Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufukiza Kodi N’kofunika pa Kulambira Koona?

Kufukiza Kodi N’kofunika pa Kulambira Koona?

 Kufukiza Kodi N’kofunika pa Kulambira Koona?

“MILUNGU imakonda zonunkhira.” Ameneŵa anali mawu odziŵika kwambiri kwa Aigupto akale. Kwa iwo, kufukiza kunali mbali ya kulambira kwawo. Pokhulupirira kuti milungu inali pafupi, Aigupto anali kufukiza tsiku lililonse m’akachisi awo ndi m’maguwa ansembe a m’nyumba zawo, ndiponso ngakhale pochita malonda. Mitundu ina ya anthu inalinso ndi miyambo ngati imeneyi.

Kodi chofukiza n’chiyani? Mawu ameneŵa angatanthauze utsi kapena chinthu chimene akuchiotchacho. Chimapangidwa ndi utomoni kapena kuti mambidza onunkhira, monga libano ndi vunguti. Amazipera ndipo nthaŵi zambiri amazisakaniza ndi zinthu zina monga zonunkhiritsa, makungwa, ndi maluwa, kuti apange fungo linalake malinga ndi ntchito yake.

Anthu anali kukonda kwambiri zofukiza ndipo motero zinali zinthu zamtengo wapatali kalelo moti zinthu zimene ankasakaniza kuti apange zofukizazo zinali zinthu zofunika kwambiri pa malonda. Magulu a anthu a paulendo wa zamalonda ankatenga zinthu zimenezi kuchokera ku mayiko akutali. Mungakumbukire kuti mwana wamng’ono wa Yakobo, Yosefe, anamugulitsa kwa amalonda achiismayeli amene “anachokera ku Gileadi ndi ngamila zawo, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi libano alinkumuka kutsikira nazo ku Aigupto.” (Genesis 37:25) Anthu ankafuna kwambiri zofukiza moti maulendo a zamalonda a libano, omwe mosakayika anayambika ndi ogulitsa zofukiza, anachititsa kuti maulendo a malonda amenewa pakati pa Asia ndi Ulaya akule.

Anthu akumafukizabe pa miyambo ya zipembedzo zambiri masiku ano. Ndiponso, anthu ambiri amafukiza m’nyumba zawo pongofuna kusangalala ndi fungo lokoma la zofukizazo. Kodi Akristu ayenera kuona bwanji kufukiza? Kodi Mulungu amavomereza kuchita zimenezi polambira? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi.

“Chopatulika cha Yehova”

Kwa Aisrayeli akale, kufukiza kunali mbali yaikulu ya ntchito ya ansembe pa chihema. Buku lakuti Cyclopedia la McClintock ndi Strong limati: “Inde, zikuoneka kuti Ahebri ankaona kuti kufukiza kunali kulambira kapena kuti kunali kopatulika moti palibe paliponse pamene timaŵerenga kuti anagwiritsa ntchito zofukiza pa chifukwa china osati chimenechi.”

Yehova Mulungu anatchula zinthu zinayi zimene anafunika kumazisakaniza ndi kuzifukiza pa chihema. Anati: “Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi libano loona; miyeso yofanana; ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosanganiza mwa machitidwe a wosanganiza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika; nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m’chihema chokomanako.” (Eksodo 30:34-36) Akatswiri ena amati patapita nthaŵi arabi achiyuda anawonjezera zosakaniza zina kuti azigwiritsa ntchito pakachisi.

 Kufukiza pa chihema kunali kopatulika, ndipo ankagwiritsa ntchito pa kulambira Mulungu kokha basi. Yehova analamula kuti: “Chofukizacho uchikonze, musadzikonzere nokha china, mwa makonzedwe ake amene; muchiyese chopatulika cha Yehova. Aliyense wokonza china chotere kununkhizapo, asadzidwe kwa anthu a mtundu wake.” (Eksodo 30:37, 38) Ansembe anali kufukiza kaŵiri patsiku pa guwa la nsembe limene analikonza kuti azichitirapo zimenezi. (2 Mbiri 13:11) Ndipo pa Tsiku la Chitetezo, mkulu wa ansembe anali kufukiza m’Malo Opatulikitsa.​—Levitiko 16:12, 13.

Mulungu sanavomereze kufukiza kulikonse. Iye analanga anthu amene sanali ansembe amene modzikuza anafukiza ngati kuti anali ansembe. (Numeri 16:16-18, 35-40; 2 Mbiri 26:16-20) Kufukiza kwa mtundu wachiyuda kunamuipira Yehova pamene mtunduwo unali kukuphatikiza ndi kulambira konyenga ndipo manja awo anadzala magazi. Chinyengo chawo chinachititsa Yehova kunena kuti: “Nsembe zofukiza zindinyansa.” (Yesaya 1:13, 15) Aisrayeli anali kunyalanyaza kwambiri malangizo a mmene anayenera kulambirira Yehova moti anatseka kachisi n’kumafukiza m’maguwa ansembe ena. (2 Mbiri 28:24, 25) Patapita zaka, anafika pogwiritsa ntchito zofukiza zopatulika pa kulambira milungu yonyenga koipa kwambiri. Kuchita zimenezo kunali kupandukira Yehova.​—Ezekieli 16:2, 17, 18.

Mmene Akristu Oyambirira Anaonera Zofukiza

Pangano la Chilamulo, kuphatikizapo lamulo loti ansembe azifukiza zopatulika, linatha pamene Yesu anakhazikitsa pangano latsopano mu 33 C.E. (Akolose 2:14) Palibe paliponse pamene pamanena kuti Akristu oyambirira anali kufukiza pa zifukwa zachipembedzo. Pofotokoza zimenezi, buku lakuti Cyclopedia la McClintock ndi Strong limati: “N’zotsimikizika kuti [Akristu oyambirira] sanali kufukiza. Ndipotu, kuchita zimenezi kunali chizindikiro cha kulambira kwachikunja . . . Munthu wokhulupirira akaponya misere ingapo pa guwa la nsembe lachikunja zinali kutanthauza kulambira.”

Akristu oyambirira analinso kukana kufukiza pofuna kuvomereza kuti mfumu ya Aroma inali “mulungu,” ngakhale kuti kutero kukanachititsa kuti aphedwe. (Luka 4:8; 1 Akorinto 10:14, 20) Poona mmene kufukiza kunali kugwiritsidwa ntchito pa kulambira mafano munthaŵi imeneyo, n’zosadabwitsa kuti Akristu oyambirira sakanachita n’komwe malonda ogulitsa zofukiza.

Kufukiza Masiku Ano

Kodi anthu akugwiritsa ntchito bwanji zofukiza masiku ano? M’Matchalitchi Achikristu ambiri, amafukiza pa miyambo ndi pa mapemphero. Mabanja ambiri a anthu a ku Asia amafukiza ku akachisi kapena pa guwa la nsembe la m’nyumba zawo polemekeza milungu yawo ndi kuteteza akufa. Pa zochitika zachipembedzo, zofukiza zagwiritsidwa ntchito kununkhiritsa, kuchiritsa, kuyeretsa, ndi kuteteza.

Posachedwapa, zofukiza zayambanso kutchuka kwambiri ngakhale kwa anthu amene sali m’chipembedzo chilichonse. Ena amafukiza  akusinkhasinkha. Buku lina lolangiza limauza anthu kugwiritsa ntchito zofukiza kuti adziŵe “zinthu zodabwitsa” ndiponso kuti akhale ndi “mphamvu zapadera” zoposa zachibadwa. Pofuna kuthetsa mavuto, bukulo limauzanso anthu kuti azichita miyambo yofukiza imene imachititsa kuti azilankhulana ndi “zolengedwa zauzimu.” Kodi Akristu angachite nawo zimenezo?

Yehova amatsutsa mwamphamvu anthu amene amaphatikiza kulambira konyenga ndi kulambira koona. Mtumwi Paulo anagwira mawu ulosi wa Yesaya ndipo anagwiritsa ntchito pa Akristu, kuwalimbikitsa kusatengera zinthu zoipa za chipembedzo chonyenga. Analemba kuti: “Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati Ambuye, ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu.” (2 Akorinto 6:17; Yesaya 52:11) Akristu oona amaonetsetsa kuti akupewa chilichonse chimene chikugwirizana ndi kulambira konyenga kapena zamizimu.​—Yohane 4:24.

Popeza kuti zofukiza zimagwiritsidwa ntchito pa miyambo ya chipembedzo ndi kukhulupirira mizimu, kodi ndiye kuti kufukiza kwina kulikonse n’kolakwika? Ayi. Mwina munthu angakonde kufukiza zonunkhira kunyumba kwake pongofuna kusangalala ndi fungo lokoma. (Miyambo 27:9) Ngakhale zili choncho, posankha zoti kaya afukize, Mkristu ayenera kuganizira zinthu zina. Kodi anthu ena m’dera limene mukukhalalo sadzagwirizanitsa kufukizako ndi kulambira konyenga? Kodi m’dera lanulo, kufukiza nthaŵi zambiri amakugwirizanitsa ndi miyambo ya kukhulupirira mizimu? Kapena kodi anthu nthaŵi zambiri amagwiritsa ntchito zofukiza pa zifukwa zosakhala zachipembedzo?

Ngati munthu asankha kufukiza, ayenera kuganizira chikumbumtima chake ndiponso mmene ena angaonere. (1 Akorinto 10:29) Zimene mtumwi Paulo anauza Aroma zikugwira ntchito pankhani imeneyi. Iye analemba kuti: “Tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake. Usapasule ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Zinthu zonse zili zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa. Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako.”​—Aroma 14:19-21.

Mapemphero Amene ‘Amaikika Ngati Chofukiza’

Kufukiza kumene Aisrayeli anali kuchita kunali chizindikiro chabwino kwambiri cha mapemphero amene Mulungu amamva. Motero, wamasalmo Davide anaimbira Yehova kuti: “Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu.”​—Salmo 141:2.

Aisrayeli okhulupirika sanaone kufukiza ngati mwambo wopanda ntchito. Anasamala kwambiri kukonza zofukiza ndi kuzifukiza motsatira zimene Yehova ananena. M’malo mogwiritsa ntchito zofukiza zenizeni, Akristu masiku ano amapereka mapemphero amene amasonyeza kuyamikira ndi kulemekeza kwambiri Atate wathu wakumwamba. Mofanana ndi zofukiza zonunkhira zimene ansembe a pakachisi anali kufukiza, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Pemphero la oongoka mtima lim’kondweretsa.”​—Miyambo 15:8.

[Zithunzi patsamba 29]

Kufukiza pa chihema ndi pakachisi kunali kopatulika

[Chithunzi patsamba 30]

Kodi Akristu angachite nawo kufukiza kophatikiza ndi kusinkhasinkha?