Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhulupirira Mulungu Amene Mwina Sitikum’dziŵa

Kukhulupirira Mulungu Amene Mwina Sitikum’dziŵa

 Kukhulupirira Mulungu Amene Mwina Sitikum’dziŵa

ANTHU aŵiri mwa atatu alionse ku Germany amakhulupirira Mulungu. Komabe, pamene anthu oposa chikwi chimodzi anafunsidwa kuti afotokoze kuti Mulungu amene amam’khulupirira ndi wotani, pafupifupi aliyense anapereka yankho losiyana. Magazini yakuti FOCUS inanena kuti: “Munthu aliyense ku Germany ali ndi malingaliro osiyana kwambiri pankhani ya Mulungu mofanana ndi mmene anthu alili osiyana.” Ngakhale kuti kukhulupirira Mulungu n’kwabwino, kodi si zomvetsa chisoni kum’khulupirira tisakum’dziŵa kuti ndi wotani?

Kusadziŵa kumeneku mmene Mulungu alili kapena umunthu wake, sikuli ku Germany kokha. Zilinso chimodzimodzi m’malo ena a ku Ulaya. Kafukufuku amene anachitidwa ku Austria, Britain, ndiponso ku Netherlands anasonyeza kuti anthu ambiri ali ndi maganizo ofanana akuti Mulungu ndi “mphamvu yapamwamba kapena chinsinsi chosafotokozeka.” Iye ali chinthu chosadziŵika makamaka pakati pa achinyamata ngakhale amene amam’khulupirira.

Kodi Mumam’dziŵa Bwinobwino Mulungu?

Pali kusiyana kwakukulu pakati pa kudziŵa za munthu ndi kum’dziŵa bwinobwino munthuyo. Kudziŵa za munthu, monga mfumu yosafikirika, katswiri wa maseŵero, katswiri wa m’mafilimu, kumangokhala kuvomereza kuti iye aliko. Komabe, kudziŵa munthu bwinobwino kumatanthauza zambiri. Kumaphatikizapo kudziŵa zochita zake, makhalidwe ake, mtima wake, zimene amakonda ndi zimene sakonda, ndiponso zomwe afuna kuchita m’tsogolo. Kudziŵa munthu wina bwinobwino kumapereka mwayi wokhala naye paubwenzi wapamtima.

Anthu ambirimbiri aona kuti kungodziŵa Mulungu pang’ono kapena kungodziŵa kuti iye aliko, sikokwanira. Iwo achita zoposa pamenepo mwa kudziŵa bwino kwambiri Mulungu. Kodi apindula nazo zimenezi? Mwamuna wina wotchedwa Paul, yemwe amakhala kumpoto kwa Germany ndipo nthaŵi ina ankakhulupirira Mulungu pang’ono, anafuna kudziŵa Mulungu bwinobwino. Paul anati: “Kudziŵa Mulungu bwino kwambiri kumafuna nthaŵi ndi khama, koma phindu lake ndi lalikulu. Kukhala paubwenzi wapamtima ndi Mlengi kumachititsa moyo kukhala wabwino.”

Kodi n’koyenera kupatula nthaŵi ndi kuchita khama kuti tidziŵe Mulungu bwino kwambiri? Taŵerengani nkhani yotsatira.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Pali kusiyana kwakukulu pakati pa kudziŵa za munthu ndi kum’dziŵa bwinobwino munthuyo