Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Ena Anapezera Mayankho

Mmene Ena Anapezera Mayankho

 Mmene Ena Anapezera Mayankho

ANTHU ambirimbiri amapemphera. Ena amakhulupirira kuti mapemphero awo amayankhidwa. Ena amakayikira ngati mapemphero awo amamvedwa n’komwe. Ndiye palinso ena amene amafunafuna mayankho koma sanaganizepo zom’pempha Mulungu.

Baibulo limanena kuti Mulungu woona ndi “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Mukamapemphera, kodi mumaonetsetsa kuti mapemphero anu akupita kwa Mulungu woona? Kodi mapemphero anu ndi oti iye angawayankhe?

Kwa anthu ambiri padziko lonse, yankho la mafunso ameneŵa n’loti inde. Kodi anapeza bwanji mayankho? Kodi anaphunzira chiyani?

Kodi Mulungu Ndani?

Mphunzitsi wina ku Portugal amene anaphunzitsidwa ndi avirigo ndi ansembe, anali kutsatira chipembedzo chake ndi mtima wonse. Mpingowo utasintha ndi kuleka kuchita zinthu zina zimene iye anaphunzitsidwa kuti zinali zofunika kwambiri, zinamusokoneza maganizo. Atapita ku mayiko a ku Asia, anakaona kalambiridwe ka kumeneko, ndipo anayamba kudzifunsa ngati pali Mulungu woona mmodzi yekha. Kodi anayenera kumalambira motani? Atafunsa kwa wansembe wake zinthu za m’Baibulo, mafunso akewo sanasamalidwe, ndipo anakhumudwa kwambiri.

Mpingo wa Akatolika unafalitsa kabuku kena mumzinda umene mphunzitsiyu anali kukhala kochenjeza akatolika kuti asalankhulane ndi Mboni za Yehova. Koma iye mafunso aja anali nawobe. Tsiku lina Mboni zitafika pa nyumba pake, anamvetsera ndipo anachita chidwi ndi zimene anamva. Imeneyi inali nthaŵi yake yoyamba kulankhula ndi Mboni.

Pofuna kupeza mayankho a mafunso ambiri amene anali nawo, mkaziyu anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Mlungu uliwonse ankakhala ndi mafunso ambiri oti awafunse a Mboniwo. Ankafuna kudziŵa dzina la Mulungu, ngati pali Mulungu m’modzi yekha woona, ngati amavomereza kugwiritsa ntchito mafano polambira, ndi zinanso zambiri. Anaona kuti zonse zimene anali kumuyankha zinali zochokera m’Baibulo, osati maganizo awo, motero anadabwa kwambiri ndipo anasangalala ndi zimene anali kuphunzirazo. Pang’ono ndi pang’ono, mafunso ake ambiri anayankhidwa. Masiku ano iye akulambira Yehova mumzimu  ndi mu choonadi, monga mmene Yesu Kristu ananenera kuti “olambira oona” adzatero.​—Yohane 4:23.

Ku Sri Lanka, anthu a m’banja lina anali kuŵerenga Baibulo pamodzi nthaŵi zonse, koma sanali kupeza mayankho a mafunso ambiri amene anali ofunika kwa iwo. Ngakhale kuti ankafuna thandizo, wansembe wawo sanathe kuwathandiza. Komabe, Mboni za Yehova zinafika panyumba pawo ndi kuwasiyira buku labwino kwambiri lothandiza kuphunzira Baibulo. Kenako, Mboni za Yehova zitayankha mogwira mtima mafunso awo okhudza Baibulo, iwo anavomera kuphunzira Baibulo. Zimene anthuwa anaphunzira zinawachititsa chidwi kwambiri.

Komabe, zimene mayi wa m’banjalo anaphunzira kutchalitchi ali mwana zinamulepheretsa kuona kuti Atate wa Yesu Kristu ndiye “Mulungu woona yekha,” monga mmene mwiniwakeyo, Yesu, ananenera. (Yohane 17:1, 3) Anaphunzira kuti Yesu ndi wofanana ndi Atate ndipo kuti “chinsinsi” chimenechi n’chosati n’kuchikayikira. Ndiyeno anapemphera kwa Yehova ndi mtima wonse ndiponso mosonyeza kuti akufuna thandizo pogwiritsa ntchito dzina Lake, ndipo anamupempha kuti amusonyeze kuti Yesu ndi ndani. Ndiyeno anapendanso mosamala malemba okhudza nkhaniyi. (Yohane 14:28; 17:21; 1 Akorinto 8:5, 6) Tsopano anaona ngati mamba agwa kuchoka m’maso mwake pamene anaona bwinobwino kuti Yehova, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi ndiponso Atate wa Yesu Kristu, ndiye Mulungu woona.​—Yesaya 42:8; Yeremiya 10:10-12.

N’chifukwa Chiyani Anthu Tikuvutika?

Yobu anavutika kosaneneka. Ana ake onse anaphedwa ndi mphepo yaikulu, ndipo iye analoŵa mu umphaŵi. Anadwalanso nthenda yopweteka kwambiri ndiponso anavutika ndi zimene anzake onyenga anali kunena. Ali ndi mavuto onseŵa, Yobu analankhula asanaganize bwino. (Yobu 6:3) Komabe Mulungu anaganizira zimene zinamuchititsa kutero. (Yobu 35:15) Anadziŵa zimene zinali mumtima mwa Yobu ndipo anam’patsa malangizo amene iye anafunikira. Yehova amachitiranso anthu zimenezi masiku ano.

Ku Mozambique, Castro anali ndi zaka khumi zokha pamene mayi ake anamwalira. Anali ndi chisoni chachikulu. Anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani amayi amwalira n’kutisiya ife?” Ngakhale kuti analeredwa ndi makolo oopa Mulungu, iye tsopano mutu wake unaima. Kodi n’chiyani chikanatonthoza maganizo ndi mtima wake? Iye anapeza chitonthozo poŵerenga Baibulo laling’ono la Chichewa ndi kumakambirana zimene anali kuŵerengazo ndi azichimwene ake.

Pang’onompang’ono, Castro anatha kumvetsa kuti mayi ake anamwalira chifukwa cha kupanda ungwiro kumene timabadwa nako osati chifukwa chakuti Mulungu alibe chilungamo. (Aroma 5:12; 6:23) Lonjezo la m’Baibulo loti anthu adzauka linamutonthoza kwambiri chifukwa linamuchititsa kukhulupirira kuti adzawaonanso mayi ake. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) N’zomvetsa chisoni kuti patangotha zaka zinayi mayi ake atamwalira, bambo ake anamwaliranso. Komano panthaŵiyi, Castro anatha kupirira kumwalira kwa bambo akewo. Masiku ano iye amakonda Yehova, ndipo akugwiritsa ntchito moyo wake kutumikira Mulungu mokhulupirika. Anthu onse amene akumudziŵa amatha kuona chisangalalo chimene anapeza.

Anthu ambiri amene okondedwa awo anamwalira amatonthozedwa ndi choonadi cha m’Baibulo chomwecho chimene chinatonthoza Castro. Ena amene avutika kwambiri chifukwa cha zochita za anthu oipa amafunsa monga mmene anafunsira Yobu kuti: “Oipa akhaliranji ndi moyo.” (Yobu 21:7) Anthu akamvetseradi mayankho a Mulungu amene ali m’Mawu ake, amaphunzira kuti mmene Mulungu amachitira zinthu amatero n’cholinga choti anthuwo ziwayendere bwino.​—2 Petro 3:9.

Barbara amene anakulira ku United States, sanavutike ndi nkhondo. Koma pamene anali kukula n’kuti mayiko ambiri akumenyana. Nkhani za anthu ovutika ndi nkhondo zinkasindikizidwa tsiku lililonse m’manyuzipepala. Ali pa sukulu, anavutika maganizo kwambiri pamene anaphunzira zimene zinachitikira anthu kale zimene zinali zosaganizirika. N’chiyani chinachititsa zimenezo? Kodi Mulungu zinamukhudza zimene zinkachitikazo? Anali kukhulupirira kuti Mulungu aliko, koma sanathe kumumvetsa bwinobwino.

Komabe, maganizo a Barbara pankhani ya moyo anasintha pang’onopang’ono atayamba  kucheza ndi a Mboni za Yehova. Anawamvetsera ndipo anayamba kuphunzira nawo Baibulo. Anasonkhana nawo pa Nyumba ya Ufumu ndipo anapita nawonso ku msonkhano wawo waukulu. Ndiponso, anaona kuti akafunsa Mboni zosiyanasiyana, sizinali kumuyankha mosiyana. M’malo mwake, mayankho a Mbonizo anali ofanana chifukwa maganizo awo anali ochokera m’Baibulo.

Mbonizo zinapereka umboni wa m’Baibulo wakuti dziko likutsogoleredwa ndi Satana Mdyerekezi, wolamulira wake, ndiponso kuti limasonyeza mtima wa Satanayo. (Yohane 14:30; 2 Akorinto 4:4; Aefeso 2:1-3; 1 Yohane 5:19) Izo zinafotokoza kuti zochitika zimene zinam’vutitsa maganizo Barbara zinaloseredwa kale m’Baibulo. (Danieli, machaputala 2, 7, ndi 8) Mulungu analosera zimenezo chifukwa chakuti amatha kuona za m’tsogolo akafuna kutero. Zina mwa zochitikazo anachititsa ndi Mulungu. Zina anangozilola kuti zichitike. Mbonizo zinamuuza Barbara kuti Baibulo linaloseranso zinthu zabwino ndi zoipa zimene zikuchitika masiku ano ndipo linafotokoza tanthauzo lake. (Mateyu 24:3-14) Zinamuonetsa malonjezo a m’Baibulo a dziko latsopano m’mene mudzakhala chilungamo ndipo kuvutika kudzakhala kutatha.​—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.

Pang’onompang’ono, Barbara anayamba kumvetsa kuti ngakhale kuti Yehova Mulungu si amene amachititsa kuti anthu azivutika, iye samaletsa kuvutikako mwa kuumiriza anthu kuti amvere malamulo ake ngati anthuwo asankha kusamvera. (Deuteronomo 30:19, 20) Mulungu wakonza zoti tidzakhale ndi moyo kosatha mosangalala, koma akutipatsa mwayi panopo wosonyeza ngati tidzatsatira njira zake zolungama kapena ayi. (Chivumbulutso 14:6, 7) Barbara anatsimikiza mtima kuphunzira zimene Mulungu amafuna ndi kuzitsatira. Ndiponso anaona kuti Mboni za Yehova zinali ndi chikondi chimene Yesu ananena kuti chidzadziŵikitsa otsatira ake oona.​—Yohane 13:34, 35.

Inunso mungapindule ndi zimene zinathandiza Barbara.

Moyo Umene Uli ndi Cholinga

Ngakhale anthu amene amaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino, angafunefune mayankho a mafunso amene amawaimitsa mutu. Mwachitsanzo, Matthew, mnyamata wina wa ku Britain anali kufuna kwambiri kupeza Mulungu woona ndiponso cholinga cha moyo. Bambo ake anamwalira pamene iye anali ndi zaka 17. Ndiyeno, Matthew anamaliza maphunziro ku yunivesite n’kupeza digiri ya zoimbaimba. Kenako iye anayamba kuzindikira pang’onopang’ono kupanda pake kwa moyo wake wokondetsa chuma. Anachoka kunyumba kwawo n’kumakakhala ku London, ndipo kumeneko anayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kupita ku madansi, kukhulupirira nyenyezi, kukhulupirira za mizimu, ndiponso kuchita nawo za chipembedzo cha Chibuda komanso kukhulupirira nzeru zina za dziko. Zonsezi anali kuchita n’cholinga choti apeze njira yomwe angatsatire kuti asangalale ndi moyo wake. Nzeru zitamuthera, anafuula kwa Mulungu, kum’pempha kuti amuthandize kupeza choonadi.

Patapita masiku aŵiri, Matthew anakumana ndi mnzake wakale ndipo anamufotokozera mavuto ake. Mnzakeyo anali ataphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pamene anamusonyeza lemba la 2 Timoteo 3:1-5, Matthew anadabwa kuona mmene Baibulo limafotokozera molondola mmene dzikoli lilili. Ataŵerenga Ulaliki wa Paphiri, zinamukhudza mtima kwambiri. (Mateyu, machaputala 5-7) Poyamba, anakayikakayika chifukwa chakuti anaŵerenga nkhani zina zonyoza Mboni za Yehova, koma kenako anaganiza zokapezeka pa misonkhano pa Nyumba ya Ufumu imene anali nayo pafupi.

Matthew anasangalala ndi zimene anamva kumeneko ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi m’modzi mwa akulu a mpingowo. Posakhalitsa, iye anazindikira kuti zimene anali kuphunzira n’zimene anali kuzifunafuna, yankho la zimene anali atapempha kwa Mulungu. Anapindula kwambiri pamene anasiya makhalidwe osasangalatsa Yehova. Pamene anayamba kuopa Mulungu, zinamulimbikitsa kutsatira malamulo a Mulungu pa moyo wake. Matthew anaphunzira kuti moyo woterowo uli ndi cholinga chenicheni.​—Mlaliki 12:13.

Sikuti zinachita kukonzedweratu kuti Matthew kapena anthu ena amene tawatchula m’nkhani ino apeze njira imene angatsatire kuti moyo wawo ukhale wosangalatsa. M’malo mwake, iwo anaphunzira  kuti Yehova Mulungu ali ndi cholinga chabwino kwa anthu onse amene amasankha kutsatira malamulo ake mokondwa. (Machitidwe 10:34, 35) Cholinga chimenecho chikuphatikizapo moyo wosatha m’dziko limene simudzakhala nkhondo, matenda, njala, ngakhalenso imfa. (Yesaya 2:4; 25:6-8; 33:24; Yohane 3:16) Kodi zimenezi n’zimene mukufuna? Ngati ndi choncho, mungaphunzire zambiri zokhudza mmene mungapezere chinsinsi cha moyo wosangalatsa mwa kupezeka pa misonkhano imene amaphunzirako Baibulo pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Tikukupemphani kuchita zimenezi.

[Chithunzi patsamba 7]

Pempherani ndi mtima wonse kwa Mulungu, pogwiritsa ntchito dzina lake lenileni

[Chithunzi patsamba 7]

Phunzirani Baibulo ndi anthu amene amaphunzitsa zimene zilidi m’Baibulomo

[Zithunzi patsamba 7]

Pitani ku misonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Hiker: Chad Ehlers/​Index Stock Photography