Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Adzayandikira kwa Inu”

“Adzayandikira kwa Inu”

 “Adzayandikira kwa Inu”

“[Mulungu] sakhala patali ndi yense wa ife.”​—MACHITIDWE 17:27.

1, 2. (a) Tikayang’ana kumwamba kopanda mitambo n’kuona nyenyezi, kodi tingadzifunse funso liti lokhudza Mlengi? (b) Kodi Baibulo limatitsimikizira bwanji kuti Yehova amaona anthu kukhala amtengo wapatali?

KODI munayang’anapo kumwamba usiku kulibe mitambo n’kuona nyenyezi ndiyeno n’kuchita nazo chidwi kwambiri? Kuchuluka kwa nyenyezi ndi kukula kwa mlengalenga kumachititsa mantha. Dziko lili ngati kadontho chabe m’chilengedwe chachikulu chimenechi. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mlengi, yemwe ndi “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,” ali pamwamba kwambiri moti anthu alibe nawo ntchito kapena ali patali kwambiri moti n’zosatheka kuti anthu am’funefune ndi kum’dziŵa?​—Salmo 83:18.

2 Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova amaona anthu kukhala amtengo wapatali. Ndipotu, Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kum’funafuna, pamene amanena kuti: “Sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:27; 1 Mbiri 28:9) Inde, ngati titsatira njira zoti tiyandikire kwa Mulungu, iye adzachitapo kanthu pa zimene tikuchitazo. Adzatani? Mawu a lemba lathu la chaka cha 2003 amayankha mosangalatsa kuti: “Adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Tiyeni tikambirane ena mwa madalitso abwino kwambiri amene Yehova amapereka kwa anthu amene ayandikira kwa iye.

Mphatso Imene Yehova Wapereka kwa Munthu Payekha

3. Kodi ndi mphatso yotani imene Yehova amapereka kwa anthu amene amayandikira kwa iye?

3 Choyamba, atumiki a Yehova ali ndi mphatso ya mtengo wapatali imene iye wawasungira. Mphamvu zonse, chuma chonse, ndiponso maphunziro onse a dzikoli sangapereke mphatso imeneyi. Imeneyi ndi mphatso ya munthu payekha, imene Yehova amapereka kwa okhawo amene ayandikira kwa iye. Kodi ndi mphatso yanji imeneyo? Mawu a Mulungu amayankha kuti: “[Uka]fuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru.” (Miyambo 2:3-6) Tangoganizani! Anthu opanda ungwiro kutha “kum’dziŵadi Mulungu”! Mphatso imeneyi, yodziŵa za m’Mawu a Mulungu, aiyerekezera ndi “chuma chobisika.” Chifukwa chiyani?

4, 5. N’chifukwa chiyani “kum’dziŵadi Mulungu” kungayerekezeredwe ndi “chuma chobisika”? Perekani chitsanzo.

 4 Mwa zina, kum’dziŵa Mulungu n’kopindulitsa kwambiri. Phindu limodzi lalikulu n’lakuti munthu angayembekezere kudzakhala ndi moyo kosatha. (Yohane 17:3) Koma kudziŵa zimenezo kumapindulitsa moyo wathu ngakhale pakalipano. Mwachitsanzo, chifukwa chophunzira mosamala Mawu a Mulungu, tadziŵa mayankho a mafunso ofunika kwambiri monga akuti: Kodi Mulungu dzina lake ndani? (Salmo 83:18) Kodi n’chiyani kwenikweni chimachitika munthu akamwalira? (Mlaliki 9:5, 10) Kodi cholinga cha Mulungu n’chotani polenga dziko lapansi ndiponso anthu? (Yesaya 45:18) Tadziŵanso kuti chinthu chabwino pa moyo wa munthu ndicho kutsatira malangizo anzeru a m’Baibulo. (Yesaya 30:20, 21; 48:17, 18) Motero, tili ndi malangizo abwino amene angatithandize kulimbana ndi mavuto a moyo ndi kutsatira njira imene ingatithandize kupeza chimwemwe chenicheni ndi kusangalala. Koposa zonse, kuphunzira kwathu Mawu a Mulungu kwatithandiza kudziŵa makhalidwe abwino kwambiri a Yehova ndipo zimenezi zatithandiza kumuyandikira. Kodi pangakhale chinthu china chabwino choposa ubwenzi wapamtima ndi Yehova umene umakhalapo chifukwa ‘chom’dziŵadi Mulungu’?

5 Palinso chifukwa china chimene kum’dziŵadi Mulungu kungayerekezeredwe ndi “chuma chobisika.” Monga mmene chimakhalira chuma chambiri, icho n’chosoŵa kwambiri m’dzikoli. Mwa anthu sikisi biliyoni amene ali padziko lapansi, olambira Yehova okwana pafupifupi sikisi miliyoni okha, kapena pafupifupi munthu m’modzi mwa anthu 1,000 alionse, ndi amene ‘am’dziŵadi Mulungu.’ Mwachitsanzo, pofuna kuona kuti ndi mwayi waukulu kudziŵa choonadi cha m’Mawu a Mulungu, taonani funso limodzi lokha ili lokhudza Baibulo: Kodi n’chiyani chimachitikira anthu akamwalira? Timadziŵa kuchokera m’Malemba kuti munthu amamwalira ndipo kuti anthu akufa sadziŵa kena kalikonse. (Yesaya 38:18) Komabe zipembedzo zambiri za m’dzikoli zimavomereza chikhulupiriro chabodza chakuti pali chinachake m’thupi la munthu chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira. Chimenechi ndi chimodzi mwa zikhulupiriro zazikulu za m’zipembedzo za Matchalitchi Achikristu. Zipembedzo za Chibuda, Chihindu, Chijaini, Chishinto, Chisikhi, Chisilamu, Chitao, ndi Chiyuda zimakhulupiriranso chimodzimodzi. Tangoganizani! Anthu miyandamiyanda apusitsidwa ndi chiphunzitso chonyenga chimenechi!

6, 7. (a) Kodi ndani okha amene ‘angam’dziŵedi Mulungu’? (b) Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuti Yehova watidalitsa kuti tizindikire zinthu zimene anthu ambiri “anzeru ndi akudziŵitsa” sanazizindikire?

6 N’chifukwa chiyani anthu ambiri ‘sanam’dziŵedi Mulungu’? Chifukwa chakuti munthu sangamvetse tanthauzo la Mawu a Mulungu popanda thandizo Lake. Kumbukirani kuti kum’dziŵadi Mulungu ndi mphatso. Yehova amapereka mphatso imeneyi kwa anthu okhawo amene ali ofunitsitsa kufufuza m’Mawu ake moona mtima ndiponso modzichepetsa. Anthu oterowo angakhale oti si “anzeru, monga mwa thupi.” (1 Akorinto 1:26) Ambiri mwa iwo angamaonedwe ngati “osaphunzira ndi opulukira” malinga ndi kuona kwa dzikoli. (Machitidwe 4:13) Koma zimenezo zilibe ntchito. Yehova amatipatsa mphoto ya “kum’dziŵadi [iye]” chifukwa cha makhalidwe amene iye waona mumtima mwathu.

7 Taonani chitsanzo ichi. Akatswiri ambiri a m’Matchalitchi Achikristu apanga mabuku ambirimbiri ofotokoza Baibulo. Mabuku amenewo angafotokoze zimene zinachitika, matanthauzo a mawu a Chihebri ndi Chigiriki, ndi zinanso zambiri. Ngakhale kuti aphunzira kwambiri, kodi akatswiriwo ‘am’dziŵadi Mulungu’? Chabwino, kodi amadziŵa bwino mfundo yaikulu ya Baibulo lonse, yomwe ndi kutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndipo kuti adzachita zimenezo kudzera mu Ufumu wake wakumwamba? Kodi amadziŵa kuti Yehova Mulungu si wa Utatu? Ife timadziŵa zolondola pa nkhani zimenezo. Chifukwa chiyani? Yehova watidalitsa kuti tizindikire choonadi chauzimu chimene anthu ambiri “anzeru ndi akudziŵitsa” sanachizindikire. (Mateyu 11:25) Inde, Yehova amadalitsadi anthu amene amayandikira kwa iye.

 “Yehova Asunga Onse Akukondana Naye”

8, 9. (a) Kodi Davide anafotokoza bwanji dalitso lina la anthu amene amayandikira kwa Yehova? (b) N’chifukwa chiyani Akristu oona amafunikira kutetezedwa ndi Mulungu?

8 Anthu amene ayandikira kwa Yehova amapezanso dalitso lina. Yehova amawateteza. Wamasalmo Davide amene anakumana ndi mavuto ambiri, analemba kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m’choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kupfuula kwawo, nadzawapulumutsa. Yehova asunga onse akukondana naye.” (Salmo 145:18-20) Inde, Yehova ali pafupi ndi onse amene amamukonda ndipo angayankhe mofulumira kufuulira kwawo thandizo.

9 N’chifukwa chiyani timafunikira Mulungu kutiteteza? Kuwonjezera pa kukumana ndi mavuto obwera chifukwa cha “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, Mdani wamkulu wa Yehova, Satana Mdyerekezi, amasakasaka kwambiri Akristu oona. (2 Timoteo 3:1) Mdani wochenjera ameneyu wafiira maso kuti ‘atilikwire.’ (1 Petro 5:8) Satana amatizunza, kutivutitsa, ndi kutiyesa. Iye amaona zoganiza za mtima wa munthu ndi kuzigwiritsa ntchito. Iye m’maganizo mwake ali ndi cholinga chofooketsa chikhulupiriro chathu ndi kuwononga moyo wathu wauzimu. (Chivumbulutso 12:12, 17) Popeza tili ndi mdani wamphamvu wotereyu woti tilimbane naye, kodi si zosangalatsa kudziŵa kuti “Yehova asunga onse akukondana naye”?

10. (a) Kodi Yehova amateteza bwanji anthu ake? (b) Kodi chitetezo chofunika kwambiri kuposa china chilichonse n’chiti, ndipo n’chifukwa chiyani?

10 Koma kodi Yehova amateteza bwanji anthu ake? Kulonjeza kwake kuti adzatiteteza sikutanthauza kuti sitidzakumana ndi mavuto m’dziko lino. Ndiponso sikutanthauza kuti iye afunika kuchita zozizwitsa kuti atiteteze. Komabe, Yehova amateteza anthu ake monga gulu. Ndiponso, iye sadzalola kuti Mdyerekezi awononge olambira oona onse padziko lapansi. (2 Petro 2:9) Koposa zonse, Yehova amatiteteza mwauzimu. Amatipatsa zinthu zimene timafunikira kuti tipirire mayesero ndi kuteteza ubwenzi wathu ndi iye. Mwa zonse, chitetezo chauzimu ndicho chofunika kwambiri kuposa chitetezo china chilichonse. Chifukwa chiyani? Ngati tili pa ubwenzi ndi Yehova, palibe china chilichonse chimene chingativulaze kotheratu, ngakhale imfa imene.​—Mateyu 10:28.

11. Kodi Yehova wapereka zinthu ziti kuti ziteteze anthu ake mwauzimu?

11 Yehova wapereka zinthu zambiri zoti ziteteze mwauzimu anthu amene ayandikira kwa iye. Kudzera m’Mawu ake, Baibulo, iye watipatsa nzeru zoti tithe kulimbana ndi mayesero osiyanasiyana. (Yakobo 1:2-5) Kugwiritsa ntchito malangizo a m’Malemba kumathandiza. Ndiponso, Yehova amapereka “Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye.” (Luka 11:13) Mzimu umenewo ndi wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse, motero ungatikonzekeretsedi kulimbana bwino ndi mayesero kapena zokopa zilizonse zimene tingakumane nazo. Kudzera mwa Kristu, Yehova amapereka “mphatso mwa amuna.” (Aefeso 4:8, NW) Amuna oyeneretsedwa mwauzimu ameneŵa pothandiza olambira anzawo amayesetsa kusonyeza chifundo kuchokera pansi pa mtima monga mmene Yehova amachitira. (Yakobo 5:14, 15)

12, 13. (a) Kodi Yehova amatipatsa chakudya chauzimu panthaŵi yake kudzera m’njira ziti? (b) Kodi mumamva bwanji ndi zimene Yehova amatipatsa kuti zitithandize pa moyo wathu wauzimu?

12 Yehova amaperekanso chinthu china choti chititeteze. Chimenechi ndi chakudya chauzimu  cha panthaŵi yake. (Mateyu 24:45) Yehova amatipatsa zimene tikufunikira tikazifuna kudzera m’zofalitsa monga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndiponso kudzera m’misonkhano yampingo ndi misonkhano yaikulu. Kodi mungakumbukire nthaŵi ina imene munamva mfundo ina yake pa msonkhano wa mpingo kapena pa msonkhano waukulu imene inakukhudzani kwambiri mtima ndi kukulimbikitsani kapena kukutonthozani? Kodi munaŵerengapo nkhani ya m’magazini amene tawatchula pamwambapa ndi kuona kuti inalembedwera inu?

13 Chimodzi mwa zida zamphamvu za Satana ndicho kukhumudwa, ndipo mavuto amene amabwera chifukwa cha kukhumudwa angatichitikire. Iye amadziŵa bwino kuti kutaya mtima kwa nthaŵi yaitali kungatifooketse, ngakhalenso kukhala osavuta kuti atiukire. (Miyambo 24:10) Popeza Satana amayesetsa kupezerapo mwayi pa kukhumudwa kwathu, tifunika thandizo. Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! nthaŵi zina afalitsa nkhani zimene zingatithandize kulimbana ndi kukhumudwa. Pofotokoza za nkhani ina yotero, mlongo wina wachikristu analemba kuti: “Ndimaŵerenga nkhaniyo pafupifupi tsiku lililonse, ndipo ndimagwetsa misozi nthaŵi zonse. Magaziniyo ndimaiika pafupi ndi bedi langa kuti ndiŵerenge ndikakhumudwa. Ndikamaŵerenga nkhani zotere ndimamva ngati manja oteteza a Yehova akundikumbatira.” * Kodi sitikuthokoza Yehova chifukwa chotipatsa chakudya chauzimu panthaŵi yake? Kumbukirani kuti zimene amatipatsa kuti zitithandize pa moyo wathu wauzimu ndi umboni wakuti iye ali pafupi nafe ndipo akutiteteza.

N’zotheka Kufikira “Wakumva Pemphero”

14, 15. (a) Kodi ndi dalitso lotani limene Yehova amapereka kwa anthu amene ayandikira kwa iye? (b) N’chifukwa chiyani kuloledwa kulankhula momasuka ndi Yehova m’pemphero ndi mwayi waukulu?

14 Kodi mwaonapo kuti anthu akapeza mphamvu ndi ulamuliro nthaŵi zambiri zimavuta kuti anthu amene iwo akuwalamulirawo alankhule nawo? Koma bwanji Yehova Mulungu? Kodi ali kutali kwambiri moti sangasamale zimene anthu angalakhule kwa iye? Ayi ndithu! Mphatso ya pemphero ndi dalitso linanso limene Yehova wapereka kwa anthu amene ayandikira kwa iye. Ndi mwayidi waukulu kuloledwa kulankhula momasuka ndi “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Chifukwa chiyani tikuti ndi mwayi waukulu?

15 Taonani chitsanzo ichi: Mkulu wa pa kampani yaikulu amakhala ndi ntchito zambiri. Amaona kuti ndi nkhani ziti zimene angazisamalire yekha ndipo ndi ziti zimene angauze ena kuti asamalire. Mofananamo, Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse amasankha kuti ndi nkhani ziti zimene adzasamalira yekha ndipo ndi ziti zimene angauze ena kuti asamalire. Tangoganizani zonse zimene Yehova wapereka kwa Mwana wake wokondedwa, Yesu, kuti asamalire. Mwanayo wapatsidwa “mphamvu ya kuchita mlandu.” (Yohane 5:27) Angelo afunika ‘kumugonjera.’ (1 Petro 3:22) Yesu angathe kugwiritsa ntchito mzimu woyera wamphamvu wa Yehova kuti umuthandize kutsogolera ophunzira ake padziko lapansi. (Yohane 15:26;  16:7) N’chifukwa chake, Yesu anatha kunena kuti: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Komatu, pankhani ya mapemphero athu, Yehova wasankha kuti asamalire yekha mbali imeneyi. N’chifukwa chake Baibulo limatilangiza kupemphera kwa Yehova yekha, m’dzina la Yesu.​—Salmo 69:13; Yohane 14:6, 13.

16. N’chifukwa chiyani tingakhulupirire kuti Yehova amamvadi mapemphero athu?

16 Kodi Yehova amamvadi mapemphero athu? Akanakhala kuti alibe nawo ntchito mapemphero athu, sakanatilimbikitsa ‘kulimbika chilimbikire m’kupemphera’ kapena kumusenza nkhaŵa zathu. (Aroma 12:12; Salmo 55:22; 1 Petro 5:7) Atumiki okhulupirika a nthaŵi za m’Baibulo anali ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova amamva mapemphero. (1 Yohane 5:14) Motero, wamasalmo Davide anati: “[Yehova] adzamva mawu anga.” (Salmo 55:17) Ifenso tili ndi zifukwa zonse zokhulupirira kuti Yehova ali pafupi ndipo ndi wokonzeka kumva maganizo ndi mavuto athu onse.

Yehova Amapereka Mphoto kwa Atumiki Ake

17, 18. (a) Kodi Yehova amamva bwanji ndi kutumikira mokhulupirika kwa zolengedwa zake zanzeru? (b) Fotokozani mmene lemba la Miyambo 19:17 limasonyezera kuti Yehova amaona ntchito zathu zachifundo zimene timachita.

17 Udindo wa Yehova monga Wolamulira Wachilengedwe Chonse sukhudzidwa ndi zimene anthu angachite kapena kukana kuchita. Komabe, Yehova ndi Mulungu woyamikira. Iye amayamikira ndiponso amasangalala ndi kutumikira mokhulupirika kwa zolengedwa zake zanzeru. (Salmo 147:11) Limeneli ndi dalitso linanso limene anthu oyandikira kwa Yehova amakhala nalo: Iye amapereka mphoto kwa atumiki ake.​—Ahebri 11:6.

18 Baibulo limasonyeza bwino kuti Yehova amayamikira zimene olambira ake amachita. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti: “Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzam’bwezera chokoma chakecho.” (Miyambo 19:17) Kuchitira chifundo aumphawi kumene Yehova amachita kunaonekera m’Chilamulo cha Mose. (Levitiko 14:21; 19:15) Kodi Yehova amamva bwanji  tikamatsanzira chifundo chake pochita zinthu ndi aumphaŵi? Tikamapereka kwa aumphawi, osayembekezera kuti atibwezere, Yehova amaona zimenezi ngati ngongole imene tamukongoza Iye. Yehova akulonjeza kuti adzatibwezera ngongole imeneyo mwa kutiyanja ndi kutidalitsa. (Miyambo 10:22; Mateyu 6:3, 4; Luka 14:12-14) Inde, tikasonyeza chifundo kwa wolambira mnzathu amene akusoŵa thandizo, zimakhudza mtima wa Yehova. Tikuyamikiratu kwambiri kudziŵa kuti Atate wathu wakumwamba amaona ntchito zachifundo zimene timachita.​—Mateyu 5:7.

19. (a) N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti Yehova amayamikira zimene timachita pantchito yolalikira ndi kupanga ophunzira? (b) Kodi Yehova amapereka bwanji mphoto pa utumiki umene munthu amachita pothandizira Ufumu wake?

19 Yehova amayamikira makamaka zimene timachita pothandizira Ufumu wake. Tikamayandikira kwa Yehova, n’kwachibadwa kuti timafuna kugwiritsa ntchito nthaŵi yathu, mphamvu zathu, ndi chuma chathu kuti tigwire nawo ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira monga mmene tingathere. (Mateyu 28:19, 20) Nthaŵi zina tingaone kuti tikuchita zochepa. Mtima wathu wopanda ungwiro ungatichititse kukayikira ngati Yehova akusangalala ndi zimene tikuchita. (1 Yohane 3:19, 20) Koma Yehova amayamikira mphatso iliyonse imene munthu angapereke ndi mtima wonse ndiponso chifukwa cha chikondi ngakhale itakhala yochepa bwanji. (Marko 12:41-44) Baibulo limatitsimikizira kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Inde, Yehova amakumbukira ndipo amapereka mphoto ngakhale pa utumiki wochepa chabe umene munthu angachite pothandizira Ufumu wake. Kuwonjezera pa madalitso aakulu auzimu amene tikupeza pakalipano, tingayembekezere kudzasangalala ndi moyo m’dziko latsopano limene likubwera, mmene Yehova adzaoloŵetsa dzanja lake ndi kupatsa onse amene ayandikira kwa iye zinthu zabwino zimene iwo akufuna.​—Salmo 145:16; 2 Petro 3:13.

20. M’chaka chonse cha 2003, kodi tingasunge bwanji m’maganizo mwathu mawu a lemba lathu la chaka, ndipo n’chiyani chingachitike tikatero?

20 M’chaka chonse cha 2003, tiyeni tidzifunse ngati tikuyesetsa nthaŵi zonse kuyandikira kwa Atate wathu wakumwamba. Ngati tikutero, tingatsimikize kuti iye adzachita monga mmene walonjezera. Ndipotu, ‘Mulungu sanama.’ (Tito 1:2) Ngati muyandikira kwa iye, adzayandikira kwa inu. (Yakobo 4:8) Ndiyeno kodi n’chiyani chidzachitike? Tidzalandira madalitso ochuluka pakalipano ndipo tingayembekezere kudzayandikira kwambiri kwa Yehova mpaka kalekale!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Mlongoyu anali kuyamikira nkhani yakuti “Yehova Ali Wamkulu Kuposa Mitima Yathu,” ya mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2000, masamba 28 mpaka 31.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Yehova amapereka mphatso yotani kwa anthu amene amayandikira kwa iye?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova amapereka kuti ateteze anthu ake mwauzimu?

• N’chifukwa chiyani kuloledwa kulankhula momasuka ndi Yehova m’pemphero ndi mwayi waukulu kwambiri?

• Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amayamikira kutumikira mokhulupirika kwa zolengedwa zake zanzeru?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Yehova watidalitsa kuti tizindikire choonadi chauzimu

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Yehova amateteza mwauzimu

[Chithunzi patsamba 18]

Yehova ali pafupi ndipo ndi wokonzeka kumva pemphero lathu lililonse