Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Onani Zinthu Momwe Mulungu Amazionera

Onani Zinthu Momwe Mulungu Amazionera

 Onani Zinthu Momwe Mulungu Amazionera

PANALI pa September 14, 2002, mu mzinda wa New York, ku United States. Patsikuli dzuŵa linaŵala bwino kwabasi. Khamu la anthu 6,521 a m’mayiko osiyanasiyana linasonkhana ku Malikulu a Maphunziro ku Patterson ndiponso m’malo ena aŵiri a Mboni za Yehova m’chigawochi. Khamuli linasonkhana kudzaonerera mwambo wokondwerera kuti ophunzira a m’kalasi ya nambala 113 amaliza maphunziro awo, pa Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo. Ophunzirawa anali ochokera m’mayiko 14 ndipo atha miyezi isanu akukonzekera utumiki waumishonale umene akachite m’mayiko 19 amene atumizidwa.

Carey Barber, amene ali ndi zaka 98 komanso wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ndi amene anali tcheyamani pa mwambowu. Anafotokoza zimene Sukulu ya Gileadi yachita kwa zaka pafupifupi 60, imene yakonzekeretsa anthu ambiri kukachita umishonale m’mayiko ena. Mbale Barber anati: “Sikukokomeza kunena kuti pakhala zotsatira zabwino chifukwa cha kuphunzira kwawo zambiri. Kunena zoona, anthu ofatsa ambiri padziko lonse apatulira moyo wawo kwa Yehova ndipo alandira kulambira kwake koona ndi utumiki wopatulika chifukwa chakuti amishonale ophunzitsidwawo anawathandiza.”

Ophunzira ambiri asanapite ku Sukulu ya Gileadi, anasonyeza kufuna kuwonjezera zimene amachita mu utumiki. Banja lina linatha zaka zingapo kuphunzira chinenero cha Chimandarini pofuna kulalikira kwa Atchaina ambiri amene amakhala m’dziko la kwawo ku Canada. Banja lina linayamba kuphunzira palokha Chialubaniya ndipo mapeto ake linasamukira ku Albania kukathandiza anthu amene ankachita chidwi kwambiri ndi Baibulo kumeneko. Ophunzira ena m’kalasili anachokera ku Hungary, Guatemala ndi ku Dominican Republic, kumene anasamukira n’cholinga chokatumikira kumene kunali kusoŵa kwambiri aphunzitsi a Mawu a Mulungu.

Tsopano asanapite ku Africa, Kum’maŵa kwa Ulaya, Central ndi South America ndiponso ku Far East, kumene azikatumikira, ophunzira onse omaliza maphunzirowo analimbikitsidwa kuti azilingalira Mulungu m’zochita zawo zonse.

Onani Zinthu Momwe Mulungu Amazionera

Mbale Barber atatha mawu a malonje, anaitana Maxwell Lloyd, wa m’Komiti ya Nthambi ku United States. Anakamba nkhani yakuti, “Onani Zinthu Zonse Momwe Mulungu Amazionera.” Mbale Lloyd anafotokoza zitsanzo za Davide ndi za Yesu, Mwana wa Mulungu. (1 Samueli 24:6; 26:11; Luka 22:42) Wokamba nkhaniyi atakumbutsa ophunzira kuti miyezi isanu imene aphunzira Baibulo aphunzira kuona zinthu momwe Mulungu amazionera, anati: “Pochititsa maphunziro a Baibulo ndi anthu mu gawo lanu latsopano, kodi mudzawathandiza kuona zinthu momwe Mulungu amazionera?” Ndipo pa nkhani yolangiza ena, anawauza ophunzirawo kuti: “Musamanene kuti, ‘Mmene ndikuonera, ndikuganiza kuti . . . ’ Koma, athandizeni kuona mmene  Mulungu amaonera zimenezo. Ngati mutsatira zimenezi, mudzathandiza kwambiri anthu amene mukakumane nawo m’gawo lanu.”

Kenako, panabwera Gerrit Lösch, wa m’Bungwe Lolamulira. Pokamba nkhani yakuti “Ine Ndili Ndi Iwe,” anafotokoza nthaŵi zambiri zimene Yehova anauza atumiki ake okhulupirika kuti, “Ine ndili ndi iwe.” (Genesis 26:23, 24; 28:15; Yoswa 1:5; Yeremiya 1:7, 8) Masiku ano, tingakhalenso ndi chikhulupiriro chimenechi mwa Yehova malinga ngati tikhalabe okhulupirika. Mbale Lösch anati: “Kodi mukukayikira zoti mukapeza anthu ophunzira nawo Baibulo? Kumbukirani kuti Yehova anati, ‘Ine ndili ndi iwe.’ Kodi mukukayikira zoti mukapeza zofunika pamoyo zokwanira? Yehova anati: ‘Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.’ (Ahebri 13:5) Mbale Lösch anamaliza nkhani yake mwa kukumbutsa ophunzirawo kuti Yesu analonjeza kuti adzakhala ndi otsatira ake okhulupirika mu ntchito yopanga ophunzira.​—Mateyu 28:20.

“Kodi Mutha Kupeza Chitetezo Muli Pamoto?” ndiwo unali mutu wankhani wa mlangizi wa Sukulu ya Gileadi, Lawrence Bowen. Iye anati chifukwa cha nkhani imene inabuka mu Edene, anthu onse amene amafuna kulambira Yehova yekha basi amakumana ndi mavuto ndipo  nthaŵi zina, amakumana ndi mayeso angati moto. Analimbikitsa ophunzirawo kutsatira chitsanzo cha Yesu, amene anapeza chitetezo chenicheni chifukwa cha kudalira kwambiri Yehova ndiponso kulolera mayeso angati moto amene Yehova analola kuchitika kuti kumvera kwa Mwana wake kukhale kwamphumphu. (Ahebri 5:8, 9) Yehova angayerekezedwe ndi woyenga golide amene amaika moto woyenera pochotsa zosafunika. N’zoona kuti chikhulupiriro choyesedwa ndi moto chimateteza kwambiri kuposa golide woyengedwa. Chifukwa chiyani? “Chifukwa chakuti chikhulupiriro choyengedwa chingapirire mayesero alionse ndipo chimatikonzekeretsa kupirira mpaka ‘kuchimaliziro,’” anatero Mbale Bowen.​—Mateyu 24:13.

Mlangizi wina wa Sukulu ya Gileadi, Mark Noumair, anafunsa kuti: “Kodi Mudzakhala Wokondeka?” Mutu wake wankhani unagona pa mawu a pa 1 Samueli 2:26 (NW), amene amanena kuti Samueli anali “wokondeka kwa Yehova ndi anthu omwe.” Mbale Noumair, amene watha zaka zoposa 10 mu utumiki waumishonale ku Africa, atafotokoza za chitsanzo cha Samueli, anati: “Inunso mungakhale wokondeka kwambiri kwa Mulungu mwa kukakamira ndiponso kukhulupirika ku ntchito imene Mulungu wakupatsani kuti mugwire. Wakupatsani ntchito yamtengo wapatali yaumishonale.” Ndiyeno Mbale Noumair analimbikitsa anthu omaliza maphunzirowo kuti aziiona ntchito yawo kukhala udindo wopatulika umene Mulungu wawapatsa ndiponso azikhala ndi maganizo a Mulungu pogwira ntchito yawo.

Ophunzirawo ali pasukuluyi, anali ndi mipata yambiri pa mapeto a sabata yokauza anthu a m’derali “zazikulu za Mulungu” za m’Baibulo. (Machitidwe 2:11) Ndipotu, ankalankhula zinthu zimenezi m’zinenero khumi. Wallace Liverance, mlangizi wina wa Sukulu ya Gileadi, pa nkhani yakuti “‘Zazikulu za Mulungu’ Zimalimbikitsa Kugwira Ntchito,” anafunsa kagulu ka ophunzira kusimba zimene akumana nazo. Iye anati: “Mzimu unalimbikitsa amene anali m’chipinda chapamwamba pa Pentekoste kulankhula ‘zazikulu za Mulungu.’ Mzimu womwewo masiku ano ukugwira ntchito pa atumiki okhulupirika onse a Mulungu.” Ena alimbikitsidwa ngakhale kuphunzira chinenero china n’cholinga cholalikira anthu ena ambiri.

Malangizo Othandiza pa Nkhani Yoona Zinthu Momwe Mulungu Amazionera

Nkhani zotsegulira zitatha, Gary Breaux ndi William Young, a panthambi ya ku United States, anafunsa anthu m’makomiti a nthambi za m’mayiko osiyanasiyana kumene kuli amishonale. Anafunsanso banja lina limene latha zaka 41 mu utumiki waumishonale. China chimene ananena n’chakuti: “Amene salira zambiri amakhalitsa. Amaika maganizo pachifukwa chimene anapitira kumeneko. Amadziŵa kuti anapita kukalalikira uthenga wabwino ndiponso kuthandiza anthu kudziŵa Yehova.”

David Splane, wa m’Bungwe Lolamulira, anamaliza mwambowu ndi nkhani yamutu wakuti “Simukupita Kutali!” Kodi anatanthauzanji ndi mawu ameneŵa, popeza kuti tsopano anthu 46 omaliza maphunzirowo anali kutumizidwa m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse? Iye anati: “Kaya muli kuti padziko lapansi, nthaŵi zonse mumakhala mu nyumba ya Mulungu ngati mukhalabe wokhulupirika.” Inde, Akristu onse okhulupirika, kaya amakhala kuti, amatumikira m’kachisi wamkulu wauzimu wa Mulungu, kapena nyumba, amene anakhazikitsidwa nthaŵi imene Yesu anabatizidwa m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. (Ahebri 9:9) Amene analipo pa mwambowu analimbikitsidwa kwambiri kudziŵa kuti Yehova ali pafupi ndi atumiki ake onse okhulupirika apadziko lapansi. Monga momwe Yehova anali wosangalala ndi Yesu ali padziko lapansi, amasangalalanso ndi ife tonse ndiponso utumiki wathu, mosasamala kanthu za kumene timakhala. Choncho pa nkhani ya kulambira, sititalikirana ndi anzathu ndiponso Yehova ndi Yesu.

Atamaliza kupereka moni wochokera m’mayiko ena, kulengeza kumene ophunzirawo azikatumikira ndiponso kuŵerenga kalata imene ophunzirawo analemba poyamikira zimene anaphunzira pa Sukulu ya Gileadi, tcheyamani anamaliza mwambowu bwinobwino. Analimbikitsa amishonale atsopanowo kupitiriza ntchito yawo yabwino ndiponso kukondwera potumikira Yehova.​—Afilipi 3:1.

[Bokosi patsamba 23]

ZIŴERENGERO ZA KALASI

Chiŵerengero cha mayiko kumene ophunzira anachokera: 14

Chiŵerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 19

Chiŵerengero cha ophunzira: 46

Avareji ya zaka zakubadwa: 35.0

Avareji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 17.2

Avareji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthaŵi zonse: 13.7

[Chithunzi patsamba 24]

Kalasi la 113 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

M’ndandanda umene uli pansipa, mizera taiiŵerenga kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kumka kumanja mumzera uliwonse.

(1) Ligthart, M.; Hosoi, S.; Berktold, A.; Liem, C.; Aoki, J. (2) Baglyas, J.; Bouqué, S.; Bossi, A.; Alton, J.; Escobar, I.; Escobar, F. (3) Stoica, A.; Stoica, D.; Freimuth, S.; Karlsson, M.; LeBlanc, R. (4) Bianchi, R.; Bianchi, S.; Kaminski, L.; Joseph, L.; Paris, S.; LeBlanc, L. (5) Paris, M.; Skidmore, B.; Horton, J.; Horton, L.; Skidmore, G. (6) Liem, B.; Alton, G.; Quirici, E.; Langlois, M.; Steininger, S.; Aoki, H. (7) Langlois, J.; Steininger, M.; Bossi, F.; Kaminski, J.; Bouqué, J.; Ligthart, E.; Hosoi, K. (8) Baglyas, J.; Quirici, M.; Karlsson, L.; Freimuth, C.; Berktold, W.; Joseph, R.