Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi pa Ahebri 2:14 pakutanthauzanji ponena kuti Satana ndi “amene anali nayo mphamvu ya imfa”?

Kuyankha mwachidule, Paulo anali kutanthauza kuti Satana, weniweniyo kapena anthu amene amawagwiritsira ntchito, angachititse anthu kufa. Mogwirizana ndi zimenezi, Yesu anatcha Satana “wambanda kuyambira pachiyambi.”​—Yohane 8:44.

Pangakhale kusamvetsa tanthauzo la lemba la Ahebri 2:14 chifukwa cha mmene mawuŵa alili pa lembali, ndiponso mmene mabaibulo ena amasulira lembali, kuti Satana ali ndi “mphamvu paimfa.” (Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Mawuŵa amasonyeza ngati kuti Satana ali ndi mphamvu zopanda malire zopha aliyense amene akufuna. Koma mwachionekere, si mmene zilili. Zikanakhala choncho, bwenzi ataseseratu kalekale olambira a Yehova padziko lapansi.​—Genesis 3:15.

Mawu achigiriki amene mabaibulo ena awamasulira kuti “mphamvu paimfa” ndiponso amene awamasulira kuti “mphamvu ya imfa” mu Baibulo la Revised Nyanja (Union) Version ndi akuti “kraʹtos tou tha·naʹtou.” Mawu akuti Tou tha·naʹtou amatanthauza “imfa.” Mawu akuti Kraʹtos kwenikweni amatanthauza “mphamvu, nyonga.” Mawuŵa malinga ndi buku lakuti Theological Dictionary of the New Testament, amatanthauza “kukhala ndi mphamvu ndiponso kukula kwa mphamvuzo osati kuzigwiritsa ntchito kwake.” Choncho, pa Ahebri 2:14, Paulo sanali kutanthauza kuti Satana ali ndi mphamvu zopanda malire pa imfa. Koma anali kutanthauza kuti Satana ali ndi mphamvu yochititsa imfa.

Kodi Satana amagwiritsa ntchito bwanji “mphamvu ya imfa”? M’buku la Yobu, timaŵerenga nkhani ina imene ingakhale yapadera kwambiri. Nkhaniyo imanena kuti Satana anagwiritsa ntchito mphepo ya mkuntho kupha ana a Yobu. Komabe, onani kuti Satana anachita zimenezi Mulungu atamuloleza kuzichita, chifukwa chakuti panali nkhani yoti ithetsedwe. (Yobu 1:12, 18, 19) Inde, Satana analephera kupha Yobu weniweniyo. Sanaloledwe kuchita zimenezi. (Yobu 2:6) Izi zikusonyeza kuti ngakhale kuti nthaŵi zina Satana wachititsa imfa za anthu okhulupirika, sitifunika kuopa kuti angatiphe nthaŵi iliyonse imene akufuna.

Satana wachititsanso imfa kudzera mwa anthu amene amawagwiritsira ntchito. N’chifukwa chake, Akristu ambiri aphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, ena aphedwa ndi magulu a anthu achiwawa kapena aphedwa popanda chilungamo, akuluakulu a boma kapena oweruza achinyengo atalamula kuti aphedwe.​—Chivumbulutso 2:13.

Komanso, Satana nthaŵi zina wachititsa imfa pogwiritsa ntchito kufooka kwa anthu. Kale m’masiku a Aisrayeli, mneneri Balamu analangiza Amoabu kunyengerera Aisrayeli ‘kulakwira Yehova.’ (Numeri 31:16) Zimenezi zinaphetsa Aisrayeli oposa 23,000. (Numeri 25:9; 1 Akorinto 10:8) Chimodzimodzinso masiku ano, ena amanyengeka ndi ‘machenjera’ a Satana ndipo amachita chiwerewere kapena zinthu zina zimene Mulungu amadana nazo. (Aefeso 6:11) N’zoona kuti anthu ameneŵa safa nthaŵi yomweyo. Koma amataya mwayi wodzalandira moyo wosatha, ndipo mwa njira imeneyi Satana amawapha.

Ngakhale tikudziŵa kuti Satana angativulaze, sitifunika kumuopa kwambiri. Paulo atanena kuti Satana ali ndi mphamvu za imfa, ananenanso kuti Kristu anafa kuti “akamuwononge iye [Satana] . . . nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m’moyo wawo wonse adamangidwa ukapolo.” (Ahebri 2:14, 15) Inde, Yesu anapereka dipo ndipo motero anamasula anthu okhulupirira ku ukapolo wa uchimo ndi imfa.​—2 Timoteo 1:10.

Inde, n’zopatsa maganizo kuona kuti Satana ali ndi mphamvu ya imfa, koma tili ndi chikhulupiriro chakuti Yehova angakonze zonse zimene Satana ndi anthu amene amawagwiritsira ntchito angawononge. Yehova akutitsimikizira kuti Yesu amene anaukitsidwa ‘adzawononga ntchito za Mdyerekezi.’ (1 Yohane 3:8) Yesu mwa mphamvu ya Yehova, adzaukitsa akufa ndipo chotero adzathetsa imfa yeniyeniyo. (Yohane 5:28, 29) M’kupita kwa nthaŵi, Yesu adzasonyezeratu kuti Satana ali ndi mphamvu zochepa mwa kum’tsekera ku phompho. Mapeto ake, Satana adzaweruzidwa kuti awonongedwe kotheratu.​—Chivumbulutso 20:1-10.