Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikhulupiriro Chanu N’cholimba Bwanji?

Kodi Chikhulupiriro Chanu N’cholimba Bwanji?

 Kodi Chikhulupiriro Chanu N’cholimba Bwanji?

“Ndi chikhulupiriro muimadi.”​—2 AKORINTO 1:24.

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro, ndipo chingalimbe bwanji?

ATUMIKI a Yehova amadziŵa kuti ayenera kukhala ndi chikhulupiriro. Ndipotu, ‘popanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa Mulungu.’ (Ahebri 11:6) Motero, timachita bwino kupempherera mzimu woyera ndiponso chikhulupiriro, chomwe ndi mbali ya chipatso chabwino kwambiri cha mzimuwo. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23) Kutsanzira chikhulupiriro cha okhulupirira anzathu kungalimbitsenso khalidwe limeneli mwa ife.​—2 Timoteo 1:5; Ahebri 13:7.

2 Chikhulupiriro chathu chidzalimba kwambiri ngati tilimbikira kutsatira zimene Mawu a Mulungu amauza Akristu onse. Chikhulupiriro chingawonjezeke ngati tiŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kuphunzira mwakhama Malemba pogwiritsa ntchito zofalitsa zimene timalandira kudzera mwa “mdindo wokhulupirika.” (Luka 12:42-44; Yoswa 1:7, 8) Timalimbikitsidwa ndi chikhulupiriro cha ena mwa kupezeka nthaŵi zonse pa misonkhano yachikristu yaing’ono ndi yaikulu. (Aroma 1:11, 12; Ahebri 10:24, 25) Ndiponso chikhulupiriro chathu chimalimba tikamalankhula ndi ena muutumiki.​—Salmo 145:10-13; Aroma 10:11-15.

3. Kodi pankhani ya chikhulupiriro, akulu achikristu achikondi amatithandiza bwanji?

3 Akulu achikristu achikondi amatithandiza  kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa kutipatsa malangizo ndi chilimbikitso cha m’Malemba. Iwo ali ndi maganizo ofanana ndi a mtumwi Paulo amene anauza Akorinto kuti: “Tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.” (2 Akorinto 1:23, 24) Baibulo lina limati: “Tikugwira ntchito limodzi ndi inu kuti musangalale, chifukwa chikhulupiriro chanu n’cholimba.” (Contemporary English Version) Olungama amakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro. Kunena zoona, palibe amene angakhale ndi chikhulupiriro m’malo mwathu kapena kutichititsa kukhala anthu okhulupirika. Pankhani imeneyi, ‘tiyenera kusenza katundu wathu.’​—Agalatiya 3:11; 6:5.

4. Kodi nkhani za m’Malemba za atumiki okhulupirika a Mulungu zingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu?

4 M’Malemba muli nkhani zambiri za anthu amene anali ndi chikhulupiriro. Mwina tikudziŵa bwinobwino zinthu zambiri zapadera zimene iwo anachita, koma kodi timadziŵanso bwino chikhulupiriro chimene ankasonyeza tsiku ndi tsiku mwina kwa nthaŵi yonse ya moyo wawo wautali? Kusinkhasinkha mmene anasonyezera khalidwe limeneli m’zochitika zimene zikufanana ndi zathu kungathandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu.

Chikhulupiriro Chimatilimbitsa Mtima

5. Kodi pali umboni wotani wa m’Malemba wakuti chikhulupiriro chimatilimbikitsa kulengeza mawu a Mulungu molimba mtima?

5 Chikhulupiriro chimatilimbitsa kuti tilengeze mawu a Mulungu molimba mtima. Enoke analosera molimba mtima chiweruzo cha Mulungu. Iye anati: “Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi, kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zawo zonse zosapembedza, zimene anazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.” (Yuda 14, 15) Atamva mawu amenewo, adani a Enoke osaopa Mulungu mosakayika anafuna kumupha. Komabe, iye analankhula mopanda mantha ali ndi chikhulupiriro, ndipo Mulungu “anam’tenga” mwa kum’gonetsa m’tulo ta imfa, mwachionekere sanalole kuti avutike ndi kuwawa kwa imfa. (Genesis 5:24; Ahebri 11:5) Zozizwitsa zimenezo sizitichitikira, koma Yehova amayankha mapemphero athu kuti tilengeze mawu ake mwa chikhulupiriro ndiponso molimba mtima.​—Machitidwe 4:24-31.

6. Kodi chikhulupiriro ndi kulimba mtima zimene Mulungu anam’patsa Nowa zinamuthandiza bwanji?

6 Ndi chikhulupiriro, Nowa “anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake.” (Ahebri 11:7; Genesis 6:13-22) Nowa analinso “mlaliki wa chilungamo” amene analengeza molimba mtima chenjezo la Mulungu kwa anthu a m’nthaŵi yake. (2 Petro 2:5) Anthuwo ayenera kuti anali kunyoza uthenga wake wakuti Chigumula chinali kubwera, monga mmenenso anthu ena amanyozera tikamawauza umboni wa m’Malemba wakuti dongosolo la zinthu limene lilipoli liwonongedwa posachedwapa. (2 Petro 3:3-12) Komabe, mofanana ndi Enoke ndi Nowa, tingawauze anthu uthenga umenewo chifukwa cha chikhulupiriro ndi kulimba mtima zimene Mulungu watipatsa.

Chikhulupiriro Chimatichititsa Kuleza Mtima

7. Kodi Abrahamu ndi ena anasonyeza bwanji chikhulupiriro ndi kuleza mtima?

7 Tifunika chikhulupiriro ndi kuleza mtima, makamaka pamene tikudikira mapeto a dongosolo loipali. Ena mwa ‘amene adzaloŵa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima’ ndi kholo lakale loopa Mulungu, Abrahamu. (Ahebri 6:11, 12) Ndi chikhulupiriro, iye anachoka mumzinda wa Uri, ngakhale kuti mzindawu unali ndi zinthu zabwino zambiri, ndipo anakhala mlendo m’dziko lachilendo limene Mulungu anamulonjeza. Isake ndi Yakobo anawalonjezanso zimenezi. Komabe, “iwo  onse adamwalira m’chikhulupiriro, osalandira malonjezano.” Ndi chikhulupiriro, iwo ‘anakhumba [dziko] lina loposa, ndilo la m’Mwamba.’ Chifukwa cha zimenezi, Mulungu “adawakonzera mudzi.” (Ahebri 11:8-16) Inde, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo ndiponso akazi awo oopa Mulungu, anayembekezera moleza mtima Ufumu wakumwamba wa Mulungu, mmene iwo adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo padziko lapansi.

8. Kodi Abrahamu, Isake, ndi Yakobo anasonyeza kuleza mtima ndi chikhulupiriro ngakhale kuti zinthu zinali bwanji?

8 Abrahamu, Isake, ndi Yakobo sanataye chikhulupiriro. Dziko lolonjezedwa silinakhale m’manja mwawo, ndipo sanaone mitundu yonse ikudzidalitsa kudzera mu mbewu ya Abrahamu. (Genesis 15:5-7; 22:15-18) Ngakhale kuti ‘mudzi womangidwa ndi Mulungu’ sunakhazikitsidwe mpaka patapita zaka zambirimbiri, amuna ameneŵa anapitiriza kusonyeza chikhulupiriro ndi kuleza mtima pamoyo wawo wonse. Inde, ifenso tifunika kuchita chimodzimodzi masiku ano popeza kuti Ufumu wa Umesiya unakhazikitsidwa kumwamba.​—Salmo 42:5, 11; 43:5.

Chikhulupiriro Chimatichititsa Kukhala ndi Zolinga Zapamwamba

9. Kodi chikhulupiriro chimakhudza bwanji zolinga?

9 Makolo akale okhulupirika sanatengere makhalidwe oipa a Akanani, chifukwa anali ndi zolinga zapamwamba. Mofananamo, chikhulupiriro chimatichititsa kukhala ndi zolinga zauzimu zimene zimatithandiza kupeŵa kuloŵerera m’dziko limene lili m’manja mwa woipayo, Satana Mdyerekezi.​—1 Yohane 2:15-17; 5:19.

10. Kodi timadziŵa bwanji kuti Yosefe anali ndi zolinga zapamwamba zoposa kukhala wotchuka m’dzikoli?

10 Motsogoleredwa ndi Mulungu, Yosefe, mwana wa Yakobo anali woyang’anira zakudya ku Igupto, koma sichinali cholinga chake kukhala munthu wotchuka m’dzikoli. Chifukwa chokhulupirira kuti malonjezo a Yehova adzakwaniritsidwa, Yosefe ali ndi zaka 110 anauza abale ake kuti: “Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m’dziko muno kubwera kumka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isake, ndi kwa Yakobo.” Yosefe anapempha kuti akamuike m’manda m’dziko lolonjezedwa. Atamwalira, anakonza thupi lake n’kuliika m’bokosi ku Igupto. Koma pamene Aisrayeli anamasulidwa ku ukapolo wa ku Igupto, mneneri Mose anakonza zotenga mafupa a Yosefe kuti akawaike m’manda ku Dziko Lolonjezedwa. (Genesis 50:22-26; Eksodo 13:19) Chikhulupiriro changati cha Yosefe chiyenera kutichititsa kukhala ndi zolinga zapamwamba zoposa kukhala wotchuka m’dzikoli.​—1 Akorinto 7:29-31.

11. Kodi Mose anasonyeza m’njira zotani kuti anali ndi zolinga zauzimu?

11 Mose, ‘anasankha kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, osati kukhala nazo zokondweretsa zoipa zakanthaŵi,’ monga mmodzi mwa anthu ophunzira kwambiri a m’banja lachifumu la ku Igupto. (Ahebri 11:23-26; Machitidwe 7:20-22) Zimenezi zinamulepheretsa kukhala wotchuka m’dzikoli. Ndiponso mwina mwambo wa  maliro ake ukanakhala wapamwamba zedi, akanagona m’bokosi lapamwamba n’kumuika pa malo ena otchuka a ku Igupto, koma iye anasiya zonsezo. Kodi zimenezo zikanakhala ndi phindu lanji poyerekezera ndi mwayi wokhala “munthu wa Mulungu,” nkhoswe ya pangano la Chilamulo, mneneri wa Yehova, ndiponso wolemba Baibulo? (Ezara 3:2) Kodi mumalakalaka mutatsogola m’dzikoli, kapena chikhulupiriro chakuchititsani kukhala ndi zolinga zapamwamba zauzimu?

Chikhulupiriro Chimatithandiza Kuti Tikhale ndi Moyo Wopindulitsa

12. Kodi chikhulupiriro chinakhudza bwanji moyo wa Rahabi?

12 Chikhulupiriro chimawathandiza anthu kukhala ndi zolinga zabwino komanso moyo wopindulitsa. Rahabi wa ku Yeriko ayenera kuti anaona kuti moyo wake unali wopanda tanthauzo pamene anali mkazi wadama. Koma zimenezo zinasintha kwambiri pamene anakhulupirira. Iye ‘anayesedwa wolungama ndi ntchito [za chikhulupiriro], popeza analandira amithenga [achiisrayeli] nawatulutsa adzere njira ina,’ motero anapeŵa adani awo achikanani. (Yakobo 2:24-26) Atazindikira kuti Yehova ndiye Mulungu woona, Rahabi anasonyezanso chikhulupiriro mwa kusiya khalidwe lake ladama. (Yoswa 2:9-11; Ahebri 11:30, 31) Anakwatiwa ndi mtumiki wa Yehova, osati Mkanani wosakhulupirira. (Deuteronomo 7:3, 4; 1 Akorinto 7:39) Rahabi anali ndi mwayi waukulu wokhala kholo lachikazi la Mesiya. (1 Mbiri 2:3-15; Rute 4:20-22; Mateyu 1:5, 6) Mofanana ndi anthu ena, omwe mwa iwonso muli amene asiya makhalidwe oipa, iye adzalandiranso mphoto ina yodzaukitsidwa kudzakhala ndi moyo pa dziko lapansi.

13. Kodi Davide anachita tchimo lotani ndi Bateseba, koma kodi anasonyeza mtima wotani?

13 Atasiya moyo wake wauchimo, Rahabi mwachionekere anapitiriza kutsatira njira yoongoka. Komabe, ena amene azipatulira kwa Mulungu kwa nthaŵi yaitali achita machimo aakulu. Mfumu Davide inachita chigololo ndi Bateseba, inaphetsa mwamuna wa mkaziyu ku nkhondo, ndiyeno inamutenga kukhala mkazi wake. (2 Samueli 11:1-27) Polapa ali ndi chisoni chachikulu, Davide anachonderera Yehova kuti: “Musandichotsere mzimu wanu woyera.” Davide anakhalabe ndi mzimu wa Mulungu. Anakhulupirira kuti Yehova, mwa chifundo chake, sadzapeputsa “mtima wosweka ndi wolapa [“woswanyika,”NW]” chifukwa cha tchimo. (Salmo 51:11, 17; 103:10-14) Chifukwa  cha chikhulupiriro chawo, Davide ndi Bateseba anadalitsidwa ndi mwayi wokhala ena mwa makolo a Mesiya.​—1 Mbiri 3:5; Mateyu 1:6, 16; Luka 3:23, 31.

Chikhulupiriro Cholimbitsidwa mwa Kutsimikiziridwa

14. Kodi Gideoni anamutsimikizira bwanji, ndipo kodi nkhani imeneyi ingakhudze bwanji chikhulupiriro chathu?

14 Ngakhale kuti timayenda ndi chikhulupiriro, nthaŵi zina tingafune kutsimikiziridwa kuti Mulungu atithandiza. Zimenezo n’zimene zinachitikira Woweruza Gideoni, mmodzi mwa anthu “amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu.” (Ahebri 11:32, 33) Pamene Amidyani ndi anzawo anaukira a Israyeli, mzimu wa Mulungu unamukuta Gideoni. Pofuna kuti amutsimikizire kuti Yehova anali naye, iye anapempha kuti ayese mwa kuika chikopa chaubweya popunthira tirigu usiku. Pa mayeso oyamba, mame anakhala pa chikopa chokha pamene panthaka ponse panali pouma. Pa mayeso achiŵiri, mame anakhala panthaka pokha pamene pachikopa panali pouma. Atalimbitsidwa ndi kumutsimikizira kumeneku, Gideoni amene anali wosamala anachita zinthu mwachikhulupiriro ndipo anagonjetsa adani a Israyeli. (Oweruza 6:33-40; 7:19-25) Ngati tifuna kuti titsimikiziridwe pamene tifunika kusankha zochita, sizitanthauza kuti tikusoŵa chikhulupiriro. Ndipotu timasonyeza chikhulupiriro mwa kufufuza Baibulo ndi zofalitsa zachikristu ndiponso mwa kupemphera kuti mzimu woyera utitsogolere posankha zochita.​—Aroma 8:26, 27.

15. Kodi kusinkhasinkha chikhulupiriro cha Baraki kungatithandize bwanji?

15 Chikhulupiriro cha Woweruza Baraki chinalimbitsidwa mwa kumutsimikizira ndi mawu olimbikitsa. Mneneri wamkazi Debora anamulimbikitsa kutsogolera populumutsa Aisrayeli m’manja mwa Yabini, mfumu yachikanani, imene inali kuwapondereza. Ndi chikhulupiriro ndiponso atamutsimikizira kuti Mulungu amuthandiza, Baraki anatsogolera kunkhondo amuna okwana 10,000 amene analibe zida zokwanira ndipo anagonjetsa gulu la asilikali lalikulu la Yabini lolamulidwa ndi Sisera. Anakondwerera kupambana kumeneko m’nyimbo yosangalatsa ya Debora ndi Baraki. (Oweruza 4:1–5:31) Debora analimbikitsa Baraki kukhala mtsogoleri wa Israyeli wosankhidwa ndi Mulungu, ndipo iye anali mmodzi mwa atumiki a Yehova amene ndi chikhulupiriro “anapitikitsa magulu a nkhondo yachilendo.” (Ahebri 11:34) Kusinkhasinkha mmene Mulungu anadalitsira Baraki chifukwa chochita zinthu mwachikhulupiriro kungatilimbikitse kuchitapo kanthu ngati tikukayikakayika kukwaniritsa ntchito yovuta potumikira Yehova.

Chikhulupiriro Chimalimbikitsa Mtendere

16. Kodi Abrahamu anapereka chitsanzo chabwino chotani pochita zinthu mwamtendere ndi Loti?

16 Monga mmene chikhulupiriro chimatithandizira kukwaniritsa ntchito yovuta potumikira Mulungu, chimathandizanso kulimbikitsa bata ndi mtendere. Abrahamu amene anali wachikulire analola Loti mwana wa mphwake yemwe anali wocheperako kusankha malo abwino kwambiri odyetserako ziweto pamene abusa awo anakangana ndipo kunafunika kuti asiyane. (Genesis 13:7-12) Abrahamu ayenera kuti anali kupemphera mwachikhulupiriro kuti Mulungu amuthandize pothetsa vuto limeneli. M’malo moika zofuna zake patsogolo, iye anathetsa nkhaniyo mwamtendere. Ngati tasemphana maganizo ndi mbale wathu wachikristu, tiyeni tipemphere mwachikhulupiriro ndi ‘kufunafuna mtendere,’ tikukumbukira chitsanzo cha Abrahamu cha chikondi ndi kuganizira ena.​—1 Petro 3:10-12.

17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kusemphana maganizo kwa Paulo, Barnaba ndi Marko kunathetsedwa mwamtendere?

17 Taonani mmene kugwiritsa ntchito mfundo zachikristu mwachikhulupiriro kungatithandizire kulimbikitsa mtendere. Pamene Paulo anatsala pang’ono kuyamba ulendo wake wachiŵiri wa umishonale, Barnaba anavomereza zoti akayenderenso mipingo ya ku Kupro ndi ku Asia Minor. Komabe, Barnaba anafuna kuti atenge msuwani wake Marko paulendo wawowu. Paulo anakana chifukwa chakuti Marko anawasiya ku Pamfuliya. Panali “kupsetsana mtima,” ndipo mkanganowu unachititsa kuti asiyane. Barnaba anatengana ndi Marko kupita ku Kupro, pamene Paulo anasankha Sila kukhala nzake ndipo “anapita kupyola pa Suriya ndi Kilikiya, nakhazikitsa Mipingo.” (Machitidwe 15:36-41) Patapita nthaŵi, kusemphana maganizo kumeneku kunathetsedwa, chifukwa Marko anali ndi Paulo  ku Roma ndipo mtumwiyo anamuyamikira Marko. (Akolose 4:10; Filemoni 23, 24) Pamene Paulo anali mkaidi ku Roma cha m’ma 65 C.E., anauza Timoteo kuti: “Um’tenge Marko, adze pamodzi ndi iwe; pakuti ayenera kunditumikira.” (2 Timoteo 4:11) Paulo ayenera kuti anapempherera ndi chikhulupiriro ubwenzi wake ndi Barnaba ndi Marko, ndipo zimenezo zinachititsa kuti pakhale bata limene likugwirizana ndi “mtendere wa Mulungu.”​—Afilipi 4:6, 7.

18. N’chiyani chiyenera kuti chinachitikira Euodiya ndi Suntuke?

18 Popeza ndife opanda ungwiro, “timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri.” (Yakobo 3:2) Panabuka mavuto pakati pa akazi aŵiri achikristu, amene Paulo analemba za iwo kuti: “Ndidandaulira Euodiya, ndidandaulira Suntuke, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye. . . . Muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino.” (Afilipi 4:1-3) Mosakayika, akazi oopa Mulungu ameneŵa anathetsa vuto lawo mwamtendere pogwiritsa ntchito malangizo monga amene ali pa Mateyu 5:23, 24. Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba mwachikhulupiriro kudzathandiza kwambiri kulimbikitsa mtendere masiku ano.

Chikhulupiriro Chimatithandiza Kupirira

19. Kodi ndi vuto liti limene silinawononge chikhulupiriro cha Isake ndi Rebeka?

19 Ndi chikhulupiriro, tingapirirenso mavuto. Mwina tikuvutika maganizo chifukwa chakuti wina wa m’banja lathu wobatizidwa sanamvera Mulungu mwa kukwatira kapena kukwatiwa ndi wosakhulupirira. (1 Akorinto 7:39) Isake ndi Rebeka anavutika maganizo kwambiri chifukwa chakuti mwana wawo Esau anakwatira akazi osaopa Mulungu. Akazi ake achihiti “anapweteka mtima” wawo moti Rebeka ananena kuti: “Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Heti: akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Heti, onga ana aakazi a m’dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?” (Genesis 26:34, 35; 27:46) Komabe, vuto limeneli silinawononge chikhulupiriro cha Isake ndi Rebeka. Tiyenitu tikhalebe ndi chikhulupiriro cholimba ngati mavuto ena akutivuta kuwathetsa.

20. Kodi tikuona chitsanzo chotani cha chikhulupiriro mwa Naomi ndi Rute?

20 Naomi yemwe anali mkazi wamasiye ndiponso wokalamba anali Myuda, ndipo anadziŵa kuti akazi ena achiyuda angadzabereke ana amene adzakhala makolo a Mesiya. Komabe, popeza ana ake aamuna anamwalira opanda ana ndipo iye anapitirira msinkhu wobereka, mwayi woti banja lake lingadzakhale ena mwa makolo a Mesiya unali wochepa kwambiri. Komabe, mpongozi wake wamasiye, Rute, anakwatiwa ndi Boazi amene anali wachikulire, anam’balira mwana wamwamuna, ndipo anakhala kholo lachikazi la Yesu, Mesiyayo. (Genesis 49:10, 33; Rute 1:3-5; 4:13-22; Mateyu 1:1, 5) Chikhulupiriro cha Naomi ndi Rute chinagonjetsa mavuto ndipo chinawabweretsera chimwemwe. Ifenso tidzakhala ndi chimwemwe kwambiri ngati tikhalabe ndi chikhulupiriro ngakhale tikukumana ndi mavuto.

21. Kodi chikhulupiriro chimatichitira chiyani, ndipo tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

21 Ngakhale kuti sitikudziŵa chimene chitichitikire maŵa aliyense payekha, ndi chikhulupiriro tipirire bwinobwino vuto lililonse. Chikhulupiriro chimatichititsa kukhala olimba mtima ndiponso oleza mtima. Chimatithandiza kukhala ndi zolinga zapamwamba ndiponso moyo wopindulitsa. Chikhulupiriro chimathandiza kuti tikhale bwino ndi anthu ena ndipo chimagonjetsa mavuto. Ndiyetu tiyeni tikhale “a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Mwa mphamvu ya Mulungu wathu wachikondi Yehova, ndiponso kuti alemekezeke, tiyeni tipitirize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi pali umboni wa m’Malemba wotani wakuti chikhulupiriro chingatilimbitse mtima?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikhulupiriro chimatithandiza kukhala ndi moyo wopindulitsa?

• Kodi chikhulupiriro chimalimbikitsa bwanji mtendere?

• Kodi pali umboni wotani wakuti chikhulupiriro chimatithandiza kupirira mavuto?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 16]

Chikhulupiriro chinalimbitsa mtima Nowa ndi Enoke kulengeza mauthenga a Yehova

[Zithunzi patsamba 17]

Chikhulupiriro chonga cha Mose chimatichititsa kukhala ndi zolinga zauzimu

[Zithunzi patsamba 18]

Kutsimikiziridwa kuti Mulungu awathandiza kunalimbitsa chikhulupiriro cha Baraki, Debora, ndi Gideoni