Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumam’dziŵa Safani ndi Banja Lake?

Kodi Mumam’dziŵa Safani ndi Banja Lake?

 Kodi Mumam’dziŵa Safani ndi Banja Lake?

POŴERENGA Baibulo, kodi munayamba mwapeza pamene amatchula Safani ndi ena am’banja lake lotchukalo? Kodi iwo anali ndani? Kodi anachitanji? Kodi tingaphunzirenji kwa anthu ameneŵa?

Baibulo limatiuza koyamba za “Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu” pa nkhani ya Yosiya yoyambiranso kulambira koona cha m’ma 642 B.C.E. (2 Mafumu 22:3) M’zaka 36 zotsatira, mpaka pa kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 607 B.C.E., timauzidwa za ana ake anayi, Ahikamu, Elasa, Gemariya ndi Jazaniya ndiponso adzukulu ake aŵiri, Mikaya ndi Gedaliya. (Onani tchati.) Buku la Encyclopaedia Judaica limati: “Kwa nthaŵi yaitali banja la Safani linali ndi maudindo aakulu [mu ufumu wa Yuda] ndipo linali ndi udindo wa mlembi wa mfumu kuyambira nthaŵi ya Yosiya mpaka pamene anatengedwa Ukapolo.” Kuona zimene Baibulo limanena za Safani ndi banja lake kudzatithandiza kuzindikira momwe anathandizira mneneri Yeremiya ndiponso pa kulambira koona kwa Yehova.

Safani Anathandiza pa Kulambira Koona

Mu 642 B.C.E., pamene Mfumu Yosiya anali ndi zaka pafupifupi 25, timapeza kuti Safani anali mlembi wa mfumu. (Yeremiya 36:10) Kodi ntchito yake inaphatikizapo chiyani? Buku limene talitchula kale lija limanena kuti mlembi wa mfumu anali wolangiza weniweni wa mfumu, woyang’anira nkhani zachuma, waluso pankhani yolimbikitsa ubale ndi mayiko ena, wodziŵa nkhani za kunja komanso malamulo oyendetsera ntchito za boma zokhudza mayiko onse ndi nkhani zamalonda. Choncho, Safani monga mlembi wa mfumu, anali mmodzi wa anthu otchuka mu ufumuwo.

Zaka khumi izi zisanachitike, Yosiya wachinyamatayo “anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake.” Mwachionekere Safani anali wamkulu kuposa Yosiya, kotero kuti anali munthu wabwino kulangiza Yosiya pankhani zauzimu ndiponso kumuthandiza pantchito yake yoyamba ya kuyambitsanso kulambira koona. *​—2 Mbiri 34:1-8.

Panthaŵi yokonza kachisi, panapezeka “buku la chilamulo,” ndipo Safani anayamba ‘kuliŵerenga pamaso pa mfumu.’ Yosiya anadabwa kumva zimene zinali mmenemo ndipo anatuma amuna odalirika kwa mneneri wamkazi Hulida kuti akafunse kwa Yehova za bukulo. Mfumu inasonyeza kuti inkamukhulupirira Safani ndi mwana wake Ahikamu mwa kuwaika pagulu limene analitumalo.​—2 Mafumu 22:8-14; 2 Mbiri 34:14-22.

Ndi pokhapa m’Malemba pamene pamanena zimene Safani anachita. M’mavesi ena a m’Baibulo, amangotchulidwa kuti abambo kapena agogo. Ana a Safani anadziŵana kwambiri ndi mneneri Yeremiya.

Ahikamu ndi Gedaliya

Monga taonera, Ahikamu mwana wa Safani amatchulidwa koyamba pa anthu amene  anapita kwa mneneri wamkazi Hulida. Buku lina limati: “Ngakhale kuti m’Baibulo la Chihebri satchula udindo wa Ahikamu, n’zachidziŵikire kuti anali ndi udindo wapamwamba.”

Patatha zaka 15 izi zitachitika, moyo wa Yeremiya unali pachiswe. Atachenjeza anthu zoti Yehova akufuna kuwononga Yerusalemu, “ansembe ndi aneneri ananena kwa akulu ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa.” Ndiyeno n’chiyani chinachitika? Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Dzanja la Ahikamu mwana wa Safani linali ndi Yeremiya, kuti asam’pereke m’manja a anthu kuti amuphe.” (Yeremiya 26:1-24) Kodi izi zikusonyezanji? Buku la The Anchor Bible Dictionary limati: “Nkhani iyi imasonyeza mphamvu zimene Ahikamu anali nazo komanso kuti ankamukonda Yeremiya, monga ankachitira ena a m’banja la Safani.”

Patatha zaka pafupifupi 20, Ababulo atawononga Yerusalemu mu 607 B.C.E. ndiponso atatenga anthu ambiri ukapolo, Gedaliya mdzukulu wa Safani, mwana wa Ahikamu anasankhidwa kukhala kazembe wa Ayuda amene anatsala. Kodi iye monga ena a m’banja la Safani, anasamalira Yeremiya? Nkhani ya m’Baibulo imati: “Ndipo Yeremiya anamka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa, nakhala kumeneko.” Patatha miyezi yochepa, Gedaliya anaphedwa, ndipo Ayuda amene anatsala anam’tenga Yeremiya popita ku Igupto.​—Yeremiya 40:5-7; 41:1, 2; 43:4-7.

Gemariya ndi Mikaya

Gemariya mwana wa Safani pamodzi ndi Mikaya mdzukulu wake anachita mbali zofunika kwambiri pazochitika za m’chaputala 36 cha Yeremiya. Munali cha m’ma 624 B.C.E., m’chaka cha chisanu cha Mfumu Yehoyakimu. Baruki mlembi wa Yeremiya, anaŵerenga mokweza m’buku mawu a Yeremiya pa nyumba ya Yehova, “m’chipinda cha Gemariya mwana wa Safani.” Choncho, “Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani anamva m’buku mawu onse a Yehova.”​—Yeremiya 36:9-11.

Mikaya anadziŵitsa abambo ake ndi akalonga onse za mpukutuwo, ndipo onse ankafuna kumva zimene zinali mmenemo. Kodi anachita zotani? “Ndipo panali, pamene anamva mawu onse, anaopa nayang’anana wina ndi mnzake, nati kwa Baruki, Tidzam’fotokozeratu mfumu mawu awa onse.” Komabe, asanam’fotokozere mfumu, anauza Baruki kuti: “Pita nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziŵe kumene muli.”​—Yeremiya 36:12-19.

Monga ankayembekezera, mfumu inakana uthenga wa mu mpukutuwo ndipo anauwotcha. Akalonga ena, kuphatikizapo Gemariya  mwana wa Safani, “anapembedzera mfumu kuti asatenthe mpukutuwo; koma anakana kumvera.” (Yeremiya 36:21-25) Buku lakuti Jeremiah​—An Archaeological Companion limati: “Gemariya anali wothandiza wamphamvu wa Yeremiya pa bwalo la Mfumu Yehoyakimu.”

Elasa ndi Jazaniya

Mu 617 B.C.E., Babulo analanda ufumu wa Yuda. Ayuda ambiri “akalonga onse, ndi ngwazi zonse, . . . ndi amisiri onse, ndi osula onse,” ndi mneneri Ezekieli yemwe, anatengedwa ukapolo. Mataniya, amene Ababulo anam’sintha dzina kukhala Zedekiya, anakhala mfumu yatsopano yogonjera mfumu ya ku Babulo. (2 Mafumu 24:12-17) Kenako Zedekiya anatuma anthu kuphatikizapo Elasa mwana wa Safani kupita ku Babulo. Yeremiya anam’tuma Elasa kukapereka kalata imene inali ndi uthenga wofunika wochokera kwa Yehova kwa Ayuda amene anali ku ukapolo.​—Yeremiya 29:1-3.

Choncho, nkhani ya m’Baibulo imasonyeza kuti Safani, ana ake atatu ndi zidzukulu zake zitatu zinagwiritsa ntchito maudindo awo kuthandiza kulambira koona ndiponso mneneri wokhulupirika Yeremiya. Bwanji za Jazaniya mwana wa Safani? Mosiyana ndi ena a m’banja la Safani, mwachionekere anatenga mbali m’kulambira mafano. Patapita zaka zisanu Ezekieli ali ku ukapolo ku Babulo, kapena cha m’ma 612 B.C.E., mneneriyu anaona m’masomphenya amuna 70 akupereka nsembe kwa mafano pa kachisi ku Yerusalemu. Mmodzi wa iwo anali Jazaniya, ndi yekhayo amene amatchulidwa dzina pankhaniyi. Izi zingasonyeze kuti anali wotchuka kwambiri pa gululo. (Ezekieli 8:1, 9-12) Chitsanzo cha Jazaniya chimasonyeza kuti kukulira m’banja loopa Mulungu sizitanthauza kuti udzakhala wolambira Yehova wokhulupirika. Munthu aliyense adzaŵerengedwa mlandu pa zochita zake.​—2 Akorinto 5:10.

Umboni Wakuti Safani ndi Banja Lake Analiko

Nthaŵi imene Safani ndi banja lake anatenga mbali m’zochitika za mu Yerusalemu, n’kuti kugwiritsa ntchito zidindo kuli kotchuka ku Yuda. Zidindo anali kuzigwiritsa ntchito pochitira umboni kapena kusainira makalata ndipo zinali za miyala yamtengo wapatali, zitsulo, minyanga kapena magalasi. Nthaŵi zambiri pa chidindopo anali kulembapo dzina la mwini chidindocho, dzina la bambo ake ndiponso nthaŵi zina, udindo wa mwini chidindocho.

 Anthu apeza zidindo za dothi zambiri za Ahebri. Pulofesa Nahman Avigad, katswiri wa maphunziro a zolemba zakale za Chihebri anati: “Zidindo ndilo gwero lokha la zilembo zakale za Chihebri limene limatchula anthu amene anawafotokoza m’Baibulo.” Kodi papezekapo zidindo za Safani kapena a m’banja lake? Inde, dzina la Safani ndi la mwana wake Gemariya likuoneka pa chidindo chimene chili patsamba 19 ndi 21.

Akatswiri amanenanso kuti mwina a m’banja lake ena anayi anatchulidwa pa zidindo​—Azaliya bambo a Safani; Ahikamu mwana wa Safani; Gemariya mwana wa Safani; ndi Gedaliya amene zikuoneka kuti anatchulidwa pa chidindo kuti anali “wolamulira panyumba.” Chidindo chachinayi pa zidindo zimenezi akuti chinali cha Gedaliya mdzukulu wa Safani, ngakhale kuti abambo ake Ahikamu, sanatchulidwepo. Udindo wake pa chidindocho ukusonyeza kuti anali mmodzi wa nduna za boma zapamwamba mu ufumuwo.

Kodi Tikuphunzirapo Chiyani?

Safani ndi banja lake anapereka chitsanzo chabwino kwambiri chogwiritsa ntchito maudindo awo kuthandizira kulambira koona ndi Yeremiya amene anali wokhulupirika. Ifenso tingagwiritse ntchito zinthu zathu ndi mphamvu zathu kuthandiza gulu la Yehova ndi olambira anzathu.

N’zolimbikitsa ndiponso zolimbitsa chikhulupiriro kwa ife, kuŵerenga nthaŵi zonse Baibulo ndi kufufuza kwambiri kuti tidziŵe za mboni za Yehova zakale zoterezi monga Safani ndi banja lake. Iwonso ali mu ‘mtambo [waukulu] wa mboni’ amene tingatsanzire zitsanzo zawo.​—Ahebri 12:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Safani ayenera kuti anali wamkulu kuposa Yosiya, popeza kuti Ahikamu mwana wa Safani anali wamkulu Yosiya ali ndi zaka pafupifupi 25.​—2 Mafumu 22:1-3, 11-14.

[Bokosi patsamba 22]

Hulida​—Mneneri Wamkazi Wamphamvu

Mfumu Yosiya atamva za mu “buku la chilamulo” limene linapezeka m’kachisi, anauza Safani ndi nduna zina zapamwamba zinayi ‘kukafunsira kwa Yehova’ za bukulo. (2 Mafumu 22:8-20) Kodi anthuwo anakapeza kuti yankho? Panthaŵi imeneyo, Yeremiya mwinanso Nahumu ndi Zefaniya, omwe onse anali aneneri ndi olemba Baibulo ankakhala ku Yuda. Komabe, anthu amene anatumidwa anapita kwa mneneri wamkazi Hulida.

Buku lakuti Jerusalem​—An Archaeological Biography limati: “Chochititsa chidwi ndi nkhani iyi n’chakuti zakuti uyu ndi mwamuna kapena mkazi sanazione kukhala zofunika. Palibe anaganiza kuti n’kosayenera kuti bungwe la amuna okhaokha lipite ndi Mpukutu wa Chilamulo kwa mkazi kuti akalitsimikizire ngati ndi loona. Atalitsimikizira kuti ndi mawu a Ambuye, palibe anakayikira ulamuliro wake wogamula nkhaniyi. Nthaŵi zambiri akatswiri amanyalanyaza nkhani imeneyi poona udindo wa akazi mu Israyeli wakale.” N’zoona kuti uthenga umene analandira unali wochokera kwa Yehova.

[Chithunzi patsamba 21]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mibadwo ya Safani

Mesulamu

Azaliya

Safani

↓ ↓ ↓ ↓

Ahikamu Elasa Gemariya Jazaniya

↓ ↓

Gedaliya Mikaya

[Chithunzi patsamba 20]

Gemariya ndi anthu ena anapempha Yehoyakimu kuti asatenthe mpukutu wochokera kwa Yeremiya

[Chithunzi patsamba 22]

Ngakhale kuti Jazaniya anali wa m’banja la Safani, anaonedwa m’masomphenya akulambira mafano

[Mawu a Chithunzi patsamba 19]

Mwachilolezo cha Israel Antiquities Authority

[Mawu a Chithunzi patsamba 21]

Mwachilolezi cha Israel Antiquities Authority