Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Sukulu ya Gileadi Yatha Zaka 60 Ikuphunzitsa Amishonale

Sukulu ya Gileadi Yatha Zaka 60 Ikuphunzitsa Amishonale

 Sukulu ya Gileadi Yatha Zaka 60 Ikuphunzitsa Amishonale

“CHIFUKWA chakuti tinaliphunzira mozama Baibulo, tinayandikana naye kwambiri Yehova ndipo tinaphunzira zinthu zambiri zokhudza gulu lake. Zimenezi zinatithandiza kuti tikhale okonzeka kukatumikira ku dziko lachilendo.” Mmenemu ndi mmene wophunzira wina amene anamaliza maphunziro a kalasi loyamba la Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo anawafotokozera maphunzirowo. Chiyambire pamene Sukulu ya Gileadi inakhazikitsidwa zaka 60 zapitazo, yakhala ikutumiza amishonale m’mayiko osiyanasiyana. Pa March 8, 2003 ku Likulu la Maphunziro a Watchtower ku Patterson, ku New York, kunali mwambo womaliza maphunziro a kalasi la nambala 114. Anthu 6,404 amene anasonkhana mu holo imene amachitira mwambo umenewu komanso ena amene amaonera pulogalamu yonse pa TV kumalo ena anamvetsera mwachidwi pulogalamu yonseyo, imene inali ndi nkhani, kufunsana, ndi kukambirana kwapagulu.

Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulira, ndi amene anali tcheyamani. M’mawu ake oyamba iye anatchulapo zoti anthu amene amamvetsera pulogalamuyo anali ochokera m’mayiko osiyanasiyana, chifukwa panali alendo ochokera ku Asia, ku Caribbean, ku Central America, ku South America, ndi ku Ulaya. Pofotokoza mawu amene ali pa 2 Timoteo 4:5, Mbale Jaracz anatsindika kuti ntchito yaikulu ya mmishonale amene waphunzira Sukulu ya Gileadi ndi “[ku]chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino.” Amishonalewo amachitira umboni choonadi mwa kuphunzitsa anthu Baibulo.

Ophunzira Apatsidwa Malangizo Omaliza

Monga woyamba kulankhulapo pa mndandanda wa nkhani zifupizifupi, John Larson, amene ali mu Komiti ya Nthambi ya ku United States anakamba nkhani yolimbikitsa chikhulupiriro ya mutu wakuti: “Ngati Mulungu Ali ndi Ife, Adzatikaniza Ndani?” (Aroma 8:31) Wokamba nkhaniyo anafotokoza mfundo zochokera m’Baibulo zimene zingalimbikitse ophunzirawo kukhulupirira ndi mtima wonse kuti mphamvu ya Yehova idzawathandiza kulimbana ndi zovuta zilizonse zimene angakumane nazo kumayiko kumene akatumikire. Pogwiritsa ntchito Aroma 8:38, 39, Mbale Larson analimbikitsa ophunzirawo kuti: “Muziyamba mwaima n’kuganiza za mphamvu imene Mulungu akugwiritsa ntchito pokuthandizani, ndipo muzikumbukira kuti palibe chimene chingathetse chikondi chimene Yehova ali nacho pa inu.”

Kenaka Guy Pierce, wa m’Bungwe Lolamulira analankhulapo. Anasankha mutu wakuti “Mukhale ndi Maso Achimwemwe!” (Luka 10:23) Iye anafotokoza kuti chimwemwe chenicheni chimabwera chifukwa cha kudziŵa Yehova ndi kumvetsetsa cholinga chake chosatha, komanso kuona maulosi a Baibulo akukwaniritsidwa. Kulikonse kumene angapite, ophunzirawo angathe kukhala ndi chimwemwe chenicheni mwa kukhala ndi maso achimwemwe. Mbale Pierce analimbikitsa omaliza maphunzirowo kuti azisinkhasinkha mwakuya za ubwino wa Yehova ndipo maganizo ndi mitima yawo zizikhala pa kuchita chifuniro Chake. (Salmo 77:12) Mwa kuyang’ana mbali yabwino ya chinthu chilichonse, omaliza maphunzirowo angathane ndi mavuto alionse amene angakumane nawo.

Kenaka kalasilo linauzidwa mawu olimbikitsa olaŵirana nalo ochokera kwa aŵiri a alangizi amene ankawaphunzitsa tsiku lililonse. “Kodi Mukufuna Ulemerero?” ndilo linali funso limene anafunsa Lawrence Bowen mu nkhani yake. Anthu ambiri akamaganiza za ulemerero amaganiza za kutamandidwa, kupatsidwa  ulemu, ndi kuchita zinthu zapadera zosiyana ndi ena. Koma wamasalmo Asafu anazindikira ulemerero weniweni​—kukhala ndi chuma cha mtengo wapatali kwambiri chifukwa cha kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Salmo 73:24, 25) Ophunzira amene anamaliza maphunzirowo analimbikitsidwa kupitiriza kukhala pa ubwenzi wathithithi ndi Yehova mwa kupitiriza kuphunzira Baibulo mozama. Angelo ‘akulakalaka kusuzumira’ m’zinthu zofotokoza mmene Yehova adzakwaniritsire cholinga chake kudzera mwa Kristu. (1 Petro 1:12) Amafuna kuphunzira zonse zimene angathe zokhudza Atate wawo kuti azionetsa ulemerero wake. Ndiyeno wokamba nkhaniyo analimbikitsa ophunzirawo kuti akalemekeze Yehova mu ntchito yawo yaumishonale mwa kuthandiza ena kupeza chuma chamtengo wapatali chimenechi.

Wosunga kaundula m’sukuluyi, Wallace Liverance, anakamba nkhani yomaliza m’gawo limeneli ya mutu wakuti “Lankhulani Nzeru ya Mulungu ya m’Chinsinsi Chopatulika.” (1 Akorinto 2:7) Kodi nzeru ya Mulungu imeneyi, imene anaitchula mtumwi Paulo nthaŵi imene ankachita utumiki wake waumishonale n’chiyani? Ndi njira ya Yehova yanzeru komanso yamphamvu yobweretsera mtendere ndi mgwirizano m’chilengedwe chonse. Nzeruyi yagona pa Yesu. M’malo molalikira uthenga woti Akristu azithetsa mavuto a anthu, Paulo anathandiza anthu kuona mmene Mulungu adzathetsere mavuto onse amene anabwera chifukwa cha uchimo  wa Adamu. (Aefeso 3:8, 9) Wokamba nkhaniyo analimbikitsa omvetsera ake kuti: “Gwiritsani ntchito mwayi wanu wotumikira Mulungu ngati mmene anachitira Paulo, amene anaona umishonale wake ngati mwayi wothandizira anthu kuona mmene Yehova adzakwaniritsire chifuno chake.”

Nkhani imeneyi itatha, Mark Noumair, mlangizi winanso wa Gileadi, anatsogolera nkhani yochititsa chidwi yokambirana ndi ophunzira angapo a m’kalasili. Mutu wake woti “Kuphunzira Mawu a Mulungu Kumatulutsa Atumiki Achangu” inagogomezera mawu a Paulo a pa Aroma 10:10. Anthu a m’kalasilo anafotokoza zinthu zosangalatsa zambiri zimene zinawachitikira mu utumiki wakumunda panthaŵi imene amaphunzira maphunziro awo. Zimene zinawachitikirazi zikusonyeza kuti ngati tiphunzira ndi kusinkhasinkha za Mawu a Mulungu, zinthu zabwino zokhudza Yehova Mulungu ndi Ufumu wake zidzadzaza mitima yathu ndipo tidzayamba kuzilankhula. Kwa miyezi isanu imene ophunziraŵa anakhala ku Likulu la Maphunziro a Watchtower, anayambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba oposa 30 ndi anthu achidwi m’gawo la mipingo yozungulira maloŵa limene amalalikiramo kwambiri.

Anthu Okhwima Mwauzimu Alankhulapo

Panthaŵi imene anali kuphunzira, ophunzirawo anapindula chifukwa choyanjana ndi anthu a m’banja la Beteli la ku United States. Anthu aŵiri ogwira ntchito panthambipo, Robert Ciranko ndi Robert P. Johnson, anafunsa mafunso atumiki a Yehova angapo amene akhala okhulupirika kwa nthaŵi yaitali, kuphatikizapo oyang’anira oyendayenda amene pakadali pano akuchita maphunziro apadera ku Likulu la Maphunziro a Watchtower. Onse amene anafunsidwa mafunsowo anamaliza maphunziro a Gileadi ndipo anali amishonale m’mbuyomo. Zinali zolimbikitsa kwambiri kwa ophunzirawo ndiponso kwa mabanja ndi mabwenzi awo kumva malangizo anzeru ochokera kwa amuna achikulire mwauzimu ameneŵa.

Ena mwa malangizo awo anali oti: “Muzikhala otanganidwa kwambiri monga momwe mungathere mu utumiki ndi mu mpingo.” “Musamaganize kuti ndinu munthu wofunika kwambiri. Maganizo anu azikhala pa cholinga chanu monga mmishonale, ndipo muziona kumene mukuchita umishonaleko ngati kwanu.” Ndemanga zina zothandiza zinasonyeza mmene maphunziro a Gileadi amakonzekeretsera mtumiki kuchita ntchito yabwino, mosasamala kanthu za kumene watumizidwa. Zina mwa ndemangazo ndi izi: “Tinaphunzira kugwirizana ndi kuchitira zinthu limodzi.” “Sukuluyi inatithandiza kulolera chikhalidwe cha anthu ena.” “Inatiphunzitsa kugwiritsa ntchito Malemba m’njira yatsopano.”

John E. Barr, amene wakhala m’Bungwe Lolamulira kwa nthaŵi yaitali, anakamba nkhani yaikulu ya pulogalamu imeneyi. Nkhani yake yotengedwa m’Malemba inali ndi mutu wakuti “Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi.” (Aroma 10:18) Iye anafunsa funso lakuti, Kodi anthu a Mulungu akuikwanitsa ntchito yovuta imeneyi masiku ano? Ndithudi akutero! Kale mu 1881, anthu oŵerenga magazini ya Nsanja ya Olonda anafunsidwa kuti: “Kodi Mukulalikira?” Kenaka wokamba nkhaniyo anakumbutsa omvetsera onsewo za mawu olimbikitsa osaiŵalika amene ananenedwa pa msonkhano wa mu 1922 ku Cedar Point, Ohio, ku U.S.A akuti: “Lengezani Mfumu ndi Ufumu Wake!” M’kupita kwa nthaŵi, changu cha atumiki okhulupirika a Mulungu chinawapangitsa kulengeza choonadi chochititsa chidwi cha Ufumu ku mitundu yonse. Mwa kugwiritsa ntchito mabuku ndi mawu a pakamwa, uthenga wabwino wafika kumalekezero a dziko, kulikonse kumene kuli anthu, ndipo zonsezi zikutamanda ndi kupereka ulemu kwa Yehova. M’mawu ake omaliza okhudza mtima kwambiri, Mbale Barr analimbikitsa omaliza maphunzirowo kuti aziganizira za madalitso awo, ndipo anati: “Tsiku lililonse, mukamapemphera kwa Yehova m’gawo limene mukutumikira, muzimuthokoza kuchokera pansi pa mtima chifukwa cha mbali imene muli nayo yokwaniritsa mawu akuti, ‘Liwu lawo linatulukira ku dziko lonse lapansi.’”

Nkhani imeneyi itatha, anaŵerenga mafuno abwino ochokera ku nthambi zosiyanasiyana, ndipo tcheyamani anapereka dipuloma kwa womaliza maphunziro aliyense. Kenaka, ali ndi chimwemwe komanso chisoni chifukwa chomaliza sukulu yokondedwayo, woimira kalasilo anaŵerenga kalata yopita ku Bungwe Lolamulira ndi ku banja la Beteli. Kalatayo inafotokoza mfundo imene anthu a m’kalasilo anali otsimikiza kuchita, yoti adzatamanda Yehova “kuyambira tsopano kufikira nthaŵi yonse.”​—Salmo 115:18.

Tikuwapempherera omaliza maphunziro ameneŵa kuti akazoloŵere malo awo atsopano ndipo akathandize kwambiri pa ntchito yolalikira padziko lonse, monga momwe amishonale anzawo achitira kwa zaka 60 zapitazi.

[Bokosi patsamba 23]

ZIŴERENGERO ZA KALASI

Chiŵerengero cha mayiko kumene ophunzira anachokera: 12

Chiŵerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 16

Chiŵerengero cha ophunzira: 48

Avareji ya zaka zakubadwa: 34.4

Avareji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 17.6

Avareji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthaŵi zonse: 13.5

[Chithunzi patsamba 24]

Kalasi la 114 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pa m’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliwonse.

(1) Rosa, D.; Garrigolas, J.; Lindström, R.; Pavanello, P.; Tait, N. (2) Van Hout, M.; Donabauer, C.; Martinez, L.; Millar, D.; Festré, Y.; Nutter, S. (3) Martinez, P.; Clarke, L.; Maughan, B.; Fischer, L.; Romo, G. (4) Romo, R.; Eadie, S.; Tuynman, C.; Campbell, P.; Millar, D.; Rosa, W. (5) Lindström, C.; Garrigolas, J.; Markevich, N.; Lindala, K.; van den Heuvel, J.; Tait, S.; Nutter, P. (6) Maughan, P.; Pavanello, V.; Eadie, N.; West, A.; Clarke, D.; Markevich, J. (7) Fischer, D.; Donabauer, R.; Curry, P.; Curry, Y.; Carfagno, W.; West, M.; Tuynman, A. (8) Van Hout, M.; Campbell, C.; Festré, Y.; Carfagno, C.; van den Heuvel, K.; Lindala, D.