Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Gwiritsirani Ntchito Bwino Kusintha kwa Zinthu

Gwiritsirani Ntchito Bwino Kusintha kwa Zinthu

 Gwiritsirani Ntchito Bwino Kusintha kwa Zinthu

Pum, Jan, Dries, ndi Otto, akulu anayi achikristu amene akukhala ku Netherlands, ndi ofanana m’njira zambiri. Onseŵa ndi okwatira ndiponso ali ndi ana. Kuphatikiza apo, zaka zingapo zapitazo, onse ankagwira ntchito ndipo anali kukhala m’nyumba zabwino zedi. Komabe, onse anasiya kugwira ntchitozo ndipo anayamba kuthera nthaŵi yawo yonse ndiponso mphamvu zawo zonse popititsa patsogolo zinthu za Ufumu. N’chiyani chinawapangitsa kusintha zinthu chonchi? Onseŵa anagwiritsa ntchito bwino kusintha kwa zinthu.

NTHAŴI ina ambirife kusintha kwa zinthu kudzatikhudza. Kusintha kwa zinthu zambiri, monga kukwatira kapena kukwatiwa, kukhala ndi ana, kapena kusamalira makolo okalamba, kumabweretsa maudindo ena. Komabe, kusintha kwina, kumatipatsa ufulu waukulu wowonjezera utumiki wathu wachikristu. (Mateyu 9:37, 38) Mwachitsanzo, ana athu akuluakulu angachoke panyumba, kapena tingapume pantchito.

Komanso, ngakhale ndi zoona kuti zinthu zingasinthe kaya tifune kapena tisafune, Akristu ena zawayendera bwino pokonza okha zosintha zinthu pamoyo wawo zimene zapangitsa kuti akhale ndi mpata wochita zambiri mu utumiki. Izi n’zimene anachita Pum, Jan, Dries, ndi Otto. Anachita bwanji?

Ana Akachoka Panyumba

Pum ankagwira ntchito yolemba mmene chuma chikuyendera pa kampani ina yopanga ndi kugulitsa mankhwala. Nthaŵi zambiri, iye ndi mkazi wake Anny, ankatumikira monga apainiya othandiza pamodzi ndi ana awo aakazi aŵiri. Pum ndi Anny anali kukonzanso zocheza ndi anthu ena amene anali mu utumiki wa upainiya. Iwo anati: “Kuchita zimenezi kunathandiza kupeŵa mavuto amene kucheza ndi anthu ena kukanabweretsa.” Chifukwa cholimbikitsidwa ndi chitsanzo cha makolo awo, ana awo aakazi onse anakhala apainiya okhazikika atangomaliza sukulu ku sekondale.

Ana awo atachoka panyumba, Pum ndi Anny, anaona kuti kusintha kwa zinthu kumeneku kunawapatsa ufulu ndi ndalama zowonjezereka zimene akanatha kupitira ku malo osangalatsa kapena kukasangalala ndi zinthu zina. Komabe, m’malo mwake banjali linaganiza zogwiritsa ntchito kusintha kwa zinthu kumeneku kuwonjezera utumiki wawo wachikristu. Choncho Pum anapempha abwana ake kuti tsiku limodzi pamlungu asamagwire ntchito. Patapita nthaŵi, Pum anakonza zoti aziyamba ntchito 7 koloko m’mawa ndi kuŵeruka 2 koloko masana. Inde, chifukwa chogwira ntchito pang’ono ankalandira ndalama zochepa. Komabe, zinthu zinawayendera bwino, ndipo mu 1991, Pum anayamba upainiya wokhazikika pamodzi ndi mkazi wake amene anali atayamba kale.

Kenako, Pum anapemphedwa kukhala wachiŵiri kwa woyang’anira Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova. Pempho limeneli  linatanthauza kuti banjalo lisamuke m’nyumba imene linakhalamo zaka 30 kukakhala nyumba imene inali pa malo a Nyumba ya Msonkhano. Iwo anasamukira kumeneko. Kodi zimenezi zinali zovuta? Anny anayankha kuti nthaŵi iliyonse akayamba kukhumba kwawo, ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikufuna kufanana ndi mkazi wa Loti?’ Anny anakana ‘kucheuka.’​—Genesis 19:26; Luka 17:32.

Pum ndi Anny akuona kuti zimene anasankha zabweretsa madalitso ambiri. Mwa zina, iwo amasangalala kutumikira pa Nyumba ya Msonkhano, kukonzekera misonkhano yachigawo, ndiponso kucheza ndi oyang’anira dera (atumiki oyendayenda) amene amakamba nkhani pa nyumbayi. Nthaŵi zina, amayendera mipingo yosiyanasiyana Pum akamatumikira monga woyang’anira dera wogwirizira.

N’chiyani chinapangitsa kuti zinthu ziwayendere bwino powonjezera utumiki wawo? Pum anati: “Moyo wanu ukasintha kwambiri, muyenera kutsimikiza mtima kugwiritsira ntchito bwino mmene zinthu zasinthira tsopano.”

Kukonza Zokhala Moyo Wosalira Zambiri

Jan ndi mkazi wake, Woth, ali ndi ana atatu. Mofanana ndi Pum ndi banja lake, Jan anagwiritsira ntchito mwanzeru kusintha kwa zinthu. Kwa zaka zambiri, Jan anali kugwira ntchito ya malipiro abwino zedi ku banki, ndipo banja lake linali la mwanaalirenji. Komabe, anafunitsitsa kuwonjezera utumiki wake. Iye anati: “Pamoyo wanga, kuyamikira kwanga choonadi ndiponso kukonda kwanga Yehova kunakula.” Choncho, mu 1986, Jan anasintha zinthu pamoyo wake. Iye anati: “Ndinapezerapo mwayi nthaŵi imene ku ofesi kwathu anali kusintha zinthu ndipo ndinayamba kugwira ntchito maola ochepa. Malipiro anga anatsika ndi 40 peresenti. Ndinagulitsa nyumba yathu n’kugula boti langati nyumba kuti tizikatumikira kumene kunkafunikira ofalitsa Ufumu ambiri. Patapita nthaŵi, ndinatengerapo mwayi pa kupuma kwanga pantchito nthaŵi yake isanakwane. Malipiro anga anatsikanso ndi 20 peresenti, koma mu 1993, ndinatha kuyamba upainiya wokhazikika.”

Masiku ano, Jan ali m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ndipo nthaŵi zonse amakhala woyang’anira msonkhano wachigawo. Ngakhale kuti Woth amadwaladwala, nthaŵi zina amachita upainiya wothandiza. Ana ake onse atatu tsopano ali m’mabanja, ndipo ndi atumiki achangu a Ufumu pamodzi ndi amuna kapena akazi awo.

Kodi Jan ndi Woth anakwanitsa bwanji kukhala  bwinobwino ndi ndalama zochepa? Jan anayankha kuti: “Nthaŵi imene tinali ndi ndalama zambiri, tinkaonetsetsa kuti tisakondetse chuma. Masiku ano n’kovutirapo kudikira kwanthaŵi kuti tipeze chinthu, koma madalitso auzimu ndiponso maudindo autumiki amene talandira amakwaniritsa bwino mbali yotsalayo.”

Dries ndi mkazi wake Jenny, mofanana ndi Jan ndi Woth, anaganizanso zokhala ndi moyo wosalira zambiri kuti athere nthaŵi yambiri pa zinthu za Ufumu. Dries ndi Jenny anatumikira monga apainiya mpaka pamene anabereka mwana. Ndiyeno, kuti asamalire banja lake, Dries ankagwira ntchito monga mkulu pa kampani ina yaikulu. Abwana ake ankayamikira ntchito imene iye ankagwira ndipo anamukweza pantchito. Koma, Dries, anakana kukwezedwa chifukwa zimenezi zikanamuchepetsera nthaŵi yochitira zinthu zachikristu.

Kulera ana komanso kusamalira mayi a Jenny amene anali kudwala kunafuna kuti banjali ligwiritse ntchito nthaŵi ndi mphamvu zambiri. Komabe, anapitiriza kukhala ndi mzimu wa upainiya. N’chiyani chinawathandiza kuchita zimenezi? Jenny anati: “Tinkakhala ndi apainiya, tinkaitana apainiya kudzadya nafe chakudya, ndipo tinkapatsa malo ogona oyang’anira dera.” Dries anawonjezera kuti: “Tinkakhala moyo wosalira zambiri ndipo tinkapeŵa kuloŵa m’ngongole. Tinasankha kusaloŵa m’mabizinesi akuluakulu kapena kugula nyumba, kuti m’tsogolo zinthu zimenezi zisadzatilepheretse kuchita zinthu zina.”

Zimene Dries ndi Jenny anachita zosintha zinthu pamoyo wawo kuti akhale ndi nthaŵi yambiri yochitira zinthu za Ufumu zinawapindulitsa. Ana awo aamuna aŵiri ndi akutumikira monga akulu, ndipo mmodzi ndi mpainiya pamodzi ndi mkazi wake. Dries ndi Jenny anali apainiya apadera, ndipo kenako Jenny anali kuyendera limodzi ndi Dries mu ntchito yadera. Tsopano ndi antchito odzifunira pa Beteli, kumene Dries akutumikira m’Komiti ya Nthambi.

Kupuma Pantchito Nthaŵi Yake Isanakwane

Mofanana ndi Dries ndi Jenny, Otto ndi mkazi wake Judy anachita upainiya asanakhale ndi ana awo aakazi aŵiri. Judy ali ndi mimba ya mwana wawo woyamba, Otto anayamba ntchito yauphunzitsi.

Anawo akukula, nthaŵi zambiri Otto ndi Judy ankaitana apainiya kunyumba kwawo kuti ana awowo aone chimwemwe chimene antchito anthaŵi zonse achikristu amakhala nacho. M’kupita kwa nthaŵi mwana wawo woyamba anayamba utumiki wa upainiya. Kenako, anapita ku Sukulu ya Gileadi ndipo tsopano pamodzi ndi mwamuna wake ndi amishonale m’dziko la  mu Africa muno. Mwana wawo wamng’ono wamkazi anayamba upainiya mu 1987, ndipo Judy anayambanso upainiya.

Pamene kusintha kwa zinthu kunapangitsa Otto kuphunzitsa kwa maola ochepa kusukulu, anagwiritsa ntchito nthaŵi inayo kuchita upainiya. M’kupita kwa nthaŵi, anasiyiratu ntchitoyo. Masiku ano, Otto yemwe tsopano ali mu ntchito yoyendayenda, akugwiritsa ntchito luso lake la uphunzitsi kulimbikitsa mipingo mwauzimu.

Kodi Otto akulangiza chiyani anthu amene amapuma pantchito yolembedwa nthaŵi yake isanakwane? “Mukapuma pantchito, musangokhala osachita kanthu kwa chaka chimodzi kapena zingapo. Sizovuta kuzoloŵera moyo ‘wongokhala.’ Mudzaiŵala msanga za upainiya. M’malo mwake, yambani kuchita zambiri mu ntchito zotumikira nthaŵi yomweyo.”

Gwiritsani Ntchito Zimene Mwakumana Nazo Pamoyo Wanu

N’zoona kuti masiku ano abale monga Pum, Jan, Dries, ndi Otto alibenso mphamvu zimene anali nazo ali anyamata. Koma ndi okhwima kwambiri maganizo, amadziŵa zambiri ndiponso ndi anzeru zedi. (Miyambo 20:29) Amadziŵa zimene zimafunika kuti munthu akhale bambo, ndipo chifukwa chogwira ntchito ndi akazi awo, amadziŵako zimene zimafunika kuti munthu akhale mayi. Pamodzi ndi akazi awo, asamalira mavuto a m’banja ndipo aikira ana awo zolinga mu utumiki wa Mulungu. Otto anati: “Ndikamalangiza pankhani za banja monga woyang’anira dera, zimakhala bwino popeza inenso ndine wokwatira ndipo ndinalerapo ana.” Mofananamo, popeza Dries anakhalapo bambo tsopano amathandiza bwino kwambiri banja la Beteli, limene lili ndi antchito ambiri achinyamata.

Inde, kudziŵa kwawo zinthu kwathandiza abale ameneŵa kusamalira zinthu zambiri zofunika m’mipingo. Tingati zimene akumana nazo, zasula zida zawo zimene amagwiritsa ntchito, moti amagwiritsa ntchito mphamvu zawo m’njira yothandiza kwambiri. (Mlaliki 10:10) Ndipotu, nthaŵi zina, angachite zambiri kuposa anthu amene ali ndi mphamvu koma sadziŵa zambiri.

Abale ameneŵa, pamodzi ndi akazi awo, ndi zitsanzo zabwino kwambiri kwa achinyamata a m’gulu la anthu a Yehova. Achinyamata amaona kuti mabanja monga ameneŵa akumana ndi mavuto ndi kupeza madalitso ambiri amene amafotokozedwa m’mabuku athu achikristu. N’zolimbikitsa kuona amuna ndi akazi amene amasonyeza mtima wangati wa Kalebi amene ngakhale kuti anali wachikulire, anapempha ntchito yovuta.​—Yoswa 14:10-12.

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Kodi mungatsanzire chikhulupiriro ndi zochita za mabanja atchulidwa mu nkhani ino? Kumbukirani kuti anapanga choonadi kukhala moyo wawo. Analimbikitsa ana awo kufunitsitsa upainiya. Anachita zimenezi, monga momwe Jan akunenera, “mwa kukhala chitsanzo pokonda Yehova ndi gulu lake, mwa kukonza zocheza ndi anthu abwino, ndiponso mwa kuphunzitsa ana kukhala odziimira paokha.” Ndiponso ankagwirira ntchito pamodzi komanso kuseŵerera pamodzi monga banja. Pum anati: “Nthaŵi zambiri pa tchuti banja lonse linkapita m’mawa ku ntchito yolalikira ndipo madzulo linkapumula pamodzi.”

Kuphatikiza pa zimenezi, Akristu ameneŵa anakonzekeratu, moti moyo wawo utasintha, anali chire kugwiritsira ntchito mmene zinthu zinasinthira tsopano. Anali ndi zolinga ndipo anachita zimene zinawathandiza kukwaniritsa zolinga zawo mofulumira. Anafufuza njira zochitira ntchito yochepa ndipo anali ofunitsitsa kumagwiritsa ntchito ndalama zochepa. (Afilipi 1:10) Akaziwo anathandiza kwambiri amuna awowo. Onse pamodzi, ankafunitsitsa kwambiri kuloŵa pa “khomo lalikulu ndi lochititsa [“la zochita zambiri,” NW]” ndipo, chifukwa cha zimenezi, Yehova anawadalitsa kwambiri.​—1 Akorinto 16:9; Miyambo 10:22.

Kodi nanunso mumafuna kuwonjezera zimene mumachita mu utumiki? Ngati ndi choncho, kugwiritsa ntchito bwino kusintha kwa zinthu kungakhale chinsinsi chochitira zimenezo.

[Chithunzi patsamba 20]

Pum ndi Anny akusamalira Nyumba ya Msonkhano

[Chithunzi patsamba 20]

Jan ndi Woth akugwira ntchito yolalikira

[Chithunzi patsamba 21]

Dries ndi Jenny akutumikira pa Beteli

[Chithunzi patsamba 21]

Otto ndi Judy akukonzekera kukachezera mpingo wina