Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Taonani, Uyu Ndiye Mulungu Wathu”

“Taonani, Uyu Ndiye Mulungu Wathu”

 “Taonani, Uyu Ndiye Mulungu Wathu”

Nkhani ziŵiri zophunzira za m’magazini ino zachokera m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, limene linatuluka pa misonkhano yachigawo imene inachitika padziko lonse mu 2002/03.​—Onani nkhani yakuti “Linakwaniritsa Chimene Mtima Wanga Unkafuna Kwambiri,” patsamba 20.

“Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tam’lindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova.”​—YESAYA 25:9.

1, 2. (a) Kodi Yehova anatcha kholo lakale Abrahamu kuti ndani wake, ndipo kodi zimenezi zingatipangitse kufunsa kuti chiyani? (b) Kodi Baibulo limatitsimikizira bwanji kuti n’kotheka kukhala paubwenzi wapamtima ndi Mulungu?

“BWENZI langa.” Umu ndi mmene Yehova, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, anatchulira kholo lakale Abrahamu. (Yesaya 41:8) Tangolingalirani, munthu wamba kukhala paubwenzi ndi Ambuye Mfumu yachilengedwe chonse! Mungafunse kuti, ‘Kodi ine ndingakhale paubwenzi umenewu ndi Mulungu?’

2 Baibulo limatitsimikizira kuti n’kotheka kukhala paubwenzi wapamtima ndi Mulungu. Abrahamu anali paubwenzi woterewo chifukwa “anakhulupirira Mulungu.” (Yakobo 2:23) Masiku anonso, Yehova “ndi bwenzi la oongoka.” (Miyambo 3:32, NW) Pa Yakobo 4:8, Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” Ndithudi, tikayamba kuchita zinthu zofunika kuti tiyandikire kwa Yehova, iye adzachitapo kanthu. Inde, iye adzayandikira kwa ife. Koma kodi mawu ouziridwa ameneŵa akutanthauza kuti ifeyo, anthu ochimwa ndi opanda ungwiro, ndi amene timakhala oyamba kuchitapo kanthu? Ayi, sakutanthauza choncho. N’kotheka kukhala paubwenzi ndi Yehova chifukwa chakuti Mulungu wathu wachikondi anachita kale zinthu ziŵiri zofunika kuti tikhale naye paubwenzi.​—Salmo 25:14.

3. Kodi n’zinthu ziŵiri ziti zimene Yehova wachita kuti tithe kukhala naye paubwenzi?

3 Choyamba, Yehova anakonza kuti Yesu ‘apereke moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Timayandikira kwa Mulungu chifukwa cha nsembe ya dipo imeneyo. Baibulo limati: “Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Inde, popeza kuti Mulungu ndiye ‘anayamba kutikonda,’ anatiyalira maziko okhala naye paubwenzi.  Chinthu chachiŵiri chimene Yehova wachita ndi chakuti watidziŵitsa za iye. Paubwenzi uliwonse umene timapanga, timakhala ogwirizana kwambiri ndi mnzathuyo chifukwa chakuti timam’dziŵa bwino, timachita kaso ndi makhalidwe ake ndiponso timaona makhalidwewo kukhala abwino. Onani tanthauzo la zimenezi. Yehova akanakhala kuti ndi Mulungu wobisika ndiponso wosadziŵika, sitikanatha kuyandikira kwa iye. Koma m’malo modzibisa, Yehova amafuna kuti timudziŵe. (Yesaya 45:19) M’Mawu ake, Baibulo, iye amadziulula mosavuta kumva, womwe ndi umboni wakuti amatikonda komanso kuti amafuna kuti timudziŵe ndi kumukonda monga Atate wathu wakumwamba.

4. Kodi tidzamuona bwanji Yehova tikadziŵa bwino makhalidwe ake?

4 Kodi munamuonapo mwana wamng’ono akulozera anzake bambo ake ndiyeno mwachimwemwe ndi monyadira bwino n’kunena kuti, “Mwawaona ababa anga”? Amene amalambira Mulungu ali ndi zifukwa zomveka zomuona choncho Yehova. Baibulo limaneneratu za nthaŵi imene anthu okhulupirika adzafuula kuti: “Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu.” (Yesaya 25:8, 9) Pamene tizindikira kwambiri makhalidwe ake, m’pamenenso tidzaona kwambiri kuti tili ndi Atate abwino zedi ndiponso Bwenzi lapamtima kwambiri. Inde, kumvetsa makhalidwe a Yehova kumatipatsa zifukwa zambiri zoyandikirira kwa iye. Choncho tiyeni tione momwe Baibulo limaululira makhalidwe ofunika kwambiri a Yehova omwe ndi mphamvu, chilungamo, nzeru, ndi chikondi. M’nkhani ino, tikambirana makhalidwe atatu oyambawo.

“Wa Mphamvu Yoposa”

5. N’chifukwa chiyani n’koyenera kuti Yehova yekha ndi amene amatchedwa “Wamphamvuyonse,” ndipo kodi amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake zochititsa manthazo?

5 Yehova “ndiye wa mphamvu yoposa.” (Yobu 37:23) Yeremiya 10:6 amati: “Palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkulu, ndipo dzina lanu lili lalikulu ndi lamphamvu.” Mosiyana ndi cholengedwa chilichonse, Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire. Pa chifukwa chimenechi, iye yekha ndi amene amatchedwa kuti “Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 15:3) Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake zochititsa manthazo polenga, kuwononga, kuteteza, ndiponso kubwezeretsa. Taonani zitsanzo ziŵiri zokha zotsatirazi zokhudza mphamvu zake zolenga ndiponso zoteteza.

6, 7. Kodi dzuŵa n’lamphamvu motani, ndipo limachitira umboni mfundo yofunika iti?

6 Mukaimirira panja masana tsiku lowala bwino m’chilimwe, kodi thupi lanu limamva chiyani? Limamva kutentha kwa dzuŵa. Komatu, kwenikweni mumakhala mukumva zotsatira za mphamvu za kulenga za Yehova. Kodi dzuŵa n’lamphamvu motani? Pakatikati pa dzuŵa m’potentha pafupifupi madigiri seshasi 15,000,000. Ngati mutatenga kachibenthu ka pakati pa dzuŵa kakakulu ngati njere ya therere lobala n’kukaika pa dziko lapansi pano, kuti musapse mungafunike kuima pa mtunda wa makilomita 140 kuchokera pamene mwakaikapo! Pa sekondi iliyonse, dzuŵa limatulutsa mphamvu zofanana ndi zimene zingatuluke pataphulika mabomba a nyukiliya mamiliyoni mazana ochuluka. Komatu, dziko lapansi limazungulira ng’anjo yaikulu  yotentha kwambiri imeneyo litatalikana nayo bwino zedi. Ngati likanayandikira kwambiri, madzi onse padziko lapansi akanaphwera; likanatalikira kwambiri, madzi onse akanaundana. Kuyandikira kwambiri kapena kutalikira kwambiri kukanachititsa dziko lathuli kukhala lopanda chamoyo.

7 Anthu ambiri saliŵerengera kwenikweni dzuŵa ngakhale kuti moyo wawo umadalira dzuŵa. Motero sazindikira zimene dzuŵa lingatiphunzitse. Salmo 74:16 limanena za Yehova kuti: “Munakonza kuunika ndi dzuŵa.” Inde, dzuŵa limalemekeza Yehova, “amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi.” (Salmo 146:6) Ngakhale zili choncho, dzuŵa ndi cholengedwa chimodzi chabe mwa zolengedwa zosaŵerengeka zomwe zimatiphunzitsa mphamvu zazikulu za Yehova. Pamene tikuphunzira zochuluka za mphamvu za kulenga za Yehova, m’pamenenso timakhala ndi mantha aulemu kwambiri.

8, 9. (a) Kodi ndi chithunzi chabwino kwambiri chiti chimene chikutionetsa kuti Yehova amafunitsitsa kuteteza ndi kusamalira anthu amene amamulambira? (b) Kodi mbusa m’nthaŵi za m’Baibulo ankasamalira bwanji nkhosa zake, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za Mbusa wathu Wamkulu?

8 Yehova amagwiritsanso ntchito mphamvu zake zochulukazo kuteteza ndi kusamalira atumiki ake. Baibulo limagwiritsa ntchito mafanizo omveka bwino ndi ogwira mtima pofotokoza lonjezo la Yehova loteteza anthu ake. Mwachitsanzo, onani pa Yesaya 40:11. Pa lembali Yehova akudziyerekezera ndi mbusa, ndipo akuyerekeza anthu ake ndi nkhosa. Timaŵerenga kuti: “Iye adzadyetsa zoŵeta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.” Kodi mukutha kuona m’maganizo mwanu zimene zikulongosoledwa pa vesili?

9 Pali nyama zochepa zomwe zimafuna kuthandizidwa kwambiri monga zimachitira nkhosa zoŵeta. Mbusa m’nthaŵi za m’Baibulo ankafunika kukhala wolimba mtima kuti ateteze nkhosa zake ku mimbulu, zimbalangondo, ngakhalenso ku mikango. (1 Samueli 17:34-36; Yohane 10:10-13) Koma panali nthaŵi zina pamene kuteteza ndi kusamalira nkhosa kunafuna kuti munthuyo asonyeze chifundo. Mwachitsanzo, nkhosa ikaberekera kutali ndi khola, kodi mbusa ankateteza bwanji kamwana kobadwa kumene kamene sikangathe kudziteteza kokha? Anali kukanyamula, mwina kwa masiku angapo, “pa chifuwa chake,” kapena kuti pa chovala chake chakumtunda chomwe anali kuchipinda. Koma kodi kamwana ka nkhosa kakanakhala bwanji pa chifuwa cha mbusa? Mwina kamwana kankhosako kanali kufika pamene panali mbusayo ndi kumakhudzakhudza mwendo wake. Koma ndi mbusayo amene anayenera kuŵerama n’kunyamula kankhosako ndi kukaika pa chifuwa chake pomwe kangakhale motetezeka. Ndi chithunzithunzi chabwinotu kwambiri choonetsa kuti Mbusa wathu Wamkulu amafunitsitsa kuteteza ndi kusamalira atumiki ake.

10. Kodi masiku ano Yehova amapereka chitetezo chotani, ndipo n’chifukwa chiyani chimenechi chili chitetezo chofunika kwambiri?

10 Yehova sanangolonjeza kupereka chitetezo; wachitanso zina zambiri. M’nthaŵi za m’Baibulo, anaonetsa m’njira zozizwitsa kuti ndi wokhoza “kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo.” (2 Petro 2:9) Nanga bwanji lerolino? Timazindikira kuti masiku ano sagwiritsa ntchito mphamvu zake kutiteteza ku masoka onse. Komabe, amapereka chinachake chofunika kwambiri, chomwe ndi chitetezo chauzimu. Mulungu wathu wachikondi amatiteteza kuti tisavulale mwauzimu potipatsa zomwe timafunikira kuti tithe kupirira ziyeso ndiponso kuteteza ubwenzi wathu ndi iye. Mwachitsanzo, pa Luka 11:13 pamati: “Ngati inu, okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?” Mphamvu yaikulu imeneyi ingatipatse makhalidwe ofunika kuti tithane ndi chiyeso kapena vuto lililonse limene tingakumane nalo. (2 Akorinto 4:7) Motero Yehova amachita zinthu kuti apulumutse moyo wathu, osati kwa zaka zoŵerengeka chabe koma kosatha. Popeza tili ndi chiyembekezo chimenechi, tingaone kuvutika kulikonse m’dzikoli monga ‘kopepuka ndi kwa kanthaŵi.’ (2 Akorinto 4:17) Kodi sitikulakalaka titayandikana ndi Mulungu amene mwachikondi amagwiritsa ntchito mphamvu zake potithandiza?

“Yehova Akonda Chilungamo”

11, 12. (a) N’chifukwa chiyani chilungamo cha Yehova chimatiyandikizitsa kwa iye? (b) Kodi Davide ananena chiyani za chilungamo cha Yehova, nanga mawu ouziridwa ameneŵa angatilimbikitse motani?

11 Yehova amachita zinthu zoyenera ndi zosakondera, ndipo nthaŵi zonse amachita zimenezi mopanda tsankhu. Chilungamo cha Mulungu si khalidwe losasangalatsa kapena lopanda chifundo limene limatipangitsa kuipidwa naye, koma ndi  khalidwe labwino limene limatipangitsa kumuyandikira Yehova. Baibulo limalongosola momveka bwino kuti khalidwe limeneli n’losangalatsa zedi. Motero tiyeni tione njira zitatu zimene Yehova amasonyezera chilungamo chake.

12 Njira yoyamba, chilungamo cha Yehova chimamuchititsa kukhala wodalirika ndi wokhulupirika kwa atumiki ake. Wamasalmo Davide anachita kudzionera yekha mbali imeneyi ya chilungamo cha Yehova. Mwa zimene zinamuchitikira ndiponso mwa kuphunzira kwake njira za Mulungu, kodi Davide anafika ponena chiyani? Iye anati: “Yehova akonda chiweruzo [“chilungamo,” NW] ndipo sataya okondedwa ake: asungika kosatha.” (Salmo 37:28) Ameneŵatu ndi mawu olimbikitsa kwambiri! Nthaŵi zonse Mulungu wathu sadzataya anthu amene ali okhulupirika kwa iye. Motero tingakhale ndi chidaliro chakuti amakhala nafe pafupi ndiponso amatisamalira chifukwa amatikonda. Chilungamo chake chimatitsimikizira zimenezi!​—Miyambo 2:7, 8.

13. Kodi Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisrayeli chimaonetsa motani kuti iye amadera nkhaŵa anthu ovutika?

13 Njira yachiŵiri, popeza Mulungu ndi wachilungamo, amazindikira bwino kwambiri zimene anthu ovutika akufunika. Yehova amadera nkhaŵa anthu ovutika, ndipo zimenezi zikuoneka mosavuta m’Chilamulo chimene anapatsa Aisrayeli. Mwachitsanzo, m’Chilamulocho munali makonzedwe otsimikizira kuti ana amasiye ndi akazi amasiye anali kusamalidwa. (Deuteronomo 24:17-21) Pozindikira kuti moyo udzakhala wovuta kwa mabanja oterowo, Yehova mwiniyo anali Woweruza wawo ndi Mtetezi wawo monga ngati tate. (Deuteronomo 10:17, 18) Iye anachenjeza Aisrayeli kuti ngati angazunze akazi ndi ana osoŵa chitetezo, iye adzamva kulira kwawo. “Mkwiyo wanga udzayaka,” iye anatero malinga n’kunena kwa Eksodo 22:22-24. Ngakhale kuti mkwiyo si khalidwe lina lalikulu la Mulungu, iye amakwiya molungama ngati anthu mwadala sakuchita zachilungamo, makamaka pamene ovutitsidwawo ndi anthu osavuta kuwadyera masuku pamutu.​—Salmo 103:6.

14. Kodi ndi umboni wochititsa chidwi kwambiri uti umene umasonyeza kuti Yehova alibe tsankhu?

14 Njira yachitatu, pa Deuteronomo 10:17 Baibulo likutitsimikizira kuti Yehova ‘sasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.’ Mosiyana ndi anthu ambiri amene ali ndi udindo kapena mphamvu, Yehova satengeka ndi chuma cha munthu kapena maonekedwe a munthu. Iye sakondera kaya kuchita tsankhu m’pang’onong’ono pomwe. Umboni wochititsa chidwi kwambiri wakuti Yehova alibe tsankhu ndi uwu: Mwayi wokhala olambira ake oona, omwe akuyembekeza kukhala ndi moyo kosatha, sanaupereke kwa anthu osankhika ochepa okha. M’malo mwake, Machitidwe 10:34, 35 amati: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” Aliyense akhoza kukhala ndi chiyembekezo chimenechi mosasamala kanthu kuti ndi munthu wotani m’dera lakwawo, kaya kuti ali ndi khungu lamtundu wanji, kapenanso kuti akukhala m’dziko liti. Kodi chimenechi sindicho chilungamo chenicheni? Ndithudi, kumvetsa bwino chilungamo cha Yehova kumatiyandikizitsa kwa iye.

‘Ha! Kuya Kwake kwa Nzeru za Mulungu!’

15. Kodi nzeru n’chiyani, ndipo kodi Yehova amasonyeza motani kuti ndi wanzeru?

15 Mtumwi Paulo anafika ponena mawu omwe ali pa Aroma 11:33, akuti: “Ha! Kuya kwake kwa . . . nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu!” Inde, pamene tisinkhasinkha mbali zosiyanasiyana za nzeru zochuluka za Yehova, sitilephera kuzizwa. Komabe, kodi tingamasulire bwanji khalidwe limeneli? Nzeru ndizo kugwiritsa ntchito zimene munthu ukudziŵa, ndi kuzindikira, ndiponso kumvetsa kwako zinthu. Chifukwa chodziŵa zinthu zambirimbiri ndiponso chifukwa chozimvetsa bwino, Yehova nthaŵi zonse amapanga zosankha zabwino kwambiri ndipo amazichita m’njira yabwino koposa.

16, 17. Kodi zimene Yehova analenga zikutsimikizira bwanji kuti ndi wanzeru zochuluka? Perekani chitsanzo.

16 Kodi ndi umboni wina uti umene ukusonyeza kuchuluka kwa nzeru za Yehova? Salmo 104:24 limati: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.” Inde, pamene tiphunzira kwambiri zinthu zimene Yehova analenga, m’pamenenso timazizwa kwambiri ndi nzeru zake. Tangolingalirani zimene asayansi aphunzira popenda chilengedwe cha Yehova! Pali gawo lina la uinjiniya limene limafufuza mmene zinthu zachilengedwe zinalinganizidwira ndi kumayesa kupanga zinthu mofananitsa ndi zimene apeza m’chilengedwecho.

 17 Mwachitsanzo, mwinamwake inu munachitapo chidwi ndi kukongola kwa utatavu, kapena kuti ukonde wa kangaude. Indedi, ndi wopangidwa mwaukatswiri. Mautatavu ena amene amaoneka ngati osalimba atakhala aakulu mofanana ndi chitsulo kapenanso ulusi wa zovala zimene zipolopolo za mfuti zimalephera kuboola, tingaone kuti ndi olimba kuposa zinthu zimenezi. Kodi zimenezi zikutanthauzanji kwenikweni? Talingalirani kuti mwakulitsa utatavu mpaka kukhala waukulu ngati ukonde umene anthu amagwiritsa ntchito posodza ndi bwato. Utatavu woterowo ukhoza kukhala wamphamvu kwambiri moti ungaimitse ndege imene ikuuluka ndi liŵiro lake lonse! Zoonadi, Yehova anazipanga “mwanzeru” zinthu zonsezi.

18. Kodi nzeru za Yehova zikuoneka motani pogwiritsa ntchito anthu kulemba Mawu ake, Baibulo?

18 Umboni waukulu kwambiri wa nzeru za Yehova tingaupeze m’Mawu ake, Baibulo. Uphungu wanzeru umene uli m’buku limeneli umatisonyezadi mmene tingakhalire ndi moyo m’njira yabwino kwambiri. (Yesaya 48:17) Koma nzeru zosayerekezeka za Yehova zimaonekanso m’njira imene Baibulo linalembedwera. Motani? Mwa nzeru zake, Yehova anasankha kugwiritsa ntchito anthu kuti alembe Mawu ake. Akanagwiritsa ntchito angelo, kodi Baibulo likanakhala logwira mtima ngati mmene lilili panopa? N’zoona kuti angelo akanalongosola za Yehova mwapamwamba monga mmene iwo amamuonera, ndipo akananena mmene iwo alili odzipereka kwa iye. Koma kodi tikanathadi kuzimvetsa zimenezi kuchokera pa kaonedwe ka zolengedwa zauzimu zangwiro, zomwe zimadziŵa zinthu zochuluka, zaona zinthu zambiri, ndiponso zili ndi mphamvu kwambiri kuposa ife?​—Ahebri 2:6, 7.

19. Kodi n’chitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuti kugwiritsa ntchito anthu kulemba Baibulo kumalipangitsa kukhala losangalatsa ndi lokopa kwambiri?

19 Baibulo limasangalatsa poŵerenga ndipo n’lokopa kwambiri chifukwa choti linalembedwa ndi anthu. Olembawo anali anthu omva zinthu zomwe ife timamva. Popeza anali opanda ungwiro, anakumana ndi ziyeso komanso mavuto ofanana ndi amene ife timakumana nawo. Nthaŵi zina, anali kulemba m’mawu osonyeza kuti nkhaniyo inali kuchitikira iwo, mmene iwo anali kumvera mumtima mwawo ndiponso zimene anali kulimbana nazo. (2 Akorinto 12:7-10) Motero polemba anagwiritsa ntchito mawu amene mngelo sakanawalemba choncho. Mwachitsanzo, talingalirani mawu a Davide omwe ali mu Salmo 51. Malinga ndi timawu ta pamwamba pa Salmoli, Davide analemba salmo limeneli atachita tchimo lalikulu. Ananenamo mawu a kukhosi kwake osonyeza kuti anali wachisoni kwambiri ndipo anapempha Mulungu kuti  amukhululukire. Mu vesi 2 ndi 3, anati: “Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire.” Taonani m’vesi 5 limene likuti: “Onani, ndinabadwa m’mphulupulu: ndipo mayi wanga anandilandira m’zoipa.” Vesi 17 likuti: “Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.” Kodi simukukhudzika mtima ndi mmene wolembayo anavutikira? Ndaninso wina akananena mawu otereŵa kuchokera pansi pamtima kupatulapo munthu wopanda ungwiro?

20, 21. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo lili ndi nzeru za Yehova ngakhale kuti analemba ndi anthu? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

20 Mwa kugwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro oterowo, Yehova anatipatsa zimene timafunikadi, buku ‘louziridwa ndi Mulungu’ koma lofotokozabe zinthu m’njira imene anthu angathe kumvetsa. (2 Timoteo 3:16) Inde, olembawo anali kutsogoleredwa ndi mzimu woyera. Motero iwo analemba nzeru za Yehova osati zawo. Nzeru zimenezo n’zodalirika kwambiri. Nzeru zimenezi zimapambana kwambiri nzeru zathu moti Mulungu amatilangiza mwachikondi kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umulemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Mwa kutsatira malangizo anzeru ameneŵa, timayandikira kwambiri kwa Mulungu wathu wanzeru zonse.

21 Mwa makhalidwe onse a Yehova, khalidwe losangalatsa kwambiri ndiponso labwino zedi ndi chikondi. Tikambirana mu nkhani yotsatira mmene Yehova wasonyezera chikondi.

Kodi Mungakumbukire?

Kodi Yehova wachita zotani kuti tikhale naye paubwenzi wapamtima?

Kodi zina mwa zitsanzo za mphamvu za Yehova za kulenga ndi zoteteza n’ziti?

Kodi Yehova amasonyeza bwanji chilungamo chake?

Kodi nzeru za Yehova zimaoneka bwanji m’zimene analenga komanso m’Baibulo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Monga mbusa amene wanyamula mwana wa nkhosa pa chifuwa chake, Yehova amasamalira nkhosa zake mwachikondi

[Chithunzi patsamba 13]

Timaona nzeru za Yehova mmene Baibulo linalembedwera