Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:

Kodi luso la “kulingalira” lingatiteteze bwanji? (Miyambo 1:4)

Lingatithandize kuona ngozi zauzimu ndipo lingatichititse kukonza zinthu zanzeru zoti tichite, monga kupeŵa ziyeso za chiwerewere kuntchito. Limatithandiza kuzindikira kuti Akristu anzathu ndi opanda ungwiro, zimene zingatichititse kupeŵa kuchita zinthu mopupuluma munthu akatilakwira. Lingatithandizenso kupeŵa vuto la kukondetsa chuma limene lingatisocheretse mwauzimu.​—8/15 masamba 21 mpaka 24.

Kodi munthu amakhala bwanji wofunika kwambiri kwa anthu amene amakhala naye pafupi?

Njira ziŵiri zokhalira mnansi wabwino ndizo kupatsa moolowa manja ndiponso kuthokoza ukapatsidwa kanthu. N’chinthu chamtengo wapatali kukhala munthu wabwino wokhala naye pafupi pakagwa mavuto. Mboni za Yehova zimayesetsa kukhala anansi abwino mwa kuchenjeza ena zimene zichitike posachedwapa, zimene Mulungu adzachita kuti athetse kuipa.​—9/1, masamba 4 mpaka 7.

Malinga ndi Baibulo, kodi anthu oyera mtima enieni ndani, ndipo kodi adzathandiza bwanji anthu?

Akristu oyambirira onse anali oyera mtima enieni, kapena kuti opatulika, ndipo Mulungu ndi amene anawapanga kukhala oyera mtima osati anthu kapena mabungwe ena ake. (Aroma 1:7) Akaukitsidwa n’kukakhala ndi moyo kumwamba, opatulika ameneŵa adzagwira ntchito pamodzi ndi Kristu kudalitsa anthu okhulupirika amene adzakhala padziko lapansi. (Aefeso 1:18-21)​—9/15, masamba 5 mpaka 7.

Kodi kudziŵa zochitika pa maseŵero akale a ku Greece kungapindulitse bwanji Akristu?

Zimene mtumwi Petro ndi mtumwi Paulo analemba zili ndi mafanizo okhudza maseŵero akale. (1 Akorinto 9:26; 1 Timoteo 4:7; 2 Timoteo 2:5; 1 Petro 5:10) Wochita maseŵero kalelo anafunika kukhala ndi mphunzitsi wabwino kwambiri, kukhala wodziletsa, ndi kulunjikitsa bwino mphamvu zake. N’chimodzimodzinso masiku ano, Akristu afunika kuyesetsa mwauzimu.​—10/1, masamba 28 mpaka 31.

Kodi ndi mavuto ati komanso mphoto zotani zimene zimakhalapo polera ana m’dziko lachilendo?

Ana ambiri amaphunzira chinenero chatsopano mofulumira kuposa makolo awo, amene zimawavuta kumvetsa maganizo ndi zochita za ana awowo. Ndipo anawo angavutike kumva ziphunzitso za Baibulo m’chinenero cha makolo awo. Komabe, mgwirizano wa banja ungalimbe ngati makolo aphunzitsa ana awo chinenero chawocho, omwe mwa kuchita zimenezo angadziŵe zinenero ziŵiri ndi kudziŵa bwino zikhalidwe zonse ziŵiri.​—10/15, masamba 22 mpaka 26.

N’chifukwa chiyani kuphunzira kupepesa n’kofunika?

Nthaŵi zambiri, kupepesa ndi mtima wonse ndi njira yokonzera ubale umene wasokonezeka. Baibulo limapereka zitsanzo zosonyeza mphamvu imene kupepesa kungakhale nayo. (1 Samueli 25:2-35; Machitidwe 23:1-5) Nthaŵi zambiri, anthu aŵiri akasiyana maganizo, aliyense mwa anthuwo amakhala kuti ali ndi vuto. Motero, onse afunika kuvomereza vutolo ndi kupepesana.​—11/1, masamba 4 mpaka 7.

N’chifukwa chiyani n’kulakwa kutchova njuga ngakhale ndalama zobetcherana zitakhala zochepa chabe?

Kutchova njuga kungayambitse kudzikuza, mtima wampikisano, ndiponso dyera, zimene Baibulo limatsutsa. (1 Akorinto 6:9, 10) Anthu ambiri oloŵerera ndi kutchova njuga anayamba ali aang’ono mwa kubetcherana ndalama zochepa.​—11/1, tsamba 31.

Popeza mabuku ambiri a m’Baibulo analembedwa m’Chigiriki, n’chifukwa chiyani panafunika kumasulira Baibulo m’Chigiriki, ndipo pakhala zotsatira zotani?

Chigiriki chamakono n’chosiyana kwambiri ndi Chigiriki cha m’Baibulo la Septuagint la Malemba a Chihebri ndiponso cha m’Malemba Achigiriki Achikristu. M’zaka zaposachedwapa anthu ambiri ayesetsa kumasulira mbali zina za Baibulo kapena Baibulo lonse m’Chigiriki chimene anthu akulankhula. Tsopano, pali mabaibulo amene awamasulira pafupifupi 30 athunthu kapena mbali zake, amene anthu a ku Greece angaŵerenge, ndipo Baibulo lapadera mwa mabaibulo ameneŵa ndi la New World Translation of the Holy Scriptures, limene analisindikiza mu 1997.​—11/15, masamba 26 mpaka 29.

N’chifukwa chiyani Akristu sayenera kupereka chakhumi?

M’chilamulo chimene anachipereka kwa Aisrayeli akale, kupereka chakhumi kunali njira yothandizira fuko la Alevi ndi kusamalira osoŵa. (Levitiko 27:30; Deuteronomo 14:28, 29) Imfa ya nsembe ya Yesu inathetsa Chilamulo ndi kufunika kopereka chakhumi. (Aefeso 2:13-15) Mumpingo woyambirira, kaperekedwe kanali koti Mkristu aliyense azipereka malinga ndi mmene amapezera ndiponso mmene watsimikizira mumtima mwake. (2 Akorinto 9:5, 7)​—12/1, masamba 4 mpaka 6.

Kodi lemba la Chivumbulutso 20:8 limatanthauza kuti pa chiyeso chomaliza, Satana adzasocheretsa anthu ambiri zedi?

Mawu a pa lembalo amati amene adzasocheretsedwa adzakhala ngati “mchenga wa kunyanja.” M’Baibulo, mawu amenewo nthaŵi zambiri amatanthauza nambala yosadziŵika, popanda kusonyeza kuti ndi yaikulu zedi. Mbewu ya Abrahamu imene inali kudzakhala “monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja,” inadzakhala anthu 144,000, kupatulapo Yesu Kristu. (Genesis 22:17; Chivumbulutso 14:1-4)​—12/1, tsamba 29.