Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

M’madera ambiri pa dziko lapansi, kupereka mphatso za ukwati n’kofala. Kodi ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene tiyenera kuziganizira tikamapereka kapena kulandira mphatso zimenezi?

Baibulo sililetsa kupereka mphatso ngati cholinga chake n’chabwino komanso ngati pali pa nthaŵi yoyenera. Pa nkhani yopereka mphatso, Baibulo limalimbikitsa Akristu kutsanzira Yehova, amene amawapatsa zinthu mooloŵa manja. (Yakobo 1:17) Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Musaiŵale kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” Choncho, Akristu akulimbikitsidwa kukhala ooloŵa manja.​—Ahebri 13:16; Luka 6:38.

M’mayiko ena, n’chizoloŵezi chawo kuti anthu amene akufuna kuchita ukwati amakalembetsa ku sitolo ataona zinthu zimene zili m’sitolomo n’kulemba zinthu zimene akufuna kuti anthu adzawagulire ngati mphatso. Achibale ndi anzawo a anthu amene akufuna kuchita ukwatiwo amauzidwa kuti apite ku sitolo imene asankhayo kuti akagule mphatso imene ili pa gulu la mphatso zimene analembetsa m’sitoloyo. Zimenezi zingakhale zothandiza chifukwa munthu amene akufuna kugula mphatsoyo saononga nthaŵi yaitali pofunafuna mphatso yoti agule, pamene olandira mphatsowo amapeŵa vuto lokabweza mphatso zimene sakuzifuna ku sitoloko.

Anthu amene akuchita ukwati angasankhe okha kuti kaya alembetse ku sitolo kapena asalembetse. Komabe, Mkristu ayenera kusamala kuti apeŵe kuchita zinthu zimene zingasemphane ndi mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, bwanji ngati anthu amene akufuna kuchita ukwati alemba ndandanda ya zinthu zokwera mtengo zokhazokha? Zikatero, anthu amene ali ndi ndalama zochepa angalephere kugula mphatso, kapena angaganize kuti ndi bwino kunena kuti sadzatha kupita ku ukwatiwo n’cholinga choti asakachiteko manyazi chifukwa chobweretsa mphatso yotchipa. Mkazi wina wachikristu analemba kuti: “Tsopano kupereka mphatso kukukhala kolemetsa kwambiri. Ndayesetsa kuti ndikhale wooloŵa manja, koma masiku ano chimwemwe chonse chimene ndinkakhala nacho popereka mphatso chinatha.” Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati ukwati ungasanduke chokhumudwitsa!

Zoonadi, sitiyenera kuchititsa anthu opereka mphatso kumva kuti ayenera kugula mphatso yawo ku sitolo inayake kapena iyenera kukhala ya mtengo wakutiwakuti kuti ikhale yoyenera. Ngakhalenso Yesu Kristu anasonyeza kuti chimene chili cha mtengo wapatali kwambiri pamaso pa Mulungu ndi mtima wa munthu, osati mtengo wa mphatso yake. (Luka 21:1-4) Chimodzimodzinso ponena za kupereka mphatso kwa anthu osoŵa, mtumwi Paulo analemba kuti: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.”​—2 Akorinto 9:7.

Malinga ndi zimene Baibulo limanena, palibe cholakwika munthu akasonyeza kuti ndi iyeyo amene wapereka mphatsoyo, mwina mwa kulemba kakalata n’kukaika mu mphatsoyo. Koma m’madera ena, n’chikhalidwe chawo kuti amauza anthu onse amene abwera kuti ndi ndani wapereka mphatsoyo. Zimenezi zingabweretse mavuto. Anthu amene akupereka mphatsoyo angafune kuti asatchulidwe n’cholinga choti anthu ena asadziŵe kuti ndi iwowo amene apereka mphatsoyo. Anthu ameneŵa amakhala akutsatira mfundo imene ili pa Mateyu 6:3, pamene Yesu ananena kuti: “Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe chimene lichita dzanja lako lamanja.” Anthu ena angaone kuti kupereka mphatso ndi nkhani ya munthu payekha imene ayenera kudziŵa ndi munthu wopereka mphatsoyo ndi munthu wolandirayo basi. Ndiponso, kutchula anthu amene apereka mphatso kungachititse kuti anthu aziyerekezera mphatsozo, kumene kuli “kuyambitsa mpikisano.” (Agalatiya 5:26, NW) Ndithudi, Akristu sangafune kuchititsa munthu wina manyazi mwa kulengeza kwa anthu onse mayina a anthu amene apereka mphatso.​—1 Petro 3:8.

Inde, tikatsatira mfundo zimene zimapezeka m’Mawu a Mulungu, kupereka mphatso kudzapitirirabe kukhala kosangalatsa.​—Machitidwe 20:35.