Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muziyang’ana Ubwino wa Onse

Muziyang’ana Ubwino wa Onse

 Muziyang’ana Ubwino wa Onse

“Mundikumbukire Mulungu wanga, chindikomere [“monga mwa ubwino wanu,” NW].”​—NEHEMIYA 13:31.

1. Kodi Yehova amaonetsa ubwino kwa anthu onse motani?

PAKAPITA masiku ambiri kuli mitambo kenako dzuŵa n’kuŵala, zimakhala bwino. Anthu amasangalala, ndipo amamva bwino. Mofananamo, pakapita nyengo yaitali kuli dzuŵa loswa mtengo ndiponso kuli kouma, mvula yowaza ngakhale yamkuntho imene imabweretsa mpumulo. Mlengi wathu wachikondi, Yehova, analenga dziko lathuli kuti likhale ndi nyengo zimenezi. Nyengozi ndi mphatso yabwino kwambiri. Yesu anafotokoza kupatsa kwa Mulungu kumeneku pamene anaphunzitsa kuti: “Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu; kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa iye amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:43-45) Inde, Yehova amaonetsa ubwino kwa anthu onse. Atumiki ake ayenera kuyesetsa kumutsanzira poyang’ana ubwino wa ena.

2. (a)  Kodi Yehova ali ndi chifukwa chotani choonetsera ubwino? (b) Tikamachita zinthu chifukwa choyamikira ubwino wa Yehova, kodi iye amatani?

2 Kodi Yehova ali ndi chifukwa chotani choonetsera ubwino? Kuchokera panthaŵi imene Adamu anachimwa, Yehova sanaleke kuyang’ana ubwino wa anthu. (Salmo 130:3, 4) Cholinga chake n’choti anthu omvera adzakhalenso ndi moyo m’Paradaiso. (Aefeso 1:9, 10) Chifukwa cha kukoma mtima kwake tili ndi chiyembekezo chopulumutsidwa ku uchimo ndi kupanda ungwiro kudzera mwa Mbewu  yolonjezedwa. (Genesis 3:15; Aroma 5:12, 15) Kukhulupirira dipo kumatsegula njira yopezeranso moyo wangwiro. Chinthu chimodzi chimene Yehova tsopano akuyang’ana mwa aliyense wa ife n’chakuti akufuna aone zimene tichite chifukwa cha khalidwe lake lopatsa. (1 Yohane 3:16) Amaona zilizonse zimene timachita posonyeza kuyamikira kwathu ubwino wake. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.”​—Ahebri 6:10.

3. Kodi ndi funso liti limene tifunika kuliganizira?

3 Kodi tingatsanzire motani Yehova poyang’ana ubwino wa ena? Tiyeni tipeze mayankho a funso limeneli m’mbali zinayi za moyo: (1) mu utumiki wachikristu, (2) m’banja, (3) mu mpingo, ndi (4) pochita zinthu ndi ena.

Polalikira ndi Popanga Ophunzira

4. Kodi kuchita nawo utumiki wachikristu kumasonyeza bwanji kuti tikuyang’ana ubwino wa ena?

4 “Munda ndiwo dziko lapansi,” anatero Yesu poyankha mafunso amene ophunzira ake anafunsa onena za tanthauzo la fanizo la tirigu ndi namsongole. Ife monga Akristu amakono timazindikira mfundo yoona imeneyi tikamachita utumiki wathu. (Mateyu 13:36-38; 28:19, 20) Utumiki wathu wakumunda umaphatikizapo kulalikira poyera za chikhulupiriro chathu. Mboni za Yehova ndi zodziŵika kwambiri chifukwa cha utumiki wawo wa kunyumba ndi nyumba ndiponso wa m’misewu ndipo mfundo imeneyi payokha ndi umboni wakuti timachita khama pofunafuna onse amene akuyenerera uthenga wa Ufumu. Inde, Yesu analangiza kuti: “M’mzinda uliwonse, kapena m’mudzi mukaloŵamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo.”​—Mateyu 10:11; Machitidwe 17:17; 20:20.

5, 6.N’chifukwa chiyani timachita khama kuyendera anthu mobwerezabwereza ku nyumba zawo?

5 Tikamayendera anthu amene sanatiitane, timayang’anitsitsa zimene amachita akamva uthenga wathu. Nthaŵi zina timapeza kuti wina wa m’banjalo akumvetsera, pamene wina, wa m’banja lomwelo, amanena kuti, “Sitikufuna,” ndipo timasiyira pomwepo. Timamva chisoni chifukwa chakuti kutsutsa kapena kusoŵa chidwi kwa munthu mmodzi kumakhudzanso  munthu wina! Kodi tingachite chiyani kuti tisasiye kuyang’ana ubwino wa onse?

6 Pa ulendo wathu wotsatira ku nyumba imeneyo tikamakalalikiranso m’deralo tingakhale ndi mpata wolankhula ndi munthu amene anatilepheretsa kulalikira ulendo woyamba uja. Kukumbukira zimene zinachitika nthaŵi imeneyo kungatithandize kukonzekera. Wotsutsayo angakhale atachita zimenezo pofuna kuthandiza mnzake wachidwiyo, akukhulupirira kuti ayenera kum’letsa kuti asamvetsere uthenga wa Ufumu. Mwina malingaliro ake angakhale atasokonezeka ndi nkhani zonama zokhudza cholinga chathu. Koma zimenezo sizitilepheretsa kulimbikira polalikira uthenga wabwino wa Ufumu pa khomo limenelo, ndipo timayesetsa mwaluso kuthetsa maganizo olakwika amene angakhale nawo. Tili ndi chidwi chofuna kuthandiza onse kuti adziŵe Mulungu molondola. Mwina Yehova adzakopera munthu ameneyu kwa iye.​—Yohane 6:44; 1 Timoteo 2:4.

7. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala ndi malingaliro oti anthu akatilandira bwino tikamawalalikira?

7 Popereka malangizo kwa ophunzira ake, Yesu anatchulaponso zoti m’mabanja mudzakhala kutsutsana. Kodi sanafotokoze kuti, “ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake”? Yesu ananenanso kuti: “Apabanja ake a munthu adzakhala adani ake.” (Mateyu 10:35, 36) Komabe, zochitika ndi maganizo zimasintha. Kudwala mwadzidzi, wachibale kumwalira, masoka, kuvutika maganizo, ndi zinthu zina zambiri zimachititsa anthu kutilandira mosiyanasiyana tikamalalikira. Ngati tili ndi maganizo olakwika oti anthu amene timawalalikira adzakhalabe opanda chidwi, kodi tikuyang’anadi ubwino wa anthuwo? Bwanji osapitanso ku nyumba zawo mosangalala nthaŵi ina? Tingadabwe ndi mmene akatilandirire! Nthaŵi zina zimene zimachititsa kuti atilandire bwino si zimene timanena zokha komanso mmene timazinenera. Kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima tisanayambe kulalikira kudzatithandiza kukhala ndi malingaliro oti akatilandira bwino komanso kulalikira uthenga wa Ufumu mogwira mtima kwa onse.​—Akolose 4:6; 1 Atesalonika 5:17.

8. Kodi chingachitike n’chiyani ngati Akristu ayang’ana ubwino wa abale awo osakhulupirira?

8 M’mipingo ina anthu ambiri a banja limodzi akutumikira Yehova. Nthaŵi zambiri chimene chinachititsa chidwi achinyamata kuti asinthe maganizo awo ndi khama la mbale wawo wachikulire amene amakhala naye bwino m’banjamo komanso amene amakhala bwino ndi mkazi wake kapena mwamuna wake. Kumvera langizo la mtumwi Petro kwathandiza akazi ambiri achikristu kuti akope amuna awo ‘popanda mawu.’​—1 Petro 3:1, 2.

M’banja

9, 10. Kodi Yakobo ndi Yosefe anayang’ana bwanji ubwino m’banja lawo?

9 Ubale umene umakhalapo kwa anthu a m’banja limodzi ndi mbali ina imene ingatithandize kuyang’ana ubwino wa ena. Taganizirani phunziro lopezeka pa zimene Yakobo anachita ndi ana ake. Pa Genesis chaputala 37, mavesi 3 ndi 4, Baibulo limasonyeza kuti Yakobo anakonda kwambiri Yosefe. Abale ake a Yosefe anachita nsanje, mpaka kufika pokonza chiwembu choti amuphe. Komabe, taonani mtima umene Yakobo ndi Yosefe anadzasonyeza pambuyo  pake. Onse anayang’ana ubwino wa anthu a m’banja lawo.

10 Pamene Yosefe anali kugwira ntchito monga mkulu woyang’anira chakudya m’dziko la Igupto limene munali njala, anawalandira bwino abale ake. Ngakhale kuti sanadziulule mofulumira kuti iye anali ndani, anaonetsetsa kuti abale akewo asamalidwa bwino ndipo anali ndi chakudya chopita nacho kwa atate wawo amene anali achikulire. Inde, ngakhale kuti anadana naye ndipo anamuchitira nkhanza, Yosefe anawakomera mtima. (Genesis 41:53–42:8; 45:23) Mofananamo, nthaŵi imene Yakobo amamwalira anadalitsa ana ake onse polosera zimene zidzawachitikire m’tsogolo. Ngakhale kuti zolakwa zawo zinachititsa kuti ena a iwo alandire madalitso ochepa, palibe amene sanalandire cholowa m’dzikomo. (Genesis 49:3-28) Pamenepatu Yakobo anasonyeza chikondi chokhalitsa m’njira yodabwitsa kwambiri!

11, 12. (a) Kodi ndi chitsanzo chiti chophiphiritsira chimene chikusonyeza bwino kufunika kwa kuyang’ana ubwino m’banja? (b) Kodi tikupeza phunziro lotani pa chitsanzo chimene anasonyeza atate a m’fanizo la Yesu lokamba za mwana woloŵerera?

11 Kuleza mtima kwa Yehova pochita zinthu ndi mtundu wosakhulupirika wa Israyeli kukutithandiza kuzindikira zimene Yehova amachita poyang’ana ubwino wa anthu ake. Pogwiritsa ntchito zimene zinkachitika m’banja la mneneri Hoseya, Yehova anasonyeza chikondi chake chokhalitsa. Goma, mkazi wa Hoseya, anachita chigololo mobwerezabwereza. Ngakhale zinali choncho, Yehova analangiza Hoseya kuti: “Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israyeli, angakhale atembenukira ku milungu ina, nakonda ntchintchi za mphesa zouma.” (Hoseya 3:1) N’chifukwa chiyani anam’patsa malangizo ameneŵa? Yehova anadziŵa kuti pakati pa anthu amene anali atasiya njira zake, ena akanakopeka ndi kuleza mtima kwake. Hoseya anati: “Atatero ana a Israyeli adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wawo, ndi Davide mfumu yawo, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.” (Hoseya 3:5) Ndithudi chimenechi ndi chitsanzo chabwino choti tizichiganizira tikakumana ndi mavuto m’banja. Kupitiriza kwanu kuyang’ana ubwino wa ena m’banja lanu kungapereke chitsanzo chabwino cha kuleza mtima.

12 Fanizo la Yesu la mwana woloŵerera likutiunikiranso bwino mmene tingayang’anire ubwino m’banja lathu. Mwana wamng’onoyo  anabwerera kwawo atasiya moyo wake wosakaza chumawo. Atate wake anam’chitira chifundo. Kodi atatewo anachita chiyani mwana wawo wamkulu amene anali asanachokepo panyumbapo atadandaula? Polankhula ndi mwana wamkuluyo, atatewo anati: “Mwana wanga, iwe uli ndine nthaŵi zonse, ndipo zanga zonse zili zako.” Kumeneku sikunali kulankhula mokwiya koma amam’tsimikizira mwana wawoyo kuti amam’konda. Anapitiriza ponena kuti: “Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng’ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.” Ifenso tingapitirize kuyang’ana ubwino wa ena ngati mmene anachitira atatewo.​—Luka 15:11-32.

Mu Mpingo Wachikristu

13, 14. Kodi tingatsatire motani lamulo lachifumu la chikondi mu mpingo wachikristu?

13 Ife monga Akristu timafuna kutsata lamulo lachifumu la chikondi. (Yakobo 2:1-9) N’zoona kuti tikhoza kuona anthu a mu mpingo wathu amene amapeza zinthu mosiyana ndi ife ngati abale athu. Koma kodi timasankhana chifukwa cha kusiyana mitundu, chikhalidwe, kapena zipembedzo zimene takuliramo? Ngati ndi choncho, kodi tingamvere bwanji langizo la Yakobo?

14 Kulandira onse amene amabwera pa misonkhano yachikristu kumasonyeza kuti tili ndi mtima wokonda kucheza ndi anthu. Tikamayamba ndife kulankhula ndi atsopano amene amabwera pa Nyumba ya Ufumu, manyazi ndi mantha amene amakhala nawo poyamba angathe. Ndithudi, anthu ena amene abwera koyamba pa misonkhano yachikristu amanena kuti: “Aliyense anali wochezeka. Zinangokhala ngati kuti aliyense akundidziŵa kale. Ndinali womasuka.”

15. Kodi achinyamata mu mpingo angathandizidwe bwanji kuti asonyeze chidwi kwa achikulire?

15 M’mipingo ina, achinyamata ochepa angakumane pamodzi m’kati kapena kunja kwa Nyumba ya Ufumu pamapeto pa msonkhano, kuti apeŵe kucheza ndi anthu achikulire. Kodi tingachite chiyani kuti tiwathandize kuthetsa khalidwe limeneli? Choyamba, makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kunyumba, kuwakonzekeretsa misonkhano. (Miyambo 22:6) Angapatsidwe ntchito yopezeratu zofalitsa zosiyanasiyana kuti onse akhale ndi zimene zikufunika kuti atenge popita kumisonkhano. Makolo ndi amenenso angathe kulimbikitsa bwino ana awo kuti azichezako ndi anthu achikulire ndi a thanzi lofooka pa Nyumba ya Ufumu. Kukhala ndi mawu olimbikitsa oti anene kwa anthu otere kungachititse ana kumva kuti achitapo kanthu kothandiza.

16, 17. Kodi achikulire angachite chiyani posonyeza kuti akuyang’ana ubwino wa achinyamata mu mpingo?

16 Abale ndi alongo achikulire ayenera kusonyeza chidwi kwa achinyamata mu mpingo. (Afilipi 2:4) Achikulirewo ndi amene angayambe kulankhula ndi achinyamatawo m’njira yowalimbikitsa. Kaŵirikaŵiri pa misonkhano amafotokozapo mfundo zolimbikitsa. Achinyamata angafunsidwe ngati asangalala ndi msonkhanowo ndiponso ngati pali mfundo zina zapadera zimene azikonda komanso zimene angazigwiritse ntchito. Achinyamata ndi ofunika kwambiri mu mpingo, ndipo tiyenera kuwayamikira kwambiri chifukwa chomvetsera mwachidwi ndiponso chifukwa cha ndemanga zimene amapereka pa  msonkhano kapena chifukwa cha mbali zilizonse zimene achita pa msonkhanowo. Mmene achinyamata amachitira zinthu ndi achikulire mu mpingo ndiponso mmene amagwirira ntchito zing’onozing’ono pa khomo zidzasonyeza kuti angasamalire bwino maudindo akuluakulu m’tsogolo.​—Luka 16:10.

17 Chifukwa chosamala bwino maudindo ameneŵa, achinyamata ena amapita patsogolo mpaka kufika poti makhalidwe awo auzimu amawathandiza kulandira maudindo aakulu. Kukhala ndi chochita kungawathandizenso kupeŵa khalidwe lachibwana. (2 Timoteo 2:22) Maudindo ameneŵa amapereka mpata ‘woyesa’ abale amene akufuna kutumikira monga mtumiki wotumikira. (1 Timoteo 3:10) Kukonda kwawo kutenga nawo mbali pa misonkhano ndi changu chawo mu utumiki, komanso khalidwe lawo loganizira onse mu mpingo, limathandiza akulu kuzindikira luso la achinyamatawo pamene akuganiza zowapatsa maudindo ena.

Kuyang’ana Ubwino wa Onse

18. Kodi ndi msampha wotani umene uyenera kupeŵedwa poweruza, ndipo chifukwa chiyani?

18 Miyambo 24:23 amati: “Poweruza chetera [“tsankho,” NW] silili labwino.” Nzeru yochokera kumwamba imafuna kuti akulu apeŵe tsankho akamaweruza milandu mu mpingo. Yakobo anati: “Nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.” (Yakobo 3:17) Mosakayika, akamayang’ana ubwino wa ena, akulu azionetsetsa kuti sakukondera poweruza chifukwa cha ubale kapena kutengeka maganizo. Wamasalmo Asafu analemba kuti: “Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu [kutanthauza anthu okhala ndi ulamuliro]. Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti, ndi kusamalira nkhope ya oipa?” (Salmo 82:1, 2) Motero, akulu achikristu amapeŵa khalidwe lililonse lokondera pa nkhani zokhudza mnzawo kapena wachibale. Mwanjira imeneyi amasunga mgwirizano mu mpingo ndi kulola mzimu wa Yehova kuyenda momasuka.​—1 Atesalonika 5:23.

19. Kodi tingayang’ane ubwino wa ena m’njira zotani?

19 Tikamayang’ana ubwino wa abale ndi alongo athu, timasonyeza mzimu wa Paulo pamene analankhula ndi mpingo wa ku Tesalonika. Iye anati: “Koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani.” (2 Atesalonika 3:4) Tidzatha kunyalanyaza zofooka za ena ngati tikuyang’ana ubwino wawo. Tidzafufuza mbali zimene tingayamikire abale athu, ndipo tidzapeŵa mzimu wosuliza. Paulo analemba kuti: ‘Adindo afunika akhale okhulupirika.’ (1 Akorinto 4:2) Kukhulupirika kumene abale a udindo mu mpingo ndiponso abale ndi alongo athu onse achikristu ali nako kumatichititsa kuti tiziwakonda. Motero timayamba kuwakonda kwambiri ndipo zimenezi zimalimbitsa ubale wachikristu. Timaona abale monga mmene Paulo anawaonera mu nthaŵi yake. Iwo ndi ‘antchito anzathu mu Ufumu wa Mulungu’ ndi ‘otitonthoza.’ (Akolose 4:11) Tikamatero timasonyeza mtima wa Yehova.

20. Kodi anthu amene amayang’ana ubwino wa onse adzapeza madalitso otani?

20 Inde tikugwirizana ndi pemphero la Nehemiya lakuti: ‘Mundikumbukire, Mulungu wanga, monga mwa ubwino wanu.’ (Nehemiya 13:31) Ndife osangalala kudziŵa kuti Yehova amayang’ana ubwino wa anthu! (1 Mafumu 14:13) Tiyeni nafenso tizichita chimodzimodzi tikamachita zinthu ndi ena. Tikatero, tidzatha kupulumuka komanso kupeza moyo wosatha m’dziko latsopano limene layandikira.​—Salmo 130:3-8.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Yehova ali ndi chifukwa chotani choonetsera ubwino kwa onse?

Kodi tingayang’ane bwanji ubwino wa ena

mu utumiki wathu?

m’banja lathu?

mu mpingo wathu?

pochita zinthu ndi anthu onse?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Ngakhale kuti abale ake poyamba anamuda, Yosefe anayang’ana ubwino wawo

[Chithunzi patsamba 19]

Ngakhale ngati ena angatsutse, timapitirizabe kuthandiza anthu onse

[Chithunzi patsamba 20]

Ana a Yakobo onse analandira madalitso, mosaganizira zimene anachita kale

[Chithunzi patsamba 21]

Landirani onse pa misonkhano yachikristu