Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Maso Kuposa Kale Lonse!

Khalani Maso Kuposa Kale Lonse!

 Khalani Maso Kuposa Kale Lonse!

“Tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.”​—1 ATESALONIKA 5:6.

1, 2. (a) Kodi mizinda ya Pompeii ndi Hekuleniya inali yotani? (b) Kodi ndi chenjezo lotani limene anthu ambiri a m’mizinda ya Pompeii ndi Hekuleniya ananyalanyaza, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

M’ZAKA 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Pompeii ndi Hekuleniya inali mizinda iŵiri ya Aroma yotchuka kwambiri imene inali pafupi ndi phiri la Vesuvius. Kunali malo osangalalira otchuka kwambiri kumene Aroma olemera ankapitako. M’mabwalo awo a maseŵero munkatha kukwana anthu oposa chikwi chimodzi ndipo ku Pompeii kunali bwalo lalikulu la maseŵero mmene pafupifupi anthu onse a m’tauniyo ankatha kukwanamo. Anthu ofukula za m’mabwinja atakafukula pamene panali mzinda wa Pompeii anapeza kuti panali nyumba zomwera mowa zokwana 118, zomwe zina ankatchoveramo njuga kapena kuchitiramo uhule. Zithunzi za pakhoma ndiponso zinthu zina zakale zimasonyeza kuti kunali makhalidwe oipa ndiponso kukondetsa chuma.

2 Pa 24 August, 79 C.E., phiri la Vesuvius linayamba kuphulika. Akatswiri odziŵa za kuphulika kwa phiri amakhulupirira kuti kuphulika koyamba, kumene kunatulutsa phala ndi phulutsa limene linakuta mizinda iŵiriyo sikukanalepheretsa anthu kuthaŵa. Indedi, zikuoneka kuti ambiri anathaŵadi. Koma ena amene anaona ngati ngoziyo inali yaing’ono kapena amene anangonyalanyaza zizindikiro zochenjeza, anaganiza zongokhala. Ndiyeno, cha pakati pa usiku, mpweya, phala, ndi miyala yambiri, zomwe zinali zotentha kwambiri, zinagwera pa mzinda wa Hekuleniya ndi chimkokomo chachikulu, ndipo zinapha anthu onse amene anatsala mu mzindawo. M’mawa mwake zimenezi zinachitikanso mumzinda wa Pompeii ndipo anthu onse mumzindawo anafa. Ndi tsoka lalikulutu ili lochitika chifukwa chosamvera zizindikiro zochenjeza!

Kutha kwa Dongosolo la Zinthu la Chiyuda

3. Kodi pali kufanana kotani pa chiwonongeko cha Yerusalemu ndi cha mizinda ya Pompeii ndi Hekuleniya?

3 Kutha kochititsa mantha kwa mizinda ya Pompeii ndi Hekuleniya kunali kochepa poyerekezera ndi chiwonongeko chomvetsa chisoni cha mzinda wa Yerusalemu zaka zisanu ndi zinayi m’mbuyomo, ngakhale kuti anthu ndi amene anachititsa chiwonongekocho. Anthu amati chiwonongeko chimenecho chinali “kuzinga mzinda kwa asilikali koopsa kwambiri m’mbiri yonse,” ndipo akuti Ayuda oposa wani miliyoni anafa. Komabe, monga mmene zinalili pa kuwonongeka kwa mizinda ya Pompeii ndi Hekuleniya, chiwonongeko cha Yerusalemu sichinangochitika popanda chenjezo.

4. Kodi ndi zizindikiro ziti zaulosi zimene Yesu anapereka pochenjeza otsatira ake kuti mapeto a dongosolo la zinthu anali pafupi, ndipo kodi zimenezi zinakwaniritsidwa bwanji koyamba mu zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino?

4 Yesu Kristu anali atalosera chiwonongeko cha mzindawo, ndipo analosera zimene zinali kudzachitika chiwonongekocho chitatsala pang’ono kuti chichitike. Anati padzakhala mavuto monga nkhondo, njala, zivomezi, ndi kusaweruzika. Padzakhalanso aneneri onyenga, koma uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa padziko lonse. (Mateyu 24:4-7, 11-14) Ngakhale kuti mawu a Yesu akukwaniritsidwa kwambiri masiku ano, anakwaniritsidwanso pang’ono kalelo. Nkhani ya zochitika za m’mbiri imati ku Yudeya kunali njala yadzaoneni. (Machitidwe 11:28) Wolemba mbiri wina wachiyuda, Josephus, anati kunali chivomezi ku Yerusalemu patangotsala pang’ono kuti mzindawo uwonongedwe. Pamene mapeto a Yerusalemu anayandikira, anthu anali kuukira mosalekeza, panali nkhondo zachiweniweni pakati pa magulu a ndale achiyuda, ndiponso  panali kupulula anthu m’mizinda ingapo mmene munali Ayuda ndi Akunja. Komabe, uthenga wabwino wa Ufumu unali kulalikidwa kwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”​—Akolose 1:23.

5, 6. (a) Kodi ndi mawu ati amene Yesu analosera amene anakwaniritsidwa mu 66 C.E.? (b) N’chifukwa chiyani anthu amene anafa pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E. anali ambiri?

5 Ndiyeno, mu 66 C.E., Ayuda anapandukira Aroma. Pamene Seshasi Galasi anatsogolera asilikali kukazinga mzinda wa Yerusalemu, otsatira a Yesu anakumbukira mawu Ake akuti: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali m’kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asaloŵemo.” (Luka 21:20, 21) Nthaŵi inafika yoti achoke mu Yerusalemu, koma kodi akanatuluka bwanji? Mosayembekezeka, Galasi anachoka ndi asilikali ake, zimene zinapereka mpata woti Akristu a ku Yerusalemu ndi ku Yudeya amvere mawu a Yesu ndi kuthawira ku mapiri.​—Mateyu 24:15, 16.

6 Patapita zaka zinayi, cha panthaŵi ya Paskha, asilikali achiroma anabwereranso motsogoleredwa ndi Kazembe Tito, amene anafunitsitsa kuthetseratu kupanduka kwa Ayuda. Asilikali ake anazungulira Yerusalemu ndipo anazinga “linga,” zimene zinachititsa kuthaŵa kukhala kovuta. (Luka 19:43, 44) Ngakhale kuti zinkaonekeratu kuti kukhala nkhondo, Ayuda ambirimbiri mu ufumu wonse wa Aroma anapita ku Yerusalemu kukachita phwando la Paskha. Tsopano anasoŵa kotulukira. Malinga ndi Josephus, alendo ameneŵa omwe anachita tsoka anali ena mwa khamu la anthu limene linafa pa kuzinga kwa Aroma kumeneku. * Pamene Yerusalemu anawonongedwa, pafupifupi munthu mmodzi mwa anthu asanu ndi aŵiri alionse achiyuda mu Ufumu wa Roma anafa. Chiwonongeko cha Yerusalemu ndi kachisi wake chinachititsa kuti dziko la Ayuda lithe pamodzi ndi dongosolo lawo la chipembedzo lotsatira Chilamulo cha Mose. *​—Marko 13:1, 2.

7. N’chifukwa chiyani Akristu okhulupirika anapulumuka pamene Yerusalemu anawonongedwa?

7 Mu 70 C.E., Akristu achiyuda akanaphedwa kapena kukhala akapolo pamodzi ndi ena onse a mu Yerusalemu. Komabe, malinga ndi umboni wa zochitika m’mbiri, iwo anamvera chenjezo la Yesu limene analipereka zaka 37 zimenezi zisanachitike. Anachoka mumzindawo ndipo sanabwereremonso.

Machenjezo a Atumwi a Panthaŵi Yake

8. Kodi Petro anaona kufunika kwa chiyani, ndipo kodi ndi mawu ati amene Yesu ananena omwe Petroyo ayenera kuti anali kuwaganizira?

8 Masiku ano, chiwonongeko chachikulu kwambiri chikuyandikira, chimene chidzathetsa dongosolo lonse la zinthu lino. Zaka zisanu ndi chimodzi Yerusalemu asanawonongedwe, mtumwi Petro anapereka langizo lofunika kwambiri  komanso la panthaŵi yake limene likugwira ntchito makamaka kwa Akristu masiku ano. Linali langizo lakuti: Khalani tcheru! Petro anaona kufunika koti Akristu atsitsimutse “mtima” wawo kuti asanyalanyaze “lamulo la Mbuye,” Yesu Kristu. (2 Petro 3:1, 2) Polimbikitsa Akristu kuti akhale tcheru, Petro mwachionekere anali kuganizira zimene Yesu anauza atumwi Ake patatsala masiku angapo kuti aphedwe. Iye anati: “Yang’anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziŵa nthaŵi yake.”​—Marko 13:33.

9. (a) Kodi ena angakhale ndi maganizo ati oika moyo pachiswe? (b) N’chifukwa chiyani kukhala ndi maganizo okayikira n’kuika moyo pachiswe?

9 Masiku ano, ena amafunsa monyoza kuti: “Lili kuti lonjezano la kudza kwake?” (2 Petro 3:3, 4) Mwachionekere, anthu oterowo amaganiza kuti zinthu sizikusintha kwenikweni, m’malo mwake zili monga mmene zakhalira nthaŵi zonse kuyambira pamene dziko linalengedwa. Kukayikira koteroko n’koika moyo pachiswe. Kukayikira kungafooketse kukhala kwathu tcheru, kutipangitsa kumangochita zofuna zathu basi. (Luka 21:34) Kuwonjezeranso pamenepo, monga mmene Petro ananenera, anthu onyozawo amaiwala Chigumula cha m’nthaŵi ya Nowa, chimene chinawononga dongosolo la zinthu la dziko lonse. Dziko linasinthadi nthaŵi imeneyo.​—Genesis 6:13, 17; 2 Petro 3:5, 6.

10. Kodi Petro akulimbikitsa ndi mawu otani anthu amene angakhale osaleza mtima?

10 Petro akuthandiza oŵerenga kalata yake kuti akhale oleza mtima mwa kuwakumbutsa chifukwa chake Mulungu nthaŵi zambiri sachitapo kanthu mwamsanga. Poyamba Petro akuti: “Tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.” (2 Petro 3:8) Popeza Yehova ali ndi moyo kosatha, angaganizire zinthu zonse ndipo angasankhe nthaŵi yabwino yochitapo kanthu. Ndiyeno Petro anafotokoza kuti Yehova amafuna kuti anthu kulikonse alape. Kuleza mtima kwa Mulungu kudzapulumutsa anthu ambiri amene akanawonongeka ngati akanachitapo kanthu mwamsanga. (1 Timoteo 2:3, 4; 2 Petro 3:9) Komabe, kuleza mtima kwa Yehova sikutanthauza kuti sadzachitapo kanthu. Petro anati: ‘Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala.’​—2 Petro 3:10.

11. N’chiyani chingatithandize kukhala maso mwauzimu, ndipo tingati zimenezi ‘zidzafulumizitsa’ tsiku la Yehova motani?

 11 Kuyerekezera kwa Petro n’kochititsa chidwi. Mbala n’zovuta kuzigwira, koma mlonda amene akhala maso usiku wonse angathe kuona akuba, kusiyana ndi mlonda amene amawodzera nthaŵi zonse. Kodi mlonda angatani kuti akhale maso? Kuzungulirazungulira kungathandize kuti akhale maso kusiyana ndi kungokhala pansi usiku wonse. Mofananamo, kukhala achangu mwauzimu kudzatithandiza monga Akristu kukhalabe maso. Motero Petro akutilimbikitsa kukhala otanganidwa “m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo.” (2 Petro 3:11) Kuchita zimenezi kudzatithandiza kupitiriza kukumbukira “kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” (2 Petro 3:12) N’zoona kuti sitingasinthe ndandanda yochitira zinthu ya Yehova. Tsiku lake lidzafika panthaŵi imene iye waika. Koma nthaŵi imene ilipo kuyambira pakalipano mpaka panthaŵiyo idzaoneka kuti yatha mofulumira tikakhala otanganidwa mu utumiki wake.​—1 Akorinto 15:58.

12. Kodi ife monga munthu payekha tingapindule bwanji ndi kuleza mtima kwa Yehova?

12 Motero, aliyense amene akuganiza kuti tsiku la Yehova likuchedwa akulimbikitsidwa kutsatira langizo la Petro loti ayembekezere moleza mtima nthaŵi yoikika ya Yehova. Inde, tingagwiritse ntchito mwanzeru nthaŵi yowonjezera ya kuleza mtima kwa Mulungu. Mwachitsanzo, tingapitirize kukulitsa makhalidwe abwino achikristu ndiponso kuuza ena ambiri uthenga wabwino kuposa mmene tikanachitira ngati Yehova akanati asapitirize kuleza mtima. Ngati tikhalabe maso, Yehova adzatipeza “mumtendere, opanda banga ndi opanga chirema” pamapeto pa dongosolo lino la zinthu. (2 Petro 3:14, 15) Lidzakhalatu dalitso lalikulu limenelo!

13. Kodi ndi mawu ati amene Paulo anauza Akristu a ku Tesalonika amene makamaka ndi oyenerera kwambiri masiku ano?

13 Paulo, m’kalata yake kwa Akristu a ku Tesalonika, analankhulanso za kufunika kokhala maso. Analangiza kuti: “Tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.” (1 Atesalonika 5:2, 6) Masiku ano, pamene kuwonongedwa kwa dongosolo la zinthu la dziko lonse kukuyandikira, n’kofunika kwambiri kukhala maso. Olambira Yehova akukhala m’dziko limene anthu ambiri ndi a mphwayi pa zinthu zauzimu, ndipo zimenezi zikhoza kuwakhudza. Motero, Paulo analangiza kuti: “Tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.” (1 Atesalonika 5:8) Kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kuyanjana ndi abale athu pamisonkhano nthaŵi zonse kudzatithandiza kutsatira langizo la Paulo ndi kukhalabe maso.​—Mateyu 16:1-3.

Anthu Miyandamiyanda Ali Maso

14. Kodi ndi ziŵerengero zotani zimene zikusonyeza kuti anthu ambiri masiku ano akutsatira langizo la Petro loti akhale maso?

14 Kodi pali anthu ambiri masiku ano amene akumvera chilimbikitso chouziridwa chakuti akhale maso? Ee. M’chaka cha utumiki cha 2002, chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa okwana 6,304,645, kuwonjezeka kwa maperesenti 3.1 pa chiŵerengero cha 2001, anapereka umboni woti ali maso mwauzimu mwa kuthera maola okwana 1,202,381,302 akuuza ena za Ufumu wa Mulungu. Kwa anthu ameneŵa, ntchito imeneyi sanali kuiona mwawamba. Inali yofunika kwambiri pa moyo wawo. Eduardo ndi Noemi a ku El Salvador anapereka chitsanzo cha mmene ambiri a iwo amaganizira.

15. Kodi ndi zochitika ziti za ku El Salvador zimene zikusonyeza kuti ambiri ali maso mwauzimu?

15 Zaka zingapo m’mbuyomo, Eduardo ndi Noemi anazindikira mawu a Paulo akuti: “Maonekedwe a dziko ili apita [“akusintha,” NW].” (1 Akorinto 7:31) Iwo anayamba kukhala ndi moyo wosalira zambiri ndipo anayamba utumiki waupainiya wa nthaŵi zonse. Pamene nthaŵi inali kupita, anadalitsidwa m’njira zambiri ndipo anagwira nawo ntchito yadera ndi yachigawo. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto aakulu, Eduardo ndi Noemi akukhulupirira kuti anasankha bwino pamene anasiya moyo wa mwanaalirenji kuti achite utumiki wa nthaŵi zonse. Ambiri mwa ofalitsa 29,269, kuphatikizapo apainiya 2,454, ku El Salvador asonyeza mtima wodzimana umenewu, womwe ndi chimodzi mwa zifukwa zimene zinachititsa kuti m’dzikolo ofalitsa awonjezeke ndi 2 peresenti chaka chatha.

16. Kodi mbale wina wachinyamata wa ku Côte d’Ivoire anasonyeza mtima wotani?

 16 Ku Côte d’Ivoire, mnyamata wina wachikristu anasonyezanso mtima womwewu. Iye analembera ku ofesi ya nthambi kuti: “Ndine mtumiki wotumikira. Koma sindingawauze abale kuti achite upainiya pamene ineyo sindikupereka chitsanzo chabwino. Motero ndasiya ntchito ya malipiro abwino ndipo tsopano ndikugwira ntchito yodzilamulira ndekha, imene ikundipatsa nthaŵi yambiri yochita utumiki.” Mnyamata ameneyu ndi mmodzi mwa apainiya okwana 983 amene akutumikira ku Côte d’Ivoire, dziko limene linachitira lipoti ofalitsa okwana 6,701 chaka chatha. Kumeneku kunali kuwonjezeka kwa 5 peresenti.

17. Kodi mtsikana wina wa Mboni ku Belgium anasonyeza bwanji kuti sanachite mantha chifukwa cha malingaliro olakwika a anthu ena?

17 Kusalolerana, malingaliro olakwika, ndi tsankho zikupitirizabe kuvutitsa ofalitsa Ufumu okwana 24,961 a ku Belgium. Komabe, iwo ndi achangu ndipo sachita mantha. Mtsikana wina wa Mboni wa zaka 16 atamva kuti Mboni za Yehova anazitcha kagulu ka mpatuko pamene anali kuphunzira za chikhalidwe kusukulu, iye anapempha chilolezo kuti afotokoze maganizo a Mboni za Yehova. Pogwiritsa ntchito vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Name ndi bulosha lakuti Mboni za Yehova​—Kodi Iwo Ndani?, iye anafotokoza zimene Mboni zili. Anthu anayamikira zimene iye anafotokozazo, ndipo mlungu wotsatira ophunzira anapatsidwa mayeso amene mafunso onse anali onena za chipembedzo chachikristu cha Mboni za Yehova.

18. Kodi pali umboni wotani woti mavuto a zachuma sanadodometse ofalitsa a ku Argentina ndi ku Mozambique kutumikira Yehova?

18 Akristu ambiri amakumana ndi mavuto aakulu m’masiku otsiriza ano. Komabe amayesetsa kuti zimenezo zisawadodometse. Ngakhale kuti ku Argentina kuli mavuto aakulu a zachuma, dzikoli linapereka chiwerengero chapamwamba chatsopano cha Mboni zokwana 126,709 chaka chatha. Ku Mozambique kukadali umphaŵi wadzaoneni. Komabe, anthu okwana 37,563 anachitira lipoti kuti anagwira nawo ntchito yolalikira, komwe ndi kuwonjezeka kwa 4 peresenti. Anthu ambiri ku Albania akuvutika kwambiri, komabe dzikolo linachitira lipoti kuwonjezereka kwa 12 peresenti, zimene zinachititsa kuti ofalitsa afike chiwerengero chapamwamba chokwana 2,708. N’zoonekeratu kuti atumiki ake akaika patsogolo zinthu za Ufumu, mzimu wa Yehova sudodometsedwa ndi mavuto alionse.​—Mateyu 6:33.

19. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti pakadali anthu ena ambiri onga nkhosa amene akufuna choonadi cha Baibulo? (b) Kodi ndi ziŵerengero zina ziti za m’lipoti la pachaka zimene zikusonyeza kuti atumiki a Yehova ali maso mwauzimu? (Onani tchati pa masamba 12-15.)

19 Maphunziro a Baibulo pafupifupi 5,309,289 omwe ankachitika mwezi uliwonse omwe anachitiridwa lipoti chaka chatha padziko lonse akusonyeza kuti pakadali anthu ambiri onga nkhosa amene akufuna choonadi cha Baibulo. Pa chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha anthu 15,597,746 amene anapezeka pa Chikumbutso, ambiri mwa iwo sakutumikira Yehova. Anthu ameneŵa apitirizetu kudziŵa zambiri ndi kukonda kwambiri Yehova ndi ubale wathu. N’zosangalatsa kuona kuti “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” likupitirizabe kubala zipatso pamene likutumikira Mlengi “usana ndi usiku m’Kachisi mwake” pamodzi ndi abale awo odzozedwa.​—Chivumbulutso 7:9, 15; Yohane 10:16.

Kutengera Phunziro pa Loti

20. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Loti ndi mkazi wake?

20 Komabe, ngakhale atumiki okhulupirika a Mulungu angaleke kukhala tcheru kwakanthaŵi.  Taganizirani za Loti, mwana wa mphwake wa Abrahamu. Iye anamva kwa angelo aŵiri amene anafika kunyumba kwake kuti Mulungu anali pafupi kuwononga Sodomu ndi Gomora. Nkhaniyo sinali yodabwitsa kwa Loti, amene anali “wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja.” (2 Petro 2:7) Komabe, angelo aŵiriwo atabwera kuti amutulutse m’mudzi wa Sodomu, iye “anachedwa.” Angelowo anachita kum’gwira dzanja pamodzi ndi banja lake kuti atuluke mumzindawo. Ndiyeno, mkazi wa Loti ananyalanyaza chenjezo la angelowo lakuti asayang’ane m’mbuyo. Kusasamala kwake kunamutaitsa moyo. (Genesis 19:14-17, 26) Yesu anachenjeza kuti: “Kumbukirani mkazi wa Loti.”​—Luka 17:32.

21. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti tikhale maso kuposa kale lonse?

21 Tsoka limene linachitikira mizinda ya Pompeii ndi Hekuleniya ndiponso zimene zinachitika pa chiwonongeko cha Yerusalemu, ndiponso zitsanzo za Chigumula cha m’tsiku la Nowa ndi nkhani ya Loti, zikusonyeza kufunika komvera machenjezo. Monga atumiki a Yehova, timadziŵa chizindikiro cha nthaŵi ya mapeto. (Mateyu 24:3) Tadzipatula ku chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 18:4) Monga mmene anachitira Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, tifunika kukumbukira “kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” (2 Petro 3:12) Inde, tiyenera kukhala maso kuposa kale lonse! Kodi tiyenera kuchita chiyani, ndipo tifunika kukhala ndi makhalidwe otani kuti tikhale maso? Nkhani yotsatirayi ifotokoza mfundo zimenezo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 N’zokayikitsa kuti mumzinda wa Yerusalemu munali anthu oposa 120,000 m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. Eusebius anaŵerengetsera kuti anthu 300,000 a m’chigawo cha Yudeya anapita ku Yerusalemu kukachita phwando la Paskha mu 70 C.E. Anthu ena amene anaphedwawo ayenera kuti anachokera m’madera ena a mu ufumuwo.

^ ndime 6 Koma malinga ndi Yehova, Chilamulo cha Mose chinaloŵedwa m’malo ndi pangano latsopano mu 33 C.E.​—Aefeso 2:15.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndi zochitika zotani zimene zinathandiza Akristu achiyuda kupulumuka chiwonongeko cha Yerusalemu?

• Kodi malangizo amene ali m’zimene mtumwi Petro ndi mtumwi Paulo analemba akutithandiza bwanji kukhala maso?

• Ndani amene masiku ano akupereka umboni woti ali maso?

• Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Loti ndi mkazi wake?

[Mafunso]

 [Tchati pamasamba 12-15]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 2002 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

 (Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Chithunzi patsamba 9]

Mu 66 C.E., Akristu a ku Yerusalemu anamvera chenjezo la Yesu

[Zithunzi patsamba 10]

Kukhala achangu kumathandiza Akristu kukhala maso