Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Tingakhalire ndi Chikondi Chenicheni

Mmene Tingakhalire ndi Chikondi Chenicheni

 Mmene Tingakhalire ndi Chikondi Chenicheni

“Chikondi ndi mankhwala a matenda onse; chikondi ndi moyo.”​—Linatero buku lolembedwa mu 1871 ndi Joseph Johnson lakuti, Living to Purpose.

KODI munthu amaphunzira bwanji kukonda ena? Kodi ndi mwa kuphunzira sayansi ya maganizo ndi makhalidwe a anthu? Kodi ndi mwa kuŵerenga mabuku a malangizo? Kapena mwa kuonerera mafilimu achikondi? Ayi ndithu. Anthu amayamba kuphunzira chikondi mwa chitsanzo cha makolo ndi zimene akuphunzitsidwa ndi makolowo. Ana angaphunzire tanthauzo lachikondi ngati ali pamalo achikondi, akuona makolo awo akuwasamalira ndi kuwateteza, kulankhulana nawo ndi kuwasonyeza chidwi chapadera. Iwo amaphunziranso kukonda ena ngati makolo awo awaphunzitsa kutsatira mfundo zabwino zachikhalidwe zokhudza chabwino ndi choipa.

Chikondi chenicheni si kungotengeka mtima chabe. Chikondi chenicheni nthaŵi zonse chimachita zinthu zokomera ena ngakhale kuti anthuwo sangaone ubwino wa zimenezo panthaŵiyo. Ndipo nthaŵi zambiri ndi mmene zimakhalira kwa ana pamene akupatsidwa chilango mwachikondi. Mlengi ali chitsanzo chabwino koposa chosonyeza chikondi chopanda dyera. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye; pakuti iye amene Ambuye am’konda am’langa.”​—Ahebri 12:5, 6.

Makolo, kodi mungatsatire bwanji chitsanzo cha Yehova posonyeza chikondi kwa ana anu? Ndipo kodi chitsanzo chimene mumasonyeza paubale wanu monga mwamuna ndi mkazi ndi chofunika motani?

Phunzitsani Chikondi Mwakuchisonyeza

Ngati ndinu mwamuna, kodi mumaona mkazi wanu kukhala wofunika kwambiri ndiponso mumam’lemekeza? Ngati ndinu mkazi, kodi mumakonda mwamuna wanu ndiponso mumam’thandiza? Baibulo limanena kuti mwamuna ndi mkazi ayenera kukondana ndi kulemekezana. (Aefeso 5:28; Tito 2:4) Pamene achita zimenezi, ana awo amaona chikondi chachikristu chikusonyezedwa panyumba. Zimenezi zingakhaletu phunziro logwira mtima ndiponso lothandiza!

Makolo amalimbikitsanso chikondi panyumba pamene atsatira miyezo yapamwamba ya banja yokhudza zinthu monga zosangalatsa, makhalidwe abwino ndiponso zolinga komanso zinthu zimene zifunika kukhala patsogolo. Anthu padziko lonse apeza kuti Baibulo n’lothandiza  kwambiri pokhazikitsa miyezo yabanja yotero ndipo iwo akhala umboni woti Baibulo lilidi ‘louziridwa ndi Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.’ (2 Timoteo 3:16) Ndithudi, anthu ambiri amaona mfundo zachikhalidwe ndi malangizo okhudza moyo opezeka m’Ulaliki wa pa Phiri kukhala abwino kwambiri.​—Mateyu, chaputala 5 mpaka 7.

Ngati banja lonse lipempha Mulungu kuti alitsogolere ndiponso litsatira miyezo yake, aliyense amaona kukhala wosungika, ndipo ana angakule ali ndi chikondi ndiponso kulemekeza makolo awo. Mosiyana ndi zimenezi, banja limene limanena zina ndi kuchita zina, limene limatsatira miyezo yosayenera kapena yolekerera, ana angaputidwe, kukwiya ndipo angapanduke.​—Aroma 2:21; Akolose 3:21.

Nanga bwanji makolo opanda mnzawo wa muukwati? Kodi sangathe kuphunzitsa chikondi kwa ana awo? Ayi. Ngakhale kuti palibe chimene chingapose mayi ndi bambo abwino ogwirira ntchito pamodzi, zochitika zimasonyeza kuti mmene ubwenzi ungakhalire pabanjapo ungachepetseko vuto limene lilipo la kusakhalapo kwa kholo linalo. Ngati ndinu kholo lopanda mnzanu wa muukwati, yesetsani kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo panyumba panu. Ndithudi, mwambi wina umatiuza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako,” kuphatikizapo mayendedwe aukholo.​—Miyambo 3:5, 6; Yakobo 1:5.

Achinyamata ambiri ochita bwino aleredwa ndi kholo lopanda mnzake wa muukwati ndipo tsopano akutumikira Mulungu mokhulupirika m’mipingo yachikristu ya Mboni za Yehova yokwana zikwi zambiri padziko lonse lapansi. Zimenezi zili umboni woti makolo opanda mnzawo wa muukwati angathe kuphunzitsa ana awo chikondi.

Mmene Onse Angakhalire ndi Chikondi

Baibulo linalosera kuti “masiku otsiriza” adzadziŵika ndi ‘kupanda chikondi chachibadwidwe’ kutanthauza kusoŵeka kwa ubale umene anthu am’banja limodzi amakhala nawo kwa wina ndi mnzake. (2 Timoteo 3:1, 3) Komabe, ngakhale anthu amene anakulira m’banja mmene munalibe chikondi angaphunzire kukhala ndi chikondi. Motani? Mwa kuphunzira kwa Yehova, amene ali Gwero la chikondi ndiponso amene amasonyeza chikondi kwa onse amene amam’dalira ndi mtima wonse. (1 Yohane 4:7, 8) Wamasalmo wina anati: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.”​—Salmo 27:10.

Yehova amasonyeza chikondi kwa ife m’njira zosiyanasiyana. Zimenezi zikuphatikizapo kutitsogolera monga tate pogwiritsa ntchito Baibulo, thandizo la mzimu woyera ndiponso thandizo lachikondi la abale achikristu. (Salmo 119:97-105; Luka 11:13; Ahebri 10:24, 25) Taganizirani mmene njira zitatu zimenezi zingakuthandizireni kukulitsa kukonda Mulungu ndi anzanu.

Malangizo Ouziridwa a Atate

Kuti tikhale ndi ubwenzi weniweni ndi munthu wina, tifunika kum’dziŵa bwino kwambiri munthuyo. Pozidziŵikitsa kudzera m’Baibulo, Yehova akutiuza kuti tiyandikire kwa iye. Komabe, kuŵerenga Baibulo sikokwanira. Tiyenera kugwiritsa ntchito ziphunzitso zake ndipo tidzapindula. (Salmo 19:7-10) Yesaya 48:17 akuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” Inde, Yehova, mwini  wake wa chikondi, akutilangiza kuti tipindule, osati akufuna kuchepetsa ufulu wathu ndi malamulo osathandiza.

Kudziŵa zolondola za Baibulo kumatithandizanso kukulitsa kukonda anthu anzathu. Izi zili choncho chifukwa chakuti choonadi cha Baibulo chimatiphunzitsa mmene Mulungu amaonera anthu ndiponso chimatisonyeza mfundo zimene tiyenera kugwiritsa ntchito pochitirana zinthu. Pokhala odziŵa zimenezi, tili ndi maziko olimba okondera anzathu. Mtumwi Paulo anati: ‘Ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chiwonjezere, ndi m’chidziŵitso [“kudziŵa zolondola,” NW] ndi kuzindikira konse.’​—Afilipi 1:9.

Kuti tisonyeze mmene “kudziŵa zolondola” kumathandizira kukhala ndi chikondi, taganizirani choonadi chofunika chopezeka pa Machitidwe 10:34, 35 chakuti: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” Ngati Mulungu amaweruza anthu chifukwa cha zochita zawo zolungama ndiponso chifukwa cha kumuopa Iye, osati chifukwa cha dziko la munthuyo kapena mtundu, kodi sitiyenera kuona anthu anzathu mopandanso tsankhu?​—Machitidwe 17:26, 27; 1 Yohane 4:7-11, 20, 21.

Chikondi Ndicho Chipatso cha Mzimu wa Mulungu

Monga mmene mvula ya panthaŵi yake imachititsira munda kubala zipatso zambiri, mzimu wa Mulungu ungachititse anthu oulandira kukhala ndi makhalidwe amene Baibulo limati “chipatso cha Mzimu.” (Agalatiya 5:22, 23) Choyamba cha zimenezi ndicho chikondi. (1 Akorinto 13:13) Kodi tingakhale bwanji ndi mzimu wa Mulungu? Njira yofunika kwambiri ndi kudzera m’pemphero. Ngati tipempherera mzimu wa Mulungu, iye adzatipatsa mzimuwo. (Luka 11:9-13) Kodi mumapitirizabe kupempherera mzimu woyera? Ngati mumatero, ndiye kuti chipatso chake chabwino kwambiri, kuphatikizapo chikondi, chiyenera kuonekera kwambiri m’moyo wanu.

Komabe, pali mzimu wina umene umatsutsana ndi mzimu wa Mulungu. Baibulo limatcha umenewu kuti “mzimu wa dziko lapansi.” (1 Akorinto 2:12; Aefeso 2:2) Uli ndi chikoka choipa ndipo gwero lake ndi Satana Mdyerekezi, “mkulu wa dziko ili lapansi” lolekana ndi Mulungu. (Yohane 12:31) Mofanana ndi mphepo imene imachititsa fumbi ndi zinyalala kuuluka, “mzimu wa dziko lapansi” umachititsanso zikhumbo zoipa zimene zimawononga chikondi ndipo umalimbikitsa zofooka za thupi.​—Agalatiya 5:19-21.

Anthu amatengera mzimu woipa umenewu pamene alola maganizo okondetsa zakuthupi ndi kudzikonda, kulola maganizo achiwawa ndiponso kaonedwe kopotoka ndi koipa ka chikondi kamene kali kofala padziko lapansi. Ngati mukufuna kukulitsa chikondi chenicheni, muyenera kupeŵeratu mzimu wa dziko. (Yakobo 4:7) Komabe, simuyenera kukhulupirira mphamvu yanu; pemphani Yehova kuti akuthandizeni. Mzimu wake, mphamvu yaikulu kwambiri m’chilengedwe chonse, ingakulimbitseni ndipo ingakuchititseni kupambana.​—Salmo 121:2.

Phunzirani Chikondi kwa Abale Achikristu

Monga mmene ana amaphunzirira chikondi pamene chisonyezedwa kwa iwo panyumba, ife  tonse, akulu ndi ana, tingakulitse chikondi mwa kugwirizana ndi Akristu ena. (Yohane 13:34, 35) Ndithudi, imodzi mwa ntchito zofunika kwambiri za mpingo wachikristu ndiyo kuchititsa mpingowo kukhala malo amene ‘tingafulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.’​—Ahebri 10:24.

Chikondi chimenechi n’chofunika kwambiri makamaka kwa anthu amene angakhale ali “okambululudwa ndi omwazikana” m’dziko lopanda chikondili. (Mateyu 9:36) Zochitika zasonyeza kuti kukhala ndi ubwenzi wachikondi pa uchikulire kungathetse zotsatirapo zoipa zambiri zochitika chifukwa chosasonyezedwa chikondi muli mwana. Chotero, n’kofunika kwambiri kuti Akristu onse odzipatulira azilandira ndi mtima wonse atsopano amene angoyamba kugwirizana nawo.

“Chikondi Sichitha Nthaŵi Zonse”

Baibulo limati “chikondi sichitha nthaŵi zonse.” (1 Akorinto 13:8) Kodi zimenezi zili choncho bwanji? Mtumwi Paulo akutiuza kuti: “Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa.” (1 Akorinto 13:4, 5) Mwachionekere, chikondi chimenechi si chongoyerekeza kapena kungotengeka mtima. Mosiyana ndi zimenezi, amene amachisonyeza akudziwa zokhumudwitsa za m’moyo ndiponso zovuta, koma salola zimenezi kuwononga chikondi chawo kwa anthu anzawo. Zoonadi chikondi chotero “ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”​—Akolose 3:12-14.

Taganizirani za chitsanzo cha msungwana wina wachikristu wazaka 17 wa ku Korea. Atayamba kutumikira Yehova Mulungu, a pabanja lake sanagwirizane nazo ndipo iye anafunika kuchoka panyumbapo. Komabe, m’malo mokwiya, anapempherera nkhaniyo, ndipo analola Mawu a Mulungu ndi mzimu Wake kutsogolera maganizo ake. Ndiyeno, ankalembera kalata a pabanja lake nthaŵi zambiri, akumasonyeza chikondi chenicheni chimene anali nacho kwa iwo m’makalata ake. Chifukwa cha zimenezi, achimwene ake aŵiri anayamba kuphunzira Baibulo ndipo tsopano ndi Akristu odzipatulira. Amayi ake ndi mng’ono wake nawonso analandira choonadi cha Baibulo. Pomaliza, bambo ake amene anali wotsutsa kwambiri, anasintha kwambiri maganizo awo. Mboni yachisungwanayi inalemba kuti: “Tonse tinakwatiwa ndi kukwatira Akristu anzathu ndipo tsopano banja lathu lili ndi olambira ogwirizana okwana 23.” Chikondi chinapambanadi!

Kodi mukufuna kukhala ndi chikondi chenicheni ndiponso kuthandiza ena kuchita mofanana? Ngati ndi choncho, dalirani Yehova, Gwero la khalidwe lofunika kwambiri limeneli. Inde, mverani Mawu ake, pemphererani mzimu woyera ndipo nthaŵi zonse gwirizanani ndi abale achikristu. (Yesaya 11:9; Mateyu 5:5) N’zosangalatsa kudziŵa kuti posachedwapa kuipa konse kudzatha ndipo okhawo amene amasonyeza chikondi chenicheni chachikristu ndi amene adzatsala. Zoonadi, chikondi n’chofunika kwambiri kuti tikhale osangalala ndiponso kuti tikhale ndi moyo.​—Salmo 37:10, 11; 1 Yohane 3:14.

[Zithunzi patsamba 6]

Kupemphera ndi kuphunzira Mawu a Mulungu zidzatithandiza kukhala ndi chikondi chenicheni