Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yehova Amaona Zimene Inu Mumachita?

Kodi Yehova Amaona Zimene Inu Mumachita?

 Kodi Yehova Amaona Zimene Inu Mumachita?

KODI mungayankhe bwanji funso limenelo? Ambiri anganene kuti: ‘Ndikukhulupirira kuti Mulungu anaona zimene anthu monga Mose, Gideoni, ndi Davide anachita, koma ndikukayika ngati angaone zimene ine ndingachite. Sindikufanana ndi Mose, Gideoni, kapena Davide.’

N’zoona kuti anthu ena okhulupirika a nthaŵi za m’Baibulo anachita zinthu zapamwamba zosonyeza chikhulupiriro. Iwo ‘anagonjetsa maufumu, anatseka pakamwa mikango, anazima mphamvu ya moto, ndiponso anapulumuka lupanga lakuthwa.’ (Ahebri 11:33, 34) Komabe, ena anasonyeza chikhulupiriro chawo m’njira zazing’ono, ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu anaonanso ntchito zawo zosonyeza chikhulupiriro. Mwachitsanzo, tiyeni tione zitsanzo za m’Malemba za mbusa, mneneri, ndi mkazi wamasiye.

Mbusa Anapereka Nsembe

Kodi mumakumbukira chiyani za Abele, mwana wachiŵiri wa Adamu ndi Hava? Mungakumbukire kuti iye anafera chikhulupiriro, chinthu chimene ndi ochepa okha mwa ife amene zingatichitikire. Koma Mulungu anamuonanso Abele pa chifukwa china.

Tsiku lina, Abele anasankha mwana wa nkhosa wabwino kwambiri pa nkhosa zake ndi kum’pereka nsembe kwa Mulungu. Mphatso yakeyo ingaoneke ngati yaing’ono kwambiri masiku ano, koma Yehova anaiona ndipo anasonyeza kuti anakondwera nayo. Komatu si zokhazo. Pafupifupi zaka zikwi zinayi zimenezi zitachitika, Yehova anauzira mtumwi Paulo kulemba za nsembe imeneyo m’buku la Ahebri. Mulungu anali kukumbukirabe nsembe yaing’ono imeneyo patatha zaka zambirimbiri.​—Ahebri 6:10; 11:4.

Kodi Abele anasankha bwanji nsembe yoti apereke? Baibulo silifotokoza chilichonse pa mfundo imeneyo, koma ayenera kuti anaganizira mozama nsembe imene angapereke. Iye anali mbusa, motero sizodabwitsa kuti anapereka mwana wa nkhosa. Koma onani kuti anapereka chinthu chabwino kwambiri, “mafuta.” (Genesis 4:4) N’zothekanso kuti anasinkhasinkha zimene Yehova anauza njoka m’munda wa Edene kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15; Chivumbulutso 12:9) Ngakhale kuti sanamvetse kuti “mkaziyo” ndi “mbewu” yakeyo anali ndani, Abele ayenera kuti anazindikira kuti ‘kulalira chitende’ cha mbewu ya mkaziyo kudzaphatikizapo kukhetsa magazi. Mosakayika, iye anazindikira kuti chinthu chamoyo n’chimene chingakhale chofunika kwambiri. Mulimonse mmene zinalili, mfundo ndi yakuti nsembe imene anapereka inali yoyenereradi.

Mofanana ndi Abele, Akristu masiku ano amapereka nsembe kwa Mulungu. Iwo sapereka ana oyamba a nkhosa, m’malo mwake amapereka “nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Milomo yathu imavomereza dzina la Mulungu tikamauza ena chikhulupiriro chathu.

 Kodi mukufuna kukonza nsembe yanu kuti izikhala yabwino kwambiri? Ngati ndi choncho, ganizirani mozama zimene anthu a m’gawo lanu akufunikira. Kodi ali ndi mavuto otani? Kodi amakonda chiyani? Kodi ndi uthenga uti wa m’Baibulo umene ungawasangalatse? Nthaŵi iliyonse pamene mukulalikira, pendani zimene mwalankhula ndi anthu n’cholinga choti muwongolere ulaliki wanu kuti ukhale wogwira mtima kwambiri. Ndiponso mukamalankhula za Yehova, lankhulani ndi mtima wonse. Chititsani nsembe yanu kukhaladi ‘nsembe yoyamika.’

Mneneri Analalikira kwa Anthu Osalabadira

Tsopano ganizirani za mneneri Enoke. Ayenera kuti anali yekhayekha monga mboni ya Yehova Mulungu. Kodi mofanana ndi Enoke, ndinu nokha m’banja lanu amene mukutumikira Yehova mokhulupirika? Kodi ndinu nokha m’kalasi mwanu kapena kuntchito kwanu amene mumatsatira mfundo za m’Baibulo? Ngati ndi choncho, mwina mumakumana ndi mavuto. Anzanu, achibale anu, ana a sukulu anzanu, kapena amene mukugwira nawo ntchito angakulimbikitseni kuswa malamulo a Mulungu. Mwina anganene kuti: “Palibe adziŵe zimene wachita. Sitiulula.” Iwo angalimbikire kunena kuti n’kupusa kumavutika ndi miyezo ya makhalidwe ya m’Baibulo chifukwa Mulungu alibe nazo ntchito zimene mumachita. Poipidwa kuti simuganiza ndi kuchita zinthu monga mmene iwo amachitira, angachite zonse zimene angathe kuti akugonjetseni.

N’zoona kuti sizophweka kuthana ndi ziyeso zoterozo, koma sikuti n’zosatheka kuzigonjetsa. Taganizirani za Enoke, munthu wachisanu ndi chiŵiri kuyambira pa Adamu. (Yuda 14) Panthaŵi imene Enoke anabadwa, anthu analibiretu makhalidwe. Zolankhula zawo zinali zochititsa manyazi; khalidwe lawo linali “lonyansa kwambiri.” (Yuda 15, NW) Zimene anali kuchita zikufanana ndi zimene anthu ambiri masiku ano akuchita.

Kodi Enoke anathana nazo bwanji? Yankho la funso limenelo n’lofunika kwambiri kwa ife masiku ano. Ngakhale kuti Enoke panthaŵi imeneyo ayenera kuti anali yekha wolambira Yehova padziko lapansi, sikuti anangokhaliratu yekha. Iye anayenda ndi Mulungu.​—Genesis 5:22.

Nkhani yaikulu pa moyo wa Enoke inali kusangalatsa Mulungu. Anadziŵa kuti kuyenda ndi Mulungu kumafuna zambiri osati kungokhala woyera, wa makhalidwe abwino basi ayi. Yehova anafuna kuti Enoke azilalikira. (Yuda 14, 15) Anthuwo anafunika kuchenjezedwa kuti ntchito zawo zoipa zinaonedwa. Enoke anapitiriza kuyenda ndi Mulungu kwa zaka zoposa 300, zaka zambiri kuposa zimene wina aliyense wa ife wakhala akupirira. Anapitirizabe kuyenda ndi Mulungu mpaka pamene anamwalira.​—Genesis 5:23, 24.

Mofanana ndi Enoke, ifenso tapatsidwa ntchito yolalikira. (Mateyu 24:14) Kuwonjezera pa kulalikira nyumba ndi nyumba, timayesetsanso kuwauza uthenga wabwino achibale athu, anthu amene timagwira nawo ntchito, ndiponso ana a sukulu anzathu. Komabe nthaŵi zina tingamakayikekayike kuti tilalikire. Kodi inunso muli ndi vuto limeneli? Musataye mtima. Tsanzirani Akristu oyambirira, ndipo pempherani kwa Mulungu kuti akulimbitseni mtima. (Machitidwe 4:29) Kumbukirani kuti ngati muyendabe ndi Mulungu, simuli nokha.

Mkazi Wamasiye Anakonza Chakudya

Tangoganizani! Mkazi wamasiye yemwe sanatchulidwe dzina analandira madalitso aŵiri chifukwa chakuti anangokonza chakudya chochepa chabe! Iye sanali Mwiisrayeli, anali mlendo amene anakhalako zaka za m’ma 900 B.C.E., m’mudzi wa Zarefati. Nyengo yaitali ya chilala ndi njala ikuyandikira kumapeto, chakudya cha mkazi wamasiyeyo chinatsala pang’onong’ono kuti chithe. Anangotsala ndi ufa wodzaza dzanja limodzi ndi mafuta ongokwanira kuphikira  kamodzi chakudya chomaliza cha iye ndi mwana wake basi.

Zinthu zili chonchi, panabwera mlendo. Anali mneneri wa Mulungu, Eliya, amene anapempha kudya nawo chakudya chochepa cha mkazi wamasiyeyo. Mkaziyo anangokhala ndi chakudya chokwanira iye ndi mwana wake basi, analibiretu chakudya choti n’kupatsa mlendo. Koma Eliya anamutsimikizira ndi mawu a Yehova kuti ngati adzadya nawo chakudya chakecho, iye ndi mwana wakeyo sadzakhala ndi njala. Anafunika chikhulupiriro kuti atsimikize kuti Mulungu wa Israyeli adzamuona, munthu woti anali mkazi wamasiye wachilendo. Komabe, iye anamukhulupirira Eliya, ndipo Yehova anamudalitsa. “Mbiya ya ufa siidatha, ndi nsupa ya mafuta siinachepa, monga mwa mawu a Yehova amene ananenetsa Eliya.” Mkazi wamasiyeyo ndi mwana wake chakudya sichinawathere mpaka njala inatha.​—1 Mafumu 17:8-16.

Komabe, mkazi wamasiyeyo analandiranso dalitso lina. Patangopita nthaŵi zozizwitsazi zitachitika, mwana wake amene anali kumukonda anadwala n’kumwalira. Chisoni chitamugwira, Eliya anapempha Yehova kuti aukitse mwanayo. (1 Mafumu 17:17-24) Chimenecho chinali kudzakhala chozizwitsa chomwe chinali chisanachitikepo ndi kale lonse. Palibe paliponse pamene pamanena kuti munthu anaukitsidwapo kudzafika panthaŵi imeneyi. Kodi Yehova anasonyezanso chifundo kwa mkazi wamasiye wachilendo ameneyu? Anaterodi. Yehova anam’patsa mphamvu Eliya kuti aukitse mwanayo. Patapita nthaŵi Yesu pofotokoza za mkazi yemwe anachita mwayiyu, anati: “Munali akazi amasiye ambiri m’Israyeli . . . koma [Eliya anatumidwa] ku Sarepta [Zarefati] wa ku Sidoniya, kwa mkazi wamasiye.”​—Luka 4:25, 26.

Mmene chuma chikuyendera masiku ano sizikudalirika kwenikweni, ngakhale m’mayiko olemera. Makampani ena aakulu akuchotsa ntchito anthu awo omwe agwira ntchito mokhulupirika kwa zaka zambiri. Poopa kuti akhoza kuchotsedwa ntchito, Mkristu angaganize zokhala nthaŵi yaitali mopitirira muyeso akugwira ntchito kuti kampani yake isamuchotse. Kuchita zimenezo kungam’pangitse kuti asakhale ndi nthaŵi yokwanira yokapezeka pa misonkhano yachikristu, mu utumiki wa kumunda, kapena yosonyeza chikondi anthu a m’banja lake ndi kuwaphunzitsa mwauzimu. Komabe angamaganize kuti ayenera kuteteza ntchito yakeyo ngakhale pakhale zovuta zotani.

Mkristu amene ali m’vuto la zachuma lotereli akuyeneradi kudera nkhaŵa. Ntchito n’zosoŵa masiku ano. Ambiri a ife sikuti tikufuna kuti tilemere, koma monga analili mkazi wamasiye wa ku Zarefati uja, timangofuna kupeza zinthu zofunika pamoyo. Komabe, mtumwi Paulo akutikumbutsa kuti Mulungu anati: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” Tinganene molimba mtima kuti: “Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?” (Ahebri 13:5, 6) Paulo anakhulupirira ndi mtima wonse lonjezo limenelo kufika poika moyo wake pachiswe, ndipo Yehova anamusamalira nthaŵi zonse. Mulungu adzatichitiranso ife zimenezi ngati sitimusiya.

Tingaganize kuti sitingachite zinthu ngati zimene anachita anthu okonda zauzimu monga Mose, Gideoni, ndi Davide, koma tingatsanzire chikhulupiriro chawo. Ndipo tingakumbukire ntchito zochepa zosonyeza chikhulupiro zimene anachita Abele, Enoke, ndi mkazi wamasiye wa ku Zarefati. Yehova amaona ntchito zonse za chikhulupiriro, ngakhale zazing’ono zomwe. Mwana wasukulu woopa Mulungu akamakana kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo amene mnzake akum’patsa, wantchito yemwe ndi Mkristu akamakana anthu amene akum’funsira kuntchito kuti achite naye zachiwerewere, kapena Mboni yokalamba ikamapezeka pa misonkhano ya mpingo mokhulupirika ngakhale kuti imatopa  ndiponso thanzi silili bwino, Yehova amaona zimenezo. Ndiponso amasangalala kwambiri.​—Miyambo 27:11.

Kodi Inu Mumaona Zimene Ena Amachita?

Inde, Yehova amaona zimene timachita. Motero, monga anthu otsanzira Mulungu, tiyenera kukhala tcheru kuona zimene ena akuchita. (Aefeso 5:1) Bwanji osayang’anitsitsa mavuto amene Akristu anzanu akukumana nawo kuti apezeke pa misonkhano ya mpingo, kuchita nawo utumiki wakumunda, ngakhalenso kuchita ntchito zawo za tsiku ndi tsiku?

Ndiyetu, auzeni olambira Yehova anzanu kuti mumayamikira kwambiri zimene iwo amachita. Adzasangalala kuti munaona, ndipo kuwaganizira kwanu kungawatsimikizire kuti Yehova amaonanso.