Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukambirana Nkhani Zauzimu Kumalimbikitsa

Kukambirana Nkhani Zauzimu Kumalimbikitsa

 Kukambirana Nkhani Zauzimu Kumalimbikitsa

“Nkhani yonse yovunda isatuluke mkamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.”​—AEFESO 4:29.

1, 2. (a) Kodi kulankhula n’kofunika bwanji? (b) Kodi atumiki a Yehova amafuna kugwiritsa ntchito lilime lawo motani?

WOLEMBA buku lina lotanthauzira mawu, Ludwig Koehler, analemba kuti: “Kulankhula ndi chinsinsi; ndi mphatso yozizwitsa yochokera kwa Mulungu.” Mwina timaona mopepuka mphatso yofunika kwambiri imeneyi yochokera kwa Mulungu. (Yakobo 1:17) Koma taganizirani chinthu chabwino kwambiri chimene chimatayika pamene matenda opha ziŵalo apangitsa munthu amene timam’konda kulephera kulankhula zinthu zomveka. Joan, amene mwamuna wake posachedwapa anadwala matenda opha ziŵalo anati: “Tinali kulankhulana ndiponso kugwirizana bwino kwambiri. Ndimadandaula kwambiri kuti sitilankhulananso ngati kale!”

2 Kukambirana kungalimbitse ubwenzi, kuthetsa kusamvetsetsana, kulimbikitsa ovutika maganizo, kulimbitsa chikhulupiriro ndiponso kupangitsa moyo kukhala wosangalatsa. Koma zonsezi sizimangochitika zokha. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.” (Miyambo 12:18) Monga atumiki a Yehova, timafuna zolankhula zathu zikhale zochiritsa ndiponso zolimbikitsa osati zowononga ndi kulefula. Timafunanso kugwiritsa ntchito lilime lathu kutamanda Yehova, pamene tili mu utumiki ndiponso pamene tikukambirana nkhani patokha. Wamasalmo anaimba kuti: “Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse, ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha.”​—Salmo 44:8.

3, 4. (a) Kodi ndi vuto lotani limene ife tonse timakumana nalo lokhudza zolankhula zathu? (b) N’chifukwa chiyani tifunika kusamala zolankhula zathu?

3 Wophunzira Yakobo anachenjeza kuti: “Lilime palibe munthu akhoza kulizoloŵeretsa.” Iye akutikumbutsa kuti: “Timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mawu, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.” (Yakobo 3:2, 8) Tonse ndife opanda ungwiro. Chifukwa cha zimenezi, sinthaŵi zonse pamene zolankhula zathu zimakhala zolimbikitsa ena kapena zotamanda Mlengi wathu ngakhale kuti tingafune kutero. Chotero, tifunika kukhala osamala ndi zolankhula zathu. Ndiponso, Yesu anati: “Mawu onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawaŵerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mawu ako, ndipo ndi mawu ako omwe udzatsutsidwa.” (Mateyu 12:36, 37) Ndithudi, Mulungu woona adzatiimba mlandu chifukwa cha zolankhula zathu.

4 Njira imodzi yabwino kwambiri yopeŵera kulankhula koipa ndiyo kukhala ndi chizoloŵezi chokambirana nkhani zauzimu. Nkhaniyi ipenda mmene tingachitire zimenezi ndiponso nkhani zimene tingakambirane komanso phindu limene tingapeze chifukwa cholankhula nkhani zolimbikitsa.

Samalani ndi Zimene Zili mu Mtima

5. Kodi mtima umachita mbali yofunika iti polimbikitsa kukambirana nkhani zolimbikitsa?

5 Kuti tikhale ndi chizoloŵezi chokambirana  nkhani zolimbikitsa, choyamba tiyenera kuzindikira kuti zolankhula zathu zimasonyeza zimene zili mu mtima mwathu. Yesu anati: “Mkamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.” (Mateyu 12:34) Kunena mwachidule, timakonda kulankhula zinthu zimene zili zofunika kwa ife. Chotero, tifunika kudzifunsa kuti: ‘Kodi zolankhula zanga zimavumbula chiyani za mmene mtima wanga ulili? Pamene ndili ndi banja langa kapena okhulupirira anzanga, kodi zolankhula zanga nthaŵi zambiri zimakhudza zinthu zauzimu kapena nthaŵi zonse zimangokhala za maseŵera, zovala, mafilimu, chakudya, zinthu zatsopano zimene ndagula kapenanso nkhani zina zopanda pake?’ Mwina mosadziŵa, moyo wathu ndiponso maganizo athu amangokhala pa zinthu zosafunika kwenikweni. Kusintha zinthu zimene timaona kuti n’zofunika kwambiri kudzawongolera zolankhula zathu ndiponso moyo wathu.​—Afilipi 1:10.

6. Kodi kusinkhasinkha kumatithandiza bwanji pankhani zimene timalankhula?

6 Kusinkhasinkha kokhala ndi cholinga ndi njira ina yowongolera zimene timalankhula. Ngati timafunitsitsa kuganizira zinthu zauzimu, kukambirana nkhani zauzimu kudzakhala kosavuta. Mfumu Davide anaona kugwirizana kumeneku. Iye anaimba kuti: “Mawu a mkamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova.” (Salmo 19:14) Ndiponso, wamasalmo Asafu anati: “Ndidzalingalira ntchito yanu yonse [ya Mulungu], ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.” (Salmo 77:12) Mtima ndi maganizo amene amakonda kwambiri choonadi cha Mawu a Mulungu sadzavutika kulankhula zambiri zotamandika. Yeremiya sanasiye kulankhula zinthu zimene Yehova anam’phunzitsa. (Yeremiya 20:9) Tingachite zofananazo ngati nthaŵi zonse tisinkhasinkha zinthu zauzimu.​—1 Timoteo 4:15.

7, 8. Kodi ndi nkhani ziti zimene zingakhale zabwino pokambirana nkhani zolimbikitsa?

7 Kukhala ndi chizoloŵezi chabwino chochita zinthu zauzimu kumatipatsa nkhani zambiri zolimbikitsa zomwe tingakambirane. (Afilipi 3:16) Misonkhano yadera, yachigawo, yampingo, zofalitsa zatsopano ndiponso lemba latsiku ndi tsiku ndi ndemanga zake, zonsezi zimatipatsa zinthu zabwino kwambiri zauzimu zimene tingauze ena. (Mateyu 13:52) Ndiponso zokumana nazo za mu utumiki wachikristu zingakhale zolimbikitsa kwambiri mwauzimu.

8 Mfumu Solomo anachita chidwi kwambiri ndi mitengo, nyama, mbalame ndi nsomba zambiri zosiyanasiyana zimene anaona m’Israyeli. (1 Mafumu 4:33) Iye ankasangalala kulankhula za ntchito zolenga za Mulungu. Nafenso tingachite mofananamo. Atumiki a Yehova amakonda kukambirana nkhani zosiyanasiyana koma nthaŵi zonse anthu okonda zauzimu amakambirana nkhani zauzimu.​—1 Akorinto 2:13.

‘Zilingalireni Izi’

9. Kodi ndi malangizo otani amene Paulo apatsa Afilipi?

9 Kaya tikukambirana nkhani zotani, zolankhula zathu zidzalimbikitsa ena ngati zikugwirizana ndi malangizo a mtumwi Paulo ku mpingo wa ku Filipi. Iye analemba kuti: ‘Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingalireni izi.’ (Afilipi 4:8) Zinthu zimene Paulo anatchula n’zofunika kwambiri, n’chifukwa chake anati ‘zilingalireni izi.’ Tiyenera kudzaza maganizo ndi mitima yathu ndi zinthu zimenezi. Chotero, tiyeni tione mmene kusamalira zinthu zonse zisanu ndi zitatu zimene Paulo anatchulazi kungatithandizire pa zokambirana zathu.

10. Kodi zokambirana zathu zingakhale bwanji ndi zinthu zimene zili zoona?

10 Zinthu zimene zili zoona zimaphatikizapo zambiri osati chabe zinthu zimene zili zolondola ndiponso zimene sizili zabodza. Zimatanthauza chinthu cholungama ndi chodalirika, monga choonadi cha Mawu a Mulungu. Chotero tikamakambirana ndi anthu ena za choonadi cha Baibulo chimene chinatisangalatsa, nkhani zimene zinatilimbikitsa kapena malangizo a m’Malemba amene anatithandiza, timakhala tikulingalira zinthu zoona. Komabe, timakana ‘chotchedwa chizindikiritso chonama’ chimene  chimangooneka ngati zoona. (1 Timoteo 6:20) Ndipo timapeŵa kufalitsa miseche kapena kusimba zokumana nazo zopanda umboni.

11. Kodi ndi zinthu zolemekezeka ziti zimene tingakambirane?

11 Zinthu zolemekezeka ndi nkhani zomwe zili zoyenera ndiponso zofunika osati zopanda pake. Zimaphatikizapo zinthu zofunika zokhudza utumiki wathu wachikristu, masiku owawitsa omwe tikukhalamo ndiponso kufunika kokhala ndi khalidwe labwino. Tikamakambirana zinthu zofunika zimenezi, timalimbitsa kutsimikiza mtima kwathu kukhala watcheru mwauzimu, wokhulupirika ndiponso kupitiriza kulalikira uthenga wabwino. Ndithudi, zokumana nazo zosangalatsa za mu utumiki wathu ndiponso zomwe zikuchitika panopo zimene zimatikumbutsa kuti tikukhala m’masiku otsiriza zimatipatsa nkhani zambiri zolimbikitsa zoti n’kukambirana.​—Machitidwe 14:27; 2 Timoteo 3:1-5.

12. Malinga ndi malangizo a Paulo okhudza kulingalira zinthu zolungama ndi zoyera, kodi tiyenera kupeŵa chiyani?

12 Mawu akuti zolungama amatanthauza zimene zili zabwino pamaso pa Mulungu, zogwirizana ndi miyezo yake. Mawu akuti zoyera akupereka tanthauzo  lokhala ndi maganizo ndiponso makhalidwe abwino. Zokambirana zathu sizifunika kukhala zosinjirira, nthabwala zotukwana kapena mawu oipa onena zogonana. (Aefeso 5:3; Akolose 3:8) Pamene zokambirana za kuntchito kapena kusukulu zikhala ndi mawu ameneŵa, mochenjera Akristu amachokapo.

13. Perekani zitsanzo za nkhani zokhudza zinthu zokongola ndi zomveka zokoma.

13 Pamene Paulo anati tilingalire zinthu zokongola, anatanthauza zinthu zimene zili zosangalatsa ndiponso zabwino kapena zimene zimalimbikitsa chikondi osati zoyambitsa udani, mkwiyo kapena mkangano. Zinthu zomveka zokoma zikutanthauza nkhani kapena mbiri yabwino. Nkhani zabwino zimenezi zingaphatikizepo nkhani za moyo wa abale ndi alongo okhulupirika zimene nthaŵi ndi nthaŵi zimasindikizidwa m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Bwanji osauzako ena zimene mwamva mukatha kuŵerenga nkhani zolimbitsa chikhulupiriro zimenezi? Ndipo n’zolimbikitsa zedi kumva zimene ena achita mwauzimu! Kukambirana zinthu zimenezi kudzakulitsa chikondi ndi kugwirizana mumpingo.

14. (a) Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tisonyeze chokoma? (b) Kodi zolankhula zathu zingakhale bwanji ndi zinthu zotamandika?

14 Paulo ananena za “chokoma mtima china.” Chokoma chikutanthauza ubwino kapena khalidwe labwino koposa. Tifunika kusamala kuti mfundo za m’Malemba zizitsogolera zolankhula zathu ndipo zizikhala zolungama, zoyera ndiponso zokoma. Chitamando chikutanthauza “zoyamikika.” Mukamvera nkhani yabwino kapena mukaona chitsanzo cha kukhulupirika mu mpingo, kambiranani zimenezo ndi omwe zikuwakhudzawo ndiponso anthu ena. Mtumwi Paulo nthaŵi zonse ankayamikira makhalidwe abwino a olambira anzake. (Aroma 16:12; Afilipi 2:19-22; Filemoni 4-7) Ndipo mosakayikira, zinthu zimene Mlengi wathu anapanga n’zoyamikika. Pa zinthu zimenezi timapeza nkhani zambiri zogwiritsa ntchito pokambirana nkhani zolimbikitsa.​—Miyambo 6:6-8; 20:12; 26:2.

Kambiranani Nkhani Zolimbikitsa

15. Kodi ndi lamulo liti la m’Malemba limene limapatsa makolo udindo wokambirana nkhani zothandiza ndi ana awo?

15 Pa Deuteronomo 6:6, 7 pakuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” Mwachionekere, lamulo limeneli limafuna kuti makolo azikambirana nkhani zothandiza ndiponso zauzimu ndi ana awo.

16, 17. Kodi makolo achikristu angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yehova ndi Abrahamu?

16 Tingathe kuona m’maganizo kuti Yesu ndi Atate wake wakumwamba anakambirana kwa nthaŵi yaitali za ntchito yake padziko lapansi. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule.” (Yohane 12:49; Deuteronomo 18:18) Kholo lakale Abrahamu ayenera kuti anakhala nthaŵi yaitali akukambirana ndi mwana wake Isake mmene Yehova anadalitsira iwo ndi makolo awo. Ndithudi, kukambirana kotero kunathandiza Yesu ndi Isake kugonjera modzichepetsa chifuniro cha Mulungu.​—Genesis 22:7-9; Mateyu 26:39.

17 Ana athunso afunika kukambirana nawo  nkhani zolimbikitsa. Makolo afunika kupatula nthaŵi pa zochita zawo zambiri yocheza ndi ana awo. Ngati n’kotheka, bwanji kukonza zodyera pamodzi monga banja kamodzi chabe patsiku? Pamene mukudya ndiponso mukamaliza, padzakhala nthaŵi yokambirana nkhani zolimbikitsa zimene zingakhale zothandiza kwambiri pa moyo wauzimu wa banja.

18. Fotokozani chochitika chimene chikusonyeza phindu la kulankhulana kwabwino pakati pa makolo ndi ana.

18 Alejandro, yemwe ndi wazaka zoyambirira za m’ma 20 ndipo ndi mpainiya, amakumbukira maganizo okayikira amene anali nawo ali ndi zaka 14. Iye anati: “Chifukwa cha anzanga ndiponso aphunzitsi, ndinali kukayikira ngati Mulungu aliko ndiponso ngati Baibulo ndi loona. Makolo anga anali kukambirana nane moleza mtima kwa maola ambiri. Kukambirana kumeneku kunandithandiza kuthetsa maganizo anga okayikira panthaŵi yovuta imeneyi komanso kupanga zosankha zabwino pa moyo wanga.” Nanga bwanji panopo? Alejandro anapitiriza kuti: “Ndikukhalabe ndi makolo. Koma n’kovuta kuti ndicheze ndi bambo anga chifukwa cha kutanganidwa kwathu. Chotero aŵirife timadyera pamodzi kuntchito kwawo kamodzi pamlungu. Kukambirana kumeneku ndimakuona kuti n’kofunika kwambiri.”

19. Kodi n’chifukwa chiyani tonsefe tifunika kukambirana nkhani zauzimu?

19 Kodi ifenso sitiona nthaŵi zopindulitsa zimene timakambirana nkhani zauzimu ndi okhulupirira anzathu kukhala zofunika kwambiri? Nthaŵi imeneyi imakhalako pamisonkhano, mu utumiki wakumunda ndi pamacheza komanso pamene tili paulendo. Paulo analakalaka kulankhulana ndi Akristu a ku Roma. Iye anawalembera kuti: “Ndilakalaka kuonana ndinu, . . . kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse aŵiri, chanu ndi changa.” (Aroma 1:11, 12) Johannes yemwe ndi mkulu wachikristu anati: “Kukambirana nkhani zauzimu ndi Akristu anzathu kumathandiza kwambiri. Kumalimbikitsa mtima ndiponso kumapepuza mavuto athu atsiku ndi tsiku. Nthaŵi zambiri ndimafunsa okalamba kuti andiuze za moyo wawo ndiponso chimene chawachititsa kukhala okhulupirika. Pazaka zapitazi, ndalankhula ndi anthu ambiri ndipo aliyense wandipatsa nzeru kapena kundiuza kanthu kena kamene kapangitsa moyo wanga kukhala wosangalatsa.”

20. Kodi tingachite chiyani tikakumana ndi munthu wamanyazi?

20 Bwanji ngati wina sachita chidwi pamene muyamba nkhani yauzimu? Musataye mtima. Mwina mungapeze nthaŵi yabwino m’tsogolo mwake. Solomo anati: “Mawu oyenera a pa nthaŵi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.” (Miyambo 25:11) Sonyezani kuganizira anthu amanyazi. “Uphungu wa m’mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.” * (Miyambo 20:5) Koposa zonse, musalole maganizo a anthu ena kukulepheretsani kulankhula zinthu zimene zimakhudza mtima wanu.

Kukambirana Nkhani Zauzimu Kumapindulitsa

21, 22. Kodi ndi phindu lotani limene timapeza pokambirana nkhani zauzimu?

21 Paulo analangiza kuti: “Nkhani yonse yovunda isatuluke mkamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.”  (Aefeso 4:29; Aroma 10:10) Zingafune kuyesetsa kwambiri kuti tipangitse nkhani kukhala yolimbikitsa koma phindu lake ndi lochuluka. Kukambirana nkhani zauzimu kumatichititsa kuuza ena chikhulupiriro chathu ndiponso kukulitsa ubale wathu.

22 Chotero, tiyeni tigwiritse ntchito mphatso ya kulankhula kulimbikitsa anthu ena ndi kutamanda Mulungu. Zokambirana zotero zidzatisangalatsa ndiponso zidzalimbikitsa ena. Koposa zonse, zidzasangalatsa mtima wa Yehova chifukwa amamvetsera zokambirana zathu ndipo amasangalala ngati tilankhula zabwino. (Salmo 139:4; Miyambo 27:11) Ngati tikambirana zauzimu, tingakhale otsimikiza kuti Yehova sadzatiiŵala. Ponena za amene akutumikira Yehova masiku ano, Baibulo limati: “Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” (Malaki 3:16; 4:5) N’kofunika kwambiri kuti zokambirana zathu zizikhala zolimbikitsa mwauzimu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Zitsime zina m’Israyeli zinali zakuya kwambiri. Ku Gibeoni, ofukula za m’mabwinja apeza chitsime chachikulu chakuya mamita 25. Chili ndi masitepe, amene anali kuthandiza anthu kutsikira pansi kuti akatunge madzi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi zolankhula zathu zimavumbula chiyani za ife?

• Kodi ndi zinthu zolimbikitsa ziti zimene tingakambirane?

• Kodi kukambirana kumagwira ntchito yofunika kwambiri iti m’banja ndi mu mpingo wachikristu?

• Kodi kukambirana nkhani zolimbikitsa kuli ndi phindu lotani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 12]

Nkhani zolimbikitsa zimakhudza . . .

“zinthu zilizonse zoona”

“zilizonse zolemekezeka”

‘chitamando china chilichonse’

“zilizonse zimveka zokoma”

[Mawu a Chithunzi]

Video cover, Stalin: U.S. Army photo; Creator book cover, Eagle Nebula: J. Hester and P. Scowen (AZ State Univ.), NASA

[Chithunzi patsamba 13]

Nthaŵi yachakudya ndi yabwino kwambiri kukambirana zinthu zauzimu