Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”

Kodi Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”

 Kodi Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”

“Andichokera kunka kutali . . . Osati, Ali kuti Yehova?”​—YEREMIYA 2:5, 6.

1. N’chifukwa chiyani anthu amafunsa kuti, “Ali kuti Mulungu?”?

“ALI kuti Mulungu?” Anthu ambiri amafunsa funso limeneli. Ena amafunsa pongofuna kumvetsa mfundo yosavuta yokhudza Mlengi, yakuti, kodi amakhala kuti? Ena amafunsa funsoli pakachitika mavuto okhudza anthu ambiri kapena iwowo akakhala pamavuto aakulu kwambiri ndipo sakumvetsa chifukwa chake Mulungu sanachitepo kanthu. Ena safunsa n’komwe, chifukwa ngakhale mfundo yeniyeniyo yakuti Mulungu alipo saivomereza.​—Salmo 10:4.

2. Kodi ndani amene zimawayendera bwino pofunafuna Mulungu?

2 N’zoona kuti pali anthu ambiri amene amaona umboni wokwanira wakuti Mulungu alipo. (Salmo 19:1; 104:24) Ena mwa anthu ameneŵa amaona kuti kungokhala ndi chipembedzo chinachake n’kokwanira. Koma kukonda kwambiri choonadi kwachititsa anthu ena ambiri, padziko lonse, kufunafuna Mulungu woona. Khama lawo silinapite pachabe popeza Mulungu “sakhala patali ndi yense wa ife.”​—Machitidwe 17:26-28.

3. (a) Kodi Mulungu amakhala kuti? (b) Kodi funso la m’Malemba lakuti, “Ali kuti Yehova?” limatanthauza chiyani?

3 Munthu akapezadi Yehova, amazindikira kuti “Mulungu ndiye mzimu,” ndipo anthu sangamuone. (Yohane 4:24) Yesu anatcha Mulungu woona kuti ‘Atate wanga wa Kumwamba.’ Kodi zimenezi zimatanthauzanji? Zimatanthauza kuti kumene kuli Atate wathu wakumwamba, mwauzimu, ndi malo apamwamba kwambiri monga mmene mlengalenga mulili kutali kwambiri ndi dziko lapansi. (Mateyu 12:50; Yesaya 63:15) Komabe, ngakhale kuti sitingamuone Mulungu, iye wapanga zotheka kuti timudziŵe ndi kuphunzira zambiri pankhani ya zolinga zake. (Eksodo 33:20; 34:6, 7) Iye amayankha mafunso a anthu oona mtima amene amafuna kudziŵa cholinga cha moyo. Pankhani zokhudza moyo wathu, iye amatipatsa mfundo zodalirika zotithandiza kudziŵa maganizo ake, kutanthauza momwe amaonera nkhani zimenezo ndiponso ngati zofuna zathu zikugwirizana ndi zolinga zake. Iye amafuna kuti tifufuze nkhani zimenezo ndipo tiyesetse kupeza mayankho. Kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova anadzudzula Aisrayeli akale chifukwa cholephera kuchita zimenezi. Iwo ankadziŵa dzina la Mulungu, koma sanafunse kuti, “Ali kuti Yehova?” (Yeremiya 2:6) Zolinga za Yehova analibe nazo ntchito kwenikweni. Sankafuna kuti awatsogolere. Mukafuna kusankha zochita, kaya pankhani yaikulu kapena yaing’ono, kodi mumafunsa kuti, “Ali kuti Yehova?”

Anthu Amene Anafunsira kwa Mulungu

4. Kodi tingapindule bwanji ndi chitsanzo cha Davide chofunsira kwa Yehova?

4 Davide, mwana wa Jese, akadali mnyamata, anakhulupirira kwambiri Yehova. Ankadziŵa kuti Yehova anali “Mulungu wamoyo.” Davide anatetezedwa ndi Yehova. Chifukwa chokhulupirira ndi kukonda “dzina la Yehova,” Davide anapha Goliati, chimphona chachifilisti, chomwe chinali ndi zida zankhondo zambiri. (1 Samueli 17:26, 34-51) Komabe, ngakhale kuti Davide anapambana sanayambe kudzithemba. Iye sanaganize kuti tsopano Yehova azidalitsa zochita zake zonse. Kuyambira pamenepo, nthaŵi zonse Davide ankafunsira kwa Yehova akafuna kuchita kanthu. (1 Samueli 23:2; 30:8;  2 Samueli 2:1; 5:19) Iye nthaŵi zonse ankapempha kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.” (Salmo 25:4, 5) Ndi chitsanzotu chabwino kwambiri kwa ife choti titsatire!

5, 6. Kodi Yehosafati anafuna bwanji Yehova panthaŵi zosiyanasiyana pa moyo wake?

5 M’masiku a Mfumu Yehosafati, yemwe anali mfumu yachisanu mu mzera wachifumu wa Davide, magulu ankhondo ophatikizana a mitundu itatu anabwera kudzamenyana ndi Yuda. Ankhondo ameneŵa atafika, Yehosafati “[a]nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova.” (2 Mbiri 20:1-3) Aka sikanali koyamba Yehosafati kufuna Yehova. Mfumuyi inakana kulambira Baala, kumene ufumu wakumpoto wa Israyeli wa mpatuko unali kuchita ndipo inasankha kuyenda m’njira za Yehova. (2 Mbiri 17:3, 4) Tsopano atakumana ndi vuto, kodi Yehosafati ‘anafuna Yehova’ motani?

6 Pemphero la Yehosafati pamaso pa anthu ku Yerusalemu panthaŵi yovuta kwambiri imeneyi, linasonyeza kuti anakumbukira kuti Yehova ndi wamphamvuyonse. Iye anaganizira mofatsa cholinga cha Yehova chimene anachionetsa mwa kuthamangitsa mitundu ina ndi kupatsa Aisrayeli dziko lina monga cholowa chawo. Mfumuyi inazindikira kuti inafunika thandizo la Yehova. (2 Mbiri 20:6-12) Kodi Yehova anapezeka panthaŵiyi? Inde. Yehova anapereka malangizo omveka bwino kudzera mwa Yahazieli, yemwe anali Mlevi, ndipo tsiku lotsatira Iye anathandiza anthu Ake kupambana. (2 Mbiri 20:14-28) Kodi mungatsimikize bwanji kuti inunso mudzam’peza Yehova mukam’pempha malangizo?

7. Kodi Mulungu amamva mapemphero a ndani?

7 Yehova alibe tsankho. Amapempha anthu a mitundu yonse kuti am’funefune m’pemphero. (Salmo 65:2; Machitidwe 10:34, 35) Iye amadziŵa za m’mitima ya anthu omwe amamupempha. Amatitsimikizira kuti amamva mapemphero a anthu olungama. (Miyambo 15:29) Iye amapezeka kwa anthu amene kale analibe naye chidwi koma amene tsopano amafuna malangizo ake modzichepetsa. (Yesaya 65:1) Iye amamva ngakhale mapemphero a anthu amene analephera kusunga lamulo lake koma tsopano alapa modzichepetsa. (Salmo 32:5, 6; Machitidwe 3:19) Komabe, mtima wa munthu ukapanda kugonjera Mulungu, mapemphero a munthuyo amangopita pachabe. (Marko 7:6, 7) Taonani zitsanzo zotsatirazi.

Anapempha Koma Sanayankhidwe

8. Kodi n’chiyani chinapangitsa kuti Yehova asayankhe mapemphero a Mfumu Sauli?

8 Mneneri Samueli atauza Mfumu Sauli kuti Mulungu wamukana chifukwa chakuti ndi wosamvera, Sauli analambira Yehova. (1 Samueli 15:30, 31) Koma kulambirako kunali kwa chiphamaso chabe. Cholinga cha Sauli sichinali kumvera Mulungu, koma kuti anthu azimulemekeza. Patapita nthaŵi, Afilisti akumenyana ndi Israyeli, Sauli anafunsira kwa Yehova mwamwambo chabe. Komabe, ataona kuti sanayankhidwe; anakafunsira kwa wobwebweta, ngakhale kuti ankadziŵa kuti Yehova amaletsa zimenezi. (Deuteronomo 18:10-12; 1 Samueli 28:6, 7) Mwachidule, pofotokoza za Sauli, pa 1 Mbiri 10:14 pamati: ‘Sanafunsire  kwa Yehova.’ N’chifukwa chiyani pamanena chonchi? Chifukwa chakuti Sauli sanali kupempha mwa chikhulupiriro. Chotero, zinkangokhala ngati sanapemphere n’komwe.

9. Kodi chinalakwika n’chiyani ndi pempho la Zedekiya lopempha Yehova malangizo?

9 Mofananamo, ufumu wa Yuda uli pafupi kutha, anthu anali kupemphera kwambiri ndiponso anali kukafunsira kwa aneneri a Yehova. Komabe, anthu anali kuphatikiza kupembedza mafano ndi kulemekeza Yehova. (Zefaniya 1:4-6) Ngakhale kuti anafunsira kwa Mulungu mwamwambo chabe, sanatsatire zofuna zake ndi mtima wonse. Mfumu Zedekiya inapempha Yeremiya kuti imufunsire kwa Yehova. Yehova anali atauza kale mfumuyi zoyenera kuchita. Chifukwa chopanda chikhulupiriro ndi kuopa anthu, mfumuyi sinamvere mawu a Yehova, ndipo Yehova sanaiyankhe zogwirizana ndi zimene mfumuyo inkafuna.​—Yeremiya 21:1-12; 38:14-19.

10. Kodi Yohanani analakwitsa chiyani popempha malangizo kwa Yehova, ndipo kodi tikuphunzira chiyani pamenepa?

10 Yerusalemu atawonongedwa komanso ankhondo a Babulo atatenga akapolo achiyuda, Yohanani anali wokonzeka kupita ku Igupto ndi kagulu ka Ayuda kamene kanatsala m’Yuda. Anakonzekera ulendowo koma asananyamuke anapempha Yeremiya kuwapempherera ndi kufunsira malangizo kwa Yehova. Komabe, ataona kuti sanalandire yankho limene anali kufuna, anachitabe zimene iwo anakonza kale. (Yeremiya 41:16–43:7) Kodi mukutha kutola mfundo m’nkhanizi, zimene zingakuthandizeni kuti pamene mukufuna nkhope ya Yehova, mum’peze?

‘Yesani’

11. N’chifukwa chiyani tifunika kutsatira mawu a pa Aefeso 5:10?

11 Kulambira koona kumafuna zambiri osati kungosonyeza kudzipatulira kwathu mwa kumizidwa m’madzi, kupezeka pa misonkhano ya mpingo, ndiponso kuchita nawo ulaliki. Kumakhudza moyo wathu wonse. Tsiku lililonse timakumana ndi mayesero​—ena osaoneka bwinobwino, ena oonekeratu​—amene angatipatutse kuti tisapitirize kudzipereka kwa Mulungu. Kodi tidzatani pamayesero ameneŵa? Mtumwi Paulo polembera kalata Akristu okhulupirika a ku Efeso anati: ‘Yesani chokondweretsa Ambuye n’chiyani.’ (Aefeso 5:10) Nkhani zambiri za m’Malemba zimasonyeza ubwino wochita zimenezi.

12. N’chifukwa chiyani Yehova sanasangalale Davide atanyamula likasa la chipangano kupita nalo ku Yerusalemu?

12 Likasa la chipangano litabwerera ku Israyeli ndipo litakhala zaka zambiri ku Kiriyati-Yearimu, Mfumu Davide inafuna kusamutsira Likasalo ku Yerusalemu. Anakambirana ndi akulu amene anali kutsogolera anthu ndipo anawauza kuti Likasa lisamutsidwa ‘chikakomera iwo, ndipo chikachokera kwa Yehova.’ Koma sanafufuze mokwanira kuti adziŵe maganizo a Yehova pankhaniyi. Akanakhala kuti anachita zimenezo, sibwenzi atanyamulira Likasalo pa galeta. Alevi Achikohati ndi amene akananyamula pa mapeŵa pawo, monga momwe Mulungu analangizira momveka bwino. Ngakhale kuti Davide nthaŵi zonse ankafunsira kwa Yehova, analephera kuchita zimenezo moyenera panthaŵi imeneyi. Zotsatira zake zinali zomvetsa chisoni zedi. Patapita nthaŵi Davide anavomereza kuti: “Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula,  popeza sitinam’funafuna Iye monga mwa chiweruzo.”​—1 Mbiri 13:1-3; 15:11-13; Numeri 4:4-6, 15; 7:1-9.

13. Kodi ndi mawu ati okumbutsa anthu amene ali m’nyimbo imene anaimba atasamutsa bwinobwino Likasa ?

13 Tsopano Alevi atasamutsa Likasa ku Obedi-Edomu kupita nalo ku Yerusalemu, anthu anaimba nyimbo imene Davide analemba. Ena mwa mawu a m’nyimboyo anali mawu ochokera pansi pamtima owakumbutsa, akuti: “Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake; funani nkhope yake nthaŵi zonse. Kumbukirani zodabwiza zake adazichita, zizindikiro zake, ndi maweruzo a pakamwa pake.”​—1 Mbiri 16:11, 12.

14. Kodi tingapindule bwanji ndi chitsanzo chabwino cha Solomo ndi zimene analakwitsa atakalamba?

14 Davide asanamwalire, analangiza mwana wake Solomo kuti: “Ukam’funafuna [Yehova] udzampeza.” (1 Mbiri 28:9) Solomo atakhala mfumu, anapita ku Gibeoni, kumene kunali chihema chokumanira, kukapereka nsembe kwa Yehova. Ali kumeneko Yehova anauza Solomo kuti: “Pempha chomwe ndikupatse.” Yehova poyankha zimene Solomo anapempha, anamupatsa moolowa manja nzeru ndi kudziŵa zinthu kuti aweruze Israyeli, kuphatikiza pamenepo anampatsa chuma ndi ulemu. (2 Mbiri 1:3-12) Solomo anamanga kachisi wapamwamba kwambiri pogwiritsa ntchito pulani ya kamangidwe imene Yehova anapatsa Davide. Koma Solomo analephera kufunafuna Yehova pankhani yaukwati. Iye anakwatira akazi amene sanali olambira Yehova. Atakalamba, akaziwo anapambutsa mtima wake kuuchotsa kwa Yehova. (1 Mafumu 11:1-10) Kaya tikhale otchuka, anzeru kapena odziŵa zinthu bwanji, n’kofunika “kuyesera chokondweretsa Ambuye n’chiyani.”

15. Pamene Zera Mkusi anaukira Yuda, kodi n’chifukwa chiyani Asa anapemphera akudalira kuti Yehova apulumutsa Yuda?

15 Nkhani ya ufumu wa Asa, yemwe anali mdzukulutuvi wa Solomo, imagogomezera kufunika kwa zimenezi. Patatha zaka khumi ndi chimodzi Asa ali mfumu, Zera Mkusi anatsogolera ankhondo okwana wani miliyoni kukamenyana ndi Yuda. Kodi Yehova anapulumutsa Yuda? Zaka zoposa 500 zimenezi zisanachitike, Yehova anafotokoza momveka bwino zimene anthu ake ayenera kuyembekezera ngati amvera ndi kusunga malamulo ake ndiponso ngati sachita zimenezo. (Deuteronomo 28:1, 7, 15, 25) Asa kuchiyambi kwa ulamuliro wake, anachotsa m’dziko lake maguwa a nsembe ndi zipilala zimene anthu anali kugwiritsa ntchito pakulambira konyenga. Iye anapempha anthu ‘kufuna Yehova.’ Asa anachita zimenezo asanakumane ndi vuto. Choncho Asa pokhulupirira Yehova, anamupempha kuti awamenyere nkhondoyo. Chotsatira chake chinali chiyani? Yuda anapambana kwambiri.​—2 Mbiri 14:2-12.

16, 17. (a) Ngakhale kuti Asa anapambana, kodi Yehova anamukumbutsa chiyani? (b) Pamene Asa anachita mopusa, kodi anathandizidwa bwanji, koma kodi anachita zotani? (c) Kodi tingapindule bwanji polingalira khalidwe la Asa?

16 Komabe, Asa atapambana, Yehova anatumiza Azariya kukakumana naye n’kumuuza kuti: “Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukam’funa Iye, mudzam’peza; koma mukam’siya adzakusiyani.” (2 Mbiri 15:2) Atalimbikitsidwa ndi mawuŵa, Asa anapititsa patsogolo kulambira koona. Koma patapita zaka 24, akufuna kumenya nkhondo ina, Asa analephera kufuna Yehova. Sanafufuze Mawu a Mulungu, ndipo sanakumbukire zimene Yehova anachita nthaŵi imene ankhondo a Akusi anaukira Yuda. Iye mopusa anagwirizana ndi Aramu.​—2 Mbiri 16:1-6.

17 Pachifukwa chimenechi, Yehova anatuma mlauli Hanani kukadzudzula Asa. Ngakhale panthaŵi imeneyi, Asa atauzidwa maganizo a Yehova pankhaniyo, akanatha kusintha. Koma, anakwiya ndipo anaika Hanani mu ukaidi. (2 Mbiri 16:7-10) Koma ndiye zomvetsa chisoni bwanji! Nanga bwanji ifeyo? Kodi timafuna Mulungu ndiyeno n’kukana malangizo ake? Kodi akulu amene amatiganizira ndi kutikonda akagwiritsa ntchito Baibulo kutilangiza poona kuti tikuloŵerera kwambiri m’zadziko, timayamikira thandizo lachikondi limene  akutipatsa kuti tidziŵe “chokondweretsa Ambuye n’chiyani”?

Musaiŵale Kufunsa

18. Kodi tingapindule bwanji ndi mawu amene Elihu anauza Yobu?

18 Pamavuto, ngakhale amene ali ndi mbiri yabwino potumikira Yehova angalakwitse. Yobu atadwala matenda oipa kwambiri, atataya ana ake ndi chuma chake, ndiponso anzake atamuimba mlandu wabodza, ankangoganiza za iye yekha basi. Elihu anamukumbutsa kuti: “Palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga.” (Yobu 35:10) Yobu anafunika kuika maganizo ake pa Yehova ndi kuona kuti kodi Iye anali kuwaona bwanji mavuto akewo. Yobu modzichepetsa anatsatira zimene anamukumbutsazi, ndipo chitsanzo chake chingatithandize kuchita zomwezo.

19. Kodi nthaŵi zambiri Aisrayeli ankalephera kutani?

19 Aisrayeli ankadziŵa mbiri ya zimene Mulungu anachitira mtundu wawo. Koma nthaŵi zambiri sanakumbukire zimenezi posamalira mavuto ena apadera pamoyo wawo. (Yeremiya 2:5, 6, 8) Pofuna kuchita kanthu pamoyo wawo, anachita zofuna zawo m’malo mofunsa kuti, “Ali kuti Yehova?”​—Yesaya 5:11, 12.

Pitirizani Kufunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”

20, 21. (a) Kodi ndani amene masiku ano asonyeza mtima wa Elisa pofunsira malangizo kwa Yehova? (b) Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha chikhulupiriro chawo ndipo tingapindule nacho bwanji?

20 Eliya atamaliza kutumikira anthu, mnyamata wake Elisa anatenga chofunda chimene chinam’tayika Eliya, ndikupita ku Yordano, ndipo anapanda madzi, n’kufunsa kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” (2 Mafumu 2:14) Yehova anayankha mwa kusonyeza kuti mzimu wake tsopano unali pa Elisa. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa?

21 Chinthu chofanana ndi chimenechi chachitikanso makono ano. Akristu ena odzozedwa amene ankatsogolera ntchito yolalikira  atamwalira, anthu amene panthaŵiyo anapatsidwa ntchito yoyang’anira anafufuza m’Malemba ndi kupempha kuti Yehova awatsogolere. Iwo sanaiŵale kufunsa kuti, “Ali kuti Yehova?” Chifukwa cha zimenezi, Yehova wapitiriza kutsogolera anthu ake ndiponso kudalitsa ntchito yawo. Kodi timatsatira chikhulupiriro chawo? (Ahebri 13:7) Ngati timatero, tidzayandikira kwambiri gulu la Yehova, tidzatsatira zimene limanena, ndi kuchita nawo mokwanira ntchito imene gululi likugwira motsogoleredwa ndi Yesu Kristu.​—Zekariya 8:23.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tiyenera kufunsa kuti, “Ali kuti Yehova?” n’cholinga chanji?

• Kodi masiku ano tingapeze bwanji yankho la funso lakuti, “Ali kuti Yehova?”

• N’chifukwa chiyani mapemphero ena opempha Mulungu malangizo sayankhidwa?

• Kodi ndi zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zikusonyeza kufunika ‘koyesa chokondweretsa Ambuye n’chiyani’?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi Mfumu Yehosafati anafuna bwanji Yehova?

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi n’chifukwa chiyani Sauli anafunsira kwa wobwebweta?

[Zithunzi patsamba 12]

Pempherani, ŵerengani, ndipo sinkhasinkhani kuti mudziŵe ‘kumene Yehova ali’