Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi N’chofunika Kwambiri

Chikondi N’chofunika Kwambiri

 Chikondi N’chofunika Kwambiri

KAYA munthu ndi wa msinkhu wotani, wa chikhalidwe chotani, wa chinenero chanji, kapena mtundu wotani, aliyense amafuna kwambiri kukondedwa. Ngati sakukondedwa, sasangalala. Wofufuza za mankhwala wina analemba kuti: “Chikondi ndiponso ubwenzi wa pamtima n’zimene kwenikweni zimatidwalitsa ndiponso kutichiritsa. N’zimenenso zimachititsa chisoni komanso chisangalalo, zimachititsanso kuvutika ndipo zimathandiza kuchira. Pakanakhala mankhwala atsopano amene anali ndi mphamvu ngati imeneyi, ndiye kuti dokotala aliyense m’dziko angalembere odwala ake mankhwala amenewo. Kungakhale kuswa malamulo kusalembera odwala mankhwalawo.”

Komabe, anthu masiku ano, makamaka zoulutsira nkhani zawo ndiponso anthu otchuka amaika patsogolo chuma, mphamvu, kutchuka ndi kugonana m’malo moika patsogolo kufunika kwachikondi pakati pa anthu. Ophunzitsa ambiri amaika patsogolo zolinga ndi ntchito za m’dziko, n’kumati kukhala ndi zimenezi n’kumene kumasonyeza kuti munthuyo ndi wopambana. N’zoona kuti maphunziro ndiponso kukhala ndi luso n’zofunika, komano kodi tifunika kuika maganizo athu onse pa zimenezi moti n’kumasoŵa nthaŵi yocheza ndi a pabanja ndiponso mabwenzi? Wolemba wina wakale yemwe anali wophunzira komanso wodziwa bwino chikhalidwe cha anthu anayerekezera munthu amene ali ndi mphatso zina yemwe alibe chikondi ndi “mkuwa woomba, kapena nguli yolira.” (1 Akorinto 13:1) Anthu otero angakhale ndi chuma chambiri, mwina angakhale otchuka, koma osasangalala kwenikweni.

Yesu Kristu, amene ankadziŵa bwino anthu ndiponso amene ankakonda anthu mwapadera, ankaona kukonda Mulungu ndi anzathu kukhala mbali yofunika kwambiri ya chiphunzitso chake. Iye anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. . . . Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.” (Mateyu 22:37-39) Okhawo amene anatsatira mawu ameneŵa ndi amene akanakhala otsatira oona a Yesu. N’chifukwa chake anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”​—Yohane 13:35.

Komabe, kodi munthu angakonde bwanji ena m’dziko lamakonoli? Ndipo kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo chikondi? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.

[Zithunzi patsamba 3]

N’kovuta kwambiri kukhala ndi chikondi m’dziko ladyera