Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Malamulo A Wanzeru” Ndiwo Kasupe wa Moyo

“Malamulo A Wanzeru” Ndiwo Kasupe wa Moyo

 “Malamulo A Wanzeru” Ndiwo Kasupe wa Moyo

“HA! KUYA kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake n’zosalondoleka!” anafuula motero mtumwi Paulo. (Aroma 11:33) Yobu nayenso, munthu wakale wokhulupirika, anati: ‘[Yehova Mulungu] ndi wa mtima wanzeru.’ (Yobu 9:4) Zoonadi, palibe wofanana nzeru ndi Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi. Nanga bwanji za malamulo, kapena Mawu olembedwa, a Mlengiyu?

Wamasalmo anaimba kuti: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru; malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima: Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.” (Salmo 19:7, 8) Mfumu Solomo ya Israyeli wakale iyenera kuti inazindikira kuti mawu ameneŵa ndi oona. Inati: “Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo, apatutsa ku misampha ya imfa.” (Miyambo 13:14) M’mavesi 13 oyambirira a Miyambo chaputala 13, Solomo anasonyeza mmene malangizo a Mawu a Mulungu angatithandizire kukhala ndi moyo wabwino ndi kupeŵa kuuika pachiswe.

Khalani Ophunzitsika

“Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate; koma wonyoza samvera chidzudzulo,” imatero Miyambo 13:1. Atate angaphunzitse mwana mwambo mwina mofeŵa kapena mokhwimirapo. Mwina angatero mwa kungom’langiza poyamba, ndipo ngati mwanayo sanazigwiritse ntchito, kenako angapereke chilango. Mwana amakhala wanzeru akamalandira mwambo wa atate ake.

Baibulo limati: “Amene Ambuye am’konda am’langa, nakwapula mwana aliyense am’landira.” (Ahebri 12:6) Imodzi mwa njira zomwe Atate wathu wakumwamba amatipatsira mwambo ndiyo kudzera m’Mawu ake olembedwa, Baibulo. Tikamaŵerenga Baibulo mosamala kwambiri n’kumachita zomwe tikuphunziramo, ndiye kuti Mawu akewo akutipatsa mwambo. Timapindula ndi zimenezi chifukwa chakuti chilichonse chomwe Yehova amanena n’choti chitipindulitse.​—Yesaya 48:17.

Tingalandirenso mwambo pamene wokhulupirira mnzathu yemwe akutifunira zabwino pamoyo wathu wauzimu atiwongolera zomwe tinalakwitsa. Malangizo alionse abwino omwe akugwirizana ndi Mawu a Mulungu tiziwaona kuti sakuchokera kwa munthuyo, koma achokera kwa Mulungu, yemwe ndi Chitsime chachikulu cha choonadi. N’chinthu chanzeru kuwalandira monga ochokera kwa Yehova. Tikachita zimenezi ndi kuwalola kutitsogolera pa zoganiza zathu, kutithandiza kumvetsa Malemba, ndiponso kukonza njira zathu, tidzapindula ndi malangizowo. N’chimodzimodzinso ndi malangizo omwe timalandira pamisonkhano yachikristu ndiponso m’mabuku ofotokoza Baibulo. Kulabadira zomwe timaphunzira poŵerenga kapena kumva ndi njira yabwino kwambiri yodzipatsira tokha mwambo.

Koma wonyoza samva mwambo. Buku lina limati, “saphunzitsika chifukwa amaganiza kuti akudziŵa chomwe chili chabwino.” Samvera  ngakhale chidzudzulo, womwe ndi mwambo wokhwima. Komano kodi angathe ngakhale pang’ono pokha kusonyeza kuti mwambo wa Atate ndi wolakwika? Yehova sanalakwepo n’kamodzi komwe, ndipo sadzatero. Mwa kukana mwambo, wonyoza amangodzipusitsa. M’mawu ochepa koma osankhidwa bwino ameneŵa, Solomo anafotokoza bwino kwambiri phindu la kukhala wophunzitsika!

Samalani ndi Lilime Lanu!

Pofuna kusonyeza kufunika kotsatira Mawu a Mulungu pamene tikulankhula, mfumu ya Israyeliyi inayerekeza mkamwa ndi mtengo wobala zipatso. Inati: “Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za mkamwa mwake; koma moyo wa achiwembu udzadya chiwawa.” (Miyambo 13:2) Mawu ndi chipatso cha mkamwa. Ndipo munthu amatuta zomwe wafesa ndi mawu ake. Katswiri wina wamaphunziro anati: “Ngati mawu ake ngacholinga chabwino ndipo ngofuna kukhazikitsa ubale wabwino ndi anzake, iye adzadya zabwino, n’kumakhala mosangalala ndi mwamtendere.” Komatu umu si mmene zimakhalira ndi munthu wachiwembu. Amafuna kuchita ziwawa ndiponso kupweteka anzake. Amakonza ziwawa, ndipo amachitidwanso ziwawa. Misampha ya imfa ili pakhomo pake.

“Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake,” anapitiriza motero Solomo. “Koma woyasamula milomo yake adzawonongeka.” (Miyambo 13:3) Kulankhula mosaganizira kapena mopusa kungapangitse munthu kukhala ndi mbiri yoipa, kuvutika maganizo, kusakhalitsana bwino ndi anzake, ndipo mwinanso kupwetekedwa kumene. Kusasamala polankhula kungaikenso munthu paudani ndi Mulungu, chifukwa Mulungu adzaimba aliyense mlandu wa zolankhula zake. (Mateyu 12:36, 37) Inde, tingapeŵe mavuto ngati tisamala kwambiri pakamwa pathu. Komano, kodi tingaphunzire motani kugwira pakamwa pathu?

Njira imodzi yosavuta yochitira zimenezi ndiyo kusalankhula zambiri. “Pochuluka mawu zolakwa sizisoŵeka,” limatero Baibulo. (Miyambo 10:19) Njira ina ndiyo kuyamba taganiza tisanalankhule. Mlembi wouziridwayu anati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.” (Miyambo 12:18) Munthu akangolankhula asanaganizire, wolankhulayo komanso womvetsera mawu akewo angathe kupwetekedwa nazo. Motero, Baibulo limatipatsa malangizo abwino kwambiri aŵa: ‘Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.’​—Miyambo 15:28.

Khalani Akhama

Solomo anati: “Moyo wa wolesi ukhumba osalandira kanthu; koma moyo wa akhama udzalemera.” (Miyambo 13:4) Buku lina limati: “Mfundo [ya mwambiwu] njakuti kungolakalaka chinthu n’kosaphula kanthu, khama ndilo lofunika kwambiri. Anthu aulesi amangovutika ndi . . . kulakalaka, ndipo sapindula chilichonse ndi ulesi wawowo.” Koma, moyo, kapena zolakalaka, za anthu akhama zimakwaniritsidwa​—zimalemeretsedwa.

Nanga bwanji za anthu omwe amalephera kudzipatulira kwa Yehova pofuna kupeŵa kukhala ndi udindo? Angamasonyeze kuti akulakalaka kudzakhala m’dziko latsopano la Mulungu, koma kodi akufunadi kuchitapo kanthu kenakake? Kuti munthu ‘adzatuluke m’chisautso chachikulu’ afunika kukhulupirira nsembe yadipo ya Yesu, kudzipatulira kwa Yehova, ndi kusonyeza kudzipatulira kwakeko mwa kubatizidwa m’madzi.​—Chivumbulutso 7:14, 15.

Taganizaninso zomwe zimafunika kuti munthu afike pokhala ndi udindo wa woyang’anira mu mpingo. Kufuna kupatsidwa ntchito yabwino  imeneyi ndi chinthu choyamikika kwambiri ndipo Malemba amalimbikitsa zimenezo. (1 Timoteo 3:1) Komano kungosonyeza mtima wofuna ntchitoyi sikokwanira. Kuti munthu ayenerere udindo umenewu ayenera kukhala ndi makhalidwe ndi luso lomwe limafunikira. Izi zimalira khama.

Chilungamo Chimatchinjiriza

Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu ndipo amalankhula zoona. Amadziŵa kuti bodza n’lotsutsana ndi malamulo a Yehova. (Miyambo 6:16-19; Akolose 3:9) Pamfundoyi, Solomo anati: “Wolungama ada mawu onama; koma woipa anyansa, nadzichititsa manyazi.” (Miyambo 13:5) Munthu wolungama sikuti amangopeŵa bodza; koma amadana nalo kumene. Amadziŵa kuti, zilibe kanthu bodza litaoneka labwino motani, koma limasokoneza ubale wabwino wa anthu. Komanso anthu sakhulupirira munthu wokonda kulankhula zabodza. Munthu woipa amachita zinthu zonyansa kaya mwa mabodza kapena m’njira zina ndi zina, ndipo zimenezo zimam’chititsa manyazi.

Pofuna kusonyeza phindu la kuchita zinthu zomwe Mulungu amati n’zabwino, mfumu yanzeruyi inati: “Chilungamo chitchinjiriza woongoka m’njira; koma udyo ugwetsa wochimwa.” (Miyambo 13:6) Monga malo otetezedwa bwino, chilungamo chimateteza munthu, pamene kuipa kumam’pweteketsa.

Osamanamizira

Kusonyeza kuti inkadziŵa bwino kwambiri chikhalidwe cha anthu, mfumu ya Israyeliyi inati: “Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu; alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi chuma chambiri.” (Miyambo 13:7) Munthu sangakhaledi mmene amaonekera. Anthu ena osauka angamanamizire kukhala olemera​—mwina kuchita zinthu modzionetsera, pofuna kuti anthu aziwaona ngati zinthu zikuwayendera bwino, kapena pofuna kuti anthu aziwatama basi. Munthu wolemera angamanamizire kukhala wosauka, pongofuna kubisa chuma chake.

Si bwino kumanamizira kukhala wolemera kapena wosauka. Ngati ndife osauka, kuwononga ndalama pogula zinthu zosafunika kwenikweni n’cholinga chongofuna kuoneka olemera kungalepheretse ifeyo ndiponso mabanja athu kupeza zinthu zofunikira kwambiri pamoyo wa munthu. Ndipo munthu akamanamizira kukhala wosauka pamene ali ndi chuma chambirimbiri zingam’pangitse kukhala woumira, n’kumulepheretsa kulandira ulemu womuyenera ndiponso kupeza chisangalalo chomwe anthu amapeza chifukwa chokhala owoloŵa manja. (Machitidwe 20:35) Moyo wabwino umadza chifukwa chokhala mmene munthuwe ulili.

 Osamalakalaka Zambiri M’moyo

Solomo anati: “Chiwombolo cha moyo wa munthu ndicho chuma chake; koma wosauka samva chidzudzulo.” (Miyambo 13:8) Kodi mwambiwu uli ndi phunziro lotani?

Kukhala wolemera kuli ndi ubwino wake, komano sikuti kukhala ndi chuma ndiye kuti basi wachipeza chimwemwe, ayi. M’nthaŵi zovuta tikukhala zino, nthaŵi zambiri anthu olemera pamodzi ndi mabanja awo amapezeka ali pangozi yoti angathe kubedwa n’kukasungidwa penapake kuti alipire dipo. Nthaŵi zina munthu wolemera angapereke dipo powombola moyo wake kapena kuwombola moyo wa munthu wina wa m’banja mwake. Koma kaŵirikaŵiri munthu wobedwayo amaphedwa. Ili ndi vuto lomwe anthu olemera amaliyembekezera nthaŵi ina iliyonse.

Munthu wosauka sada nkhaŵa ndi zimenezo. Ngakhale kuti sangathe kuchita zimene anthu olemera amachita kapenanso kupeza katundu amene anthu olemera amakhala naye, sikaŵirikaŵiri pamene anthu amam’funafuna kuti amube. Ili ndi phindu la kusalakalaka zinthu zochuluka ndiponso kusathera nthaŵi ndi nyonga zathu kusakasaka chuma.​—2 Timoteo 2:4.

Kondwerani ‘M’kuunika’

Solomo anapitiriza kusonyeza kuti timapindula kwambiri tikachita zinthu monga momwe Yehova akufunira. Iye anati: “Kuunika kwa olungama kukondwa; koma nyali ya oipa idzazima.”​Miyambo 13:9.

Nyali ikuimira chomwe timadalira kuti tiŵalitse njira yathu m’moyo. ‘Mawu a Mulungu ndiwo nyali ya ku mapazi kwa wolungama, ndi kuunika kwa panjira yake.’ (Salmo 119:105) M’mawuwo muli zinthu zambiri ndiponso nzeru zosaneneka za Mlengi. Pamene timamvetsa bwino zolinga ndi zofuna za Mulungu, m’pamenenso kuunika kwauzimu kumene kumatitsogolera kumaŵala kwambiri. N’zosangalatsatu kwambiri zimenezi! Ndiyeno kodi palinso chifukwa chosokonezekera ndi nzeru za dzikoli kapena zinthu zimene anthu amanama kuti ndi nzeru?​—1 Akorinto 1:20; Akolose 2:8; 1 Timoteo 6:20.

Kwa woipa, zilibe kanthu kuti nyali yake ingaoneke yoŵala bwino motani ndiponso kuti akuoneka kuti zinthu zikumuyendera bwino motani, nyali yake idzazima. Mapeto ake adzakhala mumdima, momwe angathe kuphunthwa. Komanso, “sadzalandira mphoto.”​—Miyambo 24:20.

Komabe, kodi tiyenera kutani ngati sitikudziŵa mmene tingachitire zinthu zinazake? Bwanji ngatinso sitikudziŵa bwinobwino ngati ndi ntchito yathu kuchita zinthuzo? Miyambo 13:10 limachenjeza kuti: “Kudzikuza kupikisanitsa.” Kuchita zinthu zomwe sitikuzidziŵa kapena zomwe sitinauzidwe kuchita n’kudzikuza ndipo mosakayikira kungapangitse kuti tikangane ndi anzathu. Kodi sichingakhale chanzeru kufunsa ena omwe akudziŵa zinthuzo ndiponso ozindikira? “Omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru,” inatero mfumu yanzeruyi.

 Samalani ndi Kudikira Pachabe

Ndalama zingathandize kwambiri. Kukhala ndi chuma chochuluka n’kwabwino kusiyana ndi kukhala n’chochepa kapena paumphaŵi. (Mlaliki 7:11, 12) Koma zomwe tingayembekezere kupindula ndi chuma chopezedwa mwachinyengo n’zosadalirika. Solomo anachenjeza kuti: “Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa; koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.”​Miyambo 13:11.

Mwachitsanzo, taganizirani za vuto la kutchova njuga. Wotchova njuga angasakaze ndalama zomwe wapeza movutikira n’kumaganiza kuti adyapo ndalama zambiri panjugapo. Ndipotu nthaŵi zambiri amachita zimenezi banja lake likuvutika! Komano kodi chimachitika n’chiyani iye akadya ndalama panjugapo? Poti ndalamazo sanazikhetsere thukuta, iye sangazisamale. Komanso, n’kutheka kuti sangathe kugwiritsa ntchito bwino ndalama zomwe wangodya panjugazo. Kodi chuma chakecho sichipululuka m’nthaŵi yochepa, ngatinso mmene anachipezera? Komano, chuma chochipeza pang’onopang’ono, mwa kugwira ntchito molimbika, chimam’ka chiwonjezeka ndipo chingagwiritsidwe ntchito moyenera.

Solomo anati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima; koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.” (Miyambo 13:12) Kumangoyembekezera zinthu koma zosachitika, mosakayikira kungathe kukhumudwitsa munthu kumene kumadwalitsa mtima. Izi zimachitika m’moyo watsiku ndi tsiku. Komabe sikuti ndi mmene zimakhalira ndi zinthu zozikidwa kwambiri pa Mawu a Mulungu zimene tikuyembekezera. Tingakhale ndi chikhulupiriro chonse kuti zidzakwaniritsidwa. Ngakhale zitaoneka ngati zikuchedwa sizingakhumudwitse munthu.

Mwachitsanzo, tikudziŵa kuti dziko latsopano la Mulungu lili pafupi. (2 Petro 3:13) Ndi mtima wonse timayembekezera mosangalala kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. Kodi chimachitika n’chiyani tikamadikirira kwinaku tili kalikiliki “mu ntchito ya Ambuye,” kulimbikitsa okhulupirira anzathu, ndiponso kulimbitsa kwambiri unansi wathu ndi Yehova? M’malo ‘modwala mtima,’ timakhala ndi chimwemwe. (1 Akorinto 15:58; Ahebri 10:24, 25; Yakobo 4:8) Zinthu zomwe takhala tikuziyembekezera kwa nthaŵi yaitali zikachitika, zimakhala mtengo wa moyo​—zimakhaladi zolimbikitsa ndi zotsitsimula.

Malamulo a Mulungu Ndiwo Kasupe wa Moyo

Popereka chitsanzo chosonyeza kufunika komvera Mulungu, Miyambo 13:13 imati: “Wonyoza mawu adziwononga yekha, koma woopa malangizo adzalandira mphoto.” Ngati munthu amene ali ndi ngongole anyozera lonjezo mwa kulephera kubweza ngongoleyo, iye amatha kulanditsa chikole chomwe analonjeza. Mofananamo, nafenso tingataye zinthu ngati tilephera kumvera malamulo a Mulungu. Kodi tingataye chiyani?

“Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo, apatutsa ku misampha ya imfa.” (Miyambo 13:14) Kukhala mosatsatira malamulo a Mulungu wanzeru zonse, Yehova, ndiko kusoŵeka chitsogozo chomwe chingatithandize kukhala moyo wabwino ndi wautali. Kumeneko kungakhaletu kumanidwa chinthu chachikulu kwambiri! Motero n’chinthu chanzeru kuti tiziphunzira ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu ndi kuwalola kukhudza maganizo, malankhulidwe ndi zochita zathu.​—2 Akorinto 10:5; Akolose 1:10.

[Zithunzi patsamba 23]

Kulabadira malangizo a m’Malemba ndi njira yabwino kwambiri yodzipatsira tokha mwambo

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

“Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe”

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Kukhala kalikiliki “mu ntchito ya Ambuye” kumatipatsa chimwemwe