Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Limene Anatitumiza Kukachita Umishonale Linadzakhala Kwathu

Dziko Limene Anatitumiza Kukachita Umishonale Linadzakhala Kwathu

Mbiri ya Moyo Wanga

 Dziko Limene Anatitumiza Kukachita Umishonale Linadzakhala Kwathu

YOSIMBIDWA NDI DICK WALDRON

Linali Lamlungu masana mu September 1953. Tinali titangofika kumene m’dziko la South-West Africa (tsopano lotchedwa Namibia). Mlungu umodzi unali usanathe kuchokera pamene tinafika m’dzikoli ndipo tinali titatsala pang’ono kuti tichititse msonkhano wa onse mu mzinda wa Windhoek, likulu la dzikoli. Kodi n’chiyani chinatiyendetsa mtunda wonse kuchoka ku Australia kubwera kuno ku Africa? Ine ndi mkazi wanga, pamodzi ndi atsikana atatu tinabwera monga amishonale a uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.​—Mateyu 24:14.

NDINABADWIRA kutali kwambiri, ku Australia, m’chaka chapadera cha 1914. Ndinali kamnyamata pamene dziko linali pa nyengo ya mavuto adzaoneni a zachuma, ndipo ndinafunika kuthandiza nawo banja lathu. Kunalibe ntchito, koma ndinapeza njira yosakira akalulu omwe analiko ambiri ku Australia. Motero mbali ina yaikulu yomwe ndinkathandizira inali kupezera banja lathu nyama ya akalulu omwe ndinkapha nthaŵi ndi nthaŵi.

Pamene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inkayamba mu 1939, ndinali nditapeza ntchito pa kampani ya sitima ndi basi ya mu mzinda wa Melbourne. Panali anthu pafupifupi 700 omwe ankagwira ntchito m’mashifiti m’basi, ndipo shifiti iliyonse ndikapita kuntchito ndinkakumana ndi dalaivala kapena wodulitsa matiki wachilendo. Nthaŵi zambiri ndinkawafunsa kuti, “Kodi mumapembedza kuti?” ndi kuwapempha kuti andifotokozere zomwe amakhulupirira. Munthu amene ankandiyankha zogwira mtima anali wa Mboni za Yehova basi. Anandifotokozera uthenga wa m’Baibulo wa dziko lapansi la paradaiso, momwe anthu oopa Mulungu adzakhale kwa muyaya.​—Salmo 37:29.

 Panthaŵiyi n’kuti amayi nawonso atadziŵana ndi Mboni za Yehova. Nthaŵi zambiri, ndikabwera kuchoka kuntchito shifiti yamadzulo, ndinkapeza chakudya changa ataika pamodzi ndi kope la magazini a Consolation (omwe tsopano akutchedwa kuti Galamukani!). Ndinkasangalala ndi zomwe ndinkaŵerenga. Patapita nthaŵi ndithu, ndinadziŵa kuti chimenechi chinali chipembedzo choona, ndipo ndinayamba kumasonkhana nawo kaŵirikaŵiri ndi kubatizidwa mu May 1940.

Ku Melbourne kunali nyumba ya apainiya, komwe kunkakhala atumiki a nthaŵi zonse a Mboni za Yehova pafupifupi 25. Ndinapita kukakhala nawo pamodzi. Tsiku ndi tsiku ndinkamvetsera nkhani za zinthu zosangalatsa zimene akumana nazo mu utumiki wakumunda, ndipo ndinayamba kulakalaka kuti nanenso ndikhale mpainiya. M’kupita kwa nthaŵi, ndinalembetsa utumiki wa upainiya. Anandivomera ndipo anandiitana kukatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Australia. Motero ndinakhala mmodzi wa a m’banja la Beteli.

Kumangidwa ndi Kuletsedwa kwa Ntchito

Ina mwa ntchito zomwe ndinkagwira pa Beteli inali yogwiritsira ntchito macheka. Tinkadula mitengo yootchera makala kuti tipange gasi. Galimoto za panthambi zinkayendera gasi ameneyu chifukwa chakuti mafuta ogulitsa ankasoŵa chifukwa cha nkhondo. Pamachekapo tinalipo anthu 12, ndipo tonsefe tinali oti tingatengedwe kupita ku usilikali. Patangopita nthaŵi pang’ono anatilamula kuti tikhale m’ndende miyezi isanu ndi umodzi chifukwa chokana zausilikali pazifukwa za m’Baibulo. (Yesaya 2:4) Anatitumiza ku munda wa ndende kuti tikagwire ukaidi. Kodi anatipatsa ntchito yanji? Zinali zodabwitsa kwambiri kuti anatipatsa ntchito yodula mitengo, ntchito yomwe tinaphunzira pa Beteli!

Tinkagwira bwino kwambiri ntchitoyo moti mkulu woyang’anira ndendeyo anatilola kukhala ndi Baibulo ndiponso mabuku athu ofotokoza Baibulo. Anachita izi ngakhale kuti panali malamulo okhwima oletsa kuti tisamakhale ndi zimenezi. Panthaŵiyi m’pamene ndinaphunzira mfundo yofunika kwambiri pa kukhala ndi anthu. Pamene ndinkagwira ntchito pa Beteli, panali mbale wina amene sindinkatha kugwirizana naye. Makhalidwe athu anali osiyana kwambiri. Komano, mukuganiza kuti anandiika kuti ndizikhala ndi ndani m’ndendemo? Inde, mbale yemwe uja. Tsopano tinali ndi nthaŵi yoti tidziŵane, ndipo zinachititsa kuti tikhale ogwirizana kwambiri ndipo ubwenzi wathu unali wokhalitsa.

M’kupita kwa nthaŵi, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa ku Australia. Ndalama zonse zinalandidwa, ndipo abale a pa Beteli anali ndi vuto la zachuma. Nthaŵi inayake, mmodzi wa abale a pa Beteli anabwera kwa ine n’kunena kuti: “Dick, ndikufuna kupita kutauni kukalalikira, koma ndilibe nsapato, ndili ndi nsapato zogwirira ntchito basi.” Ndinam’thandiza, ndipo ananyamuka kupita kutauni atavala nsapato zanga.

Kenako tinamva kuti am’manga ndi kum’tsekera m’ndende chifukwa cholalikira. Sindikanachitira mwina kusiyapo kumulembera kakalata kakuti: “Pepa bwanawe chifukwa cha zimene zakuchitikira. Mwayi kuti sindinagwidwe ndine koma nsapato zanga.” Koma patapita nthaŵi pang’ono nanenso anandimanga ndi kunditsekera m’ndende kachiŵiri chifukwa chosafuna kuloŵerera nawo pa zinthu za dziko. Nditamasulidwa, anandipatsa ntchito yoyang’anira munda womwe tinkalimamo chakudya cha banja la Beteli. Panthaŵiyi tinali titapambana mlandu ku khoti, ndipo anachotsa chiletso cha ntchito ya Mboni za Yehova.

Kukwatira Mlaliki Wachangu

Ndikugwira ntchito pa famuyo, ndinayamba kuganizira kwambiri za ukwati ndipo maso anga anadyerera mlongo wina wachitsikana amene anali mpainiya ndipo dzina lake linali Coralie Clogan. Agogo aakazi a Coralie ndiwo anali munthu woyamba m’banja mwawo kukonda uthenga wa Baibulo. Pamene ankamwalira, iwo anali atauza amayi ake a Coralie, a Vera, kuti: “Mulere ana anu moti azikonda ndi kutumikira Mulungu, ndipo tsiku lina tidzakumana m’Paradaiso padziko lapansi.” Mawu ameneŵa anayamba kukhala atanthauzo patapita nthaŵi pamene mpainiya wina anafika pa khomo la a Vera ali ndi kabuku kakuti Millions Now Living Will Never Die (Mamiliyoni Okhala ndi Moyo Tsopano Sadzafa Konse). A Vera anamvetsa kuchokera m’kabuku kameneko kuti cholinga cha Mulungu chinali  choti anthu asangalale ndi moyo padziko lapansi la paradaiso. (Chivumbulutso 21:4) Anabatizidwa chakumayambiriro kwa m’ma 1930, ndipo monga momwe amayi awo anawalangizira, a Vera anathandiza ana awo aakazi atatu, Lucy, Jean, ndi Coralie, kuti azikonda Mulungu. Komabe, bambo ake a Coralie ankatsutsa kwambiri zochita zachipembedzo za banja lawo, mofanana ndi mmene Yesu anachenjezera kuti zingachitike m’mabanja.​—Mateyu 10:34-36.

Banja la a Clogan linali banja lokonda zoimbaimba; mwana aliyense ankatha kuimba chipangizo chinachake choimbira. Coralie ankaimba vayolini, ndipo mu 1939, ali ndi zaka 15, analandira dipuloma ya zoimbaimba. Kuyambika kwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse kunapangitsa Coralie kuganizira mozama za tsogolo lake. Inali nthaŵi yoti asankhe zochita pa moyo wake. Anali ndi mwayi wogwira ntchito ya zoimbaimba ndipo anali atamuitanapo kale kuti azikaimba m’gulu la oimba la Melbourne Symphony Orchestra. Komanso panali mwayi woti nthaŵi yake yonse azithera pa ntchito yaikulu kwambiri yolalikira uthenga wa Ufumu. Atadya mutu, Coralie ndi akulu ake aŵiri anabatizidwa mu 1940 ndipo anakonzekera kuyamba ntchito ya nthaŵi zonse yolalikira.

Coralie atangotsimikiza kumene kuti achite utumiki wa nthaŵi zonse anapezedwa ndi mbale wina yemwe anali ndi udindo waukulu ku nthambi ya Australia. Anali Lloyd Barry, yemwe pambuyo pake anadzatumikira m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Anali atangokamba kumene nkhani ku Melbourne ndipo anauza Coralie kuti: “Ndikubwerera ku Beteli. Bwanji osatsagana nane pa sitima ndi kukakhala nawo m’banja la Beteli?” Anavomera mosanyinyirika.

Coralie pamodzi ndi alongo ena a banja la Beteli anathandiza kwambiri kuti m’zaka zankhondo pamene ntchito yathu inali yoletsedwa, abale mu Australia azipeza mabuku ofotokoza Baibulo. Kwenikweni anachita zambiri pa kusindikiza mabuku, moyang’aniridwa ndi Mbale Malcolm Vale. Mabuku a The New World ndi Children ankasindikizidwa ndi kumatidwa, ndipo palibe kope ndi limodzi lomwe la Nsanja ya Olonda lomwe abale anaphonya m’zaka zoposa ziŵiri za chiletsocho.

Ofesi yosindikizira mabuku anaisamutsa maulendo 15 n’cholinga choti apolisi asaitulukire. Nthaŵi inayake, mabuku ofotokoza Baibulo ankasindikizidwira m’chipinda cha pansi pa nyumba ina momwe ankasindikizamonso zinthu zina kuti anthu asadziŵe zomwe zinali kuchitika. Pakakhala choopsa chilichonse, mlongo yemwe ankakhala polandirira alendo ankadinikiza batani lomwe linkaliza belu pansi kotero kuti alongo pansipo athe kubisa mabuku munthu wina aliyense asanayambe kuchita chipikisheni.

Nthaŵi ina, chipikisheni chili m’kati, alongo ena anachita mantha kwambiri atazindikira kuti kope lina la Nsanja ya Olonda linali patebulo pomwe aliyense amaliona. Wapolisi analoŵa, n’kuika chikwama chake pa Nsanja ya Olondayo n’kupitiriza kuchita chipikisheni. Atalephera kupeza chilichonse, ananyamula chikwama chakecho n’kutuluka!

Chiletso chitachotsedwa ndipo malo a nthambi atawabwezera kwa abale, ambiri mwa abalewo anapatsidwa mwayi wokachita upainiya wapadera. Nthaŵi imeneyo ndi pamene Coralie anadzipereka kupita ku Glen Innes. Titakwatirana pa January 1, 1948, ndinapita kukakhala naye limodzi kumeneko. Pamene tinkachokako, n’kuti kutakhazikika mpingo umene unali kukulirakulira.

Titachoka ku Glen Innes tinapita kukatumikira ku Rockhampton, koma kumeneko malo ogona anali osoŵa kwambiri. Motero tinautsa tenti m’munda wa wokondwerera wina. Tinakhala mu tentiyo kwa miyezi isanu ndi inayi. Mwinanso tikanakhalamo nthaŵi yotalikirapo, koma dzinja litafika,  mphepo ndi mvula yamkuntho zinang’amba tentiyo n’kuikokolola.

Kutitumiza Kukagwira Ntchito ku Dziko Lina

Tili ku Rockhampton, tinaitanidwa kukakhala nawo m’kalasi la nambala 19 la Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo yokonzekeretsa umishonale. Ndipo ndi mmenemu momwe anatitumizira ku dziko lomwe panthaŵiyo linkatchedwa South-West Africa, titamaliza maphunzirowo mu 1952.

Atsogoleri a Matchalitchi Achikristu sanazengereze, anasonyeza mmene ankamvera chifukwa cha ntchito yathu yaumishonale. Lamlungu lililonse kwa milungu isanu ndi umodzi yotsatizana ankapita pagome kukachenjeza mipingo yawo za ife. Ankauza anthu kuti asamatiloŵetse m’nyumba ndiponso asamatilole kuŵerenga Baibulo, chifukwa chakuti zingathe kuwasokoneza. M’dera lina tinagaŵira mabuku ambiri ndithu, koma mbusa wina ankatitsatira nyumba ndi nyumba n’kumatenga mabukuwo. Tsiku lina tinacheza ndi mbusayo m’chipinda chake choŵerengera ndipo tinaona kuti ali ndi kamulu ndithu ka mabuku athu.

Sipanatenge nthaŵi yaitali kuti nawonso akuluakulu a boma m’deralo ayambe kuda nkhaŵa ndi ntchito yathu. Ankatikayikira kuti mwina tikugwirizana ndi gulu la Chikomyunizimu, zomwe mosakayikira anachititsa ndi atsogolera a matchalitchi. Motero anatidinditsa chala pa mapepala, ndipo anthu ena omwe tinapita kunyumba kwawo anawapanikiza ndi mafunso pofufuza za nkhaniyo. Ngakhale kuti panali chitsutso chonsechi, chiŵerengero cha anthu ofika pamisonkhano chinapitiriza kukula.

Chibwerereni kuno, tinkalakalaka titafalitsa uthenga wa Baibulo kwa anthu a mitundu ya Ovambo, Herero, ndi Nama, omwe ndi nzika za kuno. Komabe kuti zimenezi zichitike sinali ntchito yamaseŵera. Nthaŵi imeneyo South-West Africa ankalamulidwa ndi boma la tsankho la South Africa. Popeza ndife azungu, sankatilola kukalalikira kumadera a anthu akuda popanda chilolezo cha boma. Tinakhala tikupempha chilolezo nthaŵi zambirimbiri, koma akuluakulu a boma ankakana kutipatsa.

Titatha zaka ziŵiri tikutumikira kuno tinadzidzimuka kuona kuti Coralie anali woyembekezera. Mu October 1955, mwana wathu wamkazi, Charlotte, anabadwa. Ngakhale kuti sitikanapitirizanso kukhala amishonale, ndinapeza ntchito ya ganyu ndipo ndinapitiriza upainiya kwa kanthaŵi ndithu.

Mapemphero Athu Ayankhidwa

Mu 1960 tinakumana ndi vuto lina. Coralie analandira kalata yofotokoza kuti amayi ake adwala kwambiri moti ngati Coralie sapita kumudzi, mwina sadzawaonanso. Motero tinaganiza zochoka mu South-West Africa ndi kubwerera ku Australia. Ndiyeno zinachitika kuti, mlungu womwe tinkanyamukawo, akuluakulu a boma anandipatsa chilolezo choloŵa m’dera la anthu akuda la Katutura. Kodi tikanatani pamenepa? Kodi tikanabweza  chilolezocho pambuyo pochivutikira zaka zisanu ndi ziŵiri kuti tichipeze? Zinali zosavuta kulingalira kuti ena adzapitiriza pamene ife tasiyira. Koma kodi limeneli silinali dalitso lochokera kwa Yehova, kuyankha mapemphero athu?

Mwamsangamsanga ndinadziŵa zochita. Ndinaganiza kuti ndisachoke poopa kuti ngati tonse titapita ku Australia, tisokoneza zomwe tinkachita zofuna kuti tikhale nzika za dziko lino. Tsiku lotsatira ndinakafafanizitsa dzina langa pa mndandanda wa anthu ofuna kukwera sitima ya panyanja ndipo ndinatumiza Coralie ndi Charlotte ku Australia komwe anakakhala nthaŵi yaitali.

Ali ku Australia, ndinayamba kulalikira kwa anthu okhala m’dera la anthu akuda. Anthu anasonyeza chidwi kwambiri. Pamene Coralie ndi Charlotte ankabwerera, n’kuti anthu angapo ochokera ku dera la anthu akuda akubwera kumisonkhano.

Panthaŵiyi, ndinali ndi galimoto yakale yomwe ndinkatengera atsopano kupita nawo ku misonkhano. Ndinkayenda maulendo anayi kapena asanu msonkhano uliwonse ndipo ndinkatenga anthu asanu ndi aŵiri, asanu ndi atatu, kapena asanu ndi anayi ulendo uliwonse. Munthu womaliza akamatsika m’galimotoyo, Coralie ankandifunsa mocheza, amvekere: “Kudakali anthu angati kunsi kwa mpandoku?”

Kuti ntchito yathu yolalikira ikhale yogwira mtima kwambiri, tinafunika kukhala ndi mabuku m’zinenero za nzika zadziko lino. Motero unali mwayi wanga wapadera kukonza zoti thirakiti lakuti Moyo m’Dziko Latsopano litembenuzidwe m’zinenero zinayi zakuno. M’zinenero za Chiherero, Chinama, Chindonga, ndi Chikwanyama. Omwe anatembenuza anali anthu ophunzira omwe tinkaphunzira nawo Baibulo, koma ndinafunika kugwira nawo ntchitoyo pamodzi pofuna kuonetsetsa kuti chiganizo chilichonse chatembenuzidwa molondola. Chinama chili ndi mawu ochepa. Mwachitsanzo, ndinali kuyesa kufotokoza mfundo yakuti: “Pachiyambi Adamu anali munthu wangwiro.” Yemwe ankatembenuzayo anakanda m’mutu n’kunena kuti waiwala mawu a “wangwiro” pa Chinama. “Eya, ndakumbukira,” iye anatero. “Pachiyambi Adamu anali ngati pichesi lakupsa.”

Kusangalala ndi Dziko Limene Anatitumizako

Papita zaka ngati 49 tsopano kuchokera pamene tinafika koyamba m’dziko lino, lomwe tsopano likutchedwa Namibia. M’posafunikanso kuti munthu achite kulandira chilolezo kuti akaloŵe m’madera omwe mukukhala anthu akuda. Dziko la Namibia likulamulidwa ndi boma latsopano losatsatira malamulo a tsankho. Masiku ano, ku Windhoek tili ndi mipingo inayi ikuluikulu yomwe imasonkhana m’Nyumba za Ufumu zabwino kwambiri.

Nthaŵi zambiri takhala tikulingalira mawu omwe tinamva ku Gileadi akuti: “Kapangeni dziko lomwe mukukatumikirako kukhala kwanu.” Malinga ndi mmene Yehova wayendetsera zinthu, tikukhulupirira kuti chinali chifuniro chake kuti dziko lachilendo lino likhale kwathu. Tikuwakonda abale, pamodzi ndi chikhalidwe chawo chosiyanasiyana chochititsa chidwi. Taseka nawo akakhala pachisangalalo ndipo talira nawo akakhala pachisoni. Ena mwa atsopano omwe ankathithikana m’galimoto yanga ndi kupita nawo kumisonkhano tsopano ndi mizati m’mipingo mwawo. Pamene tinkafika m’dziko lalikulu lino mu 1953, munali ofalitsa a komwekuno osakwana khumi omwe ankalalikira uthenga wabwino. Kuchokera pamenepo pomwe tinali anthu ochepa kwambiri, chiŵerengero chathu chakwera kufika pa anthu oposa 1,200. Mogwirizana ndi lonjezo lake, Yehova wakulitsa pamene ife ndi anthu ena ‘tinaoka ndi kuthirira.’​—1 Akorinto 3:6.

Tikamayanga’ana m’mbuyo zaka zambiri za utumiki, kuyambira ku Australia ndipo tsopano tikutumikira kuno ku Namibia, ine ndi Coralie timasangalala kwambiri. Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova apitiriza kutipatsa nyonga yoti tichite chifuno chake tsopano lino ndi m’tsogolo ndipo timapempherera zimenezo.

[Chithunzi pamasamba 26, 27]

Kusamukira ku dera loti tikatumikire ku Rockhampton, ku Australia

[Chithunzi patsamba 27]

Tili padoko paulendo wopita ku Sukulu ya Gileadi

[Chithunzi patsamba 28]

Tikusangalala kwambiri kulalikira mu Namibia