Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Akumva” Uthenga wa Ufumu ku Brazil

“Akumva” Uthenga wa Ufumu ku Brazil

 Olengeza Ufumu Akusimba

“Akumva” Uthenga wa Ufumu ku Brazil

KU Brazil, anthu ambiri a Mboni za Yehova akulolera ntchito yovuta yophunzira Chinenero Cholankhula ndi Manja chakumeneko, kuti athe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu Osamva. Khama lawo likupindula kwambiri, monga momwe nkhani zotsatirazi zikusonyezera.

Eva, * yemwe ndi mayi wosamva wa ku São Paulo, anayamba kuphunzira chinenero cholankhula ndi manja nthaŵi imene iye ndi ana ake atatu anayamba kukhalira limodzi ndi mwamuna wina wosamva. Eva ndi chibwenzi chakecho atapita kusitolo, anakumana ndi gulu la Mboni zosamva ndipo anapemphedwa kuti adzafike ku msonkhano pa Nyumba ya Ufumu. Iwo anavomera akuganiza kuti kukhala kucheza.

Popeza kuti Eva sankachidziŵa kwenikweni chinenero cholankhula ndi manja, pamsonkhanowo sanatolepo zinthu zambiri. Msonkhanowo utatha, Mboni zingapo zinamuitanira ku nyumba kwawo kuti akamwe zoziziritsa kukhosi. Mwa kugwiritsira ntchito zithunzi za mu bulosha lakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, anamufotokozera lonjezo la Mulungu lakuti m’tsogolo muno dzikoli lidzakhala paradaiso. Eva anakonda zimene anaphunzira ndipo anayamba kumafika pa misonkhano nthaŵi zonse.

Patangopita kanthaŵi pang’ono, Eva anathetsa chibwenzi chake chija n’cholinga chofuna kutsatira miyezo ya m’Baibulo pamoyo wake. Ngakhale kuti achibale ake anam’tsutsa kwambiri, analimbikirabe mwauzimu ndipo anabatizidwa mu 1995. Patatha miyezi sikisi, Eva anakhala mpainiya, kapena kuti wolengeza Ufumu wanthaŵi zonse. Kuyambira nthaŵi imeneyo wathandiza anthu anayi osamva kufika pozipatulira ndi kubatizidwa.

Carlos anabadwa ali wosamva. Kuyambira ali mwana anali wokonda mankhwala osokoneza bongo, chiwerewere ndiponso umbava. Atawopsezedwa ndi zigaŵenga zimene anali kulimbana nazo, iye anathaŵira ku São Paulo ndipo anakakhala ndi João kwanthaŵi yochepa. João anali wosamva ndipo anali ndi makhalidwe oipa ngati Carlos.

Patapita zaka zingapo, Carlos anaphunzira uthenga wa Ufumu, ndipo unam’limbikitsa kuyeretsa moyo wake ndiponso kulembetsa mwalamulo ukwati wake. Atakwaniritsa zimene Malemba amafuna, Carlos anabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova. Panthaŵi imeneyi, Carlos asakudziŵa, João anamvanso uthenga wabwino ndipo nayenso anasintha kwambiri moyo wake. João ataphunzira kuti Yehova safuna kugwiritsira ntchito mafano, anataya mafano a “oyera mtima” amene anali nawo. João atasiya moyo wake wakale, nayenso anabatizidwa.

Si mmene Carlos ndi João anasangalalira atakumana ku Nyumba ya Ufumu ndi kuona mmene onse asinthira! Pano onse ndi mitu ya mabanja yodalirika ndipo ndi olengeza Ufumu achangu.

Pakalipano ku Brazil, kuli mipingo 30 ndi magulu 154 a chinenero cholankhula ndi manja. Kuli ofalitsa oposa 2,500, ndipo pa anthu ameneŵa 1,500 ndi osamva. Ku Brazil, pa Misonkhano Yachigawo ya anthu osamva ya chaka cha 2001 yakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu,” panali anthu oposa 3,000 ndipo panabatizidwa anthu 36. Ndi dalitso la Yehova, tikukhulupirira kuti anthu osamva ena ambiri adzalandira uthenga wa Ufumu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Tasintha mayina.