Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhalitsa Ndiponso Kusangalala pa Ntchito Kukuvuta

Kukhalitsa Ndiponso Kusangalala pa Ntchito Kukuvuta

 Kukhalitsa Ndiponso Kusangalala pa Ntchito Kukuvuta

“UFULU wogwira ntchito” ndi wofunika kwambiri kwa anthu onse, malinga ndi chikalata cha mfundo za ufulu wa chibadwidwe cha Universal Declaration of Human Rights, chimene bungwe la United Nations linatulutsa. Komabe, ufulu umenewo siwotsimikizika nthaŵi zonse. Pali zinthu zambiri zimene zimapangitsa kuti munthu akhalitse pantchito, kuyambira mmene chuma chikuyendera m’dzikolo mpaka mmene malonda akuyendera padziko lonse. Komabe, ntchito ikatha kapena ikamaoneka kuti itha, anthu nthaŵi zambiri amachita zionetsero, ziwawa, ndiponso kunyanyala ntchito. Ndi m’mayiko ochepa okha mmene simuchitika zimenezi. Wolemba mabuku wina ananena kuti ngakhale liwulo lakuti “ntchito, limayambitsa mkwiyo monga mmene lakhalira nthaŵi zonse.”

Timafunikira ntchito pa zifukwa zambiri. Kuwonjezera pa kutithandiza kupeza ndalama, ntchito imatithandiza kukhala ndi maganizo abwino. Imakwaniritsa chikhumbo cha munthu aliyense chofuna kukhala wopindulitsa ndiponso kukhala ndi cholinga pa moyo. Imatithandizanso kudziona kuti ndife ofunika. N’chifukwa chake, ngakhale anthu amene sasoŵa ndalama zoti azipezera zofunika pa moyo kapena amene afika poti ayenera kupuma pantchito, amafuna kupitirizabe kugwira ntchito. Inde, ntchito ndi yofunika kwambiri moti ikasoŵa pamakhala mavuto aakulu okhudza kakhalidwe ka anthu.

Komabe, pali ena amene ali pantchito koma amakumana ndi mavuto ambiri kuntchitoko moti sasangalala nayo. Mwachitsanzo, chifukwa cha mpikisano waukulu pankhani zamalonda masiku ano, makampani ambiri akuchotsa anthu ena ntchito kuti achepetse ndalama zimene amagwiritsira ntchito. Zimenezi zingawonjezere mtolo wina kwa antchito otsalawo, omwe angafunike kugwiranso ntchito ina kuwonjezera pantchito imene amagwira.

Umisiri wamakono, womwe ndi woti ufeŵetseko moyo ndiponso kuti ntchito izigwirika bwino, uyenera kuti wawonjezera mavuto ena pantchito. Mwachitsanzo, makompyuta, makina otumizira uthenga a fax, ndi intaneti zimachititsa anthu kusankha ngati akufuna kukagwirira ntchito kunyumba akaŵeruka kuntchito. Zimenezi zimachititsa kukhala kovuta kusiyanitsa kunyumba ndi kuofesi. Wantchito wina anaona kuti makina a pakampani pake amene amalira munthu amene wanyamula makinawo akamafunidwa, ndiponso telefoni ya m’manja zinali ngati chingwe chimene anam’manga nacho m’khosi, bwana wake n’kumamukoka.

M’dziko lino limene nkhani zachuma ndiponso kagwiridwe ka ntchito zikungosinthasintha, anthu achikulire ali ndi mantha aakulu akuti anthu amawaona ngati sangachite zaphindu pamene sanafike msinkhu woterowo. Pankhani  imeneyi, yemwe kale anali mtsogoleri wa bungwe loona za ufulu wa anthu la Human Rights Commission, Chris Sidoti, anati: “Zikuoneka kuti anthu ambiri akuganiza kuti munthu ukapitirira zaka 39, sungathe kugwira bwino ntchito pa kompyuta ndiponso pogwiritsa ntchito zipangizo zina za umisiri wamakono.” Motero, ogwira ntchito ambiri akhama amene kale akanaonedwa kuti ali pamsinkhu woti angachite zinthu zopindulitsa kwambiri, masiku ano akuwaona kuti akula kwambiri moti sangathe kugwira bwino ntchito. Vuto lalikulutu limeneli!

N’zomveka kuti kulimbikira ntchito ndi kukhulupirika pa kampani kwaloŵa pansi m’zaka zimene zangotha kumenezi. Magazini ina ya ku France yakuti Libération, inati: “Makampani akamachotsa anthu ntchito chifukwa choti malonda angosokonezeka pang’ono, kukhulupirika pa kampani kumakhala kopanda ntchito. Munthu ufunikadi kugwira ntchito koma uzitero kuti upindule iweyo, osati kupindulitsa kampani.”

Ngakhale kuti pali mavuto ambiri otereŵa, anthu akufunitsitsabe kugwira ntchito. Motero, kodi m’nthaŵi ino imene zinthu zikungosinthasintha, munthu angatani kuti akhale ndi maganizo abwino a ntchito ndiponso panthaŵi yomweyo, kukhala ndi maganizo okhalitsa ndi kusangalala pantchito?

[Chithunzi patsamba 3]

Umisiri wamakono uyenera kuti wawonjezera mavuto pantchito