Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Satana Mdyerekezi ali ndi mphamvu yotha kudziŵa zimene munthu akuganiza?

Ngakhale kuti sitinganene motsimikiza, zikuoneka kuti Satana ndi ziwanda zake alibe mphamvu yodziŵa zimene tikuganiza.

Taganizirani za mayina om’fotokoza amene Satana wapatsidwa. Amatchedwa Satana (Wotsutsa), Mdyerekezi (Woneneza), Chinjoka (chimodzimodzi ndi Wonyenga), Woyesa, ndi Wabodza. (Yobu 1:6; Mateyu 4:3; Yohane 8:44; 2 Akorinto 11:3; Chivumbulutso 12:9) Pa mayina ofotokoza Satana onseŵa palibe dzina limene likusonyeza kuti ali ndi mphamvu yodziŵa zimene tikuganiza.

Mosiyana ndi zimenezo, Yehova Mulungu akufotokozedwa kuti “a[ma]yesa mitima.” (Miyambo 17:3; 1 Samueli 16:7; 1 Mbiri 29:17) Ahebri 4:13 amati: “Palibe cholengedwa chosaonekera pamaso pa [Yehova], koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.” N’zosadabwitsa kuti Yehova wapatsa Mwana wake, Yesu, mphamvu yodziŵa zimene zili m’mitima ya anthu. Yesu woukitsidwayo anati: “Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.”​—Chivumbulutso 2:23.

Baibulo silinena kuti Satana amatha kuona zimene zili m’mitima ndi m’maganizo mwa anthu. Zimenezi n’zofunika kuzidziŵa, chifukwa mtumwi Paulo akutilimbikitsa ife monga Akristu kuti “sitikhala osadziŵa machenjerero a [Satana].” (2 Akorinto 2:11) Choncho, sitiyenera kuopa kuti mwina Satana ali ndi mphamvu zinazake zapadera zimene sitikuzidziŵa.

Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti Mdani wathuyu sangadziŵe kufooka kwathu. Satana wakhala zaka mazana ambiri akuphunzira khalidwe la anthu. Safunika kukhala ndi mphamvu yodziŵa zimene zili mu mtima mwa munthu kuti adziŵe khalidwe lathu, kuti aone zosangalatsa zimene timakonda, kapena kuti amve zinthu zimene timakonda kunena, ndi zina zotero. Mmene nkhope yathu ikuonekera ndi mmene thupi lathu lakhalira zingasonyezenso zimene tikuganiza kapena mmene tikumvera.

Koma nthaŵi zambiri, Satana amagwiritsa ntchito zinthu zimene anazigwiritsa ntchito m’munda wa Edene zija​—mabodza, chinyengo, ndi kusocheretsa anthu. (Genesis 3:1-5) Ngakhale kuti Akristu sayenera kuopa kuti Satana angadziŵe zimene akuganiza, ayenera kukhala maso chifukwa cha zimene Satana angayese kuika m’maganizo mwawo. Iye amafuna kuti Akristu akhale “anthu amene nzeru zawo zinawonongekeratu ndipo sazindikiranso choona.” (1 Timoteo 6:5, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Choncho, n’zosadabwitsa kuti dziko la Satana lili ndi zinthu zoipa zambiri ndiponso zosangalatsa zimene zingawononge maganizo athu. Kuti alimbane ndi zinthu zimenezi, Akristu ayenera kuteteza maganizo awo povala “chisoti cha chipulumutso.” (Aefeso 6:17) Amachita zimenezi mwa kudzaza maganizo awo ndi ziphunzitso zoona za m’Baibulo komanso mwa kupeŵa zinthu zilizonse za m’dziko la Satanali zimene zingawononge maganizo awo.

Satana ndi mdani wamphamvu kwambiri. Koma sitiyenera kukhala ndi mantha oziziritsa nkhongono chifukwa cha iye kapena ziwanda zake. Yakobo 4:7 akutilimbikitsa kuti: “Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” Tikatsatira malangizo ameneŵa, tidzatha kunena ngati mmene ananenera Yesu, kuti Satana alibe kanthu mwa ife.​—Yohane 14:30.