Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Timakumbukira za Anthu Ena

Zimene Timakumbukira za Anthu Ena

 Zimene Timakumbukira za Anthu Ena

ZAKA pafupifupi 3,000 zapitazo, Davide anali kuthaŵa Mfumu Sauli ya Israyeli. Davide anatumiza uthenga wopempha chakudya ndi madzi kwa Nabala, mbusa wa nkhosa ndi mbuzi wolemera kwambiri. Ndipotu, Nabala anali ndi zifukwa zothandizira Davide ndi gulu lake chifukwa iwo anateteza nkhosa zake. Koma, Nabala anakana kuwapatsa chilichonse. Iye anafika powakalipira anyamata a Davide. Nabala anali kuseŵera ndi moto, chifukwa Davide sanali wochita naye maseŵera.​—1 Samueli 25:5, 8, 10, 11, 14.

Zimene anachita Nabala zinali zosiyana ndi mwambo wa ku Middle East wochereza alendo owadziŵa ndi osawadziŵa omwe. Choncho, kodi Nabala anadzipangira dzina lotani? Nkhani ya m’Baibulo imanena kuti “anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake” ndiponso “woipa.” Dzina lake limatanthauza “wopusa,” ndipo anasonyezadi zimenezo. (1 Samueli 25:3, 17, 25) Kodi mukufuna kuti ena adzakukumbukireni choncho? Kodi ndinu waukali ndi wankhanza pochita zinthu ndi anthu ena, makamaka ngati ali anthu osavuta kuwadyera masuku pamutu? Kapena kodi ndinu munthu wokoma mtima, wochereza alendo, ndiponso woganizira ena?

Abigayeli​—Mkazi Wanzeru

Nabala anali pavuto chifukwa cha ukali wake. Davide ndi amuna ake 400 anamangirira malupanga awo ulendo kukathana ndi Nabala. Abigayeli, mkazi wa Nabala, anamva zimene zinachitika ndipo anadziŵa kuti nkhondo ili pafupi. Kodi anatani? Anathamanga kukakonza chakudya chambiri ndi zinthu zina, ulendo kukakumana ndi Davide ndi anyamata ake. Atakumana nawo, anapempha Davide kuti asakhetse magazi opanda chifukwa. Mtima wa Davide unakhala pansi. Anamvera zimene Abigayeli anapempha ndipo anavomerezana nazo. Zitangochitika zimenezi, Nabala anamwalira. Davide anakwatira Abigayeli ataona makhalidwe ake abwino.​—1 Samueli 25:14-42.

Kodi Abigayeli anadzipangira mbiri yotani? Anali “wa nzeru yabwino.” Anali wozindikira kwambiri ndipo ankadziŵa mochitira zinthu ndiponso pofunika kuchitapo kanthu. Anachita mokhulupirika kuteteza mwamuna wake wopusayo ndi banja lake ku tsoka. Patapita nthaŵi  Abigayeli anamwalira, koma ali ndi mbiri yabwino zedi monga mkazi wanzeru.​—1 Samueli 25:3.

Kodi Petro Anasiya Mbiri Yotani?

Tiyeni tifike mu zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, tione atumwi a Yesu 12. Mosakayikira Petro, kapena kuti Kefa, amene poyamba anali msodzi ku Galileya, ndiye anali wokonda kulankhulalankhula ndiponso wopupuluma. Zikuoneka kuti anali wojijirika, wosaopa kunena maganizo ake. Mwachitsanzo, nthaŵi imene Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake, kodi Petro anachita zotani itafika nthaŵi yake yom’sambitsa mapazi?

Petro anati kwa Yesu: “Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?” Yesu anayankha nati: “Chimene ndichita Ine, suchidziŵa tsopano; koma udzadziŵa m’tsogolo mwake.” Petro anayankha kuti: “Simudzasambitsa mapazi anga ku nthaŵi yonse.” Onani kuti Petro anayankha motsindika koma mopupuluma. Kodi Yesu anayankha bwanji?

Iye anati: “Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi Ine.” Koma Simoni Petro anati kwa iye: “Ambuye, si mapazi anga okha, komanso manja ndi mutu.” Apatu Petro anapempha zinazina. Eya, zinali zosavuta kudziŵa maganizo a Petro. Anali wopanda chinyengo.​—Yohane 13:6-9.

Timam’kumbukiranso Petro chifukwa cha zofooka zake zaumunthu. Mwachitsanzo, anakana Kristu katatu pagulu limene limanena kuti anali wotsatira wa Yesu wa ku Nazareti amene anali kuimbidwa mlandu. Petro atazindikira kulakwa kwake, analira mowawidwa mtima. Sanaope kusonyeza chisoni chake. Mfundonso ina yofunika n’njakuti nkhani ya Petro yokana Yesu  imeneyi inalembedwa ndi olemba Mauthenga Abwino​—ndipo Petro ayenera kuti anawauza zimenezo. Iye anali wodzichepetsa moti anavomereza zolakwa zake. Kodi ndilo khalidwe lanunso?​—Mateyu 26:69-75; Marko 14:66-72; Luka 22:54-62; Yohane 18:15-18, 25-27.

Patangotha milungu ingapo atakana Kristu, Petro analalikira molimba mtima kwa khamu la Ayuda pa Pentekoste atadzazidwa ndi mzimu woyera. Umenewu unali umboni wotsimikiza kuti Yesu woukitsidwayo anali kumudalira.​—Machitidwe 2:14-21.

Panthaŵi ina, Petro anagwera mu msampha wina. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti asanafike abale ena achiyuda ku Antiokeya, Petro ankacheza momasuka ndi okhulupirira amene sanali Ayuda. Komabe, anadzipatula kwa anthu ameneŵa ‘poopa iwo a ku mdulidwe’ amene anangofika kumene kuchokera ku Yerusalemu. Paulo anauza Petro mosabisa kuti akuchita tsankho.​—Agalatiya 2:11-14.

Ngakhale zili choncho, kodi ndi wophunzira uti amene analankhula panthaŵi yovuta imene otsatira a Yesu ambiri anali kuoneka kuti asiya kumutsatira? Nthaŵi yake inali imene Yesu ananena kanthu kena katsopano, kokhudza kufunika kodya thupi lake ndi kumwa magazi ake. Iye anati: “Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.” Ayuda ambiri otsatira Yesu anakhumudwa ndipo anati: “Mawu aŵa ndi osautsa; akhoza kumva aŵa ndani?” Ndiyeno chinachitika n’chiyani? “Pa ichi ambiri a akuphunzira ake anabwerera m’mbuyo, ndipo sanayendayendanso ndi Iye.”​—Yohane 6:50-66.

Panthaŵi yovuta imeneyi, Yesu anafunsa atumwi ake 12 aja funso lokhudza mtima lakuti: “Nanga inunso mufuna kuchoka?” Petro anayankha kuti: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha. Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziŵa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.”​—Yohane 6:67-69.

Kodi Petro anapanga mbiri yotani? Munthu amene amaŵerenga nkhani zake amachita chidwi ndi mtima wake wachilungamo ndiponso wosapsatira mawu, kukhulupirika kwake, komanso kulolera kuvomereza ngakhale zofooka zake. Koma ndiye anadzipangira dzina labwino bwanji!

Kodi Anthu Anakumbukira Zotani za Yesu?

Utumiki wa Yesu wa padziko lapansi unatenga zaka zitatu ndi theka zokha. Koma, kodi otsatira ake amakumbukira zotani za iye? Popeza anali wangwiro, wopanda tchimo, kodi anali wodzikonda ndi wosafuna kucheza ndi ena? Kodi anali kudzionetsera chifukwa ankadziŵa kuti ndi Mwana wa Mulungu? Kodi anali kuopseza ndi kukakamiza otsatira ake kumumvera? Kodi iye anali kufuna kwambiri kudzisungira ulemu moti n’kusachita nthabwala? Kodi anali wotanganidwa kwambiri moti analibe nthaŵi yocheza ndi anthu ofooka ndi odwala kapena ana? Kodi anali kunyoza anthu a mafuko ena ndiponso akazi, monga momwe amuna anali kuchitira nthaŵi imeneyo? Kodi mbiri yake imatiuza zotani?

Yesu anali kukonda anthu. Tikaŵerenga za utumiki wake, timaona kuti anachiritsa opunduka ndi odwala maulendo ambiri. Iye anali wodzipereka pothandiza anthu ovutika. Anakonda ana, n’kuona anauza ophunzira ake kuti: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse.” Ndiyeno Yesu “anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ake pa ito.” Kodi mumakhala ndi nthaŵi yocheza ndi ana, kapena mumakhala wotanganidwa kwambiri moti simudziŵa n’komwe zoti alipo?​—Marko 10:13-16; Mateyu 19:13-15.

Yesu ali padziko lino, Ayuda anali kuponderezedwa ndi malamulo achipembedzo amene anafuna zinthu zimene Chilamulo sichinafune. Atsogoleri awo achipembedzo anali kulemetsa anthu ndi katundu wolemera, pamene iwo eni sanali kufuna kumusuntha katunduyo ndi chala chawo. (Mateyu 23:4; Luka 11:46) Koma Yesu anali wosiyana kwambiri ndi ameneŵa. Iye anati: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.”​—Mateyu 11:28-30.

Anthu anali kupeza mpumulo pocheza ndi Yesu. Iye sanali kuopseza ophunzira ake, iwo sankaopa kunena maganizo awo. Ndipotu, anali  kuwafunsa mafunso powalimbikitsa kuti anene maganizo awo. (Marko 8:27-29) Oyang’anira achikristu ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi inenso ndili wotere kwa okhulupirira anzanga? Kodi akulu anzanga amandiuzadi maganizo awo, kapena amaopa kunena?’ Zimakhala zotsitsimula zedi oyang’anira akakhala ochezeka, omva za anzawo, ndiponso osaumirira zinthu. Kusalolera kumangolepheretsa kukambirana zoona zake zenizeni ndi momasuka.

Ngakhale kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu, sanagwiritse ntchito molakwa mphamvu kapena ulamuliro wake. M’malo mwake, anali kuthandizana kuganiza ndi omvera ake. Ndizo zimene anachita pamene Afarisi anafuna kumutchera ndale pomufunsa kuti: “Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iyayi?” Yesu anawauza kuti amuonetse ndalama ndipo anawafunsa kuti: “N’chayani chithunzithunzi ichi, ndi kulemba kwake?” Anayankha kuti: “Cha Kaisara.” Ndiye iye anati kwa iwo: “Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:15-21) Sanachite kufuna mfundo zozama kuti ayankhe.

Kodi Yesu anali wanthabwala? Anthu ena amene amaŵerenga Baibulo amaona kuti Yesu anali wanthabwala akafika pandime imene ananena kuti n’kosavuta kwa ngamila kupyola pa diso la singano koposa mwini chuma kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 19:23, 24) Mawu okhawo ofotokoza ngamila imene ikuyesa kuloŵa pa diso la singano yeniyeni ndi okokomeza. Chitsanzo china chokokomeza ngati chimenechi ndi chija choona kachitsotso ka m’diso la mbale wako koma osaona mtanda umene uli m’diso mwako. (Luka 6:41, 42) Ndithudi, Yesu sanali wokhwimitsa zinthu. Anali waubwenzi ndi wochezeka. Kwa Akristu masiku ano, nthabwala zingasangalatse mtima panthaŵi yamavuto.

Yesu Anachitira Chifundo Akazi

Kodi akazi ankamva bwanji akakhala ndi Yesu? Mwachionekere anali ndi otsatira aakazi ambiri okhulupirika, kuphatikizapo mayi ake enieni, Mariya. (Luka 8:1-3; 23:55, 56; 24:9, 10) Akazi anali kumasuka kulankhula ndi Yesu moti nthaŵi ina mkazi ‘wodziŵika kuti anali wochimwa’ anam’sambitsa mapazi ake ndi misozi yake n’kuwadzoza mafuta onunkhira bwino. (Luka 7:37, 38) Mkazi wina, amene anali ndi nthenda yokha magazi kwa zaka zambiri, anapita kukakhudza chovala chake kuti achiritsidwe. Yesu anatama chikhulupiriro cha mkaziyo. (Mateyu 9:20-22) Inde, kwa akazi Yesu anali wochezeka.

Panthaŵi ina, Yesu analankhula ndi mkazi wina Msamariya pachitsime. Mkaziyo anadabwa kwambiri moti anati: “Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya?” Eetu, Ayuda sanali kuyenderana ndi Asamariya. Yesu anapitiriza  kumuphunzitsa choonadi chapadera cha ‘madzi otumphuka opereka moyo wosatha.’ Iye anali kumasuka ndi akazi. Sanaganize kuti iwo akhoza kumuloŵerera.​—Yohane 4:7-15.

Yesu amakumbukiridwa chifukwa cha makhalidwe ake abwino ambiri, ndiponso mtima wake wodzimana. Iye anali chitsanzo chabwino kwambiri cha chikondi cha Mulungu. Yesu amapereka chitsanzo kwa anthu onse amene akufuna kukhala otsatira ake. Kodi mumatsatira chitsanzo chake kufika pati?​—1 Akorinto 13:4-8; 1 Petro 2:21.

Kodi Akristu Amasiku Ano Timawakumbukira Ngati Anthu Otani?

Masiku ano, Akristu ambiri okhulupirika amwalira, ambiri ali okalamba, ena ali achinyamata ndithu. Koma asiya mbiri yabwino. Ena monga a Crystal, amene anamwalira ali okalamba, timawakumbukira chifukwa cha khalidwe lawo lokonda anthu ndiponso locheza. Ena, monga Dirk, amene anamwalira ali m’zaka zake za m’ma 40, timawakumbukira chifukwa cha khalidwe lawo losangalala ndiponso lodzipereka.

Palinso José wa ku Spain. Cha m’ma 1960, ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova ili yoletsedwa m’dzikoli, José anakwatira ndipo anakhala ndi ana aakazi atatu. Anali pantchito yodalirika ku Barcelona. Koma panthaŵiyo, kum’mwera kwa Spain kunali kufunika akulu achikristu okhwima mwauzimu. José anasiya ntchito yake yodalirikayo n’kusamukira ku Málaga ndi banja lake. Iwo anapirira mavuto azachuma, ndipo nthaŵi zambiri anali paulova.

Komabe, José anali kudziŵika chifukwa cha kukhulupirika kwake, chitsanzo chabwino mu utumiki ndiponso chifukwa cholera bwino ana ake, zimene anakwanitsa mothandizidwa ndi mkazi wake wolimbikitsa, Carmela. Pakafunika munthu woti alinganize misonkhano ikuluikulu ya Akristu m’chigawocho, nthaŵi zonse José ankadzipereka. Mwatsoka lanji, ali m’zaka zake za m’ma 50, anadwala matenda aakulu amene anafa nawo. Komabe, anasiya mbiri yoti anali wodalirika, mkulu wolimbikira ntchito ndiponso mwamuna ndi bambo wachikondi.

Tsopano kodi ena adzakukumbukirani ngati munthu wotani? Mukanakhala kuti munamwalira dzulo, kodi lero bwenzi anthu akunena zotani za inu? Limeneli ndi funso limene lingatilimbikitse tonsefe kusintha zochita zathu kukhala zabwino.

Kodi tingatani kuti tipange mbiri yabwino? Nthaŵi zonse tingathe kuwongolera mmene timaonetsera zipatso za mzimu monga chikondi, kuleza mtima, kukoma mtima, chifatso, ndi kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Ndithudi, “mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.”​—Mlaliki 7:1; Mateyu 7:12.

[Chithunzi patsamba 5]

Timam’kumbukira Abigayeli chifukwa cha nzeru zake

[Chithunzi patsamba 7]

Timam’kumbukira Petro chifukwa cha kupupuluma kwake komanso mtima wake wachilungamo

[Chithunzi patsamba 8]

Yesu anapatula nthaŵi yocheza ndi ana