Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dalirani Yehova

Dalirani Yehova

 Dalirani Yehova

“Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika [“wodalirika,” NW] kuyambira ubwana wanga.”​—SALMO 71:5.

1. Kodi Davide, yemwe anali wachinyamata ndiponso mbusa, anakumana ndi vuto lotani?

GOLIATI anali munthu wamtali, pafupifupi mamita atatu. N’zosadabwitsa kuti ankhondo onse a Israyeli anachita mantha kuti amenyane naye. M’maŵa ndi madzulo alionse, kwa milungu ingapo, chimphona chachifilisiti chimenechi chinanyoza ankhondo a Israyeli, kuwaderera mwa kuwauza kuti atumize munthu wamphamvu kwambiri pa gulu lawo amene angamenyane naye. Kenako, mnyamata wina, osati msilikali, anadzipereka kuti akamenyane naye. Mnyamatayo anali Davide, yemwe anali mbusa, ndipo anaoneka wamng’ono kwambiri poyerekezera ndi Goliati. Ndipotu, mwina zida zokha za Goliati zodzitetezera ndi zomenyera nkhondo zinali zolemera kwambiri kuposa kulemera kwa thupi la Davide. Komabe, mnyamatayo anamenyana ndi chimphonacho n’kuchigonjetsa ndipo chifukwa cha zimenezi iye anatchuka kuti anali munthu wolimba mtima.​—1 Samueli 17:1-51.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani Davide anali ndi chidaliro pokamenyana ndi Goliati? (b) Kodi tikambirana njira ziŵiri ziti zimene tifunika kutsatira kuti tidalire Yehova?

2 Kodi n’chiyani chinachititsa Davide kulimba mtima motero? Taonani mawu ena amene mwachionekere analemba ndi Davideyo ali wachikulire. Iye anati: “Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika [“wodalirika”] kuyambira ubwana wanga.” (Salmo 71:5) Inde, Davide ali wachinyamata, anadalira Yehova ndi mtima wonse. Pokamenyana ndi Goliati, iye ananena kuti: “Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unawanyoza.” (1 Samueli 17:45) Goliati anadalira mphamvu zazikulu zimene anali nazo ndi zida zake, koma Davide anadalira Yehova. Popeza Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse anali kum’thandiza Davide, kodi akanaoperanji munthu, ngakhale kuti anali wamkulu ndiponso anali ndi zida zokwanira?

3 Mukamaŵerenga nkhani ya Davide kodi mumalakalaka kudalira Yehova mokulirapo kuposa mmene mukuchitira pakalipano? Mosakayika, ambiri a ife timatero. Motero, tiyeni tione njira ziŵiri  zimene tingatsatire kuti tizidalira Yehova. Njira yoyamba ndi yakuti tifunika kugonjetsa chinthu chimene chimalepheretsa ambiri kumudalira. Njira yachiŵiri ndi yakuti tifunika kudziŵa kuti kudalira Yehova kumatanthauza chiyani.

Kugonjetsa Chimene Chimalepheretsa Anthu Ambiri Kudalira Yehova

4, 5. N’chifukwa chiyani anthu ambiri zimawavuta kudalira Mulungu?

4 Kodi n’chiyani chimalepheretsa anthu kudalira Mulungu? Nthaŵi zambiri, ena samvetsa chifukwa chake zinthu zoipa zimachitika. Anthu ambiri amaphunzitsidwa kuti Mulungu ndi amene amachititsa anthu kuvutika. Pakachitika tsoka linalake anthu n’kumwalirapo, atsogoleri a zipembedzo amanena kuti Mulungu “watenga” anthuwo kuti akakhale nawo kumwamba. Ndiponso, atsogoleri ambiri a zipembedzo amaphunzitsa kuti Mulungu anakonzeratu zochitika zonse, ngakhalenso tsoka lililonse ndi zinthu zoipa zilizonse, zimene zimachitika m’dzikoli. Zingakhale zovuta kudalira Mulungu wouma mtima woteroyo. Satana, yemwe amachititsa khungu maganizo a osakhulupirira, amafuna kulimbikitsa kwambiri “maphunziro a ziwanda” oterowo.​—1 Timoteo 4:1; 2 Akorinto 4:4.

5 Satana akufuna kuti anthu asadalire Yehova. Mdani wa Mulungu ameneyo safuna kuti tidziŵe zimene zimachititsadi anthu kuvutika. Ndipo tikaphunzira Malemba n’kudziŵa zifukwa zake anthufe timavutika, Satana amafuna kuti tiiŵale zimenezo. Motero, ndi bwino kuti tizipenda nthaŵi ndi nthaŵi zifukwa zitatu zimene zimachititsa kuti anthufe tizivutika m’dzikoli. Mwakuchita zimenezo, tingatsimikize kuti si Yehova amene amachititsa mavuto amene timakumana nawo.​—Afilipi 1:9, 10.

6. Kodi lemba la 1 Petro 5:8 likusonyeza bwanji chifukwa choyamba chimene chimachititsa anthu kuvutika?

6 Chifukwa choyamba chimene chimachititsa anthu kuvutika n’chakuti Satana amafuna kulepheretsa anthu kukhulupirira Yehova. Iye anafuna kuthetsa chikhulupiriro cha Yobu. Nthaŵi imeneyo Satana analephera, koma sanasiye kuchita zimenezi. Monga wolamulira wa dziko lino, iye amafuna ‘kulikwira’ atumiki a Yehova okhulupirika. (1 Petro 5:8) Zimenezi zikuphatikizapo aliyense wa ife. Satana akufuna kuti tisiye kutumikira Yehova. Motero, iye nthaŵi zambiri amayambitsa chizunzo. Komabe, ngakhale kuti kuvutika motero n’kopweteka, tili ndi chifukwa chabwino chopiririra. Mwakuchita zimenezo, timathandiza kutsimikizira kuti Satana ndi wabodza ndipo timakondweretsa mtima wa Yehova. (Yobu 2:4; Miyambo 27:11) Yehova amatilimbitsa kuti tipirire chizunzo, ndipo pamene akutero, kumudalira kwathu kumakula.​—Salmo 9:9, 10.

7. Kodi lemba la Agalatiya 6:7 likutithandiza kuzindikira chifukwa chiti chimene chimachititsa anthu kuvutika?

7 Chifukwa chachiŵiri chimene chimachititsa anthu kuvutika chikupezeka pa mfundo yakuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Nthaŵi zina anthu amafesa mwa kuchita zinthu zolakwika ndipo amatuta mavuto chifukwa cha zimene achitazo. Ena amayendetsa galimoto mosasamala ndipo chifukwa cha zimenezi amachita ngozi. Anthu ambiri amasuta fodya, ndiyeno amadwala matenda a mtima kapena kansa ya m’mapapo chifukwa cha kusuta kwawoko. Amene amachita chiwerewere amakhala pa vuto loti banja lawo lingasokonezeke, amataya ulemu wawo, amatenga matenda opatsirana m’njira ya chiwerewere, ndiponso amatenga mimba yomwe sanali kuifuna. Anthu angafune kuimba mlandu Mulungu akamavutika chifukwa cha zimenezi, koma zoona zake n’zakuti akuvutika chifukwa cha zochita zawo zolakwika.​—Miyambo 19:3.

8. Malinga ndi Mlaliki 9:11, n’chifukwa chiyani anthu amavutika?

8 Chifukwa chachitatu chimene chimachititsa anthu kuvutika achifotokoza pa Mlaliki 9:11, pamene pamati: “Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m’liŵiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziŵitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zom’gwera m’nthaŵi mwake.” Nthaŵi zina zimangokhala kuti anthu ali pamalo olakwika, pa nthaŵi yolakwika. Wina aliyense wa ife akhoza kuvutika kapena kumwalira mwadzidzidzi nthaŵi ina iliyonse kaya ndife amphamvu kapena ofooka. Mwachitsanzo, m’nthaŵi ya Yesu nsanja ya ku Yerusalemu inagwa ndipo inapha anthu 18. Yesu anasonyeza kuti sikuti Mulungu anali kulanga anthuwo chifukwa cha machimo amene anachita kale. (Luka 13:4) Si Yehova amene anachititsa kuti anthuwo amwalire.

9. Kodi ndi mfundo iti imene anthu ambiri samvetsa pankhani ya kuvutika kwa anthu?

 9 Kudziŵa zina mwa zifukwa zimene zimachititsa anthu kuvutika n’kofunika. Komabe, pali mfundo ina ya nkhaniyi imene ambiri imawavuta kuimvetsa. Mfundo yake ndi yakuti: N’chifukwa chiyani Yehova Mulungu amalola kuti anthu azivutika?

N’chifukwa Chiyani Yehova Amalola Kuti Anthu Azivutika?

10, 11. (a) Malinga ndi Aroma 8:19-22, n’chiyani chinachitikira “cholengedwa chonse”? (b) Kodi tingadziŵe bwanji amene anagonjetsera cholengedwa ku utsiru?

10 Ndime ina ya kalata imene Paulo analembera Aroma imatithandiza kumvetsa nkhani yofunika kwambiri imeneyi. Iye analemba kuti: “Chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu. Pakuti tidziŵa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.”​—Aroma 8:19-22.

11 Kuti timvetse mfundo ya mavesi ameneŵa, choyamba tifunika kuyankha mafunso ena ofunika kwambiri. Mwachitsanzo, Ndani anagonjetsera cholengedwa ku utsiru? Ena amanena kuti ndi Satana ndipo ena amati ndi Adamu. Koma Satana ndi Adamu sakanachita zimenezo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti amene wagonjetsera cholengedwa ku utsiru wachita zimenezo “ndi chiyembekezo.” Inde, amapereka chiyembekezo chakuti m’kupita kwanthaŵi anthu okhulupirika ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi.’ Adamu kapena Satana sakanapereka chiyembekezo choterocho. Yehova yekha ndi amene akanatha kutero. Motero, n’zoonekeratu kuti ndi Yehova amene anagonjetsera cholengedwa ku utsiru.

12. Kodi pali maganizo osiyana ati pankhani yakuti “cholengedwa chonse” n’chiyani, ndipo tingayankhe bwanji funso limeneli?

12 Koma kodi “cholengedwa chonse” chimene achitchula m’ndime imeneyi n’chiyani? Ena amanena kuti “cholengedwa chonse” chimenechi ndi chinthu chilichonse chimene chili m’dzikoli, kuphatikizapo nyama ndi zomera. Koma kodi nyama ndi zomera zimayembekezera kuloŵa “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu”? Ayi. (2 Petro 2:12) Motero, “cholengedwa chonse” chimene akunena apa ndi anthu okha basi. Chimenechi ndicho cholengedwa chimene chakhudzidwa ndi uchimo ndi imfa chifukwa cha kupanduka kumene kunachitika mu Edene ndipo n’chimene chimafuna kwambiri chiyembekezo.​—Aroma 5:12.

13. N’chiyani chachitikira anthu chifukwa cha kupanduka kumene kunachitika mu Edene?

13 Kodi n’chiyani kwenikweni chachitikira anthu  chifukwa cha kupanduka kumeneku? Paulo anafotokoza zimene zachitika chifukwa cha kupandukako ndi mawu amodzi akuti: utsiru. * Malinga ndi buku lina laumboni, liwu limene analimasulira kuti utsiru limatanthauza “kupanda pake kwa chinthu chimene sichikugwira ntchito imene anachikonzera kuti chizigwira.” Anthu anawalenga kuti akhale ndi moyo kosatha, kuchitira zinthu limodzi monga banja langwiro, logwirizana, posamalira dziko la paradaiso. Koma m’malomwake, anthu amangokhala ndi moyo kwa nthaŵi yochepa ndipo moyo wake umakhala wopweteka ndiponso nthaŵi zambiri wokhumudwitsa. Monga mmene Yobu ananenera, “munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Kupanda pakedi kwenikweni!

14, 15. (a) Kodi tikupeza umboni wotani woti Yehova anaweruza anthu mwachilungamo? (b) N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti cholengedwa chinagonjetsedwa ku utsiru “chosafuna mwini”?

14 Tsopano tikufika pa funso lofunika kwambiri lakuti: N’chifukwa chiyani “Woweruza wa dziko lonse lapansi” anagonjetsera anthu ku moyo wopweteka, wokhumudwitsa woterewu? (Genesis 18:25) Kodi anasonyeza chilungamo pochita zimenezi? Chabwino, takumbukirani zimene makolo athu oyambawo anachita. Popandukira Mulungu, iwo anakhala kumbali ya Satana yemwe anakayikira kwambiri zoti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Mwa zimene anachita, analimbikitsa mfundo yakuti anthu zingawayendere bwino popanda Yehova, koma kuti azidzilamulira okha motsogoleredwa ndi cholengedwa chauzimu chopanduka. Yehova poweruza opandukawo, kwenikweni anawapatsa zimene iwo ankafuna. Analola kuti anthu adzilamulire okha motsogozedwa ndi Satana. Malinga ndi mmene zinalilimu, kodi pakanakhalanso chigamulo china cholungama kwambiri kuposa kuwagonjetsera anthu ku utsiru koma ndi chiyembekezo?

15 Komabe, izi zinachitika ngakhale kuti cholengedwa ‘sichinafune’ kuti zitero. Timabadwa tili akapolo a uchimo ndi chivundi popanda kuchitira mwina. Koma Yehova mwachifundo chake analola kuti Adamu ndi Hava akhale ndi moyo ndi kubereka ana. Ngakhale kuti mbadwa zawofe tagonjetsedwa ku utsiru wa uchimo ndi imfa, tili ndi mwayi wochita zimene Adamu ndi Hava analephera kuchita. Tingamvere Yehova ndi kudziŵa kuti ulamuliro wake ndi wolungama ndiponso wangwiro, pamene ulamuliro wa anthu osadalira Yehova umangobweretsa zopweteka, zokhumudwitsa ndi zinthu zopanda pake. (Yeremiya 10:23; Chivumbulutso 4:11) Ndipo zochita za Satana zikungopangitsa kuti zinthu ziipireipire. Zimene zachitikira anthu zikutsimikizira mfundo zoona zimenezi.​—Mlaliki 8:9.

16. (a) N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti si Yehova amene amachititsa kuvutika kumene tikukuona m’dzikoli? (b) Kodi Yehova wapereka chiyembekezo chotani mwachikondi kwa anthu okhulupirika?

16 Mwachionekere, Yehova anali ndi zifukwa zolungama zimene anagonjetsera anthu ku utsiru. Koma kodi zimenezo zikutanthauza kuti Yehova ndi amene wachititsa kuti anthufe tizivutika masiku ano? Taganizirani woweruza amene wapereka chigamulo cholungama kwa munthu wolakwa. Wolakwayo angavutike ndithu pamene akugwira ukaidi wake, koma kodi zingakhale zoona kunena kuti woweruzayo ndi amene wachititsa kuti iye avutike? Ayi. Ndiponso, si Yehova amene amachititsa zoipa zimene zikuchitikazi. Lemba la Yakobo 1:13 limati: “Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” Ndiponso tiyenera kukumbukira kuti Yehova anapereka chiweruzo pamodzi “ndi chiyembekezo.” Iye mwachikondi wakonza zoti mbadwa zokhulupirika za Adamu ndi Hava zidzaone kutha kwa utsiru ndi kusangalala ndi “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” Kwa nthaŵi yomka muyaya, anthu okhulupirika sadzakhala ndi nkhaŵa yakuti cholengedwa chonse chingadzabwererenso ku utsiru wopweteka. Kuchita zinthu molungama kwa Yehova kudzatsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira mpaka kalekale.​—Yesaya 25:8.

17. Kodi kupenda zifukwa zimene zimachititsa kuti tizivutika m’dzikoli masiku ano kuyenera kutikhudza bwanji?

17 Pamene tapenda zifukwa zimene zikuchititsa kuti anthu azivutika zimenezi, kodi tikuona maziko alionse onenera kuti Yehova ndi amene  wachititsa zoipa zimene zikuchitikazi, kapena kodi pali chifukwa chimene chingatichititse kusamudalira? Mosiyana ndi zimenezo, kudziŵa zimenezi kukutipatsa chifukwa chobwerezera mawu a Mose akuti: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Tiyeni tizisinkhasinkha mfundo zimenezi, ndipo nthaŵi ndi nthaŵi tizipenda mmene tikuzimvera. Mwakutero, tikakumana ndi ziyeso tidzakana zimene Satana amafuna zoti tizikayikira. Nanga bwanji za njira yachiŵiri imene taitchula kuchiyambi kwa nkhani ino? Kodi kudalira Yehova kumatanthauza chiyani?

Zimene Kudalira Yehova Kumatanthauza

18, 19. Kodi Baibulo likutilimbikitsa kudalira Yehova ndi mawu otani, koma kodi ndi maganizo olakwika ati amene anthu ena amakhala nawo pankhani imeneyi?

18 Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Ameneŵatu ndi mawu osangalatsa ndiponso olimbikitsa kwambiri. Kunena zoona, palibe aliyense m’chilengedwe chonse amene ali wodalirika kuposa Atate wathu wokondedwa wakumwamba. Komabe, kuŵerenga mawu ameneŵa m’buku la Miyambo n’kosavuta kusiyana ndi kuwatsatira.

19 Ena ali ndi maganizo olakwika pankhani ya zimene kukhulupirira Yehova kumatanthauza. Ena amaganiza kuti kudalira Yehova kumeneko kumatanthauza kumva bwino mumtima kumene kuyenera kubwera kokha mwa munthu. Ena mwina amaganiza kuti kudalira Mulungu kumatanthauza kuti tingayembekezere kuti adzatiteteza pa vuto lililonse, adzatithandiza kuthetsa mavuto athu onse monga mmene ifeyo tikufunira, ndipo adzachita zimenezi nthaŵi yomweyo. Koma maganizo amenewo alibe maziko. Kudalira Mulungu si kungomva bwino mumtima ayi ndipo sikutanthauza kuyembekezera zinthu zosatheka. Kwa anthu aakulu msinkhu, kudalira Mulungu kumatanthauza kusankha zochita mwanzeru.

20, 21. Kodi kukhulupirira Yehova kumatanthauza chiyani? Perekani chitsanzo.

20 Onaninso zimene lemba la Miyambo 3:5 likunena. Likuti tiyenera kukhulupirira Yehova, osati kuchirikizika pa luntha lathu, kusonyeza kuti sitingachite zinthu ziŵiri zonsezo. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitikuloledwa kugwiritsa ntchito luntha lathu? Ayi, sizikutanthauza zimenezi, chifukwa Yehova, amene anatipatsa lunthalo, kapena kuti “mphamvu ya kulingalira,” amafuna kuti tiligwiritse ntchito pomutumikira. (Aroma 12:1, NW) Koma kodi timachirikizika pa ndani, kapena kuti timadalira ndani? Ngati maganizo athu akusemphana ndi a Yehova, kodi timatsatira nzeru zake podziŵa kuti n’zapamwamba kuposa zathu? (Yesaya 55:8, 9) Kudalira Yehova kumatanthauza kulola kuti maganizo ake atsogolere maganizo athu.

21 Mwachitsanzo, taganizirani mwana wamng’ono amene wakhala pampando wa kumbuyo m’galimoto, ndipo makolo ake akhala pa mipando yakutsogolo. Bambo ake ndi amene akuyendetsa galimotoyo. Akakumana ndi zovuta m’kati mwa ulendowo, mwina kukayikira kuti msewu woyenera kuti ayende ndi uti, kapena vuto la nyengo, kapena mmene msewu ulili, kodi mwana wogonjera, woti akuwadalira makolo akewo amachita bwanji? Kodi amafuula ali kumbuyoko kuti atenge msewu wakuti, kuwauza bambo akewo mmene angayendetsere galimotoyo? Kodi amakayikira zimene makolo akewo asankha kuchita kapena amatsutsa makolo akewo akamuuza kuti akhazikike pampando wakewo? Ayi, iye mwachibadwa amadalira makolo akewo kuti athana ndi mavutowo, ngakhale kuti ndi opanda ungwiro. Yehova ndi Atate wathu  wangwiro. Kodi sitiyenera kumudalira ndi mtima wonse, makamaka tikakumana ndi mavuto?​—Yesaya 30:21.

22, 23. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Yehova tikakumana ndi mavuto, ndipo tingachite bwanji zimenezo? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatirayi?

22 Komabe, pa Miyambo 3:6 pakusonyeza kuti tiyenera ‘kulemekeza Yehova m’njira zathu zonse,’ osati pamavuto pokhapokha ayi. Motero, zimene timasankha kuchita tsiku ndi tsiku ziyenera kusonyeza kuti timadalira Yehova. Pakabuka mavuto, sitiyenera kutaya mtima, kugwira njakata, kapena kukana malangizo a Yehova ofotokoza njira yabwino kwambiri yothetsera mavutowo. Tiyenera kuona ziyeso monga mipata yoti tikhalire kumbuyo ulamuliro wa Yehova, kuthandiza kutsimikizira kuti Satana ndi wabodza, ndiponso kukulitsa kumvera ndi makhalidwe ena amene amakondweretsa Yehova.​—Ahebri 5:7, 8.

23 Tingasonyeze kudalira Yehova ngakhale titakumana ndi zopinga zotani. Timachita zimenezi mwa kupemphera kwa iye ndi kufufuza malangizo m’Mawu a Yehova ndi m’gulu lake kuti atitsogolere. Komabe, kodi tingasonyeze bwanji kukhulupirira Yehova tikakumana ndi mavuto amene amabuka m’dzikoli masiku ano? M’nkhani yotsatirayi tidzakambirana mfundo imeneyi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Liwu la Chigiriki limene Paulo analigwiritsa ntchito limene lamasuliridwa kuti “utsiru” ndi limenenso analigwiritsa ntchito m’Baibulo la Septuagint ya Chigiriki pomasulira mawu amene Solomo anawagwiritsa ntchito mobwerezabwereza m’buku la Mlaliki, monga pa mawu akuti ‘zonse ndi chabe.’​Mlaliki 1:2, 14; 2:11, 17; 3:19; 12:8.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti anali kudalira Yehova?

• Kodi ndi zifukwa zitatu ziti zimene zimachititsa anthu kuvutika masiku ano, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kupenda zimenezi nthaŵi ndi nthaŵi?

• Kodi Yehova anapereka chiweruzo chotani kwa anthu, ndipo n’chifukwa chiyani chiweruzo chimenechi chinali cholungama?

• Kodi kudalira Yehova kumatanthauza chiyani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 8]

Davide anadalira Yehova

[Chithunzi patsamba 10]

Yesu anasonyeza kuti nsanja ina yake itagwa ku Yerusalemu, si Yehova amene anachititsa zimenezo