Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pali Mpingo Woona Umodzi Wokha Wachikristu

Pali Mpingo Woona Umodzi Wokha Wachikristu

 Pali Mpingo Woona Umodzi Wokha Wachikristu

YESU KRISTU anakhazikitsa mpingo umodzi wokha. Mpingo umenewo unali thupi lauzimu, banja lauzimu. Pamenepa tikutanthauza kuti kunali kusonkhanitsidwa pamodzi kwa anthu osankhidwa ndi mzimu wa Mulungu, onse odziŵika kwa Mulungu kukhala “ana” ake.​—Aroma 8:16, 17; Agalatiya 3:26.

Yesu anaphunzitsa kuti Mulungu anagwiritsa ntchito njira imodzi yokha kuti atsogolere anthu ku choonadi ndi moyo. Pochitira fanizo mfundo yofunika kwambiri imeneyi, Yesu anayerekezera kupeza moyo wosatha ndi njira. Iye anati: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.”​—Mateyu 7:13, 14; Yohane 14:6; Machitidwe 4:11, 12.

Mpingo Wogwirizana

Sitiyenera kuganiza za mpingo wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino umenewo ngati “gulu la anthu a padziko lonse lolinganizidwa monga mmene zilili masiku ano tikamanena za mpingo wa katolika” linatero buku lomasulira mawu la The New Dictionary of Theology. Chifukwa chiyani? Bukulo linati: “Chifukwa chakuti kunalibe gulu la anthu lolinganizidwa motero.”

Palibe amene angatsutse zoti mpingo wachikristu woyambirira sunali wofanana ndi mipingo yolinganizidwa kwambiri yomwe tikuiona masiku ano. Komabe unali wolinganizidwa bwino. Magulu a mpingowo sankachita zinthu paokha. Onse ankalemekeza ulamuliro wa bungwe lolamulira ku Yerusalemu. Bungwe lolamulira limenelo,  limene linali lopangidwa ndi atumwi ndi amuna akulu a mpingo wa Yerusalemu, linathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana ngati “thupi limodzi” la Kristu.​—Aefeso 4:4, 11-16; Machitidwe 15:22-31; 16:4, 5.

Kodi n’chiyani chimene chinachitikira mpingo woona umodzi umenewo? Kodi unadzakhala mpingo waukulu wa Katolika? Kodi unadzakhala mipingo yogawanika ya Chipulotesitanti imene tikuiona masiku anoyi? Kapena, kodi panachitika chinachake?

“Tirigu” ndi “Namsongole”

Kuti tipeze mayankho, tiyeni tipende mwachidwi zimene Yesu Kristu mwiniyo ananena kuti zidzachitika. Mungadabwe kudziŵa kuti Yesu anayembekezera mpingo wake kuzimiririka ndiponso anati adzalola zinthu zomvetsa chisoni zimenezo kukhalapo kwa zaka mazana ambiri.

Pogwirizanitsa mpingo wake ndi “Ufumu wa Kumwamba,” iye anati: “Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbewu zabwino m’munda mwake; koma mmene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole. Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbewu zabwino m’munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo? Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wachichita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikam’sonkhanitse uyo pamodzi? Koma iye anati, Iyayi, kuti kapena mmene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye. Kazilekeni zonse ziŵiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m’nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mum’mange uyu mitolo kukam’tentha, koma musonkhanitse tirigu m’nkhokwe yanga.”​—Mateyu 13:24-30.

Yesu anafotokoza kuti iye anali ‘wofesayo.’ “Mbewu yabwino” inaimira ophunzira ake enieni. “Mdani” wake anali Satana Mdyerekezi. “Namsongole” anali Akristu onyenga amene analoŵa pang’onopang’ono mu mpingo wachikristu woyambirira. Iye anati adzalola “tirigu” ndi “namsongole” kukulira limodzi kufikira nthaŵi ya “kututa” kumene kukachitika pa “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 13:37-43) Kodi zonsezi zinatanthauza chiyani?

Mpingo Wachikristu Unaipitsidwa

Atumwi atangomwalira, aphunzitsi onyenga mu mpingomo anayamba kulamulira. Analankhula “zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.” (Machitidwe 20:29, 30) Zotsatira zake  n’zakuti, Akristu ambiri ‘anataya chikhulupiriro.’ Iwo ‘anapatutsidwa kutsata nthano zachabe.’​—1 Timoteo 4:1-3; 2 Timoteo 4:3, 4.

Buku lomasulira mawu lotchedwa The New Dictionary of Theology, linati pofika m’zaka za m’ma 300 C.E., “Chikristu cha Chikatolika chinakhala chipembedzo chovomerezeka ndi boma . . . mu ufumu wa Roma.” Panali “kugwirizana kwa anthu achipembedzo ndi a dziko”​—mgwirizano wa Tchalitchi ndi Dziko umene unali wotsutsana kwambiri ndi zikhulupiriro za Chikristu choyambirira. (Yohane 17:16; Yakobo 4:4) Buku lomweli linafotokoza kuti patapita nthaŵi, dongosolo lonse la mpingowo, komanso zikhulupiriro zake zikuluzikulu, zinasinthidwa kwambiri “chifukwa chosakaniza Chipangano Chakale ndi chiphunzitso cha Pulato, kusakaniza kumene kunali kwachilendo komanso koononga.” Monga momwe Yesu Kristu anali ataneneratu, ophunzira ake enieni sanaonekenso pamene Akristu onyenga amachuluka.

Omvetsera a Yesu anadziŵa mmene zinalili zovuta kusiyanitsa tirigu weniweni ndi namsongole. Mawu oyambirira amene anawamasulira kuti “namsongole” pano amatanthauza udzu. Chitsanzo cha udzu umenewo ndi udzu woipa kwambiri wotchedwa bearded darnel, umene ukamakula umafanana kwambiri ndi tirigu. Chotero, Yesu ankafotokoza kuti kwa kanthaŵi ndithu, kudzakhala kovuta kusiyanitsa Akristu oona ndi Akristu onyenga. Zimenezi sizikutanthauza kuti mpingo wachikristu unatheratu, chifukwa Yesu analonjeza kuti adzapitiriza kutsogolera abale ake auzimu “masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:20) Yesu anati tirigu adzapitiriza kukula. Ngakhale zinali choncho, kwa zaka zambiri, Akristu oona​—paokha kapena m’magulu​—mosakayikira anayesetsa kutsatira ziphunzitso za Kristu. Koma sanapangenso gulu lodziŵika ndi looneka bwino. Sanali ofanana ndi gulu lachipembedzo looneka lampatuko limene kwa zaka zambiri linachititsa manyazi ndi kunyozetsa dzina la Yesu Kristu.​—2 Petro 2:1, 2.

‘Avumbulutsidwa Munthu Wosayeruzika’

Mtumwi Paulo ananeneratu chinachake chimene chinali kudzazindikiritsa chipembedzo chonyenga chimenechi. Analemba kuti: “Munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika [tsiku la Yehova], koma chiyambe chifike chipatukocho, navumbulutsike munthu wosayeruzika.” (2 Atesalonika 2:2-4) “Munthu wosayeruzika” ameneyu ndi gulu la atsogoleri achipembedzo amene anadzikweza okha kukhala olamulira pa mpingo wa “Chikristu.” *

Mpatuko unayamba mu nthaŵi ya mtumwi Paulo. Unawonjezeka mofulumira kwambiri atumwi atamwalira chifukwa panalibenso choletsa. Paulo anati, udzadziŵika bwino kwambiri ndi “machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama.” (2 Atesalonika 2:6-12) Zimenezi zimafotokoza bwino kwambiri zochita za atsogoleri ambiri achipembedzo m’mbiri yonse ya anthu!

Pokhalira kumbuyo zonena zawo zoti mpingo wa Roma Katolika ndiwo mpingo woona wokha, atsogoleri Akatolika amanena kuti ansembe awo “analandira utumwi wawo kwa atumwi oyambirira kudzera mu mzera umene unayambira kuchiyambi kwa Chikristu.” Kunena zoona, palibe maziko alionse m’mbiri kapena m’Malemba osonyeza kuti atumwi analoŵedwa m’malo. Palibe umboni wodalirika wosonyeza kuti dongosolo la mpingo limene linayamba atumwi a Yesu atamwalira linatsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu.​—Aroma 8:9; Agalatiya 5:19-21.

Koma bwanji nanga za mipingo ina imene inayamba patadutsa nyengo imene amati nyengo yokonzanso zinthu pa nkhani ya chipembedzo? Kodi inayamba kutsatiranso chitsanzo cha mpingo wachikristu woyambirira? Kodi inabwezeretsanso kupatulika kwa mpingo woyambirira wachikristu? N’zoona kuti nyengo yokonzanso zinthu pa nkhani ya chipembedzo itadutsa, Baibulo linayamba kupezeka ndi anthu wamba ambiri m’zilankhulo zawo. Komabe, mbiri ikusonyeza kuti mipingo imeneyi inapitiriza kuphunzitsa zolakwika.​—Mateyu 15:7-9.

Komabe, taonani mfundo iyi. Yesu Kristu ananeneratu mosapita m’mbali kuti mpingo wake umodzi woona udzabwezeretsedwa pa nthaŵi  imene anaitcha chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano. (Mateyu 13:30, 39) Kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo kukusonyeza kuti tikukhala munthaŵi imeneyo. (Mateyu 24:3-35) Popeza zili choncho, aliyense wa ife ayenera kufunsa kuti, ‘Kodi mpingo woona umenewo uli kuti?’ Mpingowo uyenera kudziŵika bwino kwambiri tsopano.

Mwina mukuganiza kuti munapeza kale mpingo umenewo. M’pofunika kuti mutsimikizire. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti monga mmene zinalili m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, payenera kukhala mpingo umodzi wokha woona. Kodi mwapenda mofatsa kuti muone ngati mpingo wanu umagwirizana kwambiri ndi chitsanzo chimene mpingo wachikristu wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino unakhazikitsa ndiponso kuti umatsatira ziphunzitso za Yesu Kristu? Bwanji osapenda zimenezi tsopano? Mboni za Yehova zidzakondwa kukuthandizani kuti muchite zimenezo.​—Machitidwe 17:11

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Mungapeze zambiri zofotokoza za “munthu wosayeruzika” mu Nsanja ya Olonda, ya February 1, 1990, masamba 10 mpaka 14.

[Zithunzi patsamba 5]

Kodi fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole likutiphunzitsa chiyani za mpingo woona?

[Zithunzi patsamba 7]

Kodi mpingo wanu umasonyeza chitsanzo chimene chinakhazikitsidwa ndi Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino polalikira ndi pophunzira?