Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimwemwe Chosayerekezeka!

Chimwemwe Chosayerekezeka!

 Mbiri ya Moyo Wanga

Chimwemwe Chosayerekezeka!

YOSIMBIDWA NDI REGINALD WALLWORK

“Palibe chilichonse m’dzikoli chimene chingafanane ndi chimwemwe chimene tinali nacho mu utumiki waumishonale wanthaŵi zonse wotumikira Yehova!” Ndinapeza kapepala ka mawu ameneŵa pa mabuku a mkazi wanga atangomwalira kumene mu May 1994.

NDIKAMAGANIZIRA mawu a Irene ameneŵa, ndimakumbukira zaka 37 zosangalatsa zimene tinakhala amishonale ku Peru. Tinali ndi ubwenzi wamtengo wapatali wachikristu kuyambira pamene tinakwatirana mu December 1942​—ndipo pamenepa ndiye pabwino kuyambira nkhani yanga.

Irene anakulira m’banja la Mboni za Yehova ku Liverpool, m’dziko la England. Iye anali mmodzi mwa ana aakazi atatu, ndipo bambo ake anamwalira panthaŵi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Ndiyeno mayi ake anakwatiwa ndi Winton Fraser, n’kubereka mwana wamwamuna dzina lake, Sidney. Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse isanayambe, banja lawo linasamukira ku Bangor, m’dziko la North Wales, kumene Irene anabatizidwa mu 1939. Sidney anabatizidwa mu 1938, chotero iye ndi Irene anatumikira pamodzi monga apainiya​—alaliki a nthaŵi zonse​—m’mphepete mwa gombe la kumpoto kwa dziko la Wales, kuchokera ku Bangor mpaka ku Caernarvon, kudzanso pa chilumba cha Anglesey.

Panthaŵi imeneyo, ndinali mu Mpingo wa Runcorn, womwe unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 20 kumwera cha kummawa kwa Liverpool, ndinali kutumikira monga amene masiku ano amatchedwa woyang’anira wotsogolera. Pamsonkhano wadera, Irene anandifikira kundipempha ngati ndingampatse gawo loti azilalikiramo, popeza anali kudzakacheza kwa mchemwali wake Vera, amene anali  wokwatiwa ndipo ankakhala ku Runcorn. Ine ndi Irene tinagwirizana zedi m’milungu iŵiri imene anali nafe, ndiyeno atachoka ndinapita maulendo angapo ku Bangor kukamuona. Mapeto ena a sabata ndinasangalala kwambiri Irene atavomera zomanga nane banja.

Nditabwerera kunyumba Lamlungu, nthaŵi yomweyo ndinayamba kukonzekera za ukwati wathu, koma Lachiŵiri mlungu umenewo ndinalandira telegalamu. Inali ndi mawu akuti: “Pepani kuti telegalamuyi ikukhumudwitsani. Ndikufuna kusintha tsiku laukwati wathu. Mulandira posachedwapa kalata yofotokoza chifukwa chake.” Ndinadabwa zedi. Kodi vuto linali chiyani?

Kalata imene Irene analemba inafika tsiku lotsatira. Anandiuza kuti akupita ku Horsforth mu mzinda wa Yorkshire kukachita upainiya ndi Hilda Padgett. * Anafotokoza kuti chaka chapitacho anavomereza kuti angakatumikire kumene kulibe anthu olalikira ambiri, ngati atapemphedwa kutero. Analemba kuti: “Kumeneku kunali ngati kumulonjeza Yehova, ndipo ndikuona kuti popeza ndinalonjeza ndisanadziŵane ndi inu, ndiyenera kukwaniritsa zimenezo.” Ngakhale kuti ndinakhumudwa, ndinasirira kwambiri kukhulupirika kwake ndipo ndinamutumizira telegalamu poyankha kalata yake, ndinati: “Pita. Ndikudikira.”

Ndili ku Yorkshire, Irene anauzidwa kukhala m’ndende miyezi itatu chifukwa chikumbumtima chake sichinamulole kuchita nawo zinthu zina zothandizira nkhondo. Koma patatha chaka chimodzi ndi theka, tinakwatirana mu December 1942.

Zaka Zanga Zoyambirira

Mu 1919 mayi anga anagula mabuku angapo akuti Studies in the Scriptures. * Ngakhale kuti mayi anali asanaŵerengepo buku lina lililonse, monga mmene bambo ananenera atawaona akuŵerenga, mayi anatsimikiza mtima kuŵerenga mabuku ameneŵa mosamalitsa pamodzi ndi Baibulo. Anachitadi zimenezo ndipo anabatizidwa mu 1920.

Bambo anga sanali ovuta ndipo sanaletse mayi anga kuchita zofuna zawo, ndipo zimenezi zinaphatikizapo kulera ana awo anayi m’choonadi​—ine, azichemwali anga aŵiri, Gwen ndi Ivy; ndiponso mchimwene wanga, Alec. Stanley Rogers pamodzi ndi Mboni zina zokhulupirika ku Liverpool zinkapita kukakamba nkhani za Baibulo ku Runcorn, kumene patapita nthaŵi pang’ono kunakhazikitsidwa mpingo watsopano. Banja lathu linali kuchita bwino mwauzimu pamodzi ndi mpingo.

Gwen anali kuphunzira kuti akhale wa mpingo wa Tchalitchi cha ku England koma anasiya atangoyamba kuphunzira Baibulo ndi mayi. Mbusa wa tchalitchichi atabwera kudzaona chifukwa chake sanali kupitanso kukaphunzira, Gwen anam’funsa mafunso ambiri amene analephera kuyankha. Gwen anafunsa tanthauzo la Pemphero la Ambuye, mapeto ake mbusayo atalephera, Gwen anam’fotokozera. Anamaliza pogwira mawu a pa 1 Akorinto 10:21, pogogomezera mfundo yakuti sangapitirize ‘kudya pa magome aŵiri.’ Mbusayo pochoka kunyumba kwathuko, ananena kuti akamupempherera Gwen ndipo adzabweranso kudzayankha mafunso ake, koma sanabwerenso. Gwen atabatizidwa, anayamba nthaŵi yomweyo utumiki wa nthaŵi zonse.

Zinali zochititsa chidwi kwambiri kuona momwe anthu anali kukondera achichepere mu mpingo wathu. Ndimakumbukira ndikumvetsera nkhani imene mkulu wa mpingo wina anakamba mu mpingo mwathu ndili ndi zaka 7. Atatha nkhaniyo anabwera kudzandilankhula. Ndinamuuza kuti ndakhala ndikuŵerenga nkhani ya Abrahamu ndi zimene anachita pofuna kupereka nsembe mwana wake, Isake. Iye anati: “Pita pa pulatifomu, undifotokozere nkhani yonse.” Ndinasangalala zedi kuima pamenepo ndi kukamba “nkhani ya onse” yoyamba kukamba pa moyo wanga.

Ndinabatizidwa ndili ndi zaka 15 mu 1931, chaka chimene anamwalira mayi anga, ndipo ndinasiya sukulu kuti ndiphunzire ntchito ya zamagetsi kwa munthu amene ndinali kumugwirira ntchito. Mu 1936 nkhani za m’Baibulo anali kuziulutsa pa galamafoni, ndipo mlongo wina wachikulire anandilimbikitsa ine ndi mchimwene wanga kugwira nawo ntchito imeneyi. Choncho ine ndi Alec tinapita ku Liverpool kukagula njinga n’kumangilirapo ngolo  kuti tizinyamuliramo galamafoni. Makaniko anamangilira sipika kumbuyo kwa ngoloyo pa chipangizo china cha mamita aŵiri. Iye anatiuza kuti sanapangepo chinthu changati chimenechi, koma chinali kugwira ntchito bwino. Tinamaliza gawo lathu mwachangu. Timayamikira mlongo wachikulire amene anatilimbikitsa uja ndiponso mwayi wotumikira umene tinapatsidwa.

Nkhondo Yachiŵiri ya Padziko Lonse Inali Nthaŵi ya Chiyeso

Pamene zizindikiro zakuti kukubwera nkhondo zinali kuchuluka, ine ndi Stanley Rogers tinatanganidwa ndi kulengeza nkhani ya onse yakuti “Dziŵani Zoona,” yomwe inali yoti idzakambidwa ku London’s Royal Albert Hall pa September 11, 1938. Kenako ndinathandiza kugaŵira kabuku kamene munali nkhani imeneyi, ndiponso kabuku kakuti Fascism or Freedom, timene tinafalitsidwa mu 1939. Timabuku timeneti tinavumbula mooneka bwino zolinga za ulamuliro wankhanza wa Hitler wa ku Germany. Panthaŵi imeneyi, ndinali kudziŵika kwambiri ku Runcorn chifukwa cha utumiki wanga ndipo ndinali kulemekezedwa chifukwa cha zimenezi. Ndithudi, popeza ndinali kutsogolera ntchito ya Mulungu, zinandithandiza kuti zindiyendere bwino nthaŵi ina yake.

Kampani imene ndinali kugwira ntchito inapemphedwa kukamangirira mawaya a magetsi ku fakitale yatsopano imene inali kunja kwa tauni. Nditamva kuti fakitaleyo izipanga zida za nkhondo, ndinawauza kuti sindingagwire nawo ntchitoyo. Ngakhale kuti bwana anga sanasangalale, amene anali kundiyang’anira anandiikira kumbuyo, ndipo ndinapatsidwa ntchito ina. Patapita nthaŵi ndinamva kuti azakhali a munthu ameneyu analinso mmodzi wa Mboni za Yehova.

Mnzanga amene ndinali kugwira naye ntchito anandilimbikitsa pondiuza kuti: “N’zimene timayembekezera kwa iwe, Reg, popeza kuti wakhala ukugwira ntchito yokhudza Baibulo kwa zaka zambiri.” Komabe, ndinayenera kukhala maso, popeza anzanga ogwira nawo ntchito ambiri ankafuna kundiputira mavuto.

Mu June 1940 khothi la ku Liverpool linalola kundilemba kuti ndisamaloŵe usilikali pachifukwa cha chipembedzo malinga ngati ndipitirizabe kugwira ntchito ya za magetsi imene ndimagwirayo. N’zoona kuti zimenezi, zinandithandiza kuchita utumiki wanga wachikristu.

Mu Utumiki wa Nthaŵi Zonse

Nkhondo ili pafupi kutha, ndinaganiza zosiya ntchito kuti ndizichita utumiki wa nthaŵi zonse ndi Irene. Mu 1946, ndinapanga kalavani ya mamita asanu kuti ikhale nyumba yathu, ndipo chaka cha 1947, tinapemphedwa kupita ku Alveston, mudzi wa ku Gloucestershire. Kenako, tinachita upainiya m’tauni yakale ya Cirencester ndiponso mu mzinda wa Bath. Mu 1951, ndinapemphedwa kumayendera mipingo ya kumwera kwa dziko la Wales monga woyang’anira woyendayenda, koma pasanathe zaka  ziŵiri, tinapita ku Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo kukaphunzira za umishonale.

Kalasi ya 21 ya sukuluyi inachitikira ku South Lansing, cha kumpoto kwa New York, ndipo tinamaliza maphunziro athu mu 1953 pa msonkhano wakuti Anthu a M’dziko Latsopano umene unachitikira mu mzinda wa New York City. Ine ndi Irene sitinadziŵe kumene atitumize mpaka tsiku lomaliza maphunziro athu. Si mmene tinasangalalira titamva kuti tikatumikira ku Peru. Tinasangalala chifukwa chiyani? Chifukwa Sidney Fraser, mchimwene wake wa Irene wa bambo ena ndi mkazi wake, Margaret, anali akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Lima ndipo anali atakhalapo koposa chaka chimodzi kuyambira pamene anamaliza maphunziro awo m’kalasi la 19 la sukulu ya Gileadi.

Tikudikira zikalata zoyendera, tinali kugwira ntchito pa Beteli ku Brooklyn, koma patapita nthaŵi pang’ono tinanyamuka ulendo ku Lima. Gawo lathu loyamba mwa magawo khumi amene tinakachitirako umishonale linali ku Callao, doko lalikulu la ku Peru, cha kumadzulo kwa Lima. Ngakhale kuti tinali titaphunzira mawu ochepa osavuta kwenikweni a chinenero cha Chisipanya, panthaŵiyi ine ndi Irene sitinkatha kukambirana bwinobwino ndi anthu m’Chisipanya. Kodi tikanagwira bwanji ntchito yathu?

Mavuto ndi Madalitso Amene Tinapeza Polalikira

Ku Gileadi tinauzidwa kuti mayi saphunzitsa mwana wake chinenero. M’malo mwake, mwanayo amaphunzira mayi ake akamalankhula naye. Chotero malangizo amene anatipatsa ndi akuti: “Kayambeni kulalikira mukakangofika, kaphunzireni chinenero kwa anthu a kumeneko. Akakuthandizani.” Ndikuyesetsa kuphunzira chinenero chatsopanochi, tangoganizirani momwe ndinamvera atandiika kukhala woyang’anira wotsogolera mu Mpingo wa Callao, ndisanakhaleko milungu yoposa iŵiri! Ndinapita kukamuona Sidney Fraser, koma zimene anandilangiza zinali ngati zimene anatiuza ku Gileadi zoti tizicheza ndi anthu a mumpingo ndi anthu am’gawo lathu. Ndinatsimikiza mtima kutsatira langizo limeneli.

Loŵeruka lina m’maŵa, ndinapeza kalipentala pamalo ake antchito. Iye anati: “Ndizigwirabe ntchito yanga, koma inu khalani pansi mundiuze zimene mwabwerera.” Ndinamuuza kuti ndichita zimenezo koma akavomereza chinthu chimodzi ichi: “Ndikalakwitsa muzindiwongolera. Sindikhumudwa ayi.” Anaseka koma anagwirizana nazo zimene ndinamupemphazo. Ndinali kumuyendera kaŵiri pamlungu ndipo ndinaona kuti inali njira yothandiza kuzoloŵera chinenero chatsopano, monga mmene anandiuzira.

Zinangochitika kuti ku mzinda wa Ica, ku gawo lathu lachiŵiri la umishonale, ndinakumana ndi kalipentala wina ndipo ndinamufotokozera zimene ndinali kuchita ku Callao. Anavomera kuti andithandizanso, choncho ndinapitiriza kuchidziŵa Chisipanya, ngakhale kuti kunanditengera zaka zitatu kuti ndichidziŵitsitse bwino. Mwamuna ameneyu nthaŵi zonse anali wotanganidwa kwambiri, komabe ndinkatha kuchita naye phunziro la Baibulo mwa kuŵerenga Malemba ndi kumufotokozera tanthauzo lake. Mlungu wina nditapita kukamuona, bwana ake anandiuza kuti anasiya ntchito anakapeza ina ku Lima. Patapita nthaŵi ine ndi Irene titapita ku Lima ku msonkhano, ndinakumana nayenso mwamuna uja. Ndinasangalala kumva kuti anakapeza Mboni kumeneko kuti apitirize kuphunzira, ndiponso kuti iye ndi a m’banja lake, onse anali atumiki a Yehova odzipatulira.

Mu mpingo wina, tinapeza kuti banja lina lachinyamata silinali lokwatirana mwalamulo, koma linali lobatizidwa. Pamene tinali kukambirana nawo mfundo za m’Malemba, anaganiza zolembetsa ukwati wawo mwalamulo, kuti ayenerere kukhala Mboni zobatizidwa. Choncho ndinakonza zopita nawo ku maofesi a boma kukalembetsa ukwati wawo. Koma panapezeka vuto chifukwa anali ndi ana anayi amene anali asanawalembetse m’kaundula monga mwa lamulo la boma. Sitinali kudziŵa zimene woyang’anira mzindawo akachite. Koma titafika, woyang’anira mzindawo anati: “Chifukwa chakuti anthu abwino ameneŵa, anzanu a Mboni za Yehova, akonza zoti mukwatirane mwalamulo, sindikupatsani samani ya mwana aliyense, ndiwalemba m’kaundula kwaulere.” Tinasangalala kwambiri, popeza banjali linali losauka ndipo ndalama iliyonse imene akanati awalipiritse ikanawavuta kupereka.

Kenako Albert D. Schroeder wa ku likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn anatiyendera ndipo ananena kuti n’kofunika kukhala ndi nyumba yatsopano ya amishonale ku dera lina la Lima. Choncho ine ndi Irene ndi alongo aŵiri, Frances ndi Elizabeth Good a ku United States, ndi banja lina la ku Canada, tinasamukira ku chigawo cha San Borja. Zisanathe  zaka ziŵiri kapena zitatu, tinakhazikitsa mpingo wina wochita bwino.

Tikutumikira ku Huancayo, tauni yopezeka pa mtunda wa mamita 3,000 ku central highlands, tinali kusonkhana ndi mpingo wa kumeneko wa Mboni zokwana 80. Kumeneko, ndinathandiza kumanga Nyumba ya Ufumu yachiŵiri m’dzikolo. Anandiika kukhala woimira Mboni za Yehova pankhani ya zamalamulo, popeza tinkafunika kupita ku khoti katatu kukatsimikiza mwalamulo kuti malo amene tinagula ndi athu. Zimenezi pamodzi ndi kupanga ophunzira mwakhama kwa amishonale ambiri okhulupirika a m’zaka zoyambirira zimenezo, zinayala maziko olimba a kuchuluka kwa anthu kumene timakuona masiku ano ku Peru​—kuchoka pa Mboni 283 mu 1953 mpaka kupitirira 83,000 masiku ano.

Kuchoka Kosasangalatsa

Tinasangalala kucheza ndi amishonale anzathu m’nyumba zonse za amishonale zimene tinakhala, kumene nthaŵi zambiri ndinali ndi mwayi wotumikira monga woyang’anira panyumba za amishonale. Lolemba lililonse m’maŵa, tinkasonkhana kukambirana za ntchito ya mlungu umenewo ndi kugawana ntchito za panyumbapo. Tonse tinkadziŵa kuti chinthu chofunika kwambiri ndi kulalikira, chotero tonse tinkagwira ntchito mogwirizana. Ndimasangalala kuti sitinakhalepo ndi mikangano ikuluikulu m’nyumba za amishonale zonse zimene ndinakhala.

Gawo lathu lomaliza la umishonale linali ku Breña, mudzi wina wa ku Lima. Mpingo wake wabwino kwambiri wa Mboni zokwana 70 unakula mofulumira kupitirira pa anthu 100, chotero anakhazikitsa mpingo wina ku Palominia. Nthaŵiyi ndi imene Irene anayamba kudwala. Poyamba ndinkaona kuti nthaŵi zina sankatha kukumbukira zimene ananena, ndiponso ankavutika kukumbukira njira ya ku nyumba. Ngakhale kuti analandira chithandizo chabwino cha mankhwala, vutolo linapitiriza kukula.

Zachisoni kuti, mu 1990, ndinakonza zobwerera ku England kumene mchemwali wanga Ivy anatilandira ndi manja aŵiri kunyumba kwake. Patapita zaka zinayi, Irene anamwalira ali ndi zaka 81. Ndikupitirizabe utumiki wa nthaŵi zonse, kutumikira monga mkulu mu umodzi mwa mipingo itatu ya mtawuni ya kwathu. Nthaŵi zina, ndimapita ku Manchester kukalimbikitsa gulu la kumeneko la Chisipanya.

Posachedwapa ndinali ndi chokumana nacho chabwino zedi chimene chinayamba zaka zambiri zapitazo pamene ndinali kuulutsa maulaliki a mphindi zisanu kwa eninyumba pa galamafoni yanga. Ndimakumbukira bwino mtsikana wina wamng’ono wa pasukulu amene anaima pakhomo, kumbuyo kwa mayi ake n’kumamvetsera uthengawo.

M’kupita kwa nthaŵi mtsikanayu anasamukira ku Canada, ndipo mnzake amene akukhalabe ku Runcorn, amene tsopano ndi Mboni anali kulemberana naye makalata. Mtsikana ameneyo posachedwapa analemba kuti Mboni ziŵiri zinamuyendera ndipo zinagwiritsa ntchito mawu amene mosayembekezera anamukumbutsa zimene anamva pauthenga wa pa galamafoni wa mphindi zisanu uja. Pozindikira kuti ndi choonadi, tsopano ndi mtumiki wa Yehova wodzipatulira ndipo anapempha kuti amuthokozere kwa mnyamata amene anayendera mayi ake zaka zoposa 60 zapitazo. Zoonadi sitidziŵa mmene mbewu za choonadi zimamerera mizu ndiponso zimakulira.​—Mlaliki 11:6.

Inde, ndimayang’ana m’mbuyo mosangalala pamoyo wanga umene ndathera mu utumiki wamtengo wapatali wotumikira Yehova. Kuyambira mu 1931 pamene ndinadzipatulira, sindinaphonyepo msonkhano waukulu wa anthu a Yehova. Ngakhale kuti ine ndi Irene sitinabereke ana, ndimasangalala kukhala ndi ana oposa 150 auzimu, amene akutumikira Atate wathu wakumwamba, Yehova. Monga momwe ananenera mkazi wanga wokondedwa, mwayi wathu wotumikira wakhaladi wa chimwemwe chosayerekezeka.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Mbiri ya moyo wa Hilda Padgett ili mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1995, masamba 19-24 ndipo ili ndi mutu wakuti: “Kutsatira Mapazi a Makolo Anga.”

^ ndime 12 Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 24]

Mayi anga, kumayambiriro a chaka cha 1900

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Kumanzere: Hilda Padgett, ine, Irene, ndi Joyce Rowley ku Leeds, m’dziko la England, mu 1940

[Chithunzi patsamba 25]

Pamwamba: Ine ndi Irene kutsogolo kwa kalavani yathu

[Chithunzi patsamba 27]

Kulengeza nkhani ya onse ku Cardiff, m’dziko la Wales, mu 1952