Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyesedwa mu Ng’anjo Yamoto ya Mavuto

Kuyesedwa mu Ng’anjo Yamoto ya Mavuto

 Mbiri ya Moyo Wanga

Kuyesedwa mu Ng’anjo Yamoto ya Mavuto

YOSIMBIDWA NDI PERICLES YANNOURIS

Ndinkamva kuzizira chifukwa cha chinyezi komanso kununkha m’chipinda cha ndende mmene ndinali. Ndili ndekhandekha mmenemo, n’tafunda kabulangete kopyapyala, ndinkakumbukira nkhope yachisoni ya mkazi wanga yemwe anali wachitsikana, pamene asilikali anali kundikoka mnyumba yanga masiku aŵiri apitawo, n’kumusiya ndi ana athu aŵiri amene anali kudwala. Kenako, mkazi wanga amene sanali wokhulupirira mnzanga, ananditumizira zinthu ndi kakalata kamene kanali ndi mawu akuti: “Ndakutumizirani makekewo, ndipo ndikukhulupirira kuti mudwala monga ana anu.” Kodi ndidzabwerera kunyumba wamoyo kukaonana ndi banja langa?

IMENEYI ndi nkhani imodzi chabe pankhondo yanthaŵi yaitali ndi yovuta yomenyera chikhulupiriro chachikristu, yomwe inali kukhudza kutsutsidwa ndi achibale, anthu kundipatula, milandu ndiponso chizunzo chachikulu. Koma kodi zinatani ndiponso n’chifukwa chiyani munthu waphee ndi woopa Mulungu ngati ine, anafika pokhala malo oipa ngati amenewo? Ndiloleni ndifotokoze.

Mnyamata Wosauka wa Zolinga Zapamwamba

Pamene ndinkabadwa mu 1909, ku Stavromeno ku Crete, n’kuti m’dzikomo muli nkhondo, umphaŵi ndi njala. Kenako ine ndi abale anga anayi tinangopulumuka pang’onong’ono mlili wa matenda a Flu ya ku Spain. Ndimakumbukira kuti makolo athu anatitsekera m’nyumba kwa milungu ingapo kuti tisatenge matendawa.

 Bambo, amene anali mlimi wosauka, ankakonda kwambiri zachipembedzo ndiponso anali womva za ena. Popeza anakhalako ku France ndi ku Madagascar, ankadziŵa zinthu zambiri zachipembedzo. Komabe, banja lathu linali lokhulupirikabe ku Tchalitchi cha Greek Orthodox, tinkapita ku Misa Lamlungu lililonse ndiponso bishopu wa m’deralo paulendo wake wa pachaka tinali kumulola kugona ku nyumba kwathu. Ndinali mnyamata wa kwaya, ndipo ndinkafunitsitsa kudzakhala wansembe.

Mu 1929, ndinaloŵa ntchito yapolisi. Nthaŵi imene Bambo ankamwalira n’kuti ndili pantchito ku Thessalonica, chakumpoto kwa Greece. Pofuna kulimbikitsidwa ndiponso kudziŵa zambiri zauzimu, ndinapempha kuti ndizikagwirira ntchito ku polisi ya ku phiri la Athos, dera lapafupi kumene kumakhala Amonke, limene Akristu atchalitchi cha Orthodox amati ndi “phiri lopatulika.” * Ndinagwira ntchito kumeneko kwa zaka zinayi ndipo ndinauonera pafupi moyo wa amonke. M’malo moyandikira kwambiri kwa Mulungu, ndinaipidwa ndi chiwerewere ndi kulandira ziphuphu koonekeratu kwa amonke. Ndinakhumudwa pamene mtsogoleri watchalitchichi, wotsatira kwa bishopu, amene ndinali kumulemekeza anafuna kuchita nane zachiwerewere. Ngakhale kuti ndinakhumudwa chonchi, ndinkafuna ndi mtima wonse kutumikira Mulungu ndiponso kukhala wansembe. Ndinafika povala mkanjo wa wansembe ndi kujambulitsira chithunzi kuti ndizidzakumbukira zakale. Patapita nthaŵi ndinabwerera ku Crete.

“Ndi Mdyerekezi!”

Mu 1942, ndinakwatira Frosini, mtsikana wokongola kwambiri wochokera kubanja lolemekezeka. Ukwati unakulitsa maganizo anga oti ndidzakhale wansembe, popeza alamu anga anali okonda kwambiri zachipembedzo. * Ndinatsimikiza mtima kupita ku Athens kukaphunzira ku seminale. Chakumapeto kwa chaka cha 1943, ndinafika pa doko la Iráklion, ku Crete, koma sindinanyamuke ulendo wa ku Athens. Mwina chifukwa chakuti, panthaŵi imeneyi, ndinapeza gwero lina lotsitsimula mwauzimu. Kodi chinachitika n’chiyani?

Kwa zaka zingapo Emmanuel Lionoudakis, mlaliki wachinyamata wachangu, amene anali kusonkhana ndi Mboni za Yehova, anali kuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo chomveka bwino mu Crete monse. * Anthu ena anakopeka ndi Mboni chifukwa chomvetsetsa Mawu a Mulungu ndipo anasiya chipembedzo chonyenga. Mu tauni yapafupi ya Sitía anakhazikitsa kagulu kachangu ka Mboni. Izi zinavutitsa maganizo bishopu wa m’deralo, amene popeza kuti anakhalako ku United States ankadziŵa bwino momwe Mboni za Yehova zingakhalire zogwira mtima polalikira. Iye anatsimikiza mtima kuthetsa “mpatuko” umenewu m’dera lake. Chifukwa cha iye, nthaŵi zambiri apolisi ankagwira Mboni kukazitsekera kundende ndipo ankazikakamiza kukaonekera ku khoti pa milandu yosiyanasiyana yabodza.

Mmodzi mwa Mboni zimenezi anayesa kundifotokozera choonadi cha m’Baibulo, koma anaganiza kuti ndinalibe chidwi. Choncho anakatumiza mtumiki waluso kwambiri kuti adzandilankhule. Mwachionekere kuyankha kwanga mongodula kunapangitsa Mboni yachiŵiriyi kukauza kagulu kaja kuti: “Sizingatheke Pericles kukhala Mboni. Ndi Mdyerekezi!”

Nthaŵi Yoyamba Kukumana Ndi Chitsutso

Ndimasangalala kuti Mulungu sanali kundiona choncho. Mu February 1945 mchimwene wanga Demosthenes, amene anakhutira kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa choonadi, anandipatsa kabuku kakuti Comfort All That Mourn. * Ndinachita chidwi ndi nkhani za mmenemo. Nthaŵi yomweyo tinasiya kupita ku Tchalitchi cha Orthodox, ndipo tinaloŵa m’kagulu ka ku Sitía, ndipo tinalalikira kwa ang’ono athu ndi azichemwali athu za chikhulupiriro chathu chatsopano. Onse analandira choonadi cha m’Baibulo. Monga ndimayembekezera, kusiya kwanga chipembedzo chonyenga kunapangitsa mkazi wanga ndi achibale ake kusandikonda komanso kumandida. Kwa nthaŵi ndithu apongozi anga aamuna anafika posiya kundilankhula. Panyumba, panali kusagwirizana ndi mikangano yosatha. Ngakhale izi zinali choncho, pa May 21, 1945,  Mbale Minos Kokkinakis anandibatiza pamodzi ndi Demosthenes. *

Tsopano ndinatha kuchita zija ndinkakhumba kale ndipo ndinatumikira monga mtumiki weniweni wa Mulungu. Ndimakumbukirabe tsiku limene ndinayamba kupita mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Ndinali ndi timabuku 35 m’chikwama changa, ndinapita ndekha pabasi ku mudzi wina. Ndinayamba kupita nyumba ndi nyumba ndili wamantha. Pamene ndinapita nyumba zingapo, ndinayamba kulimba mtima pang’onopang’ono. Wansembe waukali atafika, ndinalimba mtima, sindinasamale zimene anali kulimbikira kunena zoti ndipite naye ku polisi. Ndinamuuza kuti ndichoka ndikafika ku nyumba zonse m’mudzimo, ndipo n’zimenedi ndinachita. Ndinasangalala kwambiri kuti pobwerera kunyumba sindinadikirire n’komwe basi kuti ibwere, ndinangoyenda pansi ulendo wa makilomita 15.

M’manja mwa Zigaŵenga Zankhanza

Mu September 1945, ndinapatsidwa maudindo ena mu mpingo wathu watsopano ku Sitía.  Patangopita nthaŵi pang’ono ku Greece kunaulika nkhondo yapachiweniweni. Magulu olimbanawo anaukirana mwankhanza zedi. Bishopu anapezerapo mwayi pa zimenezi ndipo anapempha gulu la zigaŵenga la m’deralo kuti lichotse Mboni mwa njira iliyonse imene akuona kuti ndi yabwino. (Yohane 16:2) Pamene gulu la zigaŵengalo limaloŵa m’mudzi mwathumo pabasi, mkazi wina wabwino amene anali m’basimo anamva zolinga za zigaŵengazo kuti zikukagwira ntchito imene “Mulungu wazipatsa” ndipo anabwera kudzatichenjeza. Tinapita kukabisala, ndipo mbale wathu wina anatithandiza. Tinapulumuka.

Ichi chinali chiyambi chake cha mavuto ambiri amene anali kubwera. Kumenyedwa ndi kuwopsezedwa sikunali kwachilendo. Adani athu anayesa kutikakamiza kuti tibwerere ku tchalitchicho, kuti tikabatize ana athu, ndiponso kuti tipange chizindikiro cha mtanda. Nthaŵi ina anamenya mchimwene wanga kufika poganiza kuti wafa. Zinandipweteka mtima kuona azichemwali anga aŵiri akuwang’ambira zovala n’kumawamenya. Panthaŵi imeneyi, tchalitchi chinabatiza ana asanu ndi atatu a Mboni za Yehova mowakakamiza.

Mu 1949 mayi anga anamwalira. Wansembe anatilondalondanso, n’kumati sitinatsatire malamulo pofuna kupeza chilolezo choti tiike maliro. Anakandiimba mlandu ku khoti ndipo anandipeza kuti ndilibe mlandu. Izi zinapereka umboni waukulu, popeza anthu anamva dzina la Yehova poyamba kuzenga mlanduwo. Njira yokha imene adani athu anatsala nayo kuti “atithandize kuzindikira kuti ndife olakwa” inali kutimanga ndi kutisamutsira kudera lina. Anachita zimenezi mu April 1949.

Mu Ng’anjo Yamoto

Ndinali mmodzi mwa abale atatu amene tinamangidwa. Mkazi wanga sanabwere n’komwe kudzandiona ndili ku polisi ya deralo. Tinayamba kuima pa ndende ya ku Iráklion. Monga ndanenera pachiyambi paja, ndinali wosungulumwa ndiponso wachisoni. Ndinasiya mkazi wachitsikana amene sanali wokhulupirira mnzanga ndi ana aŵiri. Ndinapempha Yehova mochokera pansi pamtima kuti andithandize. Mawu a Mulungu monga a pa Ahebri 13:5 anali kundibwerera m’maganizo. Mawuwo amati: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” Ndinazindikira kuti ndi nzeru kukhulupirira kwambiri Yehova.​—Miyambo 3:5.

Tinamva kuti atisamutsira ku Makrónisos, chilumba chopanda zomera cha m’mphepete mwa nyanja ya Attica, ku Greece. Kungotchula kokha kuti Makrónisos zinali kuchititsa mantha aliyense chifukwa chakuti msasa wandende umenewu unali wotchuka ndi nkhanza ndiponso ntchito yaukapolo. Tili paulendo wa kundende tinaima pa Piraeus. Ngakhale kuti tinali muunyolo, tinalimbikitsidwa pamene ena mwa okhulupirira anzathu anabwera pa boti n’kutikumbatira.​—Machitidwe 28:14, 15.

Moyo ku Makrónisos unali wovuta kwambiri. Asilikali anali kuzunza anthu m’ndendemo kuyambira mmaŵa mpaka usiku. Akaidi ambiri amene sanali Mboni anazungulira mitu, ena anamwalira ndipo ambiri zedi anapunduka. Usiku, tinkamva kulira ndi kubuula kwa anthu amene anali kuzunzidwa. Kabulangeti kanga kopyapyala kaja kanali kunditenthetsako usiku kukamazizira.

Pang’ono ndi pang’ono Mboni za Yehova zinayamba kudziŵika bwino pa msasawo chifukwa anali kutchula dzinali akamaitana mayina m’maŵa uliwonse. Choncho, tinali ndi mipata yambiri yolalikirira. Ndipo ndinafika pokhala ndi mwayi wobatiza mkaidi wina amene anamangidwa pa zifukwa zandale amene analimbikira mpaka kupatulira moyo wake kwa Yehova.

Ndili kudera limene anandisamutsira, ndinapitiriza kulembera makalata mkazi wanga wokondedwa popanda kundiyankha n’komwe. Izi sizinandisiyitse kumulembera makalata achikondi, kumulimbikitsa ndi kumutsimikizira kuti ameneŵa anali mavuto akanthaŵi chabe ndiponso kuti tidzakhalanso osangalala.

Panthaŵi imeneyi, chiŵerengero chathu chinakula chifukwa kunkabwera abale ambiri. Pokonza mu ofesi, ndinapanga ubwenzi ndi mtsogoleri wa asilikali pa msasawo. Popeza ankalemekeza Mboni, ndinalimba mtima kumufunsa ngati tingamalandire mabuku ofotokoza za Baibulo kuchokera ku ofesi yathu ku Athens. Iye anati: “Zimenezo sizingatheke, koma kodi anthu anu ku Athens sangatumize zimenezo m’chikwama mu dzina langa?” Ndinadabwa kwambiri! Patapita masiku angapo tikutsitsa katundu m’boti limene linangofika kumene, wapolisi anachitira shawasha mtsogoleri wa asilikali ndi kumuuza kuti: “Bwana, chikwama  chanu chafika.” Iye anayankha kuti: “Chikwama chiti?” Zinangochitika kuti panthaŵi imeneyi n’kuti ndili pafupi moti ndinamva zimene anali kukambiranazo, choncho ndinamunong’oneza kuti: “Chiyenera kuti ndi chathu, chimene chatumizidwa m’dzina lanu, monga munanenera.” Imeneyi ndi njira imodzi mwa njira zimene Yehova ankatidyetsera mwauzimu.

Dalitso Limene Sitinkaliyembekezera Kenako Mavuto Ambiri

Ndinatulutsidwa chakumapeto kwa 1950. Ndinabwerera kunyumba ndili wodwala, thupi langa lisakuoneka bwino, ndili mafupa okhaokha, komanso sindinkadziŵa kuti kunyumba akandilandira bwanji. Si mmene ndinasangalalira kuonananso ndi mkazi wanga ndi ana anga! Chosangalatsa kwambiri chinali chakuti, ndinadabwa kwambiri kupeza kuti Frosini waleka kundida. Makalata amene ndinamulembera ndili ku ndende anathandiza kwambiri. Kupirira ndi kulimbika mtima kwanga kunam’khudza mtima Frosini. Patangopita nthaŵi pang’ono, ndinakambirana naye kwanthaŵi yaitali nkhani yokhazikitsa mtendere pakati pathu. Anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kukhulupirira Yehova ndi zimene walonjeza. Limodzi la masiku amene ndinasangalala kwambiri pamoyo wanga ndi mu 1952 pamene ndinamubatiza monga mtumiki wa Yehova wodzipatulira.

Mu 1955 tinayamba kugaŵira wansembe aliyense kabuku kakuti Christendom or Christianity​—Which One Is “the Light of the World”? Ndinamangidwa ndipo ndinakaimbidwa mlandu pamodzi ndi Mboni zinzanga zingapo. Panali milandu yambiri yokhudza Mboni za Yehova moti khoti linakonza nthaŵi yapadera yozenga milandu yonseyo. Patsiku limeneli, panabwera anthu onse a zamalamulo a m’chigawochi ndipo m’chipinda chozengera milandu chinali chodzaza ndi ansembe. Bishopu ankayenda uku ndi uku m’mipata yodutsa anthu ali ndi nkhaŵa. Wansembe wina anandisumira mlandu woti ndinali kutembenuza anthu. Woweruza milandu anamufunsa kuti: “Kodi chikhulupiriro chako n’chofooka zedi moti ungatembenuke mwa kungoŵerenga bulosha?” Wansembeyo anangoti kukamwa pululu. Anandipeza kuti ndinalibe mlandu, koma abale ena anagamulidwa kuti akhale m’ndende miyezi sikisi.

Zaka zotsatira, tinali akabwerebwere ku ndende ndipo milandu ku khoti inachuluka zedi. Kusamalira milandu kunachititsa maloya athu kutanganidwa kwambiri nthaŵi zonse. Ndinatengeredwa ku khoti maulendo 17. Ngakhale kuti panali chitsutso, tinali kulalikira nthaŵi zonse. Tinalandira mosangalala ntchito imeneyi, ndipo ziyeso zamoto zinayenga chikhulupiriro chathu.​—Yakobo 1:2, 3.

Mwayi Wautumiki Watsopano Ndiponso Mavuto

Mu 1957 tinasamukira ku Athens. Patapita nthaŵi pang’ono, ndinasankhidwa kukatumikira ku mpingo watsopano wongokhazikitsidwa kumene. Chifukwa chakuti mkazi wanga anathandiza ndi mtima wonse zinapangitsa kuti moyo wathu usakhale wolira zambiri ndiponso kutsogoza zinthu zauzimu. Choncho tinkatha kuthera nthaŵi yathu  yambiri mu ntchito yolalikira. Mu zaka zapitazi, takhala tikupemphedwa kusamukira ku mipingo yosiyanasiyana kumene kunali kosoŵa olalikira.

Mu 1963 mwana wanga anakwanitsa zaka 21 ndipo anafunika kuti akamulembe usilikali. Chifukwa cha kusatenga mbali m’zinthu zimenezi, Mboni zonse zimene zinatengedwa zinamenyedwa, kunyozedwa ndiponso kuchititsidwa manyazi. N’zimenenso zinachitikira mwana wanga. Choncho ndinam’patsa bulangete langa lija limene ndinali nalo ku Makrónisos kuti limulimbikitse monga chizindikiro chakuti atsatire chitsanzo cha anthu okhulupirika a m’mbuyomo. Abale amene anadulilidwa samani anali kuwazenga milandu ku khoti la asilikali ndipo kaŵirikaŵiri anali kugamulidwa kukhala m’ndende zaka kuyambira ziŵiri mpaka zinayi. Atatulutsidwa anaitanidwanso ndipo anawagamulanso kachiŵiri. Monga mtumiki wa chipembedzo, ndinali kupita ndende zosiyanasiyana ndipo ndinkaonana nthaŵi zochepa ndi mwana wanga komanso Mboni zina zokhulupirika. Mwana wanga anakhala m’ndende kwa zaka zoposa sikisi.

Yehova Anatilimbikitsa

Ku Greece kutayambanso ufulu wachipembedzo, ndinali ndi mwayi wotumikira monga mpainiya wapadera kwa nthaŵi yochepa pachilumba cha Rhodes. Ndiyeno mu 1986 panafunika anthu olalikira ku Sitía, Crete, kumene ndinayambira ntchito yanga yachikristu. Ndinavomera mosangalala ntchito imeneyi kukatumikiranso ndi okhulupirira anzanga okondedwa amene ndinawadziŵa kuyambira ndili mwana.

Monga munthu wachikulire kwambiri pa achibale anga, ndine wosangalala kuona achibale pafupifupi 70 akutumikira Yehova mokhulupirika. Ndipo chiŵerengerochi chikukulirakulirabe. Ena atumikira monga akulu, atumiki otumikira, apainiya, pa Beteli ndiponso oyang’anira oyendayenda. Chikhulupiriro changa chayesedwa mu ng’anjo yamoto ya mavuto kwa zaka zoposa 58. Tsopano ndili ndi zaka 93, ndipo ndikayang’ana m’mbuyo sindidandaula kuti ndatumikira Mulungu. Wandipatsa mphamvu kuti ndimvere mawu ake achikondi akuti: “Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga.”​—Miyambo 23:26.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Onani Nsanja ya Olonda ya December 1, 1999, masamba 30-31.

^ ndime 11 Ansembe a Tchalitchi cha Greek Orthodox amaloledwa kukwatira.

^ ndime 12 Kuti muone mbiri ya moyo wa Emmanuel Lionoudakis, onani Nsanja ya Olonda, ya September 1, 1999, masamba 25-29.

^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma pano sililikusindikizidwanso.

^ ndime 15 Kuti muone kupambana mlandu kwa Minos Kokkinakis, onani Nsanja ya Olonda, ya September 1, 1993, masamba 27-31.

[Bokosi patsamba 27]

Makrónisos Chilumba Choopsa

Kwa zaka khumi, kuchokera mu 1947 mpaka 1957, chilumba chopanda zomera ndiponso chokhala kwa chokha cha Makrónisos chinali ndi akaidi oposa 100,000. Pa anthu ameneŵa panali Mboni zokhulupirika zambiri zimene zinatumizidwa kumeneko chifukwa cha kusaloŵerera m’zochitika za dziko monga Akristu. Kaŵirikaŵiri amene anachititsa kuti anthu ameneŵa awasamutsire kumeneko anali atsogoleri a chipembedzo cha Greek Orthodox amene ankaimba mlandu wonama Mboni kuti zinali zachikomyunizimu.

Pankhani ya “kukonza zinthu” kumene anali kuchita ku Makrónisos, insaikulopediya yachigiriki ya Papyros Larousse Britannica imati: “Njira zozunzira anthu mwankhanza, . . . mmene anthu ankakhalira kumeneko, zinali zosavomerezeka kwa anthu a maganizo awo abwino, ndipo zoipa zimene alonda anali kuchitira akaidi . . . n’zochititsa manyazi pa mbiri ya Greece.”

Mboni zina zinauzidwa kuti sizituluka mpaka zitasiya zikhulupiriro zawo zachipembedzo. Komabe, Mboni zimenezi zinakhulupirikabe kwambiri. Komanso, akaidi ena andale analandira choonadi cha Baibulo chifukwa chokhala ndi Mboni.

[Chithunzi patsamba 27]

Minos Kokkinakis (wachitatu kuyambira kumanja) ndi ine (wachinayi kuyambira kumanzere) pa chilumba cholangilako anthu cha Makrónisos

[Chithunzi patsamba 29]

Ndikugwira ntchito ndi Mboni inzanga ku Sitía, Crete, kumene ndinatumikira ndili mnyamata