Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi n’kulakwa kupha galu kapena mphaka amene akudwala kwambiri kapena yemwe wakalambitsa?

Anthu ambiri amachita chidwi ndi nyama zosiyanasiyana ndiponso zimawasangalatsa. Nyama zina zoweta zimakhala mabwenzi abwino a anthuwo. Mwachitsanzo, agalu amadziŵika kuti amamvera kwambiri ndiponso amakonda kwambiri ambuye awo. Motero, mpake kuti anthu angakonde kwambiri nyama yoteroyo, makamaka akakhala nayo kwa zaka zambiri.

Komabe, moyo wa agalu ndi amphaka ambiri si wautali kwenikweni. Agalu angakhale ndi moyo kwa zaka zoyambira pa 10 mpaka 15 kapena kungopitirira pang’ono pamenepo, monganso mmene angakhalire amphaka, ndipo zimenezi zimadalira mtundu wawo. Paukalamba, galu kapena mphaka angadwale ndiponso angalumale, zimene zingakhumudwitse mwini wake amene akukumbukira zaka za mmbuyo pamene nyamayo inali yamphamvu ndiponso yochangamuka. Kodi n’kulakwa kuthetsa kuvutika kwa nyama yoteroyo mwa kuipha?

Mkristu adzatsatira zimene Mulungu amafuna pochitira zinthu nyama. Kuchitira nkhanza nyama kumatsutsana ndi zimene Mulungu amafuna, chifukwa Mawu ake amati: “Wolungama asamalira moyo wa choweta chake.” (Miyambo 12:10) Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti Mulungu amaziona nyama mofanana ndi mmene amaonera anthu. Pamene Mulungu analenga anthu, anasonyeza kuti panali kusiyana kwakukulu pakati pa anthu ndi nyama. Mwachitsanzo, iye anapatsa anthu chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kosatha, koma sanapatse nyama chiyembekezo chimenecho. (Aroma 6:23; 2 Petro 2:12) Popeza iye ndi Mlengi, ali ndi ufulu wosankha mmene anthu azikhalira ndi nyama.

Pa Genesis 1:28 pamafotokoza mmene ayenera kukhalira. Mulungu anauza anthu oyambawo kuti: “Mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” Mofananamo, Salmo 8:6-8 limati: “[Mulungu] mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake [a munthu]; nkhosa ndi ng’ombe, zonsezo, ndi nyama za kuthengo zomwe; mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja.”

Mulungu anafotokoza momveka bwino kuti munthu angathe kuzigwiritsa ntchito nyama moyenerera kapena kuzipha. Mwachitsanzo, zikopa za nyamazo zinali kugwiritsidwa ntchito ngati zovala. Ndiponso, Chigumula cha m’nthaŵi ya Nowa chitapita, Mulungu analoleza anthu kudya nyama kuwonjezera pa zakudya zamasamba zimene anawapatsa poyambirira.​—Genesis 3:21; 4:4; 9:3.

Zimenezi sizikuloleza kupha nyama mwachisawawa pochita maseŵera. Pa Genesis 10:9, Baibulo limati Nimrode anali “mpalu wamphamvu.” Koma vesi lomwelo limati zimenezi zinamuchititsa kukhala “pamaso pa [“wotsutsana ndi,” NW] Yehova.”

Motero, ngakhale kuti munthu ali ndi ulamuliro pa nyama, sayenera kugwiritsa ntchito molakwika ulamuliro umenewo koma kuugwiritsa ntchito mogwirizana ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu. Zimenezi zingaphatikizepo kusalola kuti galu kapena mphaka avutike mosayenera chifukwa cha kukalambitsa, kuvulala kwambiri, kapena nthenda yoti adzafa nayo. Zikatero, ndi udindo wa Mkristu kuganiza zoti achite. Ngati aganiza kuti chingakhale chifundo kusalola kuti galu kapena mphaka avutike pamene palibe chiyembekezo choti achira, angasankhe kupha galuyo kapena mphakayo.