Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mgonero wa Ambuye Uli ndi Phindu Lanji kwa Inu?

Kodi Mgonero wa Ambuye Uli ndi Phindu Lanji kwa Inu?

 Kodi Mgonero wa Ambuye Uli ndi Phindu Lanji kwa Inu?

“Yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.”​—1 AKORINTO 11:27.

1. Kodi ndi mwambo wofunika kwambiri uti umene wakonzedwa m’chaka cha 2003, ndipo unayamba bwanji?

MWAMBO wofunika kwambiri umene wakonzedwa m’chaka cha 2003 udzachitika pa April 16, dzuŵa litaloŵa. Panthaŵi imeneyo, Mboni za Yehova zidzasonkhana kudzachita Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu. Monga mmene nkhani yapitayi yasonyezera, Yesu anayambitsa mwambo umenewu, wotchedwanso Mgonero wa Ambuye, iye ndi ophunzira ake atakondwerera Paskha pa Nisani 14, 33 C.E. Zizindikiro za pa Chikumbutso za mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo wofiira zimaimira thupi la Kristu lopanda uchimo ndi magazi amene iye anakhetsa, nsembe yokhayo imene ingaombole anthu ku uchimo ndi imfa zobadwa nazo.​—Aroma 5:12; 6:23.

2. Kodi ndi chenjezo lotani limene lili pa 1 Akorinto 11:27?

2 Amene amadya zizindikiro pa Chikumbutso ayenera kutero moyenera. Mtumwi Paulo anafotokoza zimenezo momveka bwino polembera Akristu a ku Korinto wakale, kumene Mgonero wa Ambuye sunali kuchitika moyenera. (1 Akorinto 11:20-22) Paulo analemba kuti: “Yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.” (1 Akorinto 11:27) Kodi mawu amenewo akutanthauza chiyani?

Ena Ankachita Chikumbutso Mosayenera

3. Kodi Akristu ambiri a ku Korinto ankachita bwanji pa chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye?

3 Akristu ambiri a ku Korinto ankadya nawo pa Chikumbutso mosayenera. Panali magawano pakati pawo, ndipo kwa nthaŵi ndithu, ena ankabweretsa chakudya chawo chamadzulo n’kudya msonkhano usanayambe kapena uli m’kati, nthaŵi zambiri ankadya ndi kumwa mopitirira malire. Sanali ogalamuka m’maganizo kapena mwauzimu. Zimenezi zinawachititsa kukhala ‘ochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.’ Amene sanabweretse chakudya cha madzulo anali  ndi njala ndipo ankadodometsedwa. Inde, ambiri ankadya mopanda ulemu ndiponso mosazindikira kuti mwambowu sunali nkhani ya maseŵera. N’zosadabwitsa kuti anadzipalamulira mlandu.​—1 Akorinto 11:27-34.

4, 5. N’chifukwa chiyani n’kofunika kuti amene amadya nawo nthaŵi zonse zizindikiro pa Chikumbutso ayenera kudzipenda?

4 Pamene Chikumbutso chikuyandikira chaka chilichonse, amene amadya zizindikiro nthaŵi zonse afunika kudzipenda. Kuti adye nawo moyenera chakudya chodyera limodzi chimenechi, ayenera kukhala ndi moyo wabwino wauzimu. Amene sasonyeza ulemu, kapena amene anachitira chipongwe nsembe ya Yesu adzakhala pangozi ‘yosadzidwa kwa anthu a Mulungu,’ monga mmene zinkachitikira Mwisrayeli akadya nawo chakudya chodyera pamodzi ali wodetsedwa.​—Levitiko 7:20; Ahebri 10:28-31.

5 Paulo anayerekezera Chikumbutso ndi chakudya chimene Aisrayeli kale ankadyera pamodzi. Ananena kuti anthu amene anali kudyawo amadyera limodzi mwa Kristu ndiyeno ananena kuti: “Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda.” (1 Akorinto 10:16-21) Ngati munthu amene nthaŵi zonse amadya nawo zizindikiro pa Chikumbutso achita tchimo lalikulu, ayenera kuulula kwa Yehova  ndi kupemphanso thandizo lauzimu kwa akulu a mpingo. (Miyambo 28:13; Yakobo 5:13-16) Ngati walapadi zenizeni ndi kusonyeza zipatso zosonyeza kulapako, sadzakhala akudya nawo mosayenera.​—Luka 3:8.

Kupezekapo Monga Oonerera Aulemu

6. Kodi Mulungu wapereka mwayi wodya nawo pa Mgonero wa Ambuye kwa ndani okha?

6 Kodi anthu amene panopa akuchitira zabwino abale a Kristu otsalira a 144,000 ayenera kudya nawo Mgonero wa Ambuye? (Mateyu 25:31-40; Chivumbulutso 14:1) Ayi. Mulungu wapereka mwayi umenewu kwa anthu okhawo amene wawadzoza ndi mzimu woyera kukhala “oloŵa [Ufumu] anzake a Kristu.” (Aroma 8:14-18; 1 Yohane 2:20) Nangano kodi amene akuyembekezera kudzakhala m’paradaiso padziko lapansi kosatha moyang’aniridwa ndi ulamuliro wa Ufumu ali ndi gawo lotani? (Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4) Popeza iwo si olowa ufumu anzake a Yesu amene akuyembekezera kupita kumwamba, amapezeka pa Chikumbutso monga oonerera aulemu.​—Aroma 6:3-5.

7. N’chifukwa chiyani Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino ankadziŵa kuti ayenera kudya nawo zizindikiro pa Chikumbutso?

7 Akristu oona a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino anadzozedwa ndi mzimu woyera. Ambiri a iwo ankatha kugwiritsa ntchito mphatso imodzi kapena zingapo za mzimu zochita zozizwitsa monga kulankhula malirime. Motero, zinali zosavuta kwa anthu oterowo kudziŵa kuti anadzozedwa ndi mzimu ndipo ayenera kudya nawo zizindikiro pa Chikumbutso. Komabe, m’nthaŵi yathu ino, zimenezo zingadziŵike poona mawu ouziridwa monga aŵa: “Onse amene atsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nawo, kuti, Abba, Atate.”​—Aroma 8:14, 15.

8. Kodi “tirigu” ndi “namsongole” zimene azitchula pa Mateyu chaputala 13 zikuimira chiyani?

8 Kuyambira nthaŵi imeneyo, odzozedwa enieni ankakula ngati “tirigu” m’munda wa “namsongole,” kapena kuti Akristu onyenga. (Mateyu 13:24-30, 36-43) Kuyambira m’ma 1870, ‘tiriguyo’ anayamba kuonekera bwino, ndipo patapita zaka, oyang’anira achikristu odzozedwa anauzidwa kuti: “Akulu . . . ayenera kuuza anthu amene asonkhana [pa Chikumbutso] kuti ayenera kukwaniritsa zinthu izi,​—(1) chikhulupiriro m’mwazi [wa Kristu]; ndi (2) kudzipatulira kwa Ambuye ndi utumiki wake ngakhale mpaka imfa. Ndiyeno apemphe onse amene akuganiza kuti akukwaniritsa zimenezi ndipo motero adzipatulira, kuti akondwerere nawo imfa ya Ambuye.​—Studies in the Scriptures, Series VI, The New Creation, tsamba 473. *

Kufunafuna a “Nkhosa Zina”

9. Kodi a “khamu lalikulu” anadziŵika bwanji mu 1935, ndipo zimenezi zinakhudza bwanji ena mwa amene anali kudya nawo zizindikiro pa Chikumbutso?

9 Patapita nthaŵi, gulu la Yehova linayamba kuganizira anthu ena kuwonjezera pa otsatira odzozedwa a Kristu. Chinthu chapadera pa nkhani imeneyi chinachitika m’kati mwa zaka za m’ma 1930. Nthaŵiyi isanafike, anthu a Mulungu ankaona ngati “khamu lalikulu” la pa Chivumbulutso 7:9 linali gulu lauzimu lachiŵiri limene lidzagwirizana ndi odzozedwa oukitsidwa a 144,000 kumwamba, monga operekeza akwati kapena anzawo a mkwatibwi wa Kristu. (Salmo 45:14, 15; Chivumbulutso 7:4; 21:2, 9) Koma pa May 31, 1935, m’nkhani imene inakambidwa pa msonkhano wa Mboni za Yehova ku Washington, D.C., U.S.A., anafotokoza kuchokera m’Malemba kuti “khamu lalikulu” linali kutanthauza “nkhosa zina” zimene zikukhala m’nthaŵi ya mapeto. (Yohane 10:16) Utatha msonkhano umenewo, ena omwe poyamba ankadya nawo zizindikiro pa Chikumbutso anasiya kudya nawo chifukwa anazindikira kuti anali kuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, osati kupita kumwamba.

10. Kodi mungafotokoze bwanji chiyembekezo ndiponso maudindo amene a “nkhosa zina” a masiku ano ali nawo?

10 Makamaka kuyambira mu 1935 pakhala kufunafuna anthu amene akukhala a “nkhosa zina,” omwe akukhulupirira dipo, adzipatulira kwa Mulungu, ndipo akuthandiza “kagulu ka nkhosa”  kodzozedwa pantchito yolalikira Ufumu. (Luka 12:32) A nkhosa zina ameneŵa akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi kosatha, koma m’mbali zina zonse, iwo amafanana ndi otsalira odzaloŵa Ufumu amene alipo masiku ano. Mofanana ndi alendo a ku Israyeli amene anali kulambira Yehova ndi kugonjera Chilamulo, a nkhosa zina a masiku ano amavomera maudindo achikristu monga kulalikira uthenga wabwino pamodzi ndi a m’gulu la Israyeli wauzimu. (Agalatiya 6:16) Komabe, monga mmene zinalili kuti mlendo aliyense sakanakhala mfumu kapena wansembe wa Israyeli, palibe aliyense mwa a nkhosa zina ameneŵa amene angadzalamulire mu Ufumu wa kumwamba kapena kukhala ansembe.​—Deuteronomo 17:15.

11. Kodi deti limene munthu anadzipatulira lingakhudze bwanji chiyembekezo chake?

11 Motero, pofika m’ma 1930 zinayamba kuonekera bwino kuti, kumbali yaikulu, gulu lopita kumwamba linali litasankhidwa. Kwa zaka makumi angapo tsopano, amene akufunidwafunidwa tsopano ndi a nkhosa zina, amene akuyembekezera kudzakhala pa dziko lapansi. Ngati wodzozedwa akhala wosakhulupirika, n’koonekeratu kuti munthu amene watumikira Mulungu mokhulupirika kwa nthaŵi yaitali monga m’modzi mwa a nkhosa zina adzamuitana kuti adzaloŵe m’malo mwa amene wachoka m’gulu la a 144,000 uja.

Zifukwa Zimene Ena Amaganizira Molakwa

12. Kodi munthu ayenera kusiya kudya zizindikiro pa Chikumbutso pa chifukwa chiti, nanga n’chifukwa chiyani?

12 Akristu odzozedwa ndi otsimikiza kuti adzapita kumwamba. Koma bwanji ngati anthu ena amene sadzapita kumwamba akhala akudya zizindikiro pa Chikumbutso? Popeza tsopano azindikira kuti sakuyembekezera kudzapita kumwamba, mosakayika chikumbumtima chawo chiwalimbikitsa kusiya kudya nawo. Mulungu sangakondwere ndi munthu amene amati anaitanidwa kukakhala mfumu ndi wansembe kumwamba pomwe akudziŵa kuti sanaitanidwe. (Aroma 9:16; Chivumbulutso 20:6) Yehova anapha Kora yemwe anali Mlevi chifukwa chodzikuza ndi kufuna unsembe wa Aroni. (Eksodo 28:1; Numeri 16:4-11, 31-35) Ngati Mkristu aliyense azindikira kuti amadya zizindikiro pa Chikumbutso molakwika, ayenera kusiya kudya nawo ndipo apemphere kwa Yehova modzichepetsa kuti amukhululukire.​—Salmo 19:13.

13, 14. N’chifukwa chiyani ena angaganize molakwika kuti adzapita kumwamba?

13 Kodi n’chifukwa chiyani ena angaganize molakwika kuti adzapita kumwamba? Kumwalira kwa mkazi kapena mwamuna wawo kapenanso mavuto ena angawachititse kusasangalala ndi moyo wa padziko lapansi. Kapena angamafune kupita kumene adzapita mnzawo wapamtima amene amati ndi Mkristu wodzozedwa. Kunena zoona, Mulungu sanapatse ntchito wina aliyense yosankha amene adzakhale ndi mwayi umenewu. Ndipo iye sadzoza oloŵa Ufumu mwa kuwachititsa kumva mawu ndi mauthenga amene angatsimikizire kuti adzozedwa.

14 Mfundo yonyenga yachipembedzo yakuti anthu onse abwino amapita kumwamba ingachititse ena kuganiza kuti adzapita kumwamba. Motero, tiyenera kupeŵa kuchita zinthu chifukwa cha maganizo olakwika akale kapena zinthu zina. Mwachitsanzo, ena angafunike kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimagwiritsa ntchito mankhwala amene amakhudza mmene ndimaganizira? Kodi ndimatengeka kwambiri maganizo zimene zingandichititse kuganiza molakwa?’

15, 16. N’chifukwa chiyani ena angaganize molakwika kuti ndi odzozedwa?

15 Ena angafunike kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikufuna kutchuka? Kodi ndikukhumbira udindo pakalipano kapena kukhumbira kudzakhala wolamulira mnzake wa Kristu?’ Pamene olowa Ufumu anali kusankhidwa m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, si onse amene anali ndi maudindo mumpingo. Ndipo anthu amene akuyembekezera kudzapita kumwamba safuna kutchuka kapena kudzitamandira kuti ndi odzozedwa. Amasonyeza kudzichepetsa kumene anthu amene ali ndi “mtima wa Kristu” amafunika kukhala nako.​—1 Akorinto 2:16.

16 Ena angaganize kuti adzapita kumwamba chifukwa chakuti akudziŵa zambiri za m’Baibulo. Koma kudzozedwa ndi mzimu sikuchititsa munthu kumvetsa Baibulo mwapadera, chifukwa Paulo anafunika kulangiza ndi kupatsa  uphungu odzozedwa ena. (1 Akorinto 3:1-3; Ahebri 5:11-14) Mulungu ali ndi makonzedwe operekera chakudya chauzimu kwa anthu ake onse. (Mateyu 24:45-47) Motero, palibe amene ayenera kuganiza kuti kukhala Mkristu wodzozedwa kumam’chititsa kukhala ndi nzeru zoposa amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi. Kuyankha mwaluso mafunso okhudza Malemba, kulalikira ndiponso kukamba nkhani za m’Baibulo mwaluso sizili umboni woti munthuyo ndi wodzozedwa ndi mzimu. Akristu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi amachitanso mwaluso mbali zimenezi.

17. Kodi kudzozedwa ndi mzimu sikufuma kwa yani, koma kwa ndani?

17 Ngati wokhulupirira wina afunsa za kupita kumwamba, mkulu kapena Mkristu wina wokhwima mwauzimu angakambirane naye nkhaniyo. Komabe, munthu sangam’pangire munthu wina zosankha zimenezi. Munthu amene alidi woti adzapita kumwamba safunsa ena ngati ali ndi chiyembekezo chimenechi. Odzozedwa ‘anabadwanso, osati ndi mbewu yofeka, komatu yosawola, mwa mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.’ (1 Petro 1:23) Mwa mzimu wake ndi Mawu ake, Mulungu amadzala “mbewu” imene imachititsa munthuyo kukhala “wolengedwa watsopano,” woyembekezera kudzapita kumwamba. (2 Akorinto 5:17) Ndipo Yehova ndi amene amasankha. Kudzozedwa ‘sikufuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu.’ (Aroma 9:16) Motero, kodi munthu angatsimikizire bwanji kuti adzapita kumwamba?

Chifukwa Chake Ali Otsimikiza

18. Kodi mzimu wa Mulungu umachita bwanji umboni ndi mzimu wa odzozedwa?

18 Umboni wa mzimu wa Mulungu umachititsa Akristu odzozedwa kukhulupirira kuti adzapita kumwamba. Paulo analemba kuti: “Munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nawo, kuti, Abba, Atate. Mzimu wokha uchita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso oloŵa nyumba; inde oloŵa nyumba ake a Mulungu, ndi oloŵa anzake a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi iye.” (Aroma 8:15-17) Mwa mphamvu ya mzimu woyera, mzimu kapena maganizo amphamvu a odzozedwa amawalimbikitsa kuona kuti zimene Malemba akunena za ana auzimu a Yehova zikukhudza iwo. (1 Yohane 3:2) Mzimu wa Mulungu umawapangitsa kuona kuti ndi ana ake ndipo umawapangitsa kukhala ndi chiyembekezo chapadera. (Agalatiya 4:6, 7) N’zoona kuti moyo wosatha padziko lapansi monga anthu angwiro, kukhala pamodzi ndi banja  lako ndi anzako zingakhale zosangalatsa kwambiri, koma Mulungu sanawapatse chiyembekezo chimenecho. Mwa mzimu wake, Mulungu waika mwa iwo chiyembekezo cholimba chopita kumwamba moti ndi ofunitsitsa kudzimana zabwino zonse ndiponso chiyembekezo cha padziko lapansi.​—2 Akorinto 5:1-5, 8; 2 Petro 1:13, 14.

19. Kodi pangano latsopano limagwira ntchito yanji m’moyo wa Mkristu wodzozedwa?

19 Akristu odzozedwa sakayikira zopita kumwamba, sakayikira za kuloŵetsedwa kwawo m’pangano latsopano. Yesu anatchula zimenezi pamene anali kuyambitsa Chikumbutso ndipo anati: “Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.” (Luka 22:20) Anthu a m’pangano latsopanoli ndiwo Mulungu ndi odzozedwa. (Yeremiya 31:31-34; Ahebri 12:22-24) Yesu ndiye mkhalapakati. Panganoli litayamba kugwira ntchito chifukwa cha magazi amene Kristu anakhetsa, linayamba kutenga anthu a dzina la Yehova ndi kuwapangitsa kukhala mbali ya “mbewu” ya Abrahamu. Anthuwa sanawatenge mwa Ayuda okha, komanso mwa amitundu. (Agalatiya 3:26-29; Machitidwe 15:14) “Chipangano chosatha” chimenechi chimathandiza Aisrayeli auzimu onse kuukitsidwa kukakhala ndi moyo wosafa kumwamba.​—Ahebri 13:20.

20. Kodi odzozedwa awaloŵetsa m’pangano liti pamodzi ndi Kristu?

20 Odzozedwa sakayikira chiyembekezo chawo. Iwo awaloŵetsanso m’pangano lina, pangano la Ufumu. Pofotokoza za kukhala kwawo mafumu pamodzi ndi Kristu, Yesu anati: “Inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine.” (Luka 22:28-30) Pangano limeneli pakati pa Kristu ndi mafumu anzake ndi logwira ntchito mpaka kalekale.​—Chivumbulutso 22:5.

Nthaŵi ya Chikumbutso Ndi Yopindulitsa

21. Kodi tingapeze bwanji phindu lalikulu pa nthaŵi ya Chikumbutso?

21 Timapindula zambiri pa nthaŵi ya Chikumbutso. Tingapindule ndi kuŵerenga Baibulo kwa panthaŵi imeneyi. Ndi nthaŵinso yabwino kwambiri kupemphera, kusinkhasinkha za moyo wa Yesu ali padziko lapansi ndi imfa yake, ndiponso kugwira nawo ntchito yolalikira Ufumu. (Salmo 77:12; Afilipi 4:6, 7) Mwambowu umatikumbutsa chikondi chimene Mulungu ndi Kristu anachisonyeza mwa nsembe ya dipo ya Yesu. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Makonzedwe ameneŵa amatipatsa chiyembekezo ndi chilimbikitso ndipo chiyenera kulimbitsa kutsimikiza mtima kwathu kutsatira njira imene Kristu anatsatira. (Eksodo 34:6; Ahebri 12:3) Chikumbutsochi chiyeneranso kutilimbikitsa kukwaniritsa kudzipatulira kwathu monga atumiki a Mulungu ndi kutsatira mokhulupirika Mwana wake wokondedwa.

22. Kodi mphatso yaikulu kuposa ina iliyonse imene Mulungu wapereka kwa anthu ndi iti, ndipo ndi njira imodzi iti imene tingasonyezere kuyamikira?

22 Yehova amatipatsadi mphatso zabwino. (Yakobo 1:17) Tili ndi Mawu ake amene amatitsogolera, mzimu wake woyera umatithandiza, ndiponso tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo kosatha. Mphatso yaikulu kuposa ina iliyonse imene Mulungu wapereka ndiyo nsembe ya Yesu imene anaipereka chifukwa cha machimo a odzozedwa ndiponso a anthu ena onse amene akukhulupirira. (1 Yohane 2:1, 2) Motero, kodi imfa ya Yesu ili ndi phindu lanji kwa inu? Kodi mudzakhala m’modzi mwa anthu amene amayamikira nsembeyo mwa kudzasonkhana nawo pa April 16, 2003 dzuwa litalowa kuti mudzachite chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma panopa sakulitsindikizanso.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndani ayenera kudya zizindikiro pa Chikumbutso?

• N’chifukwa chiyani “nkhosa zina” zimapezeka nawo pa Mgonero wa Ambuye monga oonerera aulemu basi?

• Kodi Akristu odzozedwa amadziŵa bwanji kuti ayenera kudya mkate ndi vinyo pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu?

• Kodi nthaŵi ya Chikumbutso ndi yabwino kuchita chiyani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 18]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chiŵerengero cha Anthu Opezeka pa Chikumbutso

M’MAMILIYONI

15,597,746

15

14

13,147,201

13

12

11

10

 9

 8

 7

 6

 5

4,925,643

 4

 3

 2

 1

878,303

63,146

1935 1955 1975 1995 2002

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi mudzapezekapo pa Mgonero wa Ambuye chaka chino?

[Zithunzi patsamba 21]

Nthaŵi ya Chikumbutso ndi nthaŵi yabwino kuwonjezera kuŵerenga Baibulo ndi kugwira nawo ntchito yolalikira