Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Linakwaniritsa Chimene Mtima Wanga Unkafuna Kwambiri”

“Linakwaniritsa Chimene Mtima Wanga Unkafuna Kwambiri”

 “Linakwaniritsa Chimene Mtima Wanga Unkafuna Kwambiri”

“NDIKUKUTHOKOZANI kuchokera pansi pamtima chifukwa cha mphatso yabwino ya buku lakuti Yandikirani kwa Yehova. Linakwaniritsa chimene mtima wanga unkafuna kwambiri. Ndinkafuna kuona kuti Yehova amandikonda. Panopo ndimaona kuti ndili pafupi kwambiri ndi Yehova ndi Mwana wake wokondedwa. Ndikufuna kuuza aliyense za bukuli ndiponso kuwapatsa onse amene ndimawakonda.” Umu ndi mmene mmodzi wa Mboni za Yehova anaonera buku latsopano la masamba 320 limene linatuluka pa Msonkhano Wachigawo wa 2002/03 wakuti “Olengeza Ufumu Achangu.” Tiyeni tione zina zimene zili m’buku latsopanoli ndiponso chifukwa chake bukuli linasindikizidwa.

Zina Zimene Zili M’buku Latsopanoli

Kodi m’buku latsopanoli muli zotani? Muli nkhani zophunzira zonse ziŵiri zimene zili m’magazini ino ndi zina zambiri. M’bukuli muli mitu 31, uliwonse ndi wautali ngati nkhani yophunzira ya mu Nsanja ya Olonda. Pambuyo pa mawu amalonje ndi mitu yoyambirira itatu, bukuli lagaŵidwa m’zigawo zinayi, chilichonse chikulongosola khalidwe limodzi la makhalidwe ofunika kwambiri a Yehova. Chigawo chilichonse chikuyamba ndi kufotokoza khalidwelo mwachidule. Mitu yotsatira ingapo m’chigawocho ikulongosola mmene Yehova amasonyezera khalidwe limenelo. M’chigawo chilichonse mulinso mutu wonena za Yesu. Chifukwa chiyani? Chifuwa chakuti Yesu anati: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.” (Yohane 14:9) Popeza kuti Yesu ndi chithunzithunzi chenicheni cha Yehova, iye amatipatsa chitsanzo chooneka bwino cha mmene Mulungu amasonyezera makhalidwe ake. Chigawo chilichonse chikumaliza ndi mutu wotiphunzitsa mmene tingatsanzirire Yehova poonetsa khalidwe limene alifotokozalo. Pofotokoza makhalidwe a Yehova, buku latsopanoli likupereka maumboni kuchokera m’buku lililonse la m’Baibulo.

Buku lakuti Yandikirani kwa Yehova lilinso ndi mbali zina zapadera. Kuyambira mutu 2, mutu uliwonse uli ndi bokosi lotchedwa “Mafunso Owasinkhasinkha.” Malemba ndi mafunso amene ali m’bokosimo sanalinganizidwe kuti mubwereze mutuwo. Koma cholinga chake n’kukuthandizani kugwiritsa ntchito Baibulo kuti musinkhesinkhe nkhaniyo mwakuya. Ndi bwino kuŵerenga ndime iliyonse ya m’Malemba mofatsa. Kenako sinkhasinkhani funsolo, ndipo yesetsani kugwiritsa ntchito mfundo zake m’moyo wanu. Kusinkhasinkha koteroko kungakuthandizeni kuyandikira kwambiri kwa Yehova.​—Salmo 19:14.

Zithunzinso m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova zinafufuzidwa mosamalitsa ndi kujambulidwa bwino kuti zikhale zophunzitsa ndi zolimbikitsa. Mitu 17 ili ndi zithunzi zokongola za zochitika za m’Baibulo zojambulidwa pa tsamba lathunthu.

N’chifukwa Chiyani Anasindikiza Bukuli?

N’chifukwa chiyani anasindikiza buku lakuti Yandikirani kwa Yehova? Cholinga chachikulu cha buku latsopanoli ndi kutithandiza kumudziŵa bwino Yehova kuti tikhale naye pa ubwenzi wapamtima.

Kodi pali amene mukumuganizira kuti angapindule ndi buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, kaya wophunzira Baibulo kapena Mkristu amene anasiya kulalikira? Nanga inuyo​—kodi mwayamba kuŵerenga buku latsopanoli? Ngati simunayambe, bwanji osapatula nthaŵi yoti muyambe kuŵerenga posachedwapa? Khalani ndi nthaŵi yolingalira zimene mukuŵerenga. Bukuli likuthandizenitu kuyandikira kwambiri kwa Yehova Mulungu, kotero kuti muzilengeza uthenga wake wabwino wa Ufumu muli ndi chimwemwe chodzala tsaya ndiponso mwachangu kwambiri.