Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chiyani Chikuchitika Pankhani Yothandiza Osoŵa?

Kodi N’chiyani Chikuchitika Pankhani Yothandiza Osoŵa?

 Kodi N’chiyani Chikuchitika Pankhani Yothandiza Osoŵa?

ZIGAŴENGA zitaukira mzinda wa New York City ndi Washington, D.C., pa September 11, 2001, anthu anathandiza kwambiri amene anakhudzidwa ndi vutoli. Mabungwe olandira zinthu zothandizira anthu analandira ndalama zochuluka kwambiri zokwana madola 2.7 biliyoni a ku United States zimene anthu anapereka kuti zithandize mabanja amene anakhudzidwa ndi vutoli. Chifukwa chomva chisoni kwambiri ndi mmene zinthu zinawonongekera, anthu padziko lonse anafuna kuthandiza.

Koma anthu ena anaŵaŵidwa mtima zedi patamveka kuti mabungwe otchuka othandiza anthu osoŵa sanali kugwiritsa ntchito bwino ndalama zimene anthu anali kupereka. Anthu anakwiya zedi atamva kuti bungwe lina lalikulu lothandiza anthu osoŵa linakonza zogwiritsa ntchito pa zinthu zina pafupifupi theka la ndalama zokwana madola 546 miliyoni zimene anthu anapereka ku bungweli kuti zithandizire anthu. Ngakhale kuti kenako bungweli linasintha maganizo ameneŵa ndipo linapepesa, mtolankhani wina anati: “Ofufuza akuona kuti zimenezi achita m’mbuyo mwa alendo ndipo n’kovuta kuti anthu ayambirenso kulikhulupirira” bungweli monga anali kuchitira zigaŵenga zisanaukire. Bwanji inuyo? Kodi mwayamba kuwakayikira mabungwe ameneŵa posachedwapa?

N’kothandiza Kapena N’kuwononga?

Anthu ambiri amaona kuti kupereka zinthu ku mabungwe othandiza anthu osoŵa n’kwabwino zedi. Komabe, si onse amene amaona choncho. Zaka 200 zapitazo, Samuel Johnson, yemwe anali wolemba nkhani wachingelezi, analemba kuti: “Munthu umatsimikizadi kuti ukuchita zinthu zabwino ngati upatsa ndalama anthu amene akugwira ntchito, monga malipiro a ntchito imene agwira, kusiyana ndi kungopereka ndalama kwaulere.” Anthu ena masiku ano ali ndi maganizo ofanana ndi ameneŵa, ndipo nkhani za mabungwe othandiza anthu osoŵa amene sakugwiritsa ntchito bwino ndalama zikupangitsa anthu kusakhulupirira mabungwe ameneŵa. Taonani zitsanzo ziŵiri zaposachedwapa.

Mkulu wa bungwe linalake lachipembedzo lothandiza anthu osoŵa ku San Francisco anachotsedwa ntchito, zitamveka kuti bungwelo n’limene linalipira ndalama za opaleshoni yake yoti azioneka bwino ndiponso linalipira ndalama zonse za chakudya chimene ankadya ku lesitiranti kumene anali kuwononga madola 500 mlungu uliwonse kwa zaka ziŵiri. Ku Britain, okonza zochitika zapadera zothandiza anthu osoŵa pa wailesi ya kanema anakhumudwa atazindikira kuti pa ndalama zokwana mapaundi 6.5 miliyoni (madola pafupifupi 10 miliyoni, a ku America) amene anapereka kuti amangitsire nyumba za ana amasiye ku Romania, nyumba 12 zokha zosaoneka bwino n’zimene zinamangidwa, ndipo madola a nkhaninkhani  sanaoneke kumene anapita. Nkhani zoipa ngati zimenezi zapangitsa anthu ena amene amapereka chithandizo kukhala osamala kwambiri pankhani ya ndalama zimene amapereka ndiponso kumene akupereka.

Kupereka Kapena Kusapereka

Komabe, zingakhale zomvetsa chisoni kuti zochita za anthu ena kapena mabungwe ena zitilepheretse kusonyeza kuganizira ndi kuchitira chifundo anthu ena. Baibulo limati: “Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi [“kusamalira,” NW] ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo.” (Yakobo 1:27) Inde, kuthandiza anthu osauka ndi ovutika ndi mbali yofunika pa Chikristu.

Komabe, mungafunse kuti, ‘Kodi ndizithandizabe anthu osoŵa kudzera m’mabungwe, kapena ndizingothandiza anthuwo mwa kuwapatsa mphatso aliyense payekha?’ Kodi Mulungu amafuna kuti tizipatsa mwa mtundu wanji? Nkhani yotsatirayi iyankha mafunso ameneŵa.