Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudzipangira Dzina Lotani?

Kodi Mukudzipangira Dzina Lotani?

 Kodi Mukudzipangira Dzina Lotani?

KODI munaŵerengapo m’nyuzipepala patsamba limene amalembapo za anthu akufa kapena kodi munaonapo mbiri yonse ya moyo wa munthu wakufa ndi zimene anachita? Kodi munadzifunsa kuti, ‘Kodi anthu azidzanena zotani za ine?’ Kodi ndi anthu angati amene amaganizira zimene anthu azidzanena za iwo akadzamwalira? Ndiye lingalirani mafunso osapita mbali aŵa: Kodi mukanakhala kuti munamwalira dzulo, bwenzi anthu lero akunena zotani za inu? Kodi mukudzipangira mbiri yotani? Kodi mukufuna kuti anthu amene amakudziŵani ndiponso Mulungu adzakukumbukireni ngati munthu wotani?

Munthu wanzeru amene analemba buku la m’Baibulo la Mlaliki anati: “Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.” (Mlaliki 7:1) Kodi n’chifukwa chiyani tsiku limene munthu wamwalira limaposa tsiku limene anabadwa? Chifukwa chakuti munthu pobadwa amakhala alibiretu mbiri ina iliyonse. Zochita zake pamoyo wake n’zimene zimapangitsa kuti akhale ndi mbiri yabwino kapena yoipa. Anthu amene kwa zaka zambiri apanga dzina labwino, tsiku lawo lomwalira limakhaladi labwino kuposa tsiku lobadwa pachifukwa chimenechi.

Chotero tiyenera kusankha zimene tikufuna. Ndipotu, tsiku lililonse timakhala ndi zosankha zambiri zimene zidzapange mbiri yathu patsiku lathu lomwalira, makamaka zimene Mulungu azidzakumbukira za ife. Choncho, Mhebri wanzeru yemwe uja anati: “Amayesa wolungama wodala pom’kumbukira; koma dzina la oipa lidzabvunda.” (Miyambo 10:7) Ndi mwayi waukulu kwambiri Mulungu kutikumbukira kuti tilandire madalitso.

Ngati ndife anzeru, cholinga chathu chidzakhala kukondweretsa Mulungu mwa kutsata miyezo yake. Zimenezi zikutanthauza kutsatira mfundo zikuluzikulu zimene Kristu ananena. Iye anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiŵiri lolingana nalo ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini. Pa malamulo aŵa aŵiri m’pokolowekapo chilamulo chonse ndi aneneri.”​—Mateyu 22:37-40.

Ena anthu amawakumbukira monga othandiza osoŵa, olimbikitsa ufulu wa nzika, kapena chifukwa cha zimene anachita m’zamalonda, sayansi, zamankhwala, kapena ntchito zina. Nanga za inuyo? Kodi mukufuna kuti ena adzakukumbukireni ngati munthu wotani?

Robert Burns wolemba ndakatulo wa ku Scotland (1759-96) ananena kuti zikanakhala bwino Mulungu akanatipatsa mphatso yoti tizitha kudziona ife eni monga mmene ena  amationera. Kodi mutadziyang’ana mwachifatse munganene kuti muli ndi mbiri yabwino kwa anthu ena ndiponso kwa Mulungu? Pomalizira pake, ubwenzi wathu ndi anthu ena umakhala wofunika kwambiri kuposa zinthu zilizonse zosakhalitsa zimene tingachite m’zamaseŵero kapena m’zamalonda. Choncho nali funso lofunika kwambiri: Kodi zimene timachitira anthu ena​—zolankhula zathu, khalidwe lathu, mmene thupi lathu limakhalira pochita zinthu​—zimawakhudza bwanji? Kodi iwo amationa kukhala wochezeka kapena wodzikuza? Wokoma mtima kapena wankhanza? Wololera kapena waliuma? Waubwenzi ndi woganizira ena kapena wopanda chifundo ndi wosafuna kucheza ndi ena? Kodi amationa monga munthu wongokhalira kupeza anzake zifukwa kapena monga phungu wolimbikitsa? Tiyeni tipende zitsanzo zingapo zakale ndi zamasiku ano kuti tione zimene tingaphunzirepo.

[Chithunzi patsamba 3]

Robert Burns anati zikanakhala bwino Mulungu akanatipatsa mphatso yoti tizitha kudziona ife eni monga mmene ena amationera

[Mawu a Chithunzi]

Zinatengedwa m’buku la A History of England