Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Umboni Woti Yesu Kristu Anakhalako Padziko Lapansi

Umboni Woti Yesu Kristu Anakhalako Padziko Lapansi

 Umboni Woti Yesu Kristu Anakhalako Padziko Lapansi

ANTHU ambiri sanayambe akumanapo ndi Albert Einstein, munthu wasayansi wotchuka kwambiri. M’mayiko ambiri, anthu ochuluka sam’dziŵa n’komwe. Komabe, umboni wodalirika wa zinthu zimene anachita umasonyeza kuti iye anakhalako. Anthu amadziŵa kuti iye anakhalako chifukwa amagwiritsa ntchito zinthu za sayansi zimene iye anazitulukira. Mwachitsanzo, anthu ambiri amagwiritsa ntchito magetsi, amene nthaŵi zina amapangidwa pogwiritsa ntchito mfundo zimene iye anatulukira.

Mfundo yomweyo imagwiranso ntchito pa Yesu Kristu, amene amadziŵika monga munthu amene anakhudza anthu kwambiri kuposa munthu wina aliyense. Zimene anthu analemba za iye komanso umboni wooneka ndi maso wa mmene anakhudzira  anthu zimasonyeza bwino kwambiri kuti anakhalako. Bokosi la Yakobo limene akatswiri okumba zinthu zakale anapeza limene talifotokoza mu nkhani yoyamba ija n’lochititsa chidwi. Koma umboni woti Yesu anakhalako sukudalira pa bokosi limenelo, kapena pa chinthu china chilichonse chakale chokumbidwa pansi. Zoona zake n’zakuti tingapeze umboni woti Yesu anakhalako ku zinthu zimene anthu olemba mbiri analemba za iye ndi otsatira ake.

Umboni wa Anthu Olemba Mbiri

Mwachitsanzo, taonani zimene analemba Flavius Josephus, wolemba mbiri wachiyuda wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino komanso Mfarisi. M’buku lake lakuti Jewish Antiquities, iye anatchulamo za Yesu Kristu. Ngakhale kuti anthu ena akukayikira ngati Josephus ananenadi zoona pamene anatchula koyamba zoti Yesu ndi Mesiya, Pulofesa Louis H. Feldman wa ku yunivesite ya Yeshiva anati ndi anthu ochepa chabe amene akukayikira ngati Josephus ananena zoona pamene anatchula za Yesu kachiŵiri. Mu nkhani imeneyo Josephus anati: “[Anasi mkulu wa ansembe] anaitanitsa oweruza a bwalo la Sanihedirini ndipo anawabweretsera munthu wotchedwa Yakobo, mbale wa Yesu amene ankatchedwa Kristu.” (Jewish Antiquities, XX, 200) Inde, Mfarisi, wa gulu la mpatuko limene otsatira ake anali adani a Yesu otheratu, anavomereza kuti munthu wotchedwa “Yakobo, mbale wa Yesu,” anakhalako.

Mphamvu imene Yesu anali nayo pa anthu imaonekera mu zinthu zimene otsatira ake anachita. Panthaŵi imene mtumwi Paulo anali m’ndende ku Rome cha m’ma 59 C.E., akuluakulu a Ayuda anamuuza kuti: “Pakuti za mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponseponse.” (Machitidwe 28:17-22) Ophunzira a Yesu anatchedwa “mpatuko uwu.” Ngati mpatuko umenewu amaunena paliponse, mwachidziŵikire anthu olemba mbiri akanautchulako, kodi si choncho?

Tasitasi, amene anabadwa cha m’ma 55 C.E. ndipo amene akudziŵika monga mmodzi mwa anthu olemba mbiri otchuka pa dziko lonse, anatchula Akristu mu nkhani yake yakuti Annals. Mu nkhani imene akufotokoza zoti Nero ananamizira Akristu kuti ndi amene anayambitsa moto waukulu umene unabuka ku Rome mu 64 C.E., iye analemba kuti: “Nero ananamizira ndi kuzunza mwankhanza anthu amene anali odedwa kwambiri chifukwa cha zonyansa zimene amachita, amene amadziŵika ndi dzina loti Akristu. Kristu, kumene kunachokera dzina lawoli, anaphedwa mu ulamuliro wa Tiberio motsogozedwa ndi mmodzi wa olamulira athu, Pontiyo Pilato.” Zimene analemba mu nkhani imeneyi zikufanana ndi zimene Baibulo limanena za Yesu.

Munthu wina amene analembapo za otsatira a Yesu anali Pliny Wamng’ono, amene anali wolamulira wa ku Bituniya. Pafupifupi m’chaka cha 111 C.E, Pliny analemba kalata kwa Mfumu Trajan, kufunsa zimene ayenera kuchita nawo Akristu. Pliny analemba kuti anthu amene anali atawanamizira kuti anali Akristu anapemphera kwa milungu ndi kulambira fano la Trajan, kuti asonyeze kuti sanali Akristu. Pliny anapitiriza kunena kuti: “Akuti sizingatheke kukakamiza anthu amene alidi Akristu kuti achite zinthu ngati zimenezi.” Zimenezi zikusonyeza kuti Kristu anakhalakodi, ndipo otsatira ake anali okonzeka kufa chifukwa chom’khulupirira.

Atapenda nkhani za anthu olemba mbiri a m’zaka 200 zoyambirira za nyengo yathu ino amene ananenapo za Yesu Kristu ndi otsatira  ake, olemba buku la Encyclopædia Britannica (la 2002) anapereka maganizo awo kuti: “Nkhani zolembedwa ndi anthu ena zimenezi zikusonyeza kuti kalelo ngakhale adani a Chikristu samakayikira zoti Yesu anakhalako. Kukayikirako kunachitika koyamba ndiponso popanda maziko enieni kumapeto kwa zaka za m’ma 1700, m’zaka za m’ma 1800, ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900.”

Umboni wa Otsatira a Yesu

“Chipangano Chatsopano chimatipatsa pafupifupi umboni wonse umene ukufunika kuti tithe kudziŵa tsatanetsatane wa moyo wa Yesu ndi zimene zinam’chitikira, komanso kuti tidziŵe mmene Akristu oyambirira ankaonera kufunika kwa Yesu,” inatero Encyclopedia Americana. Anthu otsutsa mwina sangavomereze kuti m’Baibulo muli umboni wosonyeza kuti Yesu anakhalako. Koma pali mfundo ziŵiri zochokera mu nkhani za m’Malemba zimene zimatithandiza kudziŵa kuti Yesu anakhalakodi.

Monga momwe taonera, mfundo zothandiza kwambiri za Einstein zimasonyeza kuti anakhalako. Chimodzimodzinso zimene Yesu anaphunzitsa zimasonyeza kuti anakhalakodi. Tangoganizirani mwachitsanzo Ulaliki wa pa Phiri, nkhani yodziŵika bwino imene Yesu anakamba. (Mateyu, chaputala 5 mpaka 7) Mtumwi Mateyu anafotokoza zimene anthu anachita atamva ulaliki umenewo: “Makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu.” (Mateyu 7:28, 29) Pofotokozapo za mmene ulaliki umenewo wakhudzira anthu zaka mazana ambiri zapitazi, Pulofesa Hans Dieter Betz anati: “Ulaliki wa pa Phiri uli ndi mphamvu imene imakhudza anthu osiyanasiyana, kuyambira Ayuda, Akristu, ngakhale Azungu.” Iye anapitiriza kunena kuti ulaliki umenewu, “mosiyana ndi maulaliki ena onse, umakhudza anthu pa dziko lonse.”

Talingalirani mawu achidule ndi othandiza ndiponso opatsa nzeru otsatiraŵa amene amapezeka mu Ulaliki wa pa Phiri: “Amene adzakupanda iwe patsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.” “Yang’anirani kuti musachite zolungama zanu pamaso pa anthu.” “Musadere nkhaŵa za maŵa; pakuti maŵa adzadzidera nkhaŵa iwo okha.” “Musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba.” “Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu.” “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” “Loŵani pa chipata chopapatiza.” “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” “Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma.”​—Mateyu 5:39; 6:1, 34; 7:6, 7, 12, 13, 16, 17.

Mosakayikira inu munamvapo ena mwa mawu ameneŵa, kapena mfundo ya mawuwo. Mwina asanduka miyambi m’chinenero chanu. Onseŵa atengedwa mu Ulaliki wa pa Phiri. Mphamvu imene ulaliki umenewu uli nayo pa anthu a mitundu ndi miyambo yosiyanasiyana ikusonyeza bwino kwambiri kuti “mphunzitsi wamkuluyo,” anakhalakodi.

Tiyeni tingoyerekezera kuti munthu wina anapeka nkhani ya munthu, n’kumutcha munthuyo Yesu Kristu. Ndiyeno tiyerekeze kuti munthuyo anali wanzeru ndithu moti mpaka anatha kupeka ziphunzitso zimene Baibulo limati anaziphunzitsa ndi Yesu. Kodi wopekayo sakanayesetsa kupanga Yesuyo komanso ziphunzitso zake kukhala zokopa kwa onse monga momwe akanathera? Koma mtumwi Paulo anati: “Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Ahelene atsata nzeru: koma ife tilalikira Kristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chinthu chopusa.” (1 Akorinto 1:22, 23) Uthenga wonena za Kristu amene anapachikidwa sunawakope Ayuda ndi anthu amitundu omwe. Koma Kristu amene Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ankalalikira anali wotero. N’chifukwa chiyani analalikira za Kristu wopachikidwa? Yankho limene lingakhale lokhutiritsa ndi loti amene analemba Malemba Achigiriki Achikristu analemba zoona zenizeni za moyo ndi imfa ya Yesu.

Mfundo ina imene imapereka umboni woti Yesu anakhalakodi ndi mmene otsatira ake analalikirira ziphunzitso zake mosabwerera m’mbuyo. Patangotha zaka pafupifupi 30 zokha kuchokera pamene Yesu anayamba utumiki wake, Paulo anatha kunena kuti uthenga wabwino ‘unalalikidwa kwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:23) Inde, ziphunzitso za Yesu zinafalikira m’dziko lonse la kalelo ngakhale kuti panali otsutsa. Paulo, amene iye mwiniyo anazunzidwa chifukwa chokhala Mkristu, analemba  kuti: “Ngati Kristu sanaukitsidwa kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.” (1 Akorinto 15:12-17) Ngati kulalikira za Kristu amene sanaukitsidwe kukanakhala kwachabe, ndiye kuti kulalikira za Kristu amene sanakhaleko n’komwe kukanakhala kungotaya nthaŵi. Monga momwe Pliny Wamng’ono analembera, Akristu m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anali okonzeka kufa chifukwa chokhulupirira Kristu Yesu. Iwo anaika miyoyo yawo pachiswe chifukwa chokhulupirira Kristu podziŵa kuti Kristuyo anali weniweni; anakhalako padziko lapansi monga mmene Mauthenga Abwino amanenera.

Inuyo Mwauona Umboni

Mkristu asanayambe kulalikira, anayenera kukhulupirira kuti Yesu Kristu anauka kwa akufa. Nanunso m’maganizo anu mungathe kumuona Yesu woukitsidwayo mwakuona zimene akuchita masiku ano.

Yesu atangotsala pang’ono kupachikidwa, anafotokoza ulosi waukulu wa kukhalapo kwake kwa m’tsogolo. Iye ananenanso kuti adzauka kwa akufa ndipo adzakhala kudzanja lamanja la Mulungu kudikira kuti nthaŵi yothana ndi adani ake ikwane. (Salmo 110:1; Yohane 6:62; Machitidwe 2:34, 35; Aroma 8:34) Kenako, anali kudzachotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba.​—Chivumbulutso 12:7-9.

Kodi zonsezi zinali kudzachitika liti? Yesu anapatsa ophunzira ake ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi mapeto a nthaŵi yathu ino.’ Chizindikiro chosonyeza kukhalapo kwake kosaoneka chinaphatikizapo nkhondo zazikulu, kupereŵera kwa zakudya, zivomezi, kubwera kwa aneneri onyenga, kuchuluka kwa kusaweruzika, ndi matenda aakulu. Zinthu zoopsa zimenezi zinayenera kuchitika, chifukwa kuchotsedwa kwa Satana Mdyerekezi kumwamba kunatanthauza ‘tsoka pa dziko lapansi.’ Mdyerekezi watsikira ku dziko lapansi “wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.” Komanso, chizindikirocho chikuphatikizapo kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu “padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.”​—Mateyu 24:3-14; Chivumbulutso 12:12; Luka 21:7-19.

Zinthu zimene Yesu ananeneratu kuti zidzachitika zachitika. Kuyambira pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse ya 1914 inachitika, taona chizindikiro chokhala ndi mbali zosiyanasiyana cha kukhalapo kwa Yesu Kristu kosaoneka ndi maso. Iye akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo akuchita zinthu zambiri zimene zikutikhudza. Kuŵerenga kwanu magazini imene ili m’manja mwanuyi kukusonyeza kuti ntchito yolalikira za Ufumu ikuchitika masiku ano.

Kuti mumvetsetse bwinobwino mmene moyo wa Yesu umatikhudzira, muyenera kuphunzira Baibulo. Bwanji osafunsa Mboni za Yehova kuti zikuuzeni zinthu zina zokhudza kukhalapo kwa Yesu?

[Zithunzi patsamba 5]

Josephus, Tasitasi, ndi Pliny Wamng’ono anatchulapo za Yesu Kristu ndi otsatira ake

[Mawu a Chithunzi]

Zithunzi zonse zitatu: © Bettmann/​CORBIS

[Chithunzi patsamba 7]

Akristu oyambirira anali otsimikiza kuti Yesu anakhalakodi