Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Yochititsa Chidwi

Nkhani Yochititsa Chidwi

Nkhani Yochititsa Chidwi

MUNTHU wofufuza malo osiyanasiyana wotchedwa Richard E. Byrd anayenda maulendo asanu opita ku Antarctica pakati pa 1928 ndi 1956. Chifukwa chakuti anali ndi buku limene ankalembamo zinthu zochitika tsiku ndi tsiku pamoyo wake komanso anali ndi mabuku amene ankalembamo nkhani yofotokoza zochitika pa ulendo wawo wonse molondola, iyeyu ndi anthu amene anali nawo anatha kudziŵa kayendedwe ka mphepo, kupanga mamapu, komanso kudziŵa zinthu zambiri zokhudza kontinenti ya Antarctica.

Maulendo a Byrd ameneŵa akusonyeza ubwino wolemba nkhani yofotokoza zochitika pa ulendo. Mu nkhani yotereyi, amalembamo tsatanetsatane yense wa ulendo wa sitima kapena ndege. Nkhani imeneyi akhoza kudzaiŵerenganso kuti adziŵe zinthu zimene zinachitika komanso zinthu zina zimene zingadzathandize anthu pa maulendo awo a m’tsogolo.

M’Malemba muli nkhani yochititsa chidwi ya Chigumula chimene chinachitika mu nthaŵi ya Nowa. Chigumula cha padziko lonse chimenecho chinatha nthaŵi yopitirira chaka chimodzi. Pokonzekera Chigumulacho, Nowa, mkazi wake, ndi ana awo aamuna atatu pamodzi ndi akazi awo anatha zaka 50 kapena 60 akumanga chingalawa, chimene chinali chombo chachikulu pafupifupi makyubiki mita 40,000. Kodi ntchito ya chingalawachi inali yotani? Inali yopulumutsa anthu ena ndi nyama ku Chigumulacho.​—Genesis 7:1-3.

Choncho, m’buku la m’Baibulo la Genesis muli nkhani ya Nowa yofotokoza zimene zinachitika kuyambira pachiyambi pa Chigumula mpaka pamene iye ndi banja lake anatuluka m’chingalawa. Kodi mu nkhani imeneyi muli chilichonse cha tanthauzo kwa ife lerolino?