Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Asanaphunzire ndi ataphunzira Mmene Baibulo Linasinthira Munthu Uyu

Asanaphunzire ndi ataphunzira Mmene Baibulo Linasinthira Munthu Uyu

 “Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa Inu”

Asanaphunzire ndi ataphunzira Mmene Baibulo Linasinthira Munthu Uyu

CHINTHU chachikulu kwambiri m’moyo wa Rolf-Michael chinali zoimbaimba. Kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kunali kudya kwake. Ali mnyamata ku Germany, anali kumwa mowa kwambiri ndiponso kugwiritsa ntchito mosadziletsa mankhwala osokoneza bongo monga LSD, cocaine, hashish, ndi ena otero.

Rolf-Michael akuzembetsa mankhwala kuloŵa nawo m’dziko lina la ku Africa kuno, anamangidwa ndipo anakhala m’ndende miyezi 13. Nthaŵi imene anali m’ndendeyo inam’patsa mpata woganizira cholinga chenicheni cha moyo.

Rolf-Michael ndi mkazi wake, Ursula, anafunafuna cholinga cha moyo ndiponso ankafufuza choonadi. Ngakhale kuti anakhumudwa ndi matchalitchi otchedwa achikristu, iwo ankafunitsitsa kudziŵa Mulungu. Anali ndi mafunso ndipo magulu osiyanasiyana azipembedzo sanawayankhe zogwira mtima. Ndiponso, zipembedzo zimenezo sizinkawalimbikitsa kusintha moyo wawo.

Kenako Rolf-Michael ndi Ursula anakumana ndi Mboni za Yehova. Atayamba kuphunzira Baibulo, Rolf-Michael, anakhudzidwa mtima kwambiri ndi chilimbikitso chakuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Anatsimikiza mtima ‘kuvula makhalidwe ake oyamba, umunthu wakale, n’kuvala umunthu watsopano, wolengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’​—Aefeso 4:22-24.

Kodi Rolf-Michael akanavala bwanji umunthu watsopano? Anamusonyeza m’Baibulo kuti mwa “chizindikiritso, [“kudziŵa zolondola,” NW]” umunthu ‘ungakonzeke watsopano, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anam’lenga iye,’ amene ndi, Yehova Mulungu.​—Akolose 3:9-11.

Pamene anali kuphunzira zolondola, Rolf-Michael ankayesa kusintha moyo wake kuti ugwirizane ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu. (Yohane 17:3) Zinali zovuta kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, koma Rolf-Michael anazindikira kufunika kolankhula ndi Yehova m’pemphero ndiponso koti Yehovayo am’thandize. (1 Yohane 5:14, 15) Kucheza kwambiri ndi Mboni za Yehova, zimene zinali kuyesetsa kuchita chifuno cha Mulungu, kunam’thandizanso.

Kudziŵa kuti dzikoli likupita ndi kuti ochita chifuno cha Mulungu adzakhala kosatha kunam’thandizanso Rolf-Michael. Kunamuthandiza kusankha osati kukonda za m’dziko zimene zili za kanthaŵi chabe, koma kusankha madalitso osatha okhala paubwenzi wolimba ndi Mulungu wachikondi, Yehova. (1 Yohane 2:15-17) Rolf-Michael anakhudzidwa mtima ndi mawu a pa Miyambo 27:11, akuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” Iye ananena mawu oyamikira akuti: “Vesi limeneli likusonyeza kuya kwa chikondi  cha Yehova, popeza amapatsa anthu mwayi wokondweretsa mtima wake.”

Monga momwe anachitira Rolf-Michael, mkazi wake, ndi ana awo atatu, anthu ambirimbiri apindula potsatira mfundo za m’Baibulo. Anthu amenewo angapezeke m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse. Chomvetsa chisoni n’chakuti, m’mayiko ena Mboni zimaimbidwa mlandu wabodza woti ndi gulu lachipembedzo loipa kwambiri limene limapasula mabanja. Zimene zinachitikira Rolf-Michael zikusonyezeratu kuti limeneli ndi bodza lamkunkhuniza.​—Ahebri 4:12.

Rolf-Michael akuti m’banja lake lemba la Mateyu 6:33, lomwe limatilimbikitsa kuika zinthu zauzimu patsogolo, lili ngati “kampasi,” yowalozera koyenera kupita. Iye ndi banja lake akuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha moyo wabanja wosangalatsa umene ali nawo monga Akristu. Amagwirizana ndi malingaliro a wamasalmo amene anaimba kuti: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?”​—Salmo 116:12.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Mulungu amapatsa anthu mwayi wokondweretsa mtima wake

[Bokosi patsamba 9]

Mfundo za M’Baibulo Zikugwira Ntchito

Zina mwa mfundo za m’Baibulo zimene zalimbikitsa anthu ambiri kusiya zizoloŵezi zomwe zingaphetse munthu ndi izi:

“Okonda Yehova, danani nacho choipa.” (Salmo 97:10) Munthu akakhulupirira kuti zizoloŵezi zomwe zingaphetse munthu ndi zoipa ndiponso akayamba kudana nazo kwambiri, savutika kuchita zokondweretsa Mulungu.

“Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Kuti munthu akane mankhwala osokoneza bongo ndiponso mankhwala ena oipa, afunika kusankha bwino anthu ocheza nawo. N’kothandiza kwambiri kupalana ubwenzi ndi Akristu amene adzamuthandiza kusiya zizoloŵezi zimenezi.

“Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Mtendere wa mu mtima ndi wa m’maganizo umenewu sungapezedwe mogwiritsa ntchito chinthu china chilichonse. Ndipo kudalira Mulungu mwa kupemphera kumathandiza munthu kuthana ndi mavuto amene akukumana nawo pamoyo wake popanda kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.