Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Yehova, Mulungu Wathu Wopanda Tsankho

Tsanzirani Yehova, Mulungu Wathu Wopanda Tsankho

 Tsanzirani Yehova, Mulungu Wathu Wopanda Tsankho

“Mulungu alibe tsankhu.”​—AROMA 2:11.

1, 2. (a) Kodi cholinga cha Yehova chokhudza Akanani onse chinali chotani? (b) Kodi Yehova anachita chiyani, ndipo kodi zimenezi zikubweretsa mafunso otani?

AISRAYELI ali m’chigwa cha Moabu m’chaka cha 1473 B.C.E., anamvetsera mwatcheru kwa Mose. Tsidya lina la mtsinje wa Yordano, kumene iwo anali kupita, kunali zovuta zambiri. Mose anafotokoza kuti cholinga cha Yehova chinali chakuti Israyeli agonjetse mitundu isanu ndi iŵiri yamphamvu ya Akanani imene inali m’Dziko Lolonjezedwa. Mose anati: ‘Adzawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo mukawawononge konse.’ Mawu ameneŵa anali olimbikitsa kwambiri! Aisrayeli anafunika kuti asachite pangano ndi mitundu imeneyi, ndiponso asaichitire chifundo.​—Deuteronomo 1:1; 7:1, 2.

2 Komabe, Yehova anapulumutsa banja limodzi mu mzinda woyamba umene Aisrayeli anamenya nawo nkhondo. Anthu okhala m’mizinda inanso inayi anatetezedwa ndi Mulungu. N’chifukwa chiyani Mulungu anachita zimenezi? Kodi zinthu zodabwitsa zimenezi zokhudza kupulumutsidwa kwa Akanani ameneŵa zikutiphunzitsa chiyani za Yehova? Ndipo kodi tingamutsanzire motani?

Zimene Anachita Atamva Mbiri ya Yehova

3, 4. Kodi nkhani ya kupambana kwa Aisrayeli inakhudza motani anthu okhala ku Kanani?

3 Nthaŵi imene Aisrayeli anakhala zaka 40 m’chipululu asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anateteza ndi kumenyera nkhondo anthu ake. Kum’mwera kwa Dziko Lolonjezedwa, Aisrayeli anayang’anizana ndi mfumu yachikanani ya mudzi wa Aradi. Mothandizidwa ndi Yehova, Aisrayeli anagonjetsa mfumuyi pamodzi ndi anthu ake pamalo otchedwa Horima. (Numeri 21:1-3) Pambuyo pake, Aisrayeli analambalala dziko la Edomu ndipo anayenda ulendo wopita kumpoto chakum’maŵa kwa Nyanja Yakufa. M’dera limeneli, limene kale munkakhala Amoabu, munali Aamori. Mfumu Sihoni ya Aamori sinalole kuti Aisrayeli adutse m’dziko lake. Aisrayeli anachita nkhondo ndi Mfumu Sihoni pa malo otchedwa Jahazi, mwachionekere kumpoto kwa chigwa cha Arinoni, kumene Sihoni anaphedwa. (Numeri 21:23, 24; Deuteronomo 2:30-33) Chakumpoto, Ogi anali wolamulira wa Aamori ena ku Basana. Ngakhale kuti Ogi anali chimphona, sanathe kulimbana ndi Yehova. Ogi anaphedwa ku Edreyi. (Numeri 21:33-35; Deuteronomo 3:1-3, 11) Mbiri ya kupambana pamodzi ndi zochitika zina za pa ulendo wa Aisrayeli wochokera ku Igupto zinakhudza kwambiri mitima ya anthu okhala mu Kanani. *

4 Pamene Aisrayeli analoŵa m’dziko la Kanani atawoloka mtsinje wa Yordano, anamanga msasa pa Giligala. (Yoswa 4:9-19) Chapafupi nawo panali mzinda wokhala ndi malinga wa Yeriko. Rahabi Mkananiyo atamva zimene Yehova anachita, zinam’limbikitsa kuchita ntchito imene inasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro. Zotsatira zake n’zakuti, pamene Yehova anaononga Yeriko, anapulumutsa Rahabi ndi a m’banja lake.​—Yoswa 2:1-13; 6:17, 18; Yakobo 2:25.

5. Kodi chinachititsa Agibeoni kuchita zinthu mwanzeru n’chiyani?

5 Kenako, Aisrayeli anasamuka m’madera a kuchigwa kufupi ndi mtsinje wa Yordano kupita ku mapiri a pakati pa deralo. Motsatira malangizo a Yehova, Yoswa analalira mzinda wa Ai ndipo anaugonetsa. (Yoswa, chaputala 8) Mbiri yakuti Ai wagonjetsedwa kotheratu itamveka, mafumu  ambiri achikanani anasonkhana kuti achite nkhondo. (Yoswa 9:1, 2) Anthu okhala mu mzinda wapafupi wa Ahivi wa Gibeoni sanagwirizane nawo. Yoswa 9:4 amafotokoza kuti: ‘Anachita mom’chenjerera.’ Mofanana ndi Rahabi, anali atamva mmene Yehova anapulumutsira anthu ake potuluka m’Igupto ndiponso pogonjetsa Sihoni ndi Ogi. (Yoswa 9:6-10) Agibeoni anazindikira kuti akanagonjetsedwa ngati akanalimbalimba. Chotero, kuti apulumutse mzinda wa Gibeoni komanso mizinda itatu yapafupi nawo ya Cefira, Beerotu, ndi Kiriyatu-Yearimu, anatumiza amithenga kwa Yoswa ku Giligala omwe ananamizira ngati kuti achokera dziko lakutali. Nzeru imeneyi inawathandizadi. Yoswa anachita nawo pangano limene linawathandiza kuti apulumuke. Patapita masiku atatu Yoswa ndi Aisrayeli anadziŵa kuti anali atanyengedwa. Komabe, anali atalumbira kwa Yehova kusunga panganolo ndipo analitsatira. (Yoswa 9:16-19) Kodi Yehova anavomereza?

6. Kodi Yehova anachita chiyani pamene Yoswa anachita pangano ndi Agibeoni?

6 Agibeoni analoledwa kukhala odula nkhuni ndi otungira madzi Aisrayeli, ngakhalenso “guwa la nsembe la Yehova” kuchihema. (Yoswa 9:21-27) Kuwonjezera pamenepo, pamene mafumu asanu a Aamori ndi asilikali awo anaopseza Agibeoni, Yehova analoŵererapo mozizwitsa. Matalala anapha adani ambiri kuposa amene anaphedwa ndi asilikali a Yoswa. Yehova anafika ngakhale poyankha pempho la Yoswa loti dzuŵa ndi mwezi ziime kuti amalizitse kugonjetsa adani. Yoswa ananena kuti: “Panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m’tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mawu a munthu; pakuti Yehova anathirira Israyeli nkhondo.”​—Yoswa 10:1-14.

7. Kodi zimene zinachitika kwa Akanani ena zinasonyeza mfundo yoona iti imene Petro anaivomereza?

7 Rahabi Mkananiyo ndi abale ake, komanso Agibeoni, anaopa Yehova ndipo anachitapo kanthu mwanzeru. Zimene zinawachitikira zikusonyeza bwino mfundo yoona imene mtumwi wachikristu Petro anafotokoza pambuyo pake kuti: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Zimene Yehova Anachita kwa Abrahamu ndi Aisrayeli

8, 9. Kodi kupanda tsankho kwa Yehova kukuoneka motani pa zimene anachita kwa Abrahamu ndi mtundu wa Israyeli?

8 Wophunzira Yakobo anafotokoza za kukoma mtima kwa Mulungu pa zochita Zake ndi Abrahamu ndi mbadwa zake. Chinali chikhulupiriro cha Abrahamu, osati fuko lake, zimene zinam’chititsa kukhala “bwenzi la Mulungu.” (Yakobo 2:23) Chikhulupiriro cha Abrahamu ndi chikondi chake pa Yehova zinadzetsa madalitso kwa mbadwa zake. (2 Mbiri 20:7) Yehova analonjeza Abrahamu kuti: “Kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” Koma taonani lonjezo limene lili mu vesi lotsatira: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.”​—Genesis 22:17, 18; Aroma 4:1-8.

9 M’malo mochita zinthu mwatsankho, Yehova anasonyeza zimene angachitire anthu amene amamumvera mwa zimene anachita kwa Aisrayeli. Zochitika zimenezi ndi zitsanzo za mmene Yehova amasonyezera chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake omvera. Ngakhale kuti Aisrayeli anali ‘chuma chapadera’ cha Yehova, sizinatanthauze kuti Mulungu sanafunikire kukomera mtima anthu amitundu ina. (Eksodo 19:5; Deuteronomo 7:6-8) Zoonadi, Yehova anawombola  Aisrayeli ku ukapolo ku Igupto ndipo n’chifukwa chake ananena kuti: “Inu nokha ndinakudziŵani mwa mabanja onse a padziko lapansi.” Koma kudzera mwa mneneri Amosi ndi aneneri ena, Yehova anapereka chiyembekezo chosangalatsa kwa anthu ‘amitundu yonse.’​—Amosi 3:2; 9:11, 12; Yesaya 2:2-4.

Yesu, Mphunzitsi Wopanda Tsankho

10. Kodi Yesu anatsanzira Atate ake motani posonyeza kupanda tsankho?

10 Nthaŵi ya utumiki wake wapadziko lapansi, Yesu, amene ali wofanana kwambiri ndi Atate ake, anatsanzira kupanda tsankho kwa Yehova. (Ahebri 1:3) Cholinga chake chachikulu panthaŵiyo chinali kupeza “nkhosa zotayika za banja la Israyeli.” Komabe, sanapeŵe kulalikira kwa mkazi wachisamariya pachitsime. (Mateyu 15:24; Yohane 4:7-30) Anachitanso chozizwitsa atapemphedwa ndi mkulu wa asilikali, amene mwachionekere sanali Myuda. (Luka 7:1-10) Anachita zimenezi kuwonjezera pa chikondi chimene anasonyeza kwa anthu a Mulungu. Ophunzira a Yesu nawonso analalikira ku madera ambiri komanso akutali. Apa zinaonekeratu kuti zinadalira mtima wa munthu, osati mtundu wake, kuti munthuyo alandire madalitso kwa Yehova. Anthu odzichepetsa ndi oona mtima amene anali kufunadi choonadi anamvetsera uthenga wabwino wa Ufumu. Mosiyana ndi amenewo, anthu onyada ndi odzitukumula ananyoza Yesu ndi uthenga wake. Yesu anati: “Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.” (Luka 10:21) Tikamachita zinthu ndi anthu chifukwa cha chikondi ndi chikhulupiriro, timachita zinthu mopanda tsankho podziŵa kuti zimenezi n’zimene Yehova amafuna.

11. Kodi mu mpingo wachikristu woyambirira kupanda tsankho kunaonekera motani?

11 Mu mpingo wachikristu woyambirira, panalibe kusiyana pakati pa anthu amene anali Ayuda ndi anthu amene sanali Ayuda. Paulo anafotokoza kuti: “Ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene; pakuti Mulungu alibe tsankhu.” * (Aroma 2:10, 11) Zimene zinachititsa kuti apindule ndi kukoma mtima kwa Yehova si mtundu wobadwira, koma zimene anachita ataphunzira za Yehova ndiponso chiyembekezo chimene dipo la Mwana wake, Yesu, linawapatsa. (Yohane 3:16, 36) Paulo analemba kuti: “Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupimo; koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m’malembo ayi.” Kenako, pogwiritsa ntchito mawu okhudza liwu lakuti “Myuda” (kutanthauza wotamandidwa kapena woyamikiridwa), Paulo anawonjezera kuti: “Kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.” (Aroma 2:28, 29) Yehova amayamikira mopanda tsankho. Kodi ifenso timatero?

12. Kodi lemba la Chivumbulutso 7:9 limapereka chiyembekezo chotani, ndipo kwa ndani?

12 Pambuyo pake, kudzera m’masomphenya, mtumwi Yohane anaona Akristu okhulupirika odzozedwa akuonetsedwa monga mtundu wauzimu wa anthu okwana 144,000, “osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana Aisrayeli.” Zimenezi zitapita, Yohane anaona ‘khamu lalikulu . . . lochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwawo.’ (Chivumbulutso 7:4, 9) Chotero, palibe fuko limene mulibe mu mpingo wamakono wachikristu. Anthu osiyanasiyana ali ndi chiyembekezo chopulumuka “chisautso chachikulu” chimene chikubwera ndi kumwa ku “akasupe a madzi a moyo” m’dziko latsopano.​—Chivumbulutso 7:14-17.

Phindu la Kupanda Tsankho

13-15. (a) Kodi tingathetse bwanji kusiyana maganizo chifukwa cha mtundu kapena chikhalidwe? (b) Tchulani zitsanzo zosonyeza phindu la kukhala waubwenzi.

13 Yehova amatidziŵa bwino kwambiri, monga mmene tate wabwino amadziŵira ana ake. Mofananamo, tikawadziŵa bwino anthu ena chifukwa chomvetsetsa chikhalidwe chawo ndi moyo wawo wakale, kusiyana maganizo sikukhalanso  vuto lalikulu. Kusagwirizana chifukwa chosiyana fuko kumatha, ubwenzi ndi chikondi chathu zimakula. Mgwirizano wathu umalimba. (1 Akorinto 9:19-23) Zimenezi zimaoneka bwino mu ntchito ya amishonale amene amakatumikira kumayiko ena. Amakhala ndi chidwi ndi anthu okhala kumene akutumikirako, ndipo zotsatira zake n’zakuti, amishonalewo amaona kuti pasanapite nthaŵi akukhala bwinobwino ndi anthu a mipingo ya kumaloko.​—Afilipi 2:4.

14 Phindu la kupanda tsankho likuoneka m’mayiko ambiri. Aklilu, wochokera ku Ethiopia, anali wosungulumwa kulikulu la dziko la Britain, ku London. Kusungulumwa kwakeko kunakula chifukwa ankaona kuti anthu akumaloko analibe chidwi ndi anthu ochokera ku mayiko ena, zimene zikuchitikanso masiku ano m’mizinda ikuluikulu yambiri ya ku Ulaya. Zimene Aklilu anaona atapita kumsonkhano wachikristu ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova zinali zosiyana kwambiri! Kumsonkhanoko anamulandira, ndipo posakhalitsa anakhala womasuka. Anapita patsogolo kwambiri mpaka anam’dziŵa bwino Mlengi. Pasanapite nthaŵi yaitali, anayamba kufunafuna mipata yolalikira nawo uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu ena m’dera limenelo. Tsiku lina mnzake wa Aklilu amene amalalikira naye atam’funsa kuti anali ndi zolinga zotani pa moyo wake, Aklilu anayankha mosazengereza kuti anali kufunitsitsa tsiku lina atakhala mu mpingo wolankhula chinenero chake, Chiamhariki. Akulu a mu mpingo wa Chingelezi kumeneko atamva zimenezi, mosazengereza anakonza zokamba nkhani ya onse yochokera m’Baibulo m’chilankhulo cha Aklilu. Chilengezo chimene chinaperekedwa cha nkhaniyi chinachititsa kuti anthu ambiri a mayiko akunja komanso akomweko apezeke pa msonkhano wa onse woyamba wa Chiamhariki ku Britain. Lerolino, anthu a ku Ethiopia komanso anthu ena kudera limeneli ndi ogwirizana mu mpingowo, umene ukukula. Anthu ambiri kumeneko apeza kuti palibe chimene chingawalepheretse kukhala kumbali ya Yehova ndipo asonyeza zimenezi kudzera mu ubatizo wachikristu.​—Machitidwe 8:26-36.

15 Anthu amasiyana khalidwe komanso mmene anakulira. Koma zimenezi si zimene zimachititsa kuti munthu akhale wapamwamba kapena wotsika; kwangokhala kusiyana basi. Poonerera ubatizo wa atumiki a Yehova amene anadzipatulira kumene pa chilumba cha Malta, Mboni za kumeneko zimasekerera pamene za ku Britain zimalira, konseku kunali kukondwa. Magulu aŵiri onseŵa, abale a ku Malta ndi abale a ku Britain, anasonyeza mmene amamvera koma anachita zimenezi m’njira zosiyana, ndipo chikondi chawo chachikulu pa Yehova chinalimbitsa ubale wawo wachikristu.​—Salmo 133:1; Akolose 3:14.

Kugonjetsa Tsankho

16-18. Fotokozani zimene zinachitika zosonyeza mmene tsankho lingagonjetsedwere mu mpingo wachikristu.

16 Chikondi chathu pa Yehova ndi pa abale athu achikristu chikamakula, tingathe kutsanzira kwambiri Yehova ndipo tingayambe kuona anthu ena monga mmene iye amawaonera. Ngati tinali ndi tsankho ndi anthu a mayiko ena, mafuko, kapena a chikhalidwe china tingathe kuligonjetsa. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira Albert, amene anali msilikali wa ku Britain nthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko  lonse. Iye anagwidwa ndi asilikali a ku Japan atalanda malo ku Singapore m’chaka cha 1942. Anakhala akugwira ntchito kwa pafupifupi zaka zitatu “pa njanji ya imfa,” kufupi ndi malo amene anadzadziŵika monga mlatho wa pamtsinje wa Kwai. Atamasulidwa kumapeto kwa nkhondoyo, amalemera makilogalamu 32, anali atatchoka nsagwada ndi mphuno, ndipo amadwala kamwazi, zipere, ndi malungo. Anzake ambiri amene anagwidwa nawo anali odwala kwambiri, ndipo ambiri sanakhale ndi moyo. Chifukwa cha nkhanza zimene Albert anaona ndi kukumana nazo, anabwerera kwawo m’chaka cha 1945 ali wokhumudwa, ndiponso alibe chidwi ndi Mulungu kapena chipembedzo.

17 Mkazi wa Albert, Irene, anakhala wa Mboni za Yehova. Kuti asangalatse mkazi wake, Albert anapezeka pa misonkhano ingapo ya Mboni za Yehova pampingo wakwawoko. Mkristu wachinyamata amene anali mu utumiki wa nthaŵi zonse wotchedwa Paul anayendera Albert kuti aziphunzira naye Baibulo. Mosakhalitsa Albert anazindikira kuti Yehova akamayang’ana munthu, amaona zimene zili mu mtima wa munthuyo. Anapatulira moyo wake kwa Yehova ndipo anabatizidwa.

18 Pambuyo pake Paul anasamukira ku London, kumene anaphunzira Chijapanizi n’kuyamba kusonkhana ndi mpingo wolankhula Chijapanizi. Pamene ananena kuti akufuna kutenga Mboni zina za ku Japan zimene zinabwera kudzacheza kuti apite nazo ku mpingo umene ankasonkhana poyamba, abale a mu mpingo wake wakalewo anakumbukira tsankho lamphamvu limene Albert anali nalo kwa anthu ochokera ku Japan. Kuchokera pa nthaŵi imene Albert anabwerera ku Britain, sanafune kukumana maso ndi maso ndi munthu aliyense wochokera ku Japan, choncho abalewo sanadziŵe kuti Albert adzachita zotani. Koma iwo sanafunike kuda nkhaŵa. Albert analandira alendowo mwachikondi ndi mwaubale.​—1 Petro 3:8, 9.

‘Kulitsani Chikondi Chanu’

19. Kodi ndi langizo lotani la mtumwi Paulo limene lingatithandize ngati tili ndi tsankho?

19 Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Chetera [tsankho, NW] silili labwino.” (Miyambo 28:21) N’zosavuta kukhala oyandikana ndi anthu amene timawadziŵa bwino. Koma nthaŵi zina, sitichita chidwi kwambiri ndi anthu amene sitikuwadziŵa bwino. Tsankho limenelo n’losayenera atumiki a Yehova. Ndithudi, tonsefe tingachite  bwino kutsanzira langizo lomveka bwino la Paulo lakuti ‘kulitsani chikondi chanu.’ Inde, tiyeni tikulitse chikondi chathu kwa Akristu anzathu achikhalidwe chosiyanasiyana.​—2 Akorinto 6:13.

20. Kodi tiyenera kutsanzira Yehova, Mulungu wathu wopanda tsankho, m’mbali ziti za moyo?

20 Kaya tili ndi mwayi wodzapita kumwamba kapena chiyembekezo chodzakhala pa dziko lapansi kwa moyo wonse, kukhala kwathu opanda tsankho kumatithandiza kusangalala ndi mgwirizano wokhala m’gulu limodzi ndi Mbusa mmodzi. (Aefeso 4:4, 5, 16) Kuyesetsa kutsanzira Yehova, Mulungu wathu wopanda tsankho, kungatithandize mu utumiki wathu wachikristu, m’mabanja athu, ndi mu mpingo wachikristu, inde, m’mbali zonse za moyo. Motani? Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Pambuyo pake analemba za kutchuka kwa Yehova m’nyimbo zopatulika.​—Salmo 135:8-11; 136:11-20.

^ ndime 11 Pano, mawu akuti Mhelene akutanthauza anthu Akunja onse.

Kodi Mungayankhe Motani?

Kodi Yehova anasonyeza motani kupanda tsankho kwa Rahabi ndi kwa Agibeoni?

Kodi Yesu anasonyeza motani kupanda tsankho pa zimene ankaphunzitsa?

Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tigonjetse tsankho la kusiyana kwa chikhalidwe ndi mitundu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Aisrayeli ayamba kugonjetsa Akanani

[Chithunzi patsamba 15]

Yesu sanapeŵe kulalikira mkazi wachisamariya pachitsime

[Chithunzi patsamba 16]

Msonkhano wa onse m’Chiamhariki ku Britain

[Chithunzi patsamba 16]

Kukonda Yehova kunamuthandiza Albert kugonjetsa tsankho