Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Zanditsegula Maso!”

“Zanditsegula Maso!”

 Olengeza Ufumu Akusimba

“Zanditsegula Maso!”

DOROTA, mtumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova ku Poland anapita ndi mwana wake wamwamuna wa zaka 14 kuchipatala cha kusukulu kwa mwanayo kuti akamuyeze, zimene amachita nthaŵi ndi nthaŵi. Pa nthaŵi imene amamuyezayo, Janina, * dokotala wake, anafunsa Dorota ntchito zimene mwana wakeyo amagwira kunyumba.

Dorota anayankha kuti: “Mwana wanga amaphika chakudya chamadzulo cha banja lathu lonse la anthu asanu ndi m’modzi, ngati ine sindingathe kutero tsiku limenelo. Amakonzanso m’nyumba ndipo amathandiza kukonza zinthu zimene zaonongeka panyumbapo. Amakonda kuŵerenga. Amalimbikira kwambiri sukulu.”

“Mukunena zoona?” anadabwa Janina. “Ndatha zaka 12 ndikugwira ntchito kuno, koma sindinamvepo zinthu ngati zimenezi.”

Ataona kuti wapeza mpata woti angachitirepo umboni, Dorota anafotokoza kuti: “Makolo ambiri masiku ano amalephera kuphunzitsa ana awo moyenera. N’chifukwa chake ana awo nthaŵi zambiri amadziona ngati anthu osafunika.”

“Kodi mukudziŵa bwanji zinthu zonsezi?” anafunsa Janina. “Makolo ambiri sadziŵa zinthu zimenezi.”

“Baibulo ndi buku lamtengo wapatali limene limafotokoza zinthu ngati zimenezi,” anayankha Dorota. “Mwachitsanzo, lemba la Deuteronomo 6:6-9 limanena zoti, kuti munthu athe kuphunzitsa ana ake, choyamba ayenera kudziphunzitsa yekha. Kodi si zoona kuti tiyenera choyamba kukhulupirira mu mtima ndi m’maganizo mwathu zinthu zofunika zimene tikufuna kuti ana athunso akhulupirire?”

“Komadi eti!” anavomereza Janina. “Mukunenadi zoona!” Kenaka anam’funsa Dorota kuti afotokoze mmene Baibulo linam’thandizira polera ndi kuphunzitsa ana ake.

“Timaphunzira Baibulo mlungu uliwonse ndi ana athu,” anafotokoza Dorota. “Timagwiritsira ntchito buku lotchedwa Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza. * Kenaka analifotokoza bukulo ndipo anatchula zina mwa nkhani zimene limafotokoza.

“Zanditsegula maso!” anatero Janina. “Kodi ndingadzalione buku limenelo?”

Patatha ola limodzi, Dorota anabweretsa bukulo.

“Kodi muli chipembedzo chanji?” anafunsa Janina, kwinaku akuyang’anitsitsa zimene zinali m’bukulo.

“Ndine m’modzi wa Mboni za Yehova.”

“Kodi Mboni za Yehova zimachita bwanji zinthu ndi anthu amene sali m’chipembedzo chawo?”

“Monga mmene ndachitira ine kwa inuyo​—mwaulemu,” anayankha Dorota, ndipo anapitiriza kuti: “Komabe, timalakalaka anthuwo ataphunzira choonadi cha m’Baibulo.”

“Zayamba kale kundithandiza zimenezi,” anaulula Janina.

Pamene amachoka, Dorota analimbikitsa Janina kuti aziŵerenga Baibulo. “Lidzakuthandizani kukhala ndi moyo watanthauzo ndipo lidzakuthandizani pa ntchito yanu.”

“Mwandilimbikitsadi kuti ndizichita zimenezo,” anavomereza Janina.

Chifukwa cha kuchita zinthu mwanzeru komanso mwakhama, Dorota anapangitsa kuti ulendo wa nthaŵi zonse wopita kwa dokotala ukhale mpata wochitira umboni wabwino.​—1 Petro 3:15.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Si dzina lake lenileni.

^ ndime 10 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.