwa Mulungu. Chifukwa? Pangakhale zifukwa zingapo.

Kodi mwina sadziŵa kufunika kochita zimenezo? Yesu ananena momveka bwino kuti: “Siyense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.” (Mateyu 7:21) Kudziŵa Baibulo kokha sikokwanira; m’pofunika kuchitapo kanthu. Mpingo woyambirira wachikristu unaika chitsanzo. Timaŵerenga za anthu ena a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino kuti: “Pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.” (Machitidwe 2:41; 8:12) Choncho, ngati munthu walandira Mawu a Mulungu mokwanira, wakhulupirira zimene akunena, ndipo moyo wake ukutsatira miyezo ya Mulungu, n’chiyani chingamulepheretse kubatizidwa posonyeza kudzipatulira kwake? (Machitidwe 8:34-38) Inde, kuti Mulungu amuvomereze, ayenera kuchita zimenezo mwa kufuna kwake ndiponso ndi mtima wosangalala.​—2 Akorinto 9:7.

Mwina ena amaona kuti sakudziŵa zambiri moti n’kupatulira moyo wawo kwa Mulungu.  Koma aliyense akamayamba kuchita chinthu chatsopano amakhala asakudziŵa zambiri. Kodi ndi katswiri uti amene anganene kuti pamene amayamba ntchito yake anali kudziŵa zimene akudziŵa panopo? Kusankha kutumikira Mulungu kumangofuna kudziŵa ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo ndi mfundo zake zamakhalidwe, ndiponso kufunitsitsa kutsatira zimenezo pamoyo.

Kodi ena amazengereza kusankha zimenezi kuopera kuti sadzakwanitsa? M’zinthu zambiri zimene anthu amachita, amadera nkhaŵa ndithu kuti akhoza kulephera kuzikwanitsa. Mwamuna amene akufuna kukwatira ndiponso kukhala ndi ana angadzione kuti sakwanitsa, koma kudzipereka kumam’limbikitsa kuchita zimene angathe. Mofananamo, mnyamata amene wapeza chilolezo choyendetsa galimoto angaope kuchita ngozi pamsewu makamaka ngati akudziŵa kuti madalaivala achinyamata ndi amene akuchita ngozi kwambiri kusiyana ndi achikulire. Komabe, kudziŵa zimenezi kungakhale kothandiza, kudzam’pangitsa kuyendetsa mosamala kwambiri. Kusakhala ndi chilolezo choyendetsera galimoto si njira yothetsera vutolo.

Sankhani Moyo!

Baibulo limasonyeza kuti ndale zamasiku ano, chuma, ndiponso dongosolo la chipembedzo lapadziko lonse ndi amene amalichirikiza posachedwapa achotsedwa padziko lapansi. Koma anthu amene mwanzeru asankha moyo ndiponso akuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezo adzatsala. Monga phata la anthu a dziko latsopano, adzathandiza kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso, monga mmene Mulungu anafunira pachiyambi. Kodi inuyo, molangizidwa ndi Mulungu, mudzagwira nawo ntchito yosangalatsa imeneyi?

Ngati ndi choncho, sankhani kuphunzira Mawu a Mulungu. Sankhani kuphunzira zimene Mulungu amafuna, zimene zimamusangalatsa. Sankhani kuzikwaniritsa. Koposa zonse, sankhani kuchita zimene mwasankhazo mpaka mapeto. Mwachidule tingoti, sankhani moyo!

[Zithunzi patsamba 4]

Osapupuluma posankha zinthu zazikulu

[Chithunzi patsamba 5]

Mverani malangizo posankha ntchito

[Zithunzi patsamba 7]

Amene pakalipano asankha kutumikira Mulungu adzathandiza kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso